Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi n’zoyenera kuti Akhristu azitentha mtembo?

Malemba satsutsa zotentha mtembo.

M’Baibulo muli nkhani za anthu amene anatentha mitembo kapena mafupa a anthu. (Yos. 7:25; 2 Mbiri 34:4, 5) Mwina anachita zimenezi chifukwa chakuti mitemboyo inali ya anthu osayenera kuwaika m’manda mwaulemu. Ngakhale zili choncho, sikuti anthu onse amene ankatentha mitembo ankaitentha pa zifukwa zimenezi.

Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Sauli ndi ana ake atatu ataphedwa pa nkhondo yomenyana ndi Afilisiti. Mmodzi mwa anawo anali Yonatani, yemwe anali mnzake wapamtima wa Davide. Aisiraeli olimba mtima a ku Yabesi-giliyadi atamva, anatenga mitembo yawo n’kuitentha kenako n’kuika m’manda mafupa awo. Davide anayamikira kwambiri zimene Aisiraeliwa anachita.—1 Sam. 31:2, 8-13; 2 Sam. 2:4-6.

Malemba amanena kuti Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira. Kaya mtembo wa munthu unachita kutenthedwa kapena ayi, Yehova akhoza kumuukitsa n’kumupatsa thupi latsopano. Aheberi atatu okhulupirika, amene anaopsezedwa kuti akhoza kutenthedwa m’ng’anjo ya moto ndi Mfumu Nebukadinezara, sanaope kuti Mulungu sadzatha kuwaukitsa. (Dan. 3:16-18) N’chimodzimodzinso ndi atumiki a Yehova amene anaphedwa n’kutenthedwa m’ndende za boma la Nazi. Palinso atumiki a Yehova amene anafa chifukwa cha mabomba kapena zinthu zina moti mitembo yawo sinapezekenso. Koma sitikayikira zoti adzaukitsidwa.—Chiv. 20:13.

Sikuti Yehova adzachita kutolera zidutswa za thupi la munthu kuti amuukitse. Umboni wake ndi zimene amachita poukitsa Akhristu odzozedwa kuti akakhale kumwamba. Pajatu Yesu “anaukitsidwa monga mzimu.” Nawonso Akhristu odzozedwa amaukitsidwa ndi thupi lauzimu koma amakhala ali munthu yemweyo. Thupi limene anali nalo padzikoli silipita kumwamba.—1 Pet. 3:18; 1 Akor. 15:42-53; 1 Yoh. 3:2.

Timakhulupirira kuti Mulungu adzaukitsa akufa chifukwa chodziwa kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake. Izi zili choncho ngakhale mtembo atautentha. (Mac. 24:15) Mwina sitingamvetse mmene Mulungu anaukitsira anthu m’mbuyomu komanso mmene adzachitire zimenezi m’tsogolo. Komabe timakhulupirira kuti adzaukitsadi anthu. ‘Watitsimikizira’ zimenezi poukitsa Yesu.—Mac. 17:31; Luka 24:2, 3.

Koma posankha zimene angachite ndi mtembo, Akhristu angachite bwino kuganizira mmene anthu ena angaonere nkhaniyi komanso zimene malamulo a boma amanena. (2 Akor. 6:3, 4) Choncho pambuyo poganizira zimenezi ndiponso zimene munthu amene wamwalirayo ankafuna, achibale angasankhe kutentha mtembo kapena ayi.