Miyambo 28:1-28
28 Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,+ koma olungama ali ngati mkango wamphamvu umene umakhala wolimba mtima.+
2 Anthu okhala m’dziko akamachimwa pamakhala akalonga ambiri otsatizanatsatizana,+ koma chifukwa cha munthu wozindikira, wodziwa zinthu zoyenera kuchita, kalonga amakhala kwa nthawi yaitali.+
3 Mwamuna wamphamvu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+ ali ngati mvula imene imakokolola zinthu moti sipakhalanso chakudya.
4 Anthu osiya chilamulo akamatamanda munthu woipa,+ anthu amene amasunga chilamulo amawaukira.+
5 Anthu okonda kuchita zoipa sangamvetse chilungamo, koma amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.+
6 Munthu wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika, ali bwino kuposa munthu aliyense woyenda m’njira zokhota, ngakhale ali wolemera.+
7 Mwana womvetsa zinthu amasunga malamulo,+ koma wochita ubwenzi ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+
8 Munthu amene amachulukitsa zinthu zamtengo wapatali kuchokera ku chiwongoladzanja ndi katapira,*+ amangosungira zinthuzo munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+
9 Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo,+ ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+
10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima+ kuti ayende m’njira yoipa, adzagwera m’dzenje lake lomwe.+ Koma anthu osalakwa adzapeza zabwino.+
11 Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru m’maso mwake,+ koma munthu wonyozeka amene ali wozindikira zinthu amam’fufuza n’kudziwa zoona zake.+
12 Anthu olungama akamasangalala+ zimakhala bwino kwambiri, koma anthu oipa akamalamulira, munthu amadzisintha maonekedwe.+
13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+
14 Wodala ndi munthu amene amaopa Mulungu nthawi zonse,+ koma woumitsa mtima wake adzagwera m’tsoka.+
15 Mtsogoleri woipa wolamulira anthu onyozeka ali ngati mkango wobangula ndiponso chimbalangondo chimene chikubwera kudzakuluma.+
16 Mtsogoleri amene ali wosazindikira kwenikweni amakhalanso wakatangale kwambiri,+ koma munthu wodana ndi phindu lachinyengo+ adzachulukitsa masiku ake.
17 Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse.
18 Woyenda mosalakwa adzapulumutsidwa,+ koma woyenda m’njira zokhota adzagwa mwadzidzidzi.+
19 Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+ ndipo amene amafunafuna zinthu zopanda phindu adzakhala ndi umphawi waukulu.+
20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
21 Si bwino kukondera.+ Si bwinonso kuti mwamuna wamphamvu achimwe chifukwa cha kachidutswa ka mkate.
22 Munthu wanjiru amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali,+ koma sadziwa kuti umphawi udzamugwera.
23 Wodzudzula munthu,+ patsogolo pake adzakondedwa kwambiri kuposa amene amakokomeza ndi lilime lake ponena zinthu zabwino za wina.
24 Wobera bambo ake ndi mayi ake+ n’kumanena kuti: “Si kulakwa,”+ amakhala mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.
25 Munthu wonyada amayambitsa mikangano,+ koma wodalira Yehova adzanenepa.+
26 Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa,+ koma woyenda mwanzeru ndi amene adzapulumuke.+
27 Wopatsa zinthu munthu wosauka sadzasowa kanthu,+ koma wophimba maso ake adzapeza matemberero ambiri.+
28 Oipa akamalamulira, munthu amadzibisa.+ Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+