Miyambo 2:1-22

2  Mwana wanga, ukamvera mawu anga+ ndi kusunga malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali,+  ukamvetsera nzeru ndi khutu lako,+ ukaika mtima wako pa kuzindikira,+  komanso ukaitana kumvetsa zinthu+ ndi kufuulira kuzindikira,+  ukamazifunafuna ngati siliva,+ ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+  udzamvetsa tanthauzo la kuopa+ Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu.+  Pakuti Yehova amapereka nzeru.+ Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.+  Anthu owongoka mtima, iye amawasungira nzeru zopindulitsa.+ Kwa anthu oyenda ndi mtima wosagawanika, iye amakhala chishango+  mwa kuyang’anitsitsa njira zachiweruzo,+ ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+  Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.+ 10  Nzeru zikalowa mumtima mwako,+ ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa m’moyo wako,+ 11  kuganiza bwino kudzakuyang’anira,+ ndipo kuzindikira kudzakuteteza,+ 12  kuti kukupulumutse kunjira yoipa,+ ndiponso kwa munthu wonena zinthu zopotoka,+ 13  komanso kwa anthu amene amasiya njira zowongoka kuti ayende m’njira za mdima.+ 14  Kudzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala kuchita zoipa,+ amene amakondwera ndi zinthu zoipa ndi zopotoka,+ 15  amene njira zawo ndi zokhota ndiponso amene ali achinyengo m’zochita zawo zonse.+ 16  Kudzakupulumutsa kwa mkazi wachilendo, mkazi wochokera kwina+ wolankhula mwaukathyali,+ 17  amene wasiya mnzake wapamtima wa pachitsikana chake+ ndiponso amene waiwala pangano limene anapangana ndi Mulungu wake.+ 18  Pakuti nyumba yake imatsikira kumanda ndipo njira zake zimatsikira kwa akufa.+ 19  Onse ogona naye sadzabwerera ndipo iwo sadzapezanso njira za amoyo.+ 20  Cholinga cha zonsezi n’chakuti uziyenda m’njira ya anthu abwino+ ndi kuti uzisunga njira za anthu olungama.+ 21  Pakuti owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi,+ ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo.+ 22  Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi+ ndipo achinyengo adzazulidwamo.+

Mawu a M'munsi