Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse

Muzimva Mawu a Yehova Nthawi Zonse

“Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako, akuti: ‘Njira ndi iyi.’”—YES. 30:21.

1, 2. Kodi Yehova amapereka bwanji malangizo kwa atumiki ake?

KUYAMBIRA kale, anthu akhala akulandira malangizo ochokera kwa Yehova m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Mulungu anauza anthu ena zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo kapena kuwapatsa ntchito zoti agwire. Iye ankachita zimenezi pogwiritsa ntchito angelo, masomphenya kapena maloto. (Num. 7:89; Ezek. 1:1; Dan. 2:19) Koma nthawi zina ankagwiritsa ntchito anthu ena kuti apereke malangizo kwa atumiki ake. Kaya malangizowo abwera bwanji, anthu amene ankawatsatira ankadalitsidwa.

2 Masiku ano, Yehova amatsogolera anthu ake pogwiritsa ntchito Baibulo, mzimu woyera ndiponso mpingo wake. (Mac. 9:31; 15:28; 2 Tim. 3:16, 17) Malangizo amene timalandira kwa Yehova ndi omveka bwino kwambiri moti zili ngati ‘makutu athu akumva mawu kumbuyo kwathu, akuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu anthu inu.”’ (Yes. 30:21) Yesu amatiuzanso mawu a Yehova akamatsogolera mpingo pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Malangizo amenewa ndi ofunika kwambiri chifukwa ndi amene angatithandize kupeza moyo wosatha.—Aheb. 5:9.

3. N’chiyani chingatilepheretse kutsatira malangizo a Yehova? (Onani chithunzi patsamba 21.)

 3 Satana Mdyerekezi amayesetsa kutisokoneza kuti tisamvere malangizo ochokera kwa Yehova. Komanso ‘mtima wathu wonyenga’ ungatilepheretse kumvera malangizowo. (Yer. 17:9) Choncho tiyeni tione mmene tingapewere zinthu zomwe zingatilepheretse kumvetsera mawu a Mulungu. Tionanso kuti kupemphera nthawi zonse kungateteze ubwenzi wathu ndi Yehova.

KODI TINGATANI KUTI SATANA ASATIPUSITSE?

4. Kodi Satana amasokoneza bwanji maganizo a anthu?

4 Satana amafalitsa mabodza n’cholinga chosokoneza maganizo a anthu. (Werengani 1 Yohane 5:19.) Padziko lonse, anthu amawerenga nyuzi ndi mabuku, kumvetsera wailesi, kuonera TV kapena kugwiritsa ntchito Intaneti. M’zinthu zimenezi mumapezeka zosangalatsa. Koma vuto ndi lakuti zimalimbikitsanso makhalidwe komanso maganizo osemphana ndi mfundo za Yehova. (Yer. 2:13) Nkhani komanso zosangalatsa zina zimasonyeza kuti palibe vuto ngati amuna kapena akazi akukwatirana okhaokha. Anthu ambiri amaona kuti mfundo za m’Baibulo pa nkhaniyi zimangophera anthu ufulu.—1 Akor. 6:9, 10.

5. Kodi tingapewe bwanji kuyendera maganizo a Satana amene afala m’dzikoli?

5 Kodi anthu amene amakonda Yehova angapewe bwanji kuyendera maganizo a Satana amene afalawa? N’chiyani chingawathandize kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika? Chofunika ndi “kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu” a Mulungu. (Sal. 119:9) Baibulo lili ndi malangizo otithandiza kusiyanitsa mfundo zoona ndi zabodza. (Miy. 23:23) Yesu anagwira Malemba n’kunena kuti “mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova” ndi amene angathandize munthu kukhala ndi moyo. (Mat. 4:4) Choncho tiyenera kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. Mwachitsanzo, Mose asanalembe lamulo la Yehova loletsa chigololo, Yosefe anazindikira kuti zimenezi n’zolakwika pamaso pa Mulungu. Mkazi wa Potifara anayesetsa kumunyengerera koma anakanitsitsa poopa kukhumudwitsa Yehova. (Werengani Genesis 39:7-9.) Zimenezi zinachitika kwa nthawi yaitali ndithu koma Yosefe sanalole kuti zonena zakezo zimulepheretse kuchita zimene Mulungu amafuna. Kuti tithe kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika, tiyenera kumvetsera mawu a Yehova n’kupeweratu mabodza amene Satana amafalitsa.

6, 7. Kodi tingapewe bwanji malangizo oipa a Satana?

6 M’dzikoli muli zipembedzo zambirimbiri zomwe zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana. Choncho anthu amaona kuti n’zosatheka kupeza chipembedzo choona. Koma Yehova amapereka malangizo omveka bwino amene angathandize anthu ofuna kumumvera. Choncho aliyense ayenera kusankha amene akufuna kumumvera. N’zosatheka kumvetsera anthu awiri nthawi imodzi. Ndiye tiyenera ‘kudziwa bwino mawu’ a Yesu n’kumawatsatira  chifukwa Yehova wasankha Yesuyo kuti azitsogolera nkhosa zake.—Werengani Yohane 10:3-5.

7 Yesu anati: “Samalani zimene mukumvazi.” (Maliko 4:24) Malangizo ochokera kwa Yehova ndi olondola komanso omveka bwino. Choncho tiyenera kukonzekeretsa mtima wathu kuti tiwalandire n’kumawatsatira. Koma tikapanda kusamala, tikhoza kumayendera malangizo a Satana m’malo motsatira malangizo othandiza a Yehova. Musalole kupusitsidwa ndi zinthu monga nyimbo, mafilimu, mapulogalamu a pa TV, mabuku, anzanu, aphunzitsi kapena akatswiri a zinthu zina.—Akol. 2:8.

8. (a) Kodi mtima wathu ungatikodwetse bwanji mu msampha wa Satana? (b) Kodi chingachitike n’chiyani tikanyalanyaza zizindikiro zoti tayamba kulakalaka zoipa?

8 Satana amadziwa kuti anthufe tili ndi zilakolako zina chifukwa cha uchimo ndiye amafuna kupezerapo mwayi. Zimakhala zovuta kukhalabe okhulupirika tikamayesedwa pa zinthu ngati zimenezi. (Yoh. 8:44-47) Kodi tingatani kuti tisagonje? Tayerekezerani kuti munthu wina akutengeka ndi zimene zikumusangalatsa pa nthawiyo mpaka kufika pochita zinthu zolakwika zimene poyamba sankaganiza kuti angazichite. (Aroma 7:15) Kodi tingati vuto lagona pati? N’kutheka kuti munthuyu ankasiya pang’onopang’ono kumvetsera mawu a Yehova. Mwina sanaone zizindikiro zoti wayamba kulakalaka zoipa mumtima mwake kapena anangonyalanyaza zizindikirozo. Mwachitsanzo, mwina anasiya kupemphera, kulalikira mwakhama kapena kupezeka pa misonkhano. Ndiyeno anayamba kutengeka ndi zofuna za mtima wake n’kuchita zinthu zimene ankadziwa kuti n’zolakwika. Tikhoza kupewa zoterezi ngati tikhala tcheru kuti tione zizindikiro zoti tayamba kulakalaka zoipa n’kusinthiratu. Tikamamvetsera mawu a Yehova tidzapeweratu zonena za ampatuko.—Miy. 11:9.

9. Kodi kuzindikira mwamsanga ngati tayamba kulakalaka zoipa kungatipulumutse bwanji?

9 Matenda akatulukiridwa mwamsanga zimathandiza kuti munthu asamwalire nawo. Nafenso tingapewe mavuto akuluakulu tikatulukira mwamsanga kuti tayamba kulakalaka zoipa. Ndiye tikangozindikira zimenezi, tizisinthiratu. Tikapanda kutero ‘Mdyerekezi angatigwire amoyo kuti akwaniritse cholinga chake.’ (2 Tim. 2:26) Kodi tingatani ngati tazindikira kuti tayamba kusochera? Tiyenera kudzichepetsa n’kubwerera kwa Yehova mwamsanga ndipo tiziyesetsa kumumvetsera ndi mtima wathu wonse. (Yes. 44:22) Tisaiwale  kuti kulakwitsa zinthu zina kungachititse kuti tizunzike ndi zotsatira zake kwa moyo wathu wonse m’dziko loipali. Bola tizisithiratu tikangozindikira kuti mtima wathu wayamba kutisocheretsa.

Kodi kuchita khama pa zinthu zokhudza kulambira kungakutetezeni bwanji kwa Satana? (Onani ndime 4 mpaka 9)

KODI TINGAPEWE BWANJI KUDZIKUZA NDIPONSO DYERA?

10, 11. (a) Kodi munthu wodzikuza amatani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Kora, Datani ndi Abiramu?

10 Tizikumbukira nthawi zonse kuti mtima wathu ungatisocheretse. Zilakolako zathu zauchimo zimakhala zamphamvu kwambiri. Mwachitsanzo, kudzikuza ndiponso dyera zingatilepheretse kumvetsera mawu a Yehova ndipo tingayambe kuyenda panjira yoipa. Munthu wodzikuza amadziona ngati wapamwamba. Mwina angaone kuti akhoza kuchita chilichonse chimene akufuna ndipo palibe amene angamuuze zochita. Choncho akhoza kuona kuti sayenera kutsatira malangizo a Akhristu anzake, akulu kapenanso gulu la Mulungu. Munthu wotereyu amayamba kutalikirana ndi Yehova moti samva bwinobwino mawu ake.

11 Pamene Aisiraeli anali m’chipululu, Kora, Datani ndi Abiramu anapandukira Mose ndi Aroni. Chifukwa chodzikuza, anakonza zoti alambire Yehova m’njira yawoyawo. Kodi Yehova anatani? Iye anangowapha basi. (Num. 26:8-10) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Tikapandukira Yehova, zidzativuta. Tizikumbukiranso kuti “kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko.”—Miy. 16:18; Yes. 13:11.

12, 13. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu akhoza kukumana ndi mavuto chifukwa cha dyera. (b) Perekani chitsanzo chosonyeza zimene zingachitike ngati munthu sakudziletsa pa nkhani ya dyera.

12 Tiyeni tsopano tikambirane za dyera. Nthawi zambiri munthu wadyera amachita zinthu mopitirira malire. Namani, yemwe anali mkulu wa asilikali a Siriya, ankadwala khate. Elisa atamuchiritsa, iye ankafuna kupereka mphatso koma Elisa anakana. Ndiyeno Gehazi, yemwe anali mtumiki wa Elisa, ankafuna kwambiri mphatsozo. Choncho ananena mumtima mwake kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, ndim’thamangira [Namani] kuti ndikatengeko zinthu zina kwa iye.” Iye anazemba n’kumuthamangiradi. Atamupeza anamunamiza kenako n’kumuuza kuti amupatse “talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.” Kodi chinachitika n’chiyani Gehazi atachita zinthu mobisira mneneri wa Yehova? Gehazi anayamba kudwala khate la Namani lija.—2 Maf. 5:20-27.

13 Dyera limayamba pang’onopang’ono. Koma ngati munthu sasintha, khalidweli limakula mwamsanga n’kufika poipa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Akani. Taonani mmene zinthu zinachitikira mofulumira kwambiri. Iye anati: “Nditaona chovala chamtengo wapatali cha ku Sinara, pakati pa katundu wotsalayo, chokongola m’maonekedwe, komanso masekeli a siliva 200, ndi mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50, ndinazikhumba zinthuzo, ndipo ndinazitenga.” M’malo modziletsa, Akani anachita dyera ndipo anaba zinthuzo n’kukazisunga muhema wake. Zimene anachitazi zitadziwika, Yoswa anamuuza kuti Yehova amulanga. Tsiku lomwelo, banja lonse la Akani linaphedwa. (Yos. 7:11, 21, 24, 25) Aliyense akhoza kuyamba dyera nthawi iliyonse. N’chifukwa chake timalangizidwa kuti “chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) N’zoona kuti nthawi zina maganizo oipa akhoza kubwera mumtima mwathu koma tiyenera kuwachotsa mwamsanga zinthu zisanafike poipa.—Werengani Yakobo 1:14, 15.

14. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikayamba mtima wodzikuza kapena wadyera?

14 Zotsatira za kudzikuza ndiponso dyera  zingakhale zoipa kwambiri. Kuganizira kwambiri zotsatirazo kungatithandize kuti tisasiye kumvetsera mawu a Yehova. (Deut. 32:29) M’Baibulo, Mulungu amatiuza zoyenera kuchita ndiponso ubwino wake. Koma amatiuzanso mavuto amene tingakumane nawo ngati sitichita zinthuzo. Tikayamba kulakalaka zinthu zina chifukwa cha kudzikuza kapena dyera tingachite bwino kwambiri kuganizira zotsatira zake. Tiziganizira mmene zingakhudzire ifeyo, anzathu komanso makamaka ubwenzi wathu ndi Yehova.

MUZIPEMPHERA KWA YEHOVA NTHAWI ZONSE

15. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yopemphera?

15 Yehova amatifunira zabwino kwambiri. (Sal. 1:1-3) Iye amatipatsa malangizo oyenera pa nthawi yoyenera. (Werengani Aheberi 4:16.) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, ankapemphera kwa Yehova nthawi zonse. Yehova ankamuthandiza ndiponso kumutsogolera m’njira zapadera. Mwachitsanzo, anatumiza angelo kudzamutumikira, anamupatsa mzimu woyera kuti uzimuthandiza ndiponso anamutsogolera posankha atumwi 12. Yehova analankhula kuchokera kumwamba mawu osonyeza kuti iye amasangalala ndi Yesu ndipo azimuthandiza. (Mat. 3:17; 17:5; Maliko 1:12, 13; Luka 6:12, 13; Yoh. 12:28) Nafenso tiyenera kupemphera kuchokera pansi pa mtima. (Sal. 62:7, 8; Aheb. 5:7) Tikatero ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambiri ndipo tizichita zinthu zomulemekeza.

16. Kodi tingatani kuti Yehova atithandize kumvetsera mawu ake?

16 Yehova amapereka malangizo ake kwaulere koma sakakamiza aliyense kuti aziwatsatira. Tiyeni tizimupempha kuti atipatse mzimu woyera chifukwa iye amapereka mowolowa manja. (Werengani Luka 11:10-13.) Ndi bwinonso kutsatira malangizo akuti: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.” (Luka 8:18) Mwachitsanzo, munthu sangapemphe Yehova kuti amuthandize kupewa chiwerewere koma pa nthawi imodzimodziyo n’kumaonera zolaula kapena mafilimu osonyeza zachiwerewerezo. Tiyenera kuchita zinthu zimene zingathandize kuti tilandire mzimu wa Yehova. N’zosachita kufunsa kuti Yehova amapereka mzimu wake pa misonkhano yampingo. Kumvetsera pa misonkhano kwathandiza atumiki a Yehova ambiri kupewa mavuto. Mfundo za pa misonkhano zinawathandiza kuzindikira kuti ayamba kulakalaka zoipa ndipo anasintha mwamsanga.—Sal. 73:12-17; 143:10.

TIZIMVETSERA MAWU A YEHOVA NTHAWI ZONSE

17. Kodi kudzidalira n’koopsa bwanji?

17 Tsopano taganizirani za Mfumu Davide. Iye ali wachinyamata anagonjetsa chimunthu champhamvu kwambiri dzina lake Goliyati. Kenako Davide anakhala msilikali komanso mfumu. Iye ankateteza Aisiraeli ndiponso kuwauza zoyenera kuchita. Koma pamene Davide anayamba kudzidalira, mtima wake unamusokoneza. Iye anafika pochita chigololo ndi Bati-seba ndipo anakonzanso zoti mwamuna wake aphedwe. Koma Davide atadzudzulidwa anadzichepetsa n’kuvomera tchimo lake ndipo anakonzanso ubwenzi wake ndi Yehova.—Sal. 51:4, 6, 10, 11.

18. N’chiyani chingatithandize kuti tizimvetsera mawu a Yehova nthawi zonse?

18 Tiyeni tizitsatira malangizo a pa 1 Akorinto 10:12 n’kumapewa kudzidalira. Anthufe ‘sitingawongolere mapazi athu’ choncho tiyenera kulola Yehova kuti azititsogolera. Tikapanda kutero, tidzatsogoleredwa ndi Satana. (Yer. 10:23) Tiyeni tizipemphera mosalekeza ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera. Tikatero tidzamvetsera mawu a Yehova nthawi zonse.