Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Uzikonda Yehova Mulungu Wako”

“Uzikonda Yehova Mulungu Wako”

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—MAT. 22:37.

1. N’chiyani chinathandiza kuti ubwenzi wa Mulungu ndi Mwana wake ulimbe kwambiri?

YESU KHRISTU ananena kuti: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Iye ananenanso kuti: “Atatewo amakonda Mwana wake.” (Yoh. 5:20) Koma zimenezi si zodabwitsa. Pajatu, kwa zaka zambirimbiri Yesu asanabwere padziko lapansi, anali “mmisiri waluso” wa Mulungu. (Miy. 8:30) Pa nthawi imene Yehova ndi Yesu ankagwira ntchito limodzi, Mwanayu ankaphunzira zambiri zokhudza makhalidwe a Atate wake. Izi zinamuchititsa kukonda kwambiri Atate wakewo. Chifukwa chogwira ntchito limodzi ubwenzi wawo unalimba kwambiri.

2. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu azitisonyeza chikondi? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.” (Sal. 18:1) Tiyenera kukonda Yehova kwambiri chifukwa nayenso amatikonda. Iye adzatisonyeza chikondi tikamamumvera. (Werengani Deuteronomo 7:12, 13.) Koma kodi n’zothekadi kukonda Mulungu pamene sitingamuone? Kodi kukonda Yehova kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera  kumukonda? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu?

KODI N’ZOTHEKADI KUKONDA MULUNGU?

3, 4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zothekadi kukonda Yehova?

3 Sitingathe kuona Mulungu chifukwa chakuti ‘iye ndi Mzimu.’ (Yoh. 4:24) Ngakhale zili choncho, n’zotheka kumukonda. M’Baibulo mulinso lamulo loti tizimukonda. Mwachitsanzo, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.”—Deut. 6:5.

4 N’chifukwa chiyani tikunena kuti n’zothekadi kukonda kwambiri Mulungu? Chifukwa chakuti iye anatilenga ndi mtima wofuna kumulambira komanso wotha kusonyeza chikondi. Ndiyeno tikamamulambira m’njira yoyenera timayamba kumukonda kwambiri ndipo timakhala osangalala. Paja Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Pa nkhani yoti tili ndi mtima wofuna kulambira Mulungu, buku lina linati: “Mfundo yakuti anthu padziko lonse amalakalaka atadziwa Mulungu ndiponso kumukhulupirira imatidabwitsa kwambiri.”—Man Does Not Stand Alone, lolembedwa ndi A. C. Morrison.

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kufufuza Mulungu n’kumupeza?

5 Koma kodi anthu amene amafufuza Mulungu amamupeza? Inde, chifukwa n’zimenenso Mulunguyo amafuna. Mtumwi Paulo ananenanso zimenezi polankhula ndi anthu amene anasonkhana pabwalo la Areopagi. Munthu akaima pabwaloli atha kuona kachisi wa mulungu wamkazi wa ku Atene dzina lake Atena. Ndiyeno kodi mukanamva bwanji mukanakhalapo pamene Paulo ankanena za “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu”? Kenako mukumumva akuti Mulunguyo “sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.” Ndiyeno akupitiriza kuti: “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi. Iye anakhazikitsa nthawi zoikidwiratu komanso anaika malire achikhalire a malo oti anthu azikhala. Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:24-27) Choncho anthu akhoza kufufuza Mulungu n’kumupeza. Panopa anthu pafupifupi 8 miliyoni a Mboni za Yehova ‘amupezadi’ ndipo amamukonda kwambiri.

KODI KUKONDA MULUNGU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

6. Kodi Yesu ananena kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi liti?

6 Tiyenera kukonda Yehova kuchokera pansi pa mtima. Yesu ananenanso zimenezi pamene Mfarisi wina anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba.”—Mat. 22:34-38.

7. Kodi zimatanthauza chiyani kukonda Mulungu ndi (a) ‘mtima wathu wonse’? (b) ‘moyo wathu wonse’? (c) ‘maganizo athu onse’?

7 Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi ‘mtima wathu wonse’? Ankatanthauza kuti chikondichi chiyenera kuonekera pa zonse zimene timalakalaka komanso mmene timamvera mumtima mwathu. Ponena kuti ndi ‘moyo wathu wonse,’ ankatanthauza zonse zimene timachita pa moyo wathu. Ndiyeno ponena kuti ndi ‘maganizo athu onse,’ ankatanthauza zonse zimene timaganiza komanso mmene timaganizira. Choncho tiyenera kukonda Mulungu mopanda malire.

8. Ngati timakonda kwambiri Mulungu, kodi tidzachita chiyani?

8 Ngati timakonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi maganizo athu onse tidzachita khama pophunzira Mawu  ake ndiponso polalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso tidzamutumikira ndi mtima wonse. (Mat. 24:14; Aroma 12:1, 2) Tikamakonda Yehova kuchokera pansi pa mtima tidzamuyandikira kwambiri. (Yak. 4:8) N’zosatheka kutchula zinthu zonse zimene zingatichititse kukonda Mulungu koma tiyeni tikambirane zinthu zingapo.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKONDA YEHOVA?

9. Perekani chifukwa china chokuchititsani kukonda Yehova.

9 Yehova ndi Mlengi wathu komanso amatisamalira. Paulo ananena kuti: “Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:28) Yehova watipatsa dziko lapansi lokongolali kuti tizikhalamo. (Sal. 115:16) Amatipatsanso chakudya ndi zinthu zina zofunika pa moyo wathu. N’chifukwa chake Paulo anauza anthu olambira mafano a ku Lusitara kuti: “Mulungu wamoyo . . . sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.” (Mac. 14:15-17) Chimenechitu ndi chifukwa china chotichititsa kukonda Mlengi wathu Wamkulu amene amatisamalira mwachikondi.—Mlal. 12:1.

10. Kodi timamva bwanji tikaganizira zimene Mulungu wachita pofuna kuchotsa uchimo ndi imfa?

10 Mulungu wakonza njira yochotsera uchimo ndiponso imfa zimene tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Malemba amati: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Timakonda kwambiri Yehova chifukwa chakuti anakonza njira yoti tikhululukidwe machimo athu ngati talapa ndiponso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu.—Yoh. 3:16.

11, 12. Kodi Yehova watipatsa chiyembekezo chotani?

11 Yehova ‘amapereka chiyembekezo chimene chimatipatsa chimwemwe ndi mtendere.’ (Aroma 15:13) Chiyembekezo chimene Mulungu watipatsa chimatithandiza kupirira mayesero. Odzozedwa amene adzasonyeza ‘kukhulupirika mpaka imfa, adzapatsidwa mphoto ya moyo’ kumwamba. (Chiv. 2:10) Koma anthu ena onse okhulupirika adzalandira madalitso osatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Kodi timamva bwanji tikaganizira zonsezi? Kunena zoona timakhala osangalala, timakhala ndi mtendere mumtima komanso timakonda kwambiri Mulungu chifukwa chotipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.”—Yak. 1:17.

12 Mulungu watipatsa chiyembekezo cholimbikitsa chakuti akufa adzauka. (Mac. 24:15) Mnzathu akamwalira zimatipweteka kwambiri. Koma popeza Mulungu walonjeza kuti akufa adzauka sitikhala ndi “chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo amachitira.” (1 Ates. 4:13) Yehova Mulungu ndi wachikondi ndipo amalakalaka kuukitsa akufa, makamaka okhulupirika monga Yobu. (Yobu 14:15) Padziko lapansi padzakhala chisangalalo chosaneneka tikadzakumananso ndi anthu amene anamwalira. Timakonda kwambiri Atate wathu wakumwamba chifukwa chotipatsa chiyembekezo chimenechi.

13. N’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambiri?

13 Yehova amatikonda kwambiri. (Werengani Salimo 34:6, 18, 19; 1 Petulo 5:6, 7.) Yehova ndi wachikondi komanso wokonzeka kuthandiza anthu okhulupirika. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tisamade nkhawa chifukwa tili ngati ‘nkhosa zake.’ (Sal. 79:13) Zimene Mulungu adzatichitire mu Ufumu wa Mesiya zidzasonyezanso kuti amatikonda kwambiri. Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, adzathetsa ziwawa, kuponderezana ndiponso zoipa zonse. Kenako adzadalitsa anthu okhulupirika kuti azikhala mwamtendere komanso mosangalala. (Sal. 72:7, 12-14, 16) Zonsezi zimatichititsa kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, mphamvu zathu zonse ndiponso maganizo athu onse.—Luka 10:27.

14. Kodi Mulungu watipatsa mwayi uti wamtengo wapatali?

 14 Yehova watipatsa mwayi wamtengo wapatali kwambiri wokhala Mboni zake. (Yes. 43:10-12) Timakonda Yehova chifukwa chotipatsa mwayi umenewu. Timathandiza anthu kudziwa kuti iye ndi woyenera kulamulira ndiponso timawathandiza kuti akhale ndi chiyembekezo m’dziko loipali. Timalalikira ndi chikhulupiriro chonse podziwa kuti uthenga wathu ndi wochokera m’Mawu a Mulungu woona, yemwe amachitadi zonse zimene walonjeza. (Werengani Yoswa 21:45; 23:14.) Kunena zoona pali madalitso ambirimbiri komanso zifukwa zina zambiri zotichititsa kukonda Mulungu. Ndiyeno kodi tingasonyeze bwanji kuti timamukonda?

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAKONDA MULUNGU?

15. Kodi kuphunzira Baibulo ndiponso kutsatira zimene timaphunzira kumatithandiza bwanji?

15 Tizichita khama pophunzira ndiponso kutsatira Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova ndipo timafuna kuti Mawu ake akhale ngati ‘kuwala kounikira njira yathu.’ (Sal. 119:105) Tikakhala ndi nkhawa, tingalimbikitsidwe ndi mawu akuti: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.” Kapena akuti: “Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza. Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” (Sal. 51:17; 94:18, 19) Yehova amachitira chifundo anthu ovutika. Yesu amamveranso chisoni anthu amene akuvutika. (Yes. 49:13; Mat. 15:32) Tikamaphunzira Baibulo timamvetsa kwambiri kuti Yehova amatikonda ndiponso kutiganizira. Ndiyeno zimenezi zimatichititsa kuti ifenso tizimukonda kwambiri.

16. Kodi kupemphera nthawi zonse kungathandize bwanji kuti tizikonda kwambiri Mulungu?

16 Tizipemphera kwa Mulungu nthawi zonse. Tikamapemphera timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Kuona kuti Mulungu akuyankha mapemphero athu kumatithandiza kumukonda kwambiri. Mwachitsanzo, mwina taonapo kuti Mulungu salola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire. (1 Akor. 10:13) Mwinanso tikakhala ndi nkhawa n’kupemphera mopembedzera kwa Yehova, timaona kuti akutipatsa ‘mtendere  wake.’ (Afil. 4:6, 7) Kapena nthawi zina tikhoza kupemphera chamumtima ngati Nehemiya n’kuona kuti pempherolo likuyankhidwa. (Neh. 2:1-6) ‘Tikamalimbikira kupemphera’ n’kuona kuti Yehova akutiyankha, timamukonda kwambiri. Komanso sitikayikira kuti Yehova adzatithandiza pa mayesero athu onse.—Aroma 12:12.

17. Ngati timakonda Mulungu, kodi tiziona bwanji misonkhano?

17 Tizipezeka nthawi zonse pa misonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu. (Aheb. 10:24, 25) Aisiraeli ankasonkhana kuti amvetsere ndiponso kuphunzira za Yehova n’cholinga choti azimuopa komanso kutsatira Chilamulo chake. (Deut. 31:12) Ngati timakondadi Mulungu sitingavutike kuchita zimene iye amafuna. (Werengani 1 Yohane 5:3.) Choncho tisayambe kuona misonkhano yathu mopepuka. Tisalolenso chilichonse kutilepheretsa kukonda Yehova mmene tinkachitira poyamba.—Chiv. 2:4.

18. Kodi kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kuchita chiyani?

18 Tizichita khama pouza anthu ena “choonadi cha uthenga wabwino.” (Agal. 2:5) Chifukwa chokonda Mulungu, timauza anthu za Ufumu wa Mwana wake, yemwe adzamenya nkhondo pa Aramagedo “chifukwa cha choonadi.” (Sal. 45:4; Chiv. 16:14, 16) Timasangalala kwambiri kuthandiza anthu kuti adziwe za chikondi cha Mulungu ndiponso za dziko latsopano limene walonjeza.—Mat. 28:19, 20.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira abusa amene Mulungu watipatsa?

19 Tiziyamikira abusa amene Mulungu watipatsa. (Mac. 20:28) Yehova watipatsa akulu mumpingo kuti azitithandiza. Akuluwo ali “ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yes. 32:1, 2) Tonse timafuna kupeza malo oti tibisale kukakhala mphepo kapena mvula yamkuntho. Dzuwa likatentha kwambiri timasangalala kupeza mthunzi wabwino. Mawu a m’lembali amatithandiza kuona kuti akulu angatithandize ndiponso kutilimbikitsa. Tikamamvera amene akutitsogolera timasonyeza kuti timayamikira kwambiri “mphatso za amuna” zimenezi. Timasonyezanso kuti timakonda kwambiri Mulungu ndiponso Khristu, yemwe ndi Mutu wa mpingo.—Aef. 4:8; 5:23; Aheb. 13:17.

Yehova watipatsa abusa amene amatithandiza kwambiri (Onani ndime 19)

MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI MULUNGU

20. Kodi munthu amene amakonda Yehova amatani?

20 Ngati mumakondadi Yehova mudzayesetsa ‘kuchita zimene mawu ake amanena, osati kungomva chabe.’ (Werengani Yakobo 1:22-25.) Munthu ‘wochita zimene mawuwo amanena’ amalalikira mwakhama komanso amayesetsa kuyankha pa misonkhano. Kukonda Yehova kungakulimbikitseni kutsatira ‘lamulo lake langwiro’ lomwe likutanthauza zinthu zonse zimene iye amafuna kuti muchite.—Sal. 19:7-11.

21. Kodi mapemphero athu ochokera pansi pa mtima amakhala ngati chiyani?

21 Kukonda Yehova kungakulimbikitseninso kuti muzipemphera kwa iye kuchokera mumtima nthawi zonse. Davide anaimba kuti: “Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu [Yehova], mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.” (Sal. 141:2; Eks. 30:7, 8) Ponena zimenezi, ayenera kuti ankaganizira za zofukiza zimene zinkaperekedwa potsatira Chilamulo cha Mose. Choncho pamene mukupempha zinthu kwa Yehova modzichepetsa, kupemphera mopembedzera ndiponso kumutamanda kapena kumuyamikira kuchokera pansi pa mtima, mapemphero anu amakhala ngati zofukiza zonunkhira kwa iye.—Chiv. 5:8.

22. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

22 Yesu ananena kuti tiyenera kukonda Mulungu komanso anzathu. (Mat. 22:37-39) M’nkhani yotsatira, tidzaona kuti kukonda Yehova ndiponso mfundo zake kungatithandize kuti tizikhala bwino ndi anzathu komanso kuwakonda.