2 Samueli 8:1-18
8 Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisiti+ ndipo anawalanda mzinda wa Metege-ama.
2 Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndipo anawagoneka pansi nʼkuyamba kuwayeza ndi chingwe. Ankati akayeza zingwe ziwiri, anthu amenewo ankawapha ndipo akayeza chingwe chimodzi, amenewo ankawasiya ndi moyo.+ Amowabuwo anakhala atumiki a Davide ndipo ankapereka msonkho kwa iye.+
3 Davide anagonjetsa Hadadezeri, mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba,+ pamene Hadadezeriyo ankapita kumtsinje wa Firate+ kukabwezeretsa ulamuliro wake.
4 Davide anagwira amuna 1,700 okwera pamahatchi ndi asilikali 20,000 oyenda pansi a Hadadezeri. Kenako Davide anapundula* mahatchi onse a magaleta nʼkungosiya mahatchi 100.+
5 Asiriya a ku Damasiko+ atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anapha Asiriya 22,000.+
6 Kenako Davide anamanga midzi ya asilikali mʼdera la Asiriya a ku Damasiko ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti ankapereka msonkho kwa iye. Yehova ankathandiza Davide kuti apambane kulikonse kumene wapita.+
7 Komanso Davide anatenga zishango zozungulira zagolide za atumiki a Hadadezeri ndipo anapita nazo ku Yerusalemu.+
8 Mfumu Davide anatenga kopa wambiri ku Beta ndi ku Berota, mizinda ya Hadadezeri.
9 Tsopano Toi, mfumu ya Hamati,+ anamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri.+
10 Choncho Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndiponso kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri nʼkumugonjetsa. (Chifukwa Hadadezeri ankakonda kumenyana ndi Toi.) Popita kwa Davide, Yoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zakopa.
11 Mfumu Davide anapereka zinthu zimenezi kwa Yehova pamodzi ndi siliva komanso golide wochokera ku mitundu yonse imene anagonjetsa.+
12 Mitundu yake inali Asiriya, Amowabu,+ Aamoni, Afilisiti+ ndi Aamaleki.+ Anaperekanso zinthu zimene anatenga kwa Hadadezeri+ mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba.
13 Komanso Davide anatchuka kwambiri atabwerako kumene anakapha Aedomu 18,000 mʼchigwa cha Mchere.+
14 Davide anakhazikitsa midzi ya asilikali ku Edomu. Mu Edomu monse anaikamo midzi ya asilikali, moti Aedomu anakhala antchito a Davide+ ndipo Yehova ankathandiza Davide kuti apambane kulikonse kumene wapita.+
15 Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli yense+ ndipo ankalimbikitsa chilungamo+ kwa anthu ake onse.+
16 Yowabu+ mwana wa Zeruya anali mkulu wa asilikali ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi ankalemba zimene zachitika.
17 Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndipo Seraya anali mlembi.
18 Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti.+ Ana aamuna a Davide anali nduna zazikulu za mfumu.*
Mawu a M'munsi
^ Ankawapundula powadula mtsempha wakuseri kwa mwendo wakumbuyo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ansembe.”