2 Samueli 2:1-32

  • Davide anakhala mfumu ya Yuda (1-7)

  • Isi-boseti anakhala mfumu ya Isiraeli (8-11)

  • Nkhondo ya pakati pa anthu a Davide ndi anthu a Sauli (12-32)

2  Kenako Davide anafunsa Yehova kuti:+ “Kodi ndipite mumzinda wina wa Yuda?” Yehova anamuyankha kuti: “Pita.” Davide anafunsanso kuti: “Ndipite kuti?” Iye anamuyankha kuti: “Ku Heburoni.”+  Choncho Davide anapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ amene anali mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.  Davide anapitanso ndi amuna amene ankayenda naye,+ aliyense ndi banja lake. Iwo anakakhala mʼmizinda yozungulira Heburoni.  Kenako amuna a ku Yuda anabwera nʼkudzoza Davide kuti akhale mfumu ya nyumba ya Yuda.+ Iwo anauza Davide kuti: “Anthu a ku Yabesi-giliyadi ndi amene anaika Sauli mʼmanda.”  Choncho Davide anatumiza uthenga kwa amuna a ku Yabesi-giliyadi wakuti: “Yehova akudalitseni, chifukwa munasonyeza mbuye wanu, Sauli, chikondi chokhulupirika pomuika mʼmanda.+  Yehova akusonyezeni chikondi chokhulupirika komanso kudalirika kwake. Inenso ndikusonyezani kukoma mtima chifukwa mwachita zimenezi.+  Tsopano limbitsani manja anu ndipo mukhale amuna olimba mtima, chifukwa mbuye wanu Sauli wamwalira ndipo anthu a nyumba ya Yuda andidzoza kuti ndikhale mfumu yawo.”  Koma Abineri+ mwana wa Nera, amene anali mtsogoleri wa asilikali a Sauli, anatenga Isi-boseti,+ mwana wa Sauli, nʼkupita naye ku Mahanaimu.+  Kumeneko anamuveka ufumu kuti azilamulira Giliyadi,+ Aasere, Yezereeli,+ Efuraimu,+ Benjamini ndi Isiraeli yense. 10  Isi-boseti mwana wa Sauli anali ndi zaka 40 pamene anakhala mfumu ya Isiraeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma anthu a nyumba ya Yuda ankatsatira Davide.+ 11  Nthawi yonse imene Davide anakhala mfumu ku Heburoni nʼkumalamulira nyumba ya Yuda, inali zaka 7 ndi miyezi 6.+ 12  Patapita nthawi, Abineri, mwana wa Nera ndi atumiki a Isi-boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu+ nʼkupita ku Gibiyoni.+ 13  Nayenso Yowabu+ mwana wa Zeruya+ ndi atumiki a Davide, anapita kudziwe la Gibiyoni ndipo magulu awiriwo anakumana kumeneko. Gulu lina linakhala pansi kumbali ina ya dziwelo ndipo gulu linalo linakhalanso kumbali inayo. 14  Kenako Abineri anauza Yowabu kuti: “Bwanji anyamata athuwa amenyane* tione?” Yowabu anayankha kuti: “Chabwino, amenyanedi.” 15  Choncho iwo ananyamuka. Kumbali ya Benjamini ndi Isi-boseti, mwana wa Sauli, anasankha anyamata 12 ndipo kwa atumiki a Davide anasankhanso anyamata 12. 16  Mnyamata aliyense anagwira mnzake kumutu ndipo aliyense anabaya mnzake ndi lupanga mʼmimba moti onsewo anafa. Malo amenewo, omwe ali ku Gibiyoni, anawapatsa dzina lakuti Helikati-hazurimu. 17  Zitatero panayambika nkhondo ndipo nkhondoyo inakula kwambiri. Abineri ndi amuna a Isiraeli anagonjetsedwa ndi atumiki a Davide. 18  Ana atatu aamuna a Zeruya,+ omwe ndi Yowabu,+ Abisai+ ndi Asaheli+ analinso pompo. Asaheli anali waliwiro kwambiri ngati mbawala. 19  Asaheli anayamba kuthamangitsa Abineri. Iye sanatembenukire kumanja kapena kumanzere pamene ankathamangitsa Abineri. 20  Abineri atayangʼana mʼmbuyo, anafunsa kuti: “Kodi ndiwe Asaheli?” Asaheli anayankha kuti: “Inde, ndi ineyo.” 21  Kenako Abineri anamuuza kuti: “Khotera kumanja kapena kumanzere ugwire mmodzi mwa anyamatawo ndipo utenge zimene ungamuvule.” Koma Asaheli anapitirizabe kumuthamangitsa. 22  Kenako Abineri anauzanso Asaheli kuti: “Siya kundithamangitsa. Ndikuphatu! Ndiye ndikakupha ndidzaonana bwanji ndi mchimwene wako Yowabu?” 23  Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa. Choncho Abineri anamubaya pamimba ndi chogwirira cha mkondo+ ndipo mkondowo unatulukira kumsana moti anagwa pansi nʼkufera pomwepo. Aliyense akafika pamalo amene Asaheli anafera, ankaima kaye. 24  Zitatero, Yowabu ndi Abisai anayamba kuthamangitsa Abineri. Pamene dzuwa linkalowa, anali atafika paphiri la Ama, limene lili pafupi ndi Giya panjira yopita kuchipululu cha Gibiyoni. 25  Anthu a fuko la Benjamini anasonkhana kumbali ya gulu la Abineri nʼkuima pamwamba paphiri lina. 26  Kenako Abineri anafuulira Yowabu kuti: “Kodi tipitiriza kuphana ndi lupanga mpaka liti? Sukudziwa kuti zimenezi zibweretsa mavuto aakulu? Kodi uwauza liti anthuwa kuti asiye kuthamangitsa abale awo?” 27  Yowabu anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Mulungu woona, ukanapanda kulankhula, anthuwa akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mʼmawa.” 28  Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anthu ake anasiya kuthamangitsa Aisiraeli moti nkhondo inathera pomwepo. 29  Abineri ndi anthu ake anayenda kudutsa ku Araba+ usiku wonse mpaka anakawoloka Yorodano. Iwo anayenda kudutsa chigwa* chonse mpaka kukafika ku Mahanaimu.+ 30  Yowabu atasiya kuthamangitsa Abineri anasonkhanitsa anthu onse. Pagulu la atumiki a Davide panasowa Asaheli ndi amuna ena 19. 31  Koma atumiki a Davidewo anagonjetsa anthu a fuko la Benjamini ndi amuna a Abineri moti anthu okwana 360 anafa. 32  Iwo ananyamula mtembo wa Asaheli+ nʼkukauika mʼmanda a bambo ake ku Betelehemu.+ Kenako Yowabu ndi amuna amene anali naye anayenda usiku wonse ndipo anafika ku Heburoni+ kukucha.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “apikisane.”
Mabaibulo ena amati, “Bitironi.”