Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 5

Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana ndi Dzikoli?

Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana ndi Dzikoli?

“Simuli mbali ya dzikoli.”—YOHANE 15:19.

1. Usiku wake womaliza kukhala padziko lapansi, kodi Yesu anasonyeza kuti ndi nkhani iti imene inali yofunika kwambiri?

USIKU wake womaliza kukhala padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti ankadera nkhawa kwambiri otsatira ake poganizira zimene zidzawachitikire m’tsogolo. Iye anapemphera za nkhaniyi kwa Atate wake kuti: “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16) Pemphero lake lochokera pansi pa mtima limeneli, limasonyeza kuti Yesu ankawakonda kwambiri otsatira ake, komanso limasonyeza kuti mawu amene anauza ena mwa otsatirawo usiku umenewo anali ofunika kwambiri. Mawu ake anali akuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Choncho Yesu ankaona kuti n’kofunika kwambiri kuti otsatira ake akhale osiyana ndi dzikoli.

2. Kodi mawu akuti “dzikoli” amene Yesu ananena ankatanthauza chiyani?

2 Ponena kuti “dzikoli,” Yesu ankatanthauza anthu onse amene sachita chifuniro cha Mulungu ndipo amalamuliridwa ndi Satana, komanso amasonyeza mzimu wodzikonda ndi wonyada umene umachokera kwa Satana. (Yohane 14:30; Aefeso 2:2; 1 Yohane 5:19) Zoonadi, kuchita “ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu.” (Yakobo 4:4) Popeza kuti ife amene tikufuna kuti Mulungu apitirize kutikonda tili m’dziko lomweli, ndiye zingatheke bwanji kuti tikhale osiyana nalo? Tingachite zimenezi mu njira 5 izi: Tizikhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Khristu ndipo tisamalowerere ndale, tizipewa mzimu wa dziko, tizivala ndi kudzikongoletsa moyenera, tizikhala moyo wosalira zambiri, ndiponso tizinyamula zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.

TIZIKHALA OKHULUPIRIKA NDIPO TISAMALOWERERE NDALE

3. (a) N’chifukwa chiyani Yesu sankalowerera ndale? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti otsatira a Yesu odzozedwa ndi akazembe? (Onaninso mawu a m’munsi.)

3 Yesu ali padziko lapansi pano sanalowerere ndale. M’malomwake iye ankakonda kulalikira za Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma la kumwamba limene iye ankayembekezera kudzakhala Mfumu yake. (Danieli 7:13, 14; Luka 4:43; 17:20, 21) Choncho, atakaonekera kwa bwanamkubwa wachiroma, Pontiyo Pilato, Yesu anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Otsatira ake okhulupirika amatengera chitsanzo chake pokhala okhulupirika kwa iye ndi Ufumu wake ndiponso polengeza Ufumuwo kwa anthu a m’dzikoli. (Mateyu 24:14) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndife akazembe m’malo mwa Khristu, . . . Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti: ‘Gwirizananinso ndi Mulungu.’” *2 Akorinto 5:20.

4. Kodi Akhristu onse oona asonyeza bwanji kuti ndi okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu? (Onani bokosi “ Akhristu Oyambirira Sankalowerera Ndale.”)

4 Akazembe salowerera ndale ndi zochitika zina za m’mayiko amene akugwirako ntchito, chifukwa ntchito yawo ndi kuimira dziko lawo basi. Iwo amagwira ntchito zopititsa patsogolo boma la dziko limene akuimira. N’chimodzimodzi ndi otsatira Khristu odzozedwa, amene ndi “nzika zakumwamba.” (Afilipi 3:20) Akhristu odzozedwa akhala akugwira ntchito yolalikira za Ufumu mwakhama, ndipo zimenezi zathandiza kuti “nkhosa zina” za Khristu ‘zigwirizanenso ndi Mulungu.’ (Yohane 10:16; Mateyu 25:31-40) A nkhosa zina ndi nthumwi za Khristu chifukwa amathandiza abale a Yesu odzozedwa.Magulu awiri onsewa akupanga gulu limodzi la nkhosa logwirizana. Gulu limeneli limagwira ntchito zopititsa patsogolo Ufumu wa Mesiya, choncho sililowerera ndale ngakhale pang’ono.—Werengani Yesaya 2:2-4.

5. Kodi mpingo wachikhristu umasiyana bwanji ndi Aisiraeli akale, ndipo kodi kusiyana kumeneku kumaonekera m’njira ziti?

5 Zoonadi, Akhristu oona salowerera ndale chifukwa amafuna kukhala okhulupirika kwa Khristu. Komabe pali zifukwa zinanso zimene iwo sachitira zimenezi. Mosiyana ndi Aisiraeli akale amene Mulungu anawapatsa dziko lawolawo, ifeyo timapanga gulu la abale la padziko lonse. (Mateyu 28:19; 1 Petulo 2:9) Choncho, ngati tingalowe m’zipani zandale sitingakhale omasuka polalikira uthenga wa Ufumu ndipo tingasokoneze mgwirizano wathu wachikhristu. (1 Akorinto 1:10) Komanso pa nthawi ya nkhondo, tingamamenyane ndi okhulupirira anzathu amene timalamulidwa kuti tiziwakonda. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12) Choncho, m’pomveka kuti Yesu anawauza ophunzira ake kuti asamamenye nkhondo. Ndipo iye anawauzanso kuti azikonda adani awo.—Mateyu 5:44; 26:52; onani bokosi lakuti “ Kodi Ndimalowerera Ndale?

6. Kodi kudzipereka kwanu kwa Mulungu kumafunanso kuti muzichita zinthu zotani kwa Kaisara?

6 Ife Akhristu oona tinadzipereka kwa Mulungu osati kwa munthu, bungwe la anthu kapenanso dziko linalake. Lemba la 1 Akorinto 6:19, 20 limati: “Mwiniwake wa inuyo si inu, pakuti munagulidwa pa mtengo wokwera.” Choncho, otsatira a Yesu akamapereka za “Kaisara” monga ulemu, misonkho ndi kugonjera mosapitirira malire, amayeneranso kupereka ‘za Mulungu kwa Mulungu.’ (Maliko 12:17; Aroma 13:1-7) Zimenezi zikutanthauza kumulambira, kumukonda ndi mtima wonse ndiponso kumumvera mokhulupirika. Ndipo iwo amakhala okonzeka kufa chifukwa chofuna kumvera Mulungu, ngati pangafunike kutero.—Luka 4:8; 10:27; werengani Machitidwe 5:29; Aroma 14:8.

TIZIPEWA “MZIMU WA DZIKO”

7, 8. Kodi “mzimu wa dziko” n’chiyani, ndipo ‘umagwira ntchito’ bwanji mwa anthu osamvera?

7 Njira ina imene Akhristu amakhalira osiyana ndi dzikoli ndi kupewa mzimu wake woipa. Paulo analemba kuti: “Sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.” (1 Akorinto 2:12) Iye anawauza abale a ku Efeso kuti: “Munali kuyenda m’zimenezo mogwirizana ndi nthawi za m’dzikoli, momveranso wolamulira wa mpweya umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.”—Aefeso 2:2, 3.

8 “Mpweya” kapena kuti mzimu wa dzikoli ndi mphamvu yosaoneka imene imalimbikitsa anthu kusamvera Mulungu komanso kukhala ndi ‘chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso.’ (1 Yohane 2:16; 1 Timoteyo 6:9, 10) Mzimu umenewu uli ndi “mphamvu” padzikoli moti umatha kutikopa chifukwa cha thupi lathu lochimwali. Mzimuwu suoneka, ndi wokakamira ndipo mofanana ndi mpweya umapezeka paliponse. ‘Umagwira ntchito’ mwa munthu, ndipo munthuyo amayamba pang’onopang’ono kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amadana nawo monga kudzikonda, kudzikweza, mtima wofuna kutchuka ndiponso mzimu wosafuna kuuzidwa zochita komanso wopanduka. * Kunena mwachidule, mzimu wa dzikoli umachititsa kuti pang’onopang’ono anthu ayambe kusonyeza makhalidwe a Mdyerekezi.—Yohane 8:44; Machitidwe 13:10; 1 Yohane 3:8, 10.

9. Kodi mzimu wa dzikoli ungalowe bwanji m’maganizo ndi mumtima mwathu?

9 Kodi mzimu wa dziko ungayambe kulamulira maganizo ndi mtima wanu? Inde, zimenezi zingachitike ngati simuteteza mtima wanu. (Werengani Miyambo 4:23.) Nthawi zambiri zimenezi zimayamba pang’onopang’ono, mwina ngati timacheza ndi anthu amene timawaona ngati abwino ngakhale kuti sakonda Yehova. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Mzimu woipa umenewu ungalowenso mumtima mwanu kudzera m’mabuku oipa, m’zolaula kapena m’nkhani za ampatuko zopezeka pa Intaneti, m’zosangalatsa zoipa ndiponso m’masewera amene osewera ake amapikisana koopsa. Tingoti ungalowe mumtima mwanu kudzera mwa wina aliyense kapena china chilichonse chimene chimasonyeza maganizo a Satana ndi dziko lakeli.

10. Kodi tingapewe bwanji mzimu wa dzikoli?

10 Kodi tingapewe bwanji mzimu woipa wa dzikoli kuti Mulungu apitirizebe kutikonda? Tiyenera kugwiritsa ntchito mokwanira zinthu zauzimu zimene Yehova amapereka komanso kupempha mzimu woyera nthawi zonse. Yehova ndi wamkulu kwambiri kuposa Mdyerekezi ndiponso dziko loipali limene Satana akulamulira. (1 Yohane 4:4) Choncho mpofunika kwambiri kuti tizipemphera pafupipafupi kwa Yehova.

TIZIVALA NDI KUDZIKONGOLETSA MOYENERA

11. Kodi mzimu wa dziko wasokoneza bwanji kavalidwe?

11 Kavalidwe, kudzikongoletsa ndi ukhondo wa munthu zimasonyeza mzimu umene ukumulamulira. M’mayiko ambiri anthu sakuvala moyenera, moti munthu wina woulutsa mawu pa TV ananena kuti posachedwapa sitidzatha kudziwa kuti hule ndi uti. Nyuzipepala ina inanena kuti ngakhale atsikana amene sanakwanitse zaka 13, atengera kavalidwe kosayenera kameneka. Nyuzipepalayo inati: “Iwo amavala zovala zoonetsa thupi kwambiri komanso zochotsa ulemu.” Khalidwe linanso limene lafala ndi kuvala mosasamala, ndipo zimenezi zimasonyeza mzimu wopanduka komanso wosadzilemekeza.

12, 13. Kodi tiziyendera mfundo ziti pa nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa?

12 Monga atumiki a Yehova tiyenera kumaoneka bwino kwambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti tizivala zovala zoyera ndi zabwino komanso zogwirizana ndi malo omwe tili. Nthawi zonse tizivala “mwaulemu ndi mwanzeru” komanso tizichita “ntchito zabwino,” zoyenera mkazi kapena mwamuna aliyense amene “amati amalemekeza Mulungu.” Komabe cholinga chathu chisakhale kudzionetsera koma kuti ‘tipitirize kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Mulungu azitikonda.’ (1 Timoteyo 2:9, 10; Yuda 21) Choncho tifunika kukongoletsa kwambiri ‘munthu wobisika wamumtima . . . , amene ali wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.’—1 Petulo 3:3, 4.

13 Tiyeneranso kukumbukira kuti kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu kumakhudza mmene ena amaonera kulambira koona. Pa nkhani ya makhalidwe abwino, mawu Achigiriki amene anamasuliridwa kuti “mwaulemu,” angatanthauzenso kulemekeza maganizo a anthu ena. Choncho, tikufunika kuganizira chikumbumtima cha ena, m’malo mongokakamira zimene tikuona kuti ndi ufulu wathu. Koposa zonse, tikufuna kulemekeza Yehova ndi anthu ake ndiponso kudzichitira umboni kuti ndife atumiki a Mulungu pochita “zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 4:9; 10:31; 2 Akorinto 6:3, 4; 7:1.

Kodi maonekedwe anga amalemekeza Yehova?

14. Kodi ndi mafunso otani amene tingadzifunse pa nkhani ya maonekedwe athu?

14 Tiyeneranso kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera komanso kukhala aukhondo makamaka tikamapita mu utumiki wakumunda ndi kumisonkhano yachikhristu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amadabwa ndi maonekedwe anga? Kodi maonekedwe anga amachititsa manyazi anthu ena? Kodi ndimaona ufulu wanga pa nkhani ya kavalidwe kukhala wofunika kwambiri kuposa kutumikira mumpingo?’—Afilipi 4:5; 1 Petulo 5:6.

15. N’chifukwa chiyani Mawu a Mulungu samapereka mndandanda wa malamulo okhudza kavalidwe, kudzikongoletsa komanso ukhondo?

15 Baibulo silipereka mndandanda wa malamulo oti Akhristu aziyendera pa nkhani ya kavalidwe, kudzikongoletsa komanso ukhondo. Yehova safuna kutilanda ufulu wathu wosankha kapena ufulu woganiza tokha zimene tikufuna kuchita. M’malomwake iye amafuna kuti tikhale anthu okhwima maganizo, otha kuganizira mfundo za m’Baibulo ndiponso kuti tikhale anthu “amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” (Aheberi 5:14) Koposa zonse, Mulungu amafuna kuti tizichita zinthu chifukwa chomukonda ndiponso kukonda anzathu. (Werengani Maliko 12:30, 31.) Kutsatira mfundo zimenezi, kumatipatsa ufulu wovala ndi kudzikongoletsa mosiyanasiyana. Timaona umboni wa zimenezi pamisonkhano ya anthu a Yehova osangalala amene amaoneka bwino chifukwa cha kavalidwe kawo kosiyanasiyana, kulikonse kumene ali.

TIZIKHALA MOYO WOSALIRA ZAMBIRI

16. Kodi mzimu wa dzikoli umasiyana bwanji ndi zimene Yesu anaphunzitsa, nanga tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

16 Mzimu wa dziko ndi wonyenga ndipo umalimbikitsa anthu ambiri kuganiza kuti ndalama ndi chuma, ndi zimene zingawabweretsere chimwemwe. Koma Yesu anati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Yesu sankalimbikitsa anthu kuti azikhala moyo wodzizunza kapena wodzimana monyanyira, koma ankaphunzitsa kuti anthu angakhale ndi chimwemwe chenicheni ngati “amazindikira zosowa zawo zauzimu” ndiponso ngati akhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi,” kapena kuti limene limangoyang’ana pa zinthu zauzimu. (Mateyu 5:3; 6:22) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakhulupiriradi zimene Yesu anaphunzitsazi, kapena kodi ndimachita zofuna za “tate wake wa bodza”? (Yohane 8:44) Kodi zolankhula zanga, zolinga zanga, zinthu zimene ndimaona kuti ndi zofunika kwambiri ndiponso zimene ndimachita pa moyo wanga, zimasonyeza kuti ndine wotani?’—Luka 6:45; 21:34-36; 2 Yohane 6.

17. Tchulani ena mwa madalitso amene anthu okhala ndi moyo wosalira zambiri amapeza.

17 Yesu anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Taganizirani zina mwa zinthu zimene anthu amene amakhala moyo wosalira zambiri amasangalala nazo. Iwo amasangalala kwambiri akamagwira ntchito yawo yolalikira za Ufumu. (Mateyu 11:29, 30) Sakhala ndi nkhawa zambiri, choncho amapewa mavuto ambiri. (Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Chifukwa chakuti amakhala okhutira ndi zofunika pa moyo zokha, amakhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi mabanja awo ndiponso mabwenzi awo achikhristu. Zimenezi zimachititsa kuti azigona tulo tabwino. (Mlaliki 5:12) Amakhalanso osangalala kwambiri chifukwa choti amagawana zilizonse zimene angakhale nazo. (Machitidwe 20:35) Ali “ndi chiyembekezo chachikulu” ndipo amakhala ndi mtendere wa mumtima. (Aroma 15:13; Mateyu 6:31, 32) Kunena zoona, madalitso amenewa ndi a mtengo wapatali.

TIZINYAMULA “ZIDA ZONSE ZANKHONDO”

18. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za mdani wathu, njira zake, ndiponso mtundu wa nkhondo yathu?

18 Anthu amene amakondedwa ndi Mulungu amatetezedwa mwauzimu kwa Satana, amene amafuna kuwalepheretsa kupeza chimwemwe ndiponso moyo wosatha. (1 Petulo 5:8) Paulo anati: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamuliro, olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12) Mawu akuti ‘kulimbana’ akusonyeza kuti nkhondo yathu si yomenyana motalikirana kapena mobisalirana, koma tingati ndi yomenyana moyandikana. Komanso mawu akuti “maboma,” “maulamuliro” ndi “olamulira dziko,” akusonyeza kuti ziwanda zimakonzekera bwino komanso zimachita zinthu ngati gulu zikafuna kutiukira.

19. Fotokozani zida zankhondo zauzimu zimene Akhristu ayenera kunyamula.

19 Tikhoza kupambana nkhondoyi ngakhale kuti ndife ofooka ndiponso timalephera kuchita zinthu zina. Kodi tingapambane bwanji? Tizinyamula “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” (Aefeso 6:13) Pofotokoza zida zimenezi, lemba la Aefeso 6:14-18 limati: “Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi m’chiuno mwanu, mutavalanso chodzitetezera pachifuwa chachilungamo, mapazi anu mutawaveka nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere. Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro, chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Komanso, landirani chisoti [kapena kuti chiyembekezo] cholimba chachipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu. Pamene mukutero, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero.”

20. Kodi ifeyo tikusiyana bwanji ndi msilikali weniweni?

20 Zida zankhondo zauzimu zimenezi zingatiteteze chifukwa n’zochokera kwa Mulungu. Koma zingatiteteze pokhapokha ngati tikuzivala nthawi zonse. Mosiyana ndi msilikali weniweni, amene nthawi zina samenya nkhondo, Akhristu ali pankhondo ya wafawafa imene ikupitirirabe mpaka pamene Mulungu adzawononge dziko la Satanali ndi kuponya ziwanda zonse kuphompho. (Chivumbulutso 12:17; 20:1-3) Choncho, ngati mukulimbana ndi zofooka kapena zilakolako zoipa, musabwerere m’mbuyo, popeza tonse timafunika ‘kumenya thupi lathu’ kuti tikhalabe okhulupirika kwa Yehova. (1 Akorinto 9:27) Koma ngati sitikulimbana ndi vuto linalake ndiye kuti penapake sipali bwino.

21. Kodi tingapambane nkhondo yathu yauzimu pokhapokha ngati tichita chiyani?

21 Komabe, sitingapambane nkhondoyi ndi mphamvu zathu zokha. N’chifukwa chake Paulo akutikumbutsa kuti tiyenera kumapemphera kwa Yehova “pa chochitika chilichonse mu mzimu.” Komanso, tiyenera kumvera Yehova pophunzira Mawu ake ndiponso kusonkhana nthawi zonse ndi amene tingati ndi asilikali anzathu, chifukwa sitikumenya tokha nkhondoyi. (Filimoni 2; Aheberi 10:24, 25) Anthu amene amachita zonsezi mokhulupirika adzapambana nkhondoyi ndiponso adzatha kuteteza chikhulupiriro chawo pamene chikutsutsidwa.

TIZIKHALA OKONZEKA KUTETEZA CHIKHULUPIRIRO CHATHU

22, 23. (a) N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kuteteza chikhulupiriro chathu, nanga kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati? (b) Kodi mutu wotsatira ufotokoza chiyani?

22 Yesu anati: ‘Popeza simuli mbali ya dzikoli, . . . dziko limadana nanu.’ (Yohane 15:19) Choncho, Akhristu ayenera kukhala okonzeka kuteteza chikhulupiriro chawo ndipo ayenera kuchita zimenezo mwaulemu ndi mofatsa. (Werengani 1 Petulo 3:15.) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamvetsa chifukwa chake Mboni za Yehova nthawi zina zimachita zinthu zosiyana ndi zimene anthu ambiri akuchita? Ndikamachita zinthu zosiyana ndi zimene anthu ambiri akuchita, kodi ndimakhulupiriradi kuti zimene Baibulo komanso zimene kapolo wokhulupirika amanena n’zoona? (Mateyu 24:45; Yohane 17:17) Kodi ndine wokonzeka kuchita zimene Yehova amaona kuti ndi zoyenera ngakhale zitakhala zosiyana ndi zimene anthu ambiri amachita? Komanso kodi ndimachita zimenezi mosangalala?’—Salimo 34:2; Mateyu 10:32, 33.

23 Ngakhale kuti cholinga chathu n’kukhala osiyana ndi dzikoli, nthawi zambiri timayesedwa pa nkhani imeneyi m’njira zosaonekera. Mwachitsanzo, monga tanenera kale, Mdyerekezi amagwiritsa ntchito zosangalatsa zosayenera pokopa atumiki a Yehova kuti akhale mbali ya dzikoli. Kodi tingasankhe bwanji zosangalatsa zabwino zimene zingatisiye ndi chikumbumtima choyera? Mutu wotsatira ufotokoza nkhani imeneyi.

^ ndime 3 Kuyambira pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Khristu wakhala akulamulira mpingo wa otsatira ake odzozedwa wapadziko lapansi pano monga Mfumu. (Akolose 1:13) Kenako mu 1914, Khristu analandira ulamuliro ndipo ali ndi mphamvu pa “ufumu wa dziko.” Choncho, Akhristu odzozedwa ndi akazembe a Ufumu wa Mesiya.—Chivumbulutso 11:15.

^ ndime 8 Onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, patsamba 323 mpaka 327, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.