Miyambo 16:1-33
16 Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake,+ koma kwa Yehova n’kumene kumachokera yankho la palilime lake.+
2 Njira zonse za munthu zimaoneka zoyera m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza zolinga zake.+
3 Pereka ntchito zako kwa Yehova,+ ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.+
4 Yehova anapanga chilichonse n’cholinga,+ ndipo ngakhale woipa anamusungira tsiku loipa.+
5 Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.+ Ngakhale anthu atagwirana manja, munthu sangapewe chilango.+
6 Cholakwa chimaphimbika ndi kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi,+ ndipo chifukwa choopa Yehova munthu amapatuka pa choipa.+
7 Yehova akasangalala ndi njira za munthu,+ amachititsa ngakhale adani a munthuyo kukhala naye pa mtendere.+
8 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa mwachilungamo+ kuposa kukhala ndi zinthu zambiri koma mopanda chilungamo.+
9 Munthu angaganize za njira zake mumtima mwake,+ koma Yehova ndiye amawongolera mayendedwe ake.+
10 Chigamulo chochokera kwa Mulungu chizikhala palilime la mfumu poweruza milandu.+ Pakamwa pake pazikhala pokhulupirika.+
11 Muyezo wachilungamo ndiponso masikelo ndi za Yehova.+ Miyala yonse ya m’thumba loyezera kulemera kwa zinthu ndiyo ntchito zake.+
12 Kuchita zinthu zoipa kumanyansa mafumu,+ chifukwa mpando wachifumu umakhazikika ndi chilungamo.+
13 Milomo yolungama imasangalatsa mfumu yaikulu,+ ndipo mfumuyo imakonda munthu wolankhula zinthu zowongoka.+
14 Mkwiyo wa mfumu umatanthauza amithenga a imfa,+ koma munthu wanzeru ndi amene amauziziritsa.+
15 Nkhope ya mfumu ikawala, zimatanthauza moyo.+ Ndipo mafuno ake abwino ali ngati mtambo wa mvula yomalizira.+
16 Kupeza nzeru n’kwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+ Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+
17 Kupewa zoipa ndiko njira ya anthu owongoka mtima.+ Munthu amene amateteza njira yake, amasunga moyo wake.+
18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+
19 Kuli bwino kukhala wodzichepetsa limodzi ndi anthu ofatsa,+ kusiyana n’kugawana katundu wolanda ndi anthu odzikuza.+
20 Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino,+ ndipo wodala ndi munthu amene amakhulupirira Yehova.+
21 Munthu wanzeru mumtima mwake adzatchedwa wozindikira,+ ndipo munthu wolankhula zabwino amakopa ena ndi mawu a pakamwa pake.+
22 Kuzindikira kumakhala ngati chitsime cha moyo kwa ozindikirawo,+ ndipo malangizo* a anthu opusa ndi uchitsiru.+
23 Mtima wa munthu wanzeru umamuchititsa kuti asonyeze kuzindikira ndi pakamwa pake,+ ndipo umachititsa milomo yake kutulutsa mawu okopa.+
24 Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.+ Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+
25 Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+
26 Munthu wakhama amadzigwirira yekha ntchito+ chifukwa chakuti pakamwa pake pamamukakamiza kwambiri.+
27 Munthu wopanda pake amafukula zinthu zoipa,+ ndipo pakamwa pake pamakhala mawu okhala ngati makala amoto.+
28 Kazitape amangokhalira kuyambitsa mikangano,+ ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.+
29 Munthu wachiwawa amakopa mnzake,+ ndipo amam’chititsa kuti ayende m’njira yoipa.+
30 Iye amatsinzinira ndi maso ake pokonza ziwembu.+ Amalumirira mano, ndipo amakwanitsadi kuchita chiwembu.
31 Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero+ zikapezeka m’njira yachilungamo.+
32 Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu,+ ndipo munthu wolamulira mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.+
33 Maere amaponyedwa pamwendo,+ koma zonse zimene maerewo amasonyeza zimachokera kwa Yehova.+