Miyambo 29:1-27
29 Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+
2 Olungama akachuluka, anthu amasangalala,+ koma aliyense woipa akayamba kulamulira, anthu amabuula.+
3 Munthu wokonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+ koma woyenda ndi mahule amawononga zinthu zamtengo wapatali.+
4 Pochita zinthu zachilungamo, mfumu imachititsa dziko kulimba,+ koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.+
5 Mwamuna wamphamvu amene amanena zabwino za mnzake mokokomeza,+ akuyalira ukonde mapazi ake.+
6 Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+ koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+
7 Wolungama amaganizira za mlandu wa anthu onyozeka.+ Woipa saganizira zimenezo.+
8 Anthu olankhula modzitama amabutsa mkwiyo wa mzinda,+ koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+
9 Munthu wanzeru akakhala pa mlandu ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso n’kumaseka, ndipo munthu wanzeruyo sapeza mpumulo.+
10 Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi aliyense wopanda cholakwa,+ koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.+
11 Wopusa amatulutsa mkwiyo* wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.+
12 Mtsogoleri akamamvera mabodza, onse omutumikira adzakhala oipa.+
13 Munthu wosauka ndiponso munthu wozunza ena n’chimodzimodzi,+ koma Yehova amawalitsa maso a onsewa.+
14 Mfumu ikamaweruza anthu onyozeka mwachilungamo,+ mpando wake wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.+
15 Chikwapu ndi chidzudzulo n’zimene zimapereka nzeru,+ koma mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.+
16 Oipa akachuluka, machimo amachuluka, koma olungama adzawaona oipawo akugwa.+
17 Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumulo ndiponso adzasangalatsa kwambiri moyo wako.+
18 Popanda kutsogozedwa ndi Mulungu, anthu amatayirira,+ koma odala ndi amene amasunga malamulo.+
19 Wantchito salola kusintha ndi mawu okha,+ chifukwa amamvetsa koma satsatira.+
20 Kodi waona munthu wopupuluma m’mawu ake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.+
21 Ngati munthu akusasatitsa* wantchito wake kuyambira ali mwana, akadzakula adzakhala wosayamika.
22 Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano,+ ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+
23 Kudzikuza kwa munthu wochokera kufumbi kudzamutsitsa,+ koma wa mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+
24 Wochita ubwenzi ndi mbala akudana ndi moyo wake.+ Iye angamve lumbiro lokhudza temberero, koma osakanena chilichonse.+
25 Kuopa anthu n’kumene kumatchera msampha,+ koma wokhulupirira Yehova adzatetezedwa.+
26 Anthu ambiri amafuna kuonana ndi mtsogoleri,+ koma chiweruzo cha munthu chimachokera kwa Yehova.+
27 Munthu wopanda chilungamo amakhala wonyansa kwa anthu olungama,+ ndipo munthu wowongoka m’njira yake amakhala wonyansa kwa munthu woipa.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mzimu.”
^ Munthu wosasatitsidwa ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.