Miyambo 24:1-34
24 Usamasirire anthu oipa,+ ndipo usamasonyeze kuti ukusirira kukhala pagulu lawo,+
2 chifukwa mtima wawo umangokhalira kuganizira zolanda zinthu za ena, ndipo milomo yawo imangokhalira kunena zobweretsera ena mavuto.+
3 Nzeru zimamanga banja la munthu,+ ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.+
4 Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda zamkati mwa nyumba zidzaze ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+
5 Munthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwanzeru ndiye mwamuna wamphamvu,+ ndipo munthu wodziwa zinthu amachulukitsa mphamvu zake.+
6 Iweyo udzatha kumenya nkhondo yako potsatira malangizo anzeru,+ ndipo pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+
7 Kwa munthu wopusa, nzeru zenizeni n’chinthu chapatali.+ Iye satsegula pakamwa pake pachipata cha mzinda.
8 Aliyense wokonzera anzake ziwembu adzatchedwa katswiri wa maganizo oipa.+
9 Khalidwe lotayirira lobwera chifukwa cha kupusa limakhala tchimo,+ ndipo munthu wonyoza, anthu amanyansidwa naye.+
10 Ukafooka pa tsiku la masautso,+ mphamvu zako zidzakhala zochepa.
11 Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe, ndipo amene akudzandira popita ku imfa, chonde uwabweze.+
12 Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo?+ Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+
13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino, ndipo uchi wotsekemera wochokera pazisa za njuchi uuike m’kamwa mwako.+
14 M’njira yomweyo, dziwa nzeru kuti upindule.+ Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+
15 Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pamalo ake okhala.+ Usamasakaze malo ake okhala,+
16 pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.+ Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa.+
17 Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere,+
18 kuti Yehova angaone ndipo zingamuipire m’maso mwake n’kuchotsa mkwiyo wake pamdani wakoyo.+
19 Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa. Usamasirire anthu oipa,+
20 pakuti aliyense woipa alibe tsogolo,+ ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+
21 Mwana wanga uziopa Yehova ndiponso mfumu.+ Usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+
22 pakuti tsoka lawo lidzagwa mwadzidzidzi,+ ndipo ndani angadziwe za kufafanizika kwa anthu ofuna kuti zinthu zisinthe?+
23 Mawu awanso akupita kwa anthu anzeru:+ Si bwino kukondera poweruza.+
24 Munthu amene amauza woipa kuti: “Ndiwe wolungama,”+ anthu adzamutemberera, ndipo mitundu ya anthu idzamutsutsa.
25 Koma anthu omudzudzula zinthu zidzawayendera bwino,+ ndipo adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+
26 Woyankha mosapita m’mbali adzapsompsona milomo ya anthu.+
27 Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo konza munda wako.+ Ukatero ukamange banja lako.
28 Usakhale mboni yotsutsana ndi mnzako popanda umboni,+ chifukwa ukhoza kukhala wopusa ndi milomo yako.+
29 Usanene kuti: “Ndim’chitira zimene iye anandichitira.+ Aliyense ndizim’bwezera mogwirizana ndi zimene anachita.”+
30 Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi+ ndiponso pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+
31 Ndipo ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.+ Zitsamba zoyabwa zinali paliponse m’mundamo komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+
32 Choncho ine nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,+ ndipo ndinaphunzirapo* kuti:+
33 Ukati, “Ndigoneko pang’ono, ndibeko katulo pang’ono, ndipindeko manja pang’ono pogona,”+
34 umphawi wako ndithu udzabwera ngati wachifwamba ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+