Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZAKUMAPETO

Kuchitira Sailuti Mbendera, Kuvota Ndiponso Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali

Kuchitira Sailuti Mbendera, Kuvota Ndiponso Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali

Kuchitira sailuti mbendera. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti kuchitira sailuti kapena kuweramira mbendera, kumene nthawi zambiri anthu amachita akamaimba nyimbo ya fuko, ndi mwambo wopembedza womwe umasonyeza kuti boma kapena atsogoleri ake ndi amene amapulumutsa anthu, osati Mulungu. (Yesaya 43:11; 1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Mmodzi wa atsogoleri ngati amenewa inali Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo. Pofuna kusonyeza mphamvu zake komanso kuti inkakonda kupembedza, mfumu yamphamvu imeneyi inamanga fano lalikulu ndipo inalamula anthu ake kuti aligwadire pamene nyimbo, yofanana ndi nyimbo ya fuko, inkaimbidwa. Komabe, anyamata atatu achiheberi, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, anakana kugwadira fanolo, ngakhale pamene anauzidwa kuti aphedwa.​—Danieli, chaputala 3.

Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Carlton Hayes, analemba kuti masiku ano, “anthu okonda kwambiri dziko lawo amakhulupirira ndiponso amalambira mbendera . . . Anthu akamadutsa ndi mbendera, amuna amavula zipewa, ndiponso alakatuli amalakatula ndakatulo ndipo ana amaimba nyimbo polemekeza mbenderayo.” Katswiriyu ananenanso kuti, posonyeza kukonda dziko lawo, maboma amakhazikitsa “masiku a holide,” monga tsiku lokumbukira kulandira ufulu wodzilamulira. Amakhazikitsanso maholide okumbukira anthu ena amene anamenyera ufulu wa dzikolo ndipo amawalemekeza kwambiri ngati mmene amalemekezera “anthu oyera mtima.” Amakhalanso ndi malo amene anthu  amapita pofuna kulemekeza kapena kupembedza boma lawo ndi zizindikiro zake, kuphatikizapo mbendera. Pa mwambo wina wa boma ku Brazil, mkulu wa Khoti Lalikulu la Asilikali m’dzikolo anati: “Mbendera imalemekezedwa kwambiri ndi kulambiridwa . . . ngati mmene timalambirira dziko lathu.” Buku lina linati: “Mbendera ndi yopatulika mofanana ndi mtanda.”​—The Encyclopedia Americana.

Buku talitchulali, posachedwapa linanenanso kuti “kuimba nyimbo ya fuko kumasonyeza kuti umakonda kwambiri dziko lako ndipo nthawi zambiri kumakhala kupempha Mulungu kuti ateteze ndi kutsogolera anthu ndi atsogoleri awo.” Choncho, atumiki a Yehova salakwitsa akamaona kuti miyambo yosonyeza kukonda dziko lako, monga kuchitira sailuti mbendera ndi kuimba nyimbo ya fuko kuli ngati kulambira. Ndipotu, pothirira ndemanga pa chifukwa chimene ana asukulu a Mboni za Yehova a ku United States amakanira kuweramira mbendera kapena kulumbira kuti adzakhala okhulupirika ku dziko lawo, buku lina linati: “Pambuyo pozenga milandu ingapo, Khoti Lalikulu [la ku United States] tsopano latsimikizira kuti miyambo ngati imeneyi, imene imachitika tsiku ndi tsiku, ndi yokhudzana ndi kupembedza.”​—The American Character.

Ngakhale kuti anthu a Yehova sachita nawo miyambo imene amaona kuti ndi yosagwirizana ndi Malemba, iwo saletsa ena amene akufuna kuchita miyambo imeneyi. Ndiponso sanyoza zizindikiro za boma monga mbendera, ndipo amadziwa kuti maboma okhazikitsidwa mwa malamulo ndi amene Baibulo limati “olamulira akuluakulu” omwe amagwira ntchito ngati “mtumiki wa Mulungu.” (Aroma 13:​1-4) Choncho, Mboni za Yehova zimatsatira malangizo akuti tizipemphera “m’malo mwa mafumu ndi m’malo mwa anthu onse apamwamba.” Komabe, cholinga chathu n’chakuti “tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso tikhale oganiza bwino.”​—1 Timoteyo 2:2.

Kuvota pa zisankho zandale. Akhristu oona saletsa anthu ena kuvota. Ndipo sachita nawo zionetsero zosonyeza kusavomereza mmene zisankho zayendera, koma amagonjera atsogoleri amene asankhidwa. Komabe, iwo salowerera ngakhale pang’ono nkhani zandale za dziko lililonse. (Mateyu 22:21; 1 Petulo 3:16) Kodi Mkhristu angatani ngati akukhala m’dziko limene limakakamiza aliyense kuvota, kapena ngati anthu amachitira nkhanza aliyense  amene sanapite kukavota? Kumbukirani kuti Sadirake, Mesake, ndi Abedinego anapita kuchigwa cha Dura monga mmene mfumu inalamulira. Choncho, Mkhristu amene ali m’dziko ngati limeneli, angathe kupita kumalo oponyera votiwo ngati chikumbumtima chake chikumulola. Komabe, ayenera kusamala kuti asachite chilichonse chosonyeza kulowerera ndale. Iye ayenera kukumbukira mfundo 6 zotsatirazi:

  1. Otsatira a Yesu ‘sali mbali ya dzikoli.’​—Yohane 15:19.

  2. Akhristu amaimira Khristu ndi Ufumu wake.​—Yohane 18:36; 2 Akorinto 5:20.

  3. Mpingo wachikhristu umakhulupirira zofanana, ndipo anthu ake ndi ogwirizana chifukwa amakondana kwambiri ngati mmene Khristu amawakondera.​—1 Akorinto 1:10; Akolose 3:14.

  4. Anthu amene amasankha mtsogoleri amakhala ngati akuchita nawo chilichonse chimene mtsogoleriyo angachite, kaya chabwino kapena choipa.​—Onani mfundo zimene zili m’mawu opezeka pa 1 Samueli 8:​5, 10-18 ndi pa 1 Timoteyo 5:22.

  5. Aisiraeli atafuna kukhala ndi munthu wowalamulira, Yehova anaona kuti chinali chizindikiro chakuti amukana ndipo sakufuna kuti akhale wolamulira wawo.​—1 Samueli 8:7.

  6. Akhristu ayenera kukhala ndi ufulu wolankhula akamauza anthu a chipani chilichonse za Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 24:14; 28:​19, 20; Aheberi 10:35.

Kugwira ntchito zosakhudzana ndi usilikali. M’mayiko ena, boma limalamula kuti anthu amene akana kulowa usilikali azigwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. Tisanavomere zogwira ntchito ngati zimenezi, tiyenera kupemphera, mwinanso kukambirana ndi Mkhristu mnzathu wachikulire mwauzimu, ndipo kenako tizigwiritsa ntchito chikumbumtima chathu posankha zochita mogwirizana ndi zimene tikudziwa pa nkhaniyi.​—Miyambo 2:​1-5; Afilipi 4:5.

Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiyenera ‘kumvera maboma ndiponso olamulira. Tikhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino. . . . Tikhale ololera.’ (Tito 3:​1, 2) Poganizira zimenezi, tingadzifunse mafunso otsatirawa: ‘Kodi kugwira ntchito imeneyi kungandichititse kulowerera ndale kapena kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga?’ (Mika 4:​3, 5; 2 Akorinto 6:​16, 17) ‘Kodi kugwira ntchito imeneyi kuzindilepheretsa kukwaniritsa maudindo anga achikhristu?’ (Mateyu 28:​19, 20; Aefeso 6:4; Aheberi 10:​24, 25) ‘Kapenanso,  kodi ntchito imeneyi ndi ya maola ochepa moti ingandipatse mpata wowonjezera utumiki wanga, kapena mpata wochita utumiki wanthawi zonse?’​—Aheberi 6:​11, 12.

Ngati Mkhristu, malinga ndi chikumbumtima chake, wasankha kugwira ntchito imeneyi m’malo mopita kundende, Akhristu anzake ayenera kulemekeza zimene wasankha. (Aroma 14:10) Komanso, ngati iye akuona kuti sangagwire ntchito imeneyi, Akhristu ena ayeneranso kulemekeza zimene wasankhazo.​—1 Akorinto 10:29; 2 Akorinto 1:24.