Miyambo 5:1-23
5 Mwana wanga, mvetsera nzeru zanga.+ Tchera makutu ako ku zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kuzindikira,+
2 kuti uteteze kuganiza bwino,+ ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+
3 Pakuti milomo ya mkazi wachilendo imakha uchi ngati chisa cha njuchi+ ndipo m’kamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+
4 Koma zotsatirapo zochokera kwa iye n’zowawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+ N’zakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+
5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.+ Miyendo yake imalowera ku Manda.+
6 Iye saganizira njira ya moyo.+ Amangoyendayenda panjira zake osadziwa kumene akupita.+
7 Tsopano ananu ndimvereni,+ ndipo musapatuke pa mawu otuluka m’kamwa mwanga.+
8 Njira yako ikhale kutali ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+
9 kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+ kapena kupereka zaka zako ku zinthu zankhanza.+
10 Ndiponso kuti alendo asakhute mphamvu zako,+ kuti zinthu zimene unazipeza movutikira* zisakhale m’nyumba ya mlendo,+
11 komanso kuti usadzabuule m’tsogolo+ mnofu ndi thupi lako zikadzafika ku mapeto kwake.+
12 Pa nthawiyo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine,+ ndipo mtima wanga sunkavomereza kudzudzula.+
13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,+ ndipo sindinatchere khutu kwa aphunzitsi anga.+
14 N’chifukwa chake mosayembekezeka ndinagwera m’zinthu zoipa zamtundu uliwonse,+ ndipo ndinachita manyazi pamaso pa mpingo wonse.”+
15 Imwa madzi ochokera m’chitsime chako, komanso madzi oyenderera kuchokera pakati pa chitsime chako.+
16 Kodi akasupe ako amwazike panja,+ ndipo mitsinje yako yamadzi imwazike m’mabwalo a mumzinda?
17 Zimenezi zikhale zako zokha osatinso za alendo amene ali nawe.+
18 Kasupe wa madzi ako akhale wodalitsidwa,+ ndipo usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.+
19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yokondedwa ndiponso ngati mbuzi yokongola ya m’mapiri.+ Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse.+ Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.+
20 Chotero pali chifukwa chanji choti usangalalire ndi mkazi wachilendo mwana wanga, kapena choti ukumbatirire chifuwa cha mkazi wina?+
21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+
22 Woipa adzagwidwa ndi zolakwa zake zomwe,+ ndipo adzamangidwa m’zingwe za tchimo lake lomwe.+
23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,+ ndiponso chifukwa chakuti amasocheretsedwa ndi zopusa zake zochuluka.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “zimene unazipeza ukumva kupweteka.”