Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 14

Timakhala Okhulupirika ku Boma la Mulungu Lokha Basi

Timakhala Okhulupirika ku Boma la Mulungu Lokha Basi

CHOLINGA CHA MUTUWU

Atumiki a Mulungu sali mbali ya dziko chifukwa chakuti ndi okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu

1, 2. (a) Kodi otsatira a Yesu akhala akutsatira mfundo iti? (b) Kodi adani athu achita zotani pofuna kutigonjetsa ndipo chachitika n’chiyani?

YESU ataimirira pamaso pa Pilato yemwe anali wolamulira wamphamvu kwambiri mu mtundu wa Ayuda ananena mfundo yomwe yakhala yothandiza kwambiri kwa otsatira ake mpaka pano. Iye ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yoh. 18:36) Pilato anachititsa kuti Yesu aphedwe koma zolinga zawo zinalephera chifukwa pasanapite nthawi yaitali, Yesu anaukitsidwa. Mafumu amene ankalamulira mu Ufumu wamphamvu wa Roma anayesetsa kupha otsatira a Khristu koma zofuna zawo zinalephereka. Akhristu analalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse.—Akol. 1:23.

2 Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa mu 1914, maboma ena amphamvu amene ankalamulidwa ndi asilikali anayesetsa kuti aphe anthu onse a Mulungu. Koma zolinga zawo zinalephereka. Maboma ambiri komanso magulu andale ayesetsa kutikakamiza kuti tilowerere nawo mikangano yawo koma nawonso alephera kutichititsa kukhala osakhulupirika ku Ufumuwu. Masiku ano, anthu amene akulamuliridwa ndi Ufumuwu amapezeka pafupifupi m’dziko lililonse. Ngakhale kuti tikukhala m’mayiko osiyanasiyana, tili pa ubale weniweni wapadziko lonse, ndipo sitilowerera ngakhale pang’ono m’ndale zimene zimachitika m’dzikoli. Ubale umenewu ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira komanso kuti Mfumu Yesu Khristu akuyenga, kutsogolera ndiponso kuteteza atumiki ake. Tiyeni tione mmene Yesu Khristu wachitira zimenezi ndiponso milandu ina imene tawina yomwe ndi yolimbitsa chikhulupiriro kwambiri pamene tikupitirizabe kusakhala “mbali ya dziko.”—Yoh. 17:14.

Nkhani Yofunika Kwambiri

3, 4. (a) Kodi chinachitika n’chiyani pa nthawi imene Ufumu unkakhazikitsidwa? (b) Kodi nthawi zonse anthu a Mulungu akhala akumvetsa kuti sayenera kulowerera ndale? Fotokozani.

3 Ufumu wa Mulungu utangokhazikitsidwa kumene, kumwamba kunachitika nkhondo ndipo Satana anaponyedwa padziko lapansi. (Werengani Chivumbulutso 12:7-10, 12.) Padziko lapansi panachitikanso nkhondo imene inayesa chikhulupiriro cha anthu a Mulungu koma anthu a Mulunguwo anali ofunitsitsa kutsatira chitsanzo cha Yesu kuti asakhale mbali ya dziko. Koma poyamba sankadziwa zoyenera kuchita kuti asalowerere nawo ndale.

 4 Mwachitsanzo, Voliyumu VI ya buku la Millennial Dawn, * lomwe linasindikizidwa mu 1904, linalimbikitsa Akhristu kuti asamachite nawo nkhondo. Komabe, bukuli linanena kuti ngati Mkhristu atamulemba usilikali aziyesetsa kupempha kuti azigwira ntchito zina, osati kumenya nawo nkhondo. Ngati wapempha koma sizinatheke ndipo watumizidwa ku nkhondo, azionetsetsa kuti asaphe munthu. Pofotokoza mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, M’bale Herbert Senior, yemwe ankakhala ku Britain ndipo anabatizidwa m’chaka cha 1905, ananena kuti: “Abale sankamvetsa bwino nkhani imeneyi komanso panalibe malangizo omveka bwino othandiza Akhristu kudziwa ngati zinali zoyenera kulowa usilikali n’kumagwira ntchito zina osati kumenya nkhondo.”

5. Kodi Nsanja ya Olonda ya September 1, 1915, inathandiza bwanji anthu kumvetsa nkhani yosalowerera ndale?

5 Komabe, Nsanja ya Olonda ya September 1, 1915, inayamba kufotokoza nkhani imeneyi momveka bwino. Pofotokoza zimene zinalembedwa m’buku la Studies in the Scriptures, magazini ya Nsanja ya Olonda imeneyi inanena kuti: “Sitikudziwa ngati kuli koyenera kuti Mkhristu azilowa usilikali koma n’kumagwira ntchito zina osati kumenya nkhondo.” Koma bwanji ngati Mkhristu akuwopsezedwa kuti aphedwa chifukwa chokana kuvala yunifomu ndiponso kugwira ntchito ya usilikali? Nkhaniyi inafotokoza kuti: “Kodi inuyo mungasankhe chiyani pa zinthu ziwiri izi: Kuphedwa chifukwa chokhala wokhulupirika kwa Kalonga Wamtendere komanso chifukwa chosafuna kuphwanya malamulo Ake, kapena kuphedwa mukuthandiza komanso kugwirira ntchito mafumu a pansi pano, zomwe ndi kusamvera mwadala zimene Mfumu ya Kumwamba imaphunzitsa? Pa imfa ziwirizi, tingasankhe kuphedwa chifukwa chokhala okhulupirika kwa Mfumu yathu ya Kumwamba.” Ngakhale kuti magaziniyi inanena mfundo yamphamvuyi, inamaliza ndi kuti: “Sitikukakamiza anthu kuti azitsatira mfundo imeneyi. Tikungopereka maganizo chabe.”

6. Kodi mwaphunzira chiyani kwa M’bale Herbert Senior?

6 Abale ena anamvetsa kuti Mkhristu sayenera kulowa usilikali ndipo anali okonzeka kukumana ndi mavuto chifukwa chotsatira mfundo imeneyi. M’bale Herbert Senior yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Ine sindinkaona kusiyana kulikonse ngati munthu akugwira ntchito yotsitsa zipolopolo m’sitima [komwe si kumenya nkhondo] ndi kuika zipolopolozo mu mfuti n’kumawombera anthu.” (Luka 16:10) M’bale Senior sanalowe usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndipo anakamutsekera kundende. M’baleyu pamodzi ndi abale ena 4 anali pagulu la anthu 16 omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Pagululi panali anthu ena ochokera m’zipembedzo zina ndipo anakawatsekera kundende ya Richmond ku Britain. Pa nthawi ina, Herbert komanso anthu ena amene ankaimbidwa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo, anatengedwa mwachinsinsi n’kupita nawo ku dziko la France kuti akamenye nkhondo. Ali kumeneko anawagamula kuti aphedwe ndipo m’baleyu pamodzi ndi anthu ena anawaika pamzere kuti awawombere koma sanawawombere. M’malomwake anawagamula kuti akhale m’ndende zaka 10.

“Ndinamvetsa kuti anthu a Mulungu ankayenera kukhala pamtendere ndi munthu aliyense ngakhale pa nthawi ya nkhondo.”—Simon Kraker (Onani ndime 7)

7. Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkayamba, kodi anthu a Mulungu anali atamvetsa mfundo iti?

 7 Pa nthawi imene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkayamba, anthu a Yehova monga gulu anamvetsa bwino zimene ayenera kuchita kuti asalowerere ndale komanso zimene ayenera kuchita ngati akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu. (Mat. 26:51-53; Yoh. 17:14-16; 1 Pet. 2:21) Mwachitsanzo, mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1939, munali nkhani yofunika kwambiri yomwe inali ndi mutu wakuti, “Kusalowerera Ndale.” Nkhaniyi inafotokoza kuti: “Anthu amene anachita pangano ndi Yehova ayenera kutsatira lamulo lakuti sayenera kulowerera nawo ngakhale pang’ono mayiko akamamenya nkhondo.” Pofotokoza mmene anamvera atawerenga nkhaniyi, M’bale Simon Kraker, yemwe kenako anakatumikira kulikulu lathu ku Brooklyn, New York, ananena kuti: “Ndinamvetsa kuti anthu a Mulungu ankayenera kukhala pamtendere ndi munthu aliyense ngakhale pa nthawi ya nkhondo.” Chakudya chauzimu chimenechi chinabwera pa nthawi yake ndipo chinathandiza anthu a Mulungu kukonzekera chizunzo chomwe anakumana nacho chifukwa chokhala okhulupirika ku Ufumuwu.

Chizunzo Chinabwera Ngati “Mtsinje”

8, 9. Kodi ulosi umene mtumwi Yohane ananena unakwaniritsidwa bwanji?

8 Mtumwi Yohane analosera kuti Ufumu ukadzabadwa mu 1914, chinjoka, yemwe ndi Satana Mdyerekezi, chidzayesa kupha atumiki a Ufumu wa Mulungu powalavulira madzi ophiphiritsa  ochuluka ngati mtsinje. * (Werengani Chivumbulutso 12:9, 15.) Kodi ulosi wa Yohane unakwaniritsidwa bwanji? Kuyambira m’zaka za m’ma 1920, anthu a Mulungu akhala akuzunzidwa kwambiri. Abale ambiri omwe ankakhala ku North America pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse anamangidwa chifukwa chokhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. Mmodzi wa abale amenewa anali M’bale Kraker. Pa nthawi ya nkhondoyi, anthu ambiri omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha chipembedzo chawo anatsekeredwa m’ndende zosiyanasiyana za ku United States. Pa anthu amenewa ambiri anali a Mboni za Yehova moti pa akaidi atatu alionse, awiri ankakhala a Mboni.

9 Satana ndi ziwanda zake anayesetsa kusokoneza chikhulupiriro cha anthu amene ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu kulikonse komwe ali. M’mayiko onse a ku Africa, Europe ndi ku United States, anthu a Mulungu anakaonekera m’makhoti. Chifukwa chosafuna kulowerera nawo ndale, ambiri anamangidwa komanso kuvulazidwa kwambiri moti ena analumala. Ku Germany anthu a Mulungu anazunzidwa kwambiri chifukwa chokana kunena mawu otamanda Hitler, komanso kukana kulowa usilikali. Anthu pafupifupi 6,000 anatsekeredwa m’ndende pa nthawi imene chipani cha Nazi chinkalamulira ndipo anthu oposa 1,600 a ku Germany komanso ochokera ku mayiko ena anafera m’manja mwa anthu amene ankawazunza. Ngakhale kuti atumiki a Mulungu anakumana ndi zinthu zonsezi, Mdyerekezi analephera kuthetseratu gulu la anthu a Mulungu.—Maliko 8:34, 35.

“Dziko Lapansi” Linameza “M’tsinje”

10. Kodi “dziko” limaimira chiyani, ndipo lathandiza bwanji anthu a Mulungu?

10 Ulosi umene mtumwi Yohane analemba unasonyeza kuti “dziko lapansi,” omwe ndi olamulira amene amachita zinthu moganizira ena, adzameza “mtsinje,” womwe ukuimira chizunzo. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu olamulirawa adzathandiza anthu a Mulungu. Kodi mbali ya ulosi imeneyi yakwaniritsidwa bwanji? Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, “dziko” lakhala likulowererapo kuti lithandize anthu amene akutumikira mokhulupirika Ufumu wolamulidwa ndi Mesiya. (Werengani Chivumbulutso 12:16.) Mwachitsanzo, makhoti ena amphamvu ateteza ufulu wa Mboni za Yehova pa nkhani yokana kulowa usilikali komanso kuchita nawo miyambo ya mayiko. Choyamba, tiyeni tikambirane milandu ikuluikulu, yokhudza kulowa usilikali, imene Yehova anathandiza anthu ake kuti awine.—Sal. 68:20.

11, 12. N’chiyani chinachitikira M’bale Sicurella ndi M’bale Thlimmenos, ndipo zinthu zinatha bwanji?

11 United States. Anthony Sicurella analeredwa m’banja la Mboni ndipo anabatizidwa ali ndi zaka 15. Atakwanitsa zaka 21 anakalembetsa ku boma kuti ndi mtumiki wachipembedzo. Patapita zaka ziwiri, mu 1950, analemba chikalata chopita ku boma chopempha kuti amuike m’gulu la anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Ngakhale kuti bungwe lofufuza milandu ya anthu la Federal Bureau of Investigation silinamupeze ndi mlandu uliwonse, a Unduna Woona za Chilungamo sanavomere pempho lake ndipo mlanduwu unakambidwa ku khoti maulendo angapo. Kenako Khoti Lalikulu linamvetsera mlandu  wa M’bale Sicurella ndipo linagamula mosiyana ndi zimene khoti laling’ono linagamula moti chigamulocho chinali chokomera m’baleyu. Zimene khotili linagamula zinathandiza nzika zonse za ku United States zomwe zinkakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo.

12 Greece. Mu 1983, M’bale Iakovos Thlimmenos anamangidwa chifukwa chokana kuvala yunifomu ya asilikali ndipo anamutsekera m’ndende. Atamasulidwa, anafunsira ntchito yowerengetsera ndalama koma sanalembedwe ntchitoyi chifukwa anali atamangidwapo. Anakasuma nkhaniyi kukhoti koma sanawine, kenako anachita apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. M’chaka cha 2000, Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, yomwe inali ndi oweruza 17, inagamula mlanduwu mokomera m’baleyu ndipo chigamulo chimenechi chathandiza nzika zonse za ku Greece kuti zisamasalidwe. Chigamulo chimenechi chisanaperekedwe, abale ndi alongo a ku Greece oposa 3,500 anali ndi mbiri yoti anamangidwapo chifukwa chosafuna kulowerera ndale. Chigamulochi chitaperekedwa, dziko la Greece linalamula kuti achotse abale amenewa m’gulu la anthu okhala ndi mbiri yoti anamangidwapo. Komanso lamulo lopereka ufulu kwa nzika zonse za ku Greece kuti zikhoza kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali, limene linali litakhazikitsidwa zaka zingapo m’mbuyomo, analiwonjezera mphamvu pamene malamulo a dzikolo ankakonzedwanso.

“Ndisanalowe m’khoti ndinapemphera kwa Yehova kenako ndinaona kuti anandithandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo.”—Ivailo Stefanov (Onani ndime 13)

13, 14. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya M’bale Ivailo Stefanov ndi M’bale Vahan Bayatyan?

13 Bulgaria. Mu 1994, M’bale Ivailo Stefanov anatengedwa kuti akayambe usilikali ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 19. Iye anakana kulowa usilikali ndiponso kugwira ntchito zina zimene ankapatsidwa ndi asilikali. Anagamulidwa kuti akakhale m’ndende miyezi 18 koma anachita apilo ponena kuti ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake. Kenako mlandu wakewo unapita ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Mu 2001, mlanduwu usanakambidwe ndi khotili, dziko la Bulgaria linakonza zoti lingokambirana ndi m’baleyu. Boma la Bulgaria linakhululukira M’bale Stefanov komanso nzika zonse za m’dzikoli zomwe zinali zokonzeka kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. *

14 Armenia. M’chaka cha 2001 M’bale Vahan Bayatyan anakwanitsa zaka zimene boma la Armenia limafuna kuti munthu alowe usilikali. * Koma m’baleyu anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndipo anamuweruza kuti akhale m’ndende. M’baleyu anachita apilo koma nthawi zonse ankaluza. Mu September, 2002, M’bale Bayatyan anamangidwa ndipo anamugamula kuti akhale m’ndende zaka ziwiri ndi hafu, koma anamasulidwa atangokhalamo miyezi 10 ndi hafu. Pa nthawi imene anali kundendeyi anachita apilo mlandu wakewu ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya ndipo khotili linamvetsera mlandu wakewu. Koma pa October 27, 2009, Khotili linagamula kuti M’bale Bayatyan ndi wolakwa. Chigamulo chimenechi chinasokoneza kwambiri abale a ku Armenia amene ankaimbidwa mlandu wofanana  ndi womwewu. Koma Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inaonanso chigamulo chimene chinaperekedwa pa mlanduwu. Pa July 7, 2011, Khotilo linagamula mlanduwu mokomera M’bale Vahan Bayatyan. Aka kanali koyamba kuti Khoti Lalikululi livomereze kuti munthu akhoza kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira m’chipembedzo chake. Izi n’zogwirizana ndi ufulu wofotokoza maganizo ake, wosankha zinthu motsatira chikumbumtima chake komanso ufulu wa chipembedzo umene uli m’dzikoli. Chigamulo chimenechi chikuteteza ufulu wa Mboni za Yehova komanso wa anthu mamiliyoni ambirimbiri m’mayiko amene ali mu Bungwe la Mayiko a ku Ulaya. *

Abale a ku Armenia amasulidwa kundende pambuyo pa chigamulo chimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka.

Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko

15. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova amakana kuchita nawo miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo?

15 Anthu a Yehova amakhala okhulupirika ku Ufumu wa Mesiya pokana kulowa usilikali komanso pokana mwaulemu kuchita nawo miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo. Anthu anayamba kukonda kwambiri dziko lawo pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Mayiko ambiri amafuna kuti nzika zawo  zizikhala zokhulupirika kudzikolo ndiponso zizichita nawo zinthu ngati kuimba nyimbo ya fuko, kulumbira kuti zidzakhala zokhulupirika kudzikolo kapena kuchitira sawatcha mbendera ya dziko lawo. Komabe, ife timadzipereka kwa Yehova yekha basi. (Eks. 20:4, 5) Chifukwa chotsatira mfundo imeneyi timazunzidwa kwambiri. Komabe, Yehova wagwiritsa ntchito “dziko” kuti athetse ena mwa mavuto amenewa. Tiyeni tione milandu ina yochititsa chidwi yomwe Yehova kudzera mwa Khristu watithandiza kuti tiwine.—Sal. 3:8.

16, 17. N’chiyani chinachitikira Lillian ndi William Gobitas, ndipo mwaphunzira chiyani pa nkhani imeneyi?

16 United States. Mu 1940, Khoti Lalikulu la ku America linagamula kuti Mboni za Yehova zinali zolakwa pa mlandu wa ana a M’bale Gobitas. Mlanduwu unali pakati pa ana a m’baleyu ndi sukulu ya Minersville School District. Lillian Gobitas, * yemwe anali ndi zaka 12, ndi mchimwene wake William, yemwe anali ndi zaka 10, ankafuna kukhala okhulupirika kwa Yehova. Anawa anakana kuchitira sawatcha mbendera komanso kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kudziko lawo. Chifukwa cha zimenezi anawachotsa sukulu. Nkhaniyi inafika ku Khoti Lalikulu ndipo khotili linagamula kuti oyang’anira sukuluyi anatsatira malamulo a dziko la America chifukwa cholinga cha malamulowo ndi “kukhazikitsa mtendere m’dzikolo.” Chigamulo chimenechi chinachititsa kuti anthu ambiri ayambe kuzunzidwa. Ana ambiri a Mboni anachotsedwa sukulu, anthu akuluakulu anachotsedwa ntchito ndipo abale ndi alongo ena anamenyedwa ndi magulu a anthu achiwawa. Buku lina lamutu wakuti, The Lustre of Our Country linanena kuti, “kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova kuyambira mu 1941 mpaka mu 1943, ndi umboni wa tsankho la zipembedzo limene linali lisanachitikepo m’zaka za m’ma 1900 ku America.”

17 Koma adani a Mulunguwa anasangalala kwa nthawi yochepa. M’chaka cha 1943, Khoti Lalikululi linaweruza mlandu wina wofanana ndi wa ana a M’bale Gobitas. Mlanduwu unali pakati pa Bungwe la zamaphunziro la West Virginia ndi Barnette. Pa nthawiyi Khoti Lalikululi linagamula mlanduwu mokomera Mboni za Yehova. Aka kanali koyamba m’mbiri yonse ya America kuti Khoti Lalikulu lisinthe zimene linali litangogamula kumene pa mlandu wina wofanana ndi womwewu. Chigamulo chimenechi chitaperekedwa, anthu anasiya kuzunza Mboni za Yehova ku America. Chigamulochi chinathandizanso kuti dzikoli lizionetsetsa kuti munthu aliyense, yemwe ndi nzika ya dzikoli, ufulu wake ukulemekezedwa.

18, 19. Kodi Pablo Barros ananena kuti n’chiyani chinamuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika, nanga atumiki ena a Yehova angatsanzire bwanji chitsanzo chake?

18 Argentina. M’chaka cha 1976, Pablo Barros yemwe anali ndi zaka 8 ndi Hugo Barros yemwe anali ndi zaka 7, anachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchita nawo mwambo wokweza mbendera. Pa nthawi ina, mphunzitsi wamkulu wa pasukulupo, yemwe anali wamkazi, anakankha Pablo ndiponso anam’menya m’mutu. Mphunzitsiyu ankauza anawa kuti azitsalira kwa ola limodzi akaweruka n’cholinga choti aziwakakamiza kuchita miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo. Pofotokoza zimene zinkachitika, Pablo anati: “Ndimaona kuti Yehova akanapanda kundithandiza, sindikanakwanitsa kukhalabe wokhulupirika.”

 19 Nkhaniyi itapita ku khoti, woweruza anagwirizana ndi zoti Pablo ndi Hugo achotsedwe sukulu. Komabe, iwo anachita apilo mlanduwu ku Khoti Lalikulu la ku Argentina. Ndipo m’chaka cha 1979, khotili linasintha chigamulo chimene khoti laling’ono lija linapereka ponena kuti: “Chilangochi [chochotsa ana sukulu] n’chosemphana ndi ufulu wophunzira (Article 14) komanso n’chosagwirizana ndi udindo wa boma womwe ndi kuonetsetsa kuti mwana aliyense alandire maphunziro (Article 5).” Chigamulo chimenechi chinathandiza ana a Mboni za Yehova pafupifupi 1,000. Ana ena amene anali atatsala pang’ono kuchotsedwa sukulu sanawachotse ndipo ena amene anali atachotsedwa kale, ngati Pablo ndi Hugo, anayambiranso kuphunzira sukulu za boma.

Achinyamata ambiri a Mboni asonyeza kuti ndi okhulupirika akamayesedwa

20, 21. Kodi mlandu wa Roel ndi Emily Embralinag walimbikitsa bwanji chikhulupiriro chanu?

20 Philippines. Mu 1990, Roel Embralinag, * wazaka 9, ndi mchemwali wake dzina lake Emily, wazaka 10, pamodzi ndi ana ena a Mboni pafupifupi 66, anachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchitira sawatcha mbendera. A Leonardo, omwe ndi bambo awo a Roel ndi Emily, anayesa kukambirana ndi akuluakulu a pasukulupo koma sizinathandize. Nkhaniyi itafika povuta, a Leonardo  anachita apilo ku Khoti Lalikulu koma analibe ndalama zolipirira loya woti akawaimire pa mlanduwu. Banja lawo lonse linapemphera kwa Yehova mochonderera kuti awathandize. Pa nthawi yonseyi, anawo ankangokhalira kunyozedwa. Leonardo ankaona kuti ngati sangapeze loya ndiye kuti sangawine mlanduwu chifukwa iwowo sanaphunzire za uloya.

21 Koma kenako zinachitika kuti loya wina, dzina lake Felino Ganal, yemwe poyamba ankagwira ntchito kukampani ina ya maloya yodziwika kwambiri m’dzikolo, anaimira banjali. Pa nthawi ya mlanduwu n’kuti M’bale Ganal atasiya kugwira ntchito kukampani ija ndipo anali atakhala wa Mboni za Yehova. Oweruza onse anagamula mlanduwu mokomera Mboni za Yehova ndipo anathetsa lamulo lochotsa sukulu ana a Mboni. Apanso, anthu amene ankafuna kusokoneza chikhulupiriro cha anthu a Mulungu analephera.

Kusalowerera Ndale Kumathandiza Anthu Kukhala Mogwirizana

22, 23. (a) Kodi n’chiyani chachititsa kuti tiwine milandu ikuluikulu yambiri? (b) Kodi ubale komanso mtendere umene tikusangalala nawo padziko lonse ndi umboni wa chiyani?

22 Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a Yehova kuti awine milandu yambirimbiri chonchi? Ngakhale kuti sitigwirizana ndi gulu lililonse la ndale, oweruza amtima wabwino a m’mayiko komanso m’makhoti ambiri atiteteza kwa anthu otsutsa, zomwe zachititsa kuti mayiko ena akhazikitse malamulo otetezera ufulu wa anthu. Sitikukayikira kuti Khristu ndi amene wakhala akutithandiza kuti tiwine milandu yonseyi. (Werengani Chivumbulutso 6:2.) Koma kodi n’chifukwa chiyani timapititsa milandu kumakhoti? Cholinga chathu sichikhala kusintha malamulo a boma. Koma timafuna kuti tikhale ndi ufulu wotumikira Mfumu yathu, Yesu Khristu, popanda chosokoneza chilichonse.—Mac. 4:29.

23 M’dziko lomwe muli mavuto a zandale komanso kusankhana mitundu, Mfumu yathu Yesu Khristu yathandiza otsatira ake padziko lonse kuti apitirizebe kusalowerera m’mikangano ya m’mayiko awo. Satana walephera kutigawanitsa ndiponso kutigonjetsa. Ufumu wasonkhanitsa anthu ambiri amene safuna ‘kuphunziranso nkhondo.’ Ubale komanso mtendere umene tikusangalala nawo padziko lonse lapansi ndi wodabwitsa kwambiri ndipo ndi umboni wosatsutsika wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira.—Yes. 2:4.

^ ndime 4 Bukuli limadziwikanso ndi mutu wakuti The New Creation. Patapita nthawi, mabuku a Millennial Dawn anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Studies in the Scriptures.

^ ndime 8 Kuti mumve zambiri za ulosiwu, werengani buku lakuti, Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira, mutu 27, patsamba 184-186.

^ ndime 13 Chigamulo chimenechi chinatanthauza kuti boma la Bulgaria linafunikanso kupereka mwayi wa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali ngakhale pang’ono kwa anthu onse amene ankakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo.

^ ndime 14 Kuti mumve nkhani yonse bwinobwino, werengani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2012, patsamba 29-31.

^ ndime 14 Pa zaka 20, boma la Armenia linamanga achinyamata a Mboni oposa 450. Mu November 2013, achinyamata omwe anali adakali m’ndende anamasulidwa.

^ ndime 16 Akhoti analakwitsa kalembedwe ka dzinali m’mabuku awo.

^ ndime 20 Akhoti analakwitsa polemba dzinali m’mabuku awo ndipo analilemba kuti Ebralinag.