Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZAKUMAPETO

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yothetsa Banja ndi Kupatukana

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yothetsa Banja ndi Kupatukana

Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azikhala okhulupirika ku pangano lawo la ukwati. Pokwatitsa mwamuna ndi mkazi oyambirira, Yehova anati: ‘Mwamuna . . . adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’ Patapita nthawi Yesu Khristu anabwereza mawu omwewo, koma anawonjezera kuti: “Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Genesis 2:24; Mateyu 19:​3-6) Chotero, Yehova ndi Yesu amafuna kuti banja lisamathe pokhapokha ngati mmodzi wamwalira. (1 Akorinto 7:39) Popeza banja ndi lopatulika, anthu sayenera kuona kuthetsa banja ngati nkhani yaing’ono. Ndipotu, Yehova safuna kuti anthu azithetsa mabanja popanda zifukwa za m’Malemba.​—Malaki 2:​15, 16.

 Kodi ndi zifukwa za m’Malemba ziti zimene zimalola anthu kuthetsa banja? Yehova amadana ndi chigololo ndiponso dama. (Genesis 39:9; 2 Samueli 11:​26, 27; Salimo 51:4) Ndipo amanyansidwa kwambiri ndi chigololo moti amaona kuti ndi chifukwa chomveka choti anthu athetse banja. (Kuti mudziwe tanthauzo la dama, onani Mutu 9, ndime 7, pamene pafotokozedwa za dama.) Yehova amapatsa munthu wosalakwayo ufulu wosankha kaya kukhalabe ndi mkazi kapena mwamuna wake amene wachita chigololo kapena kusiyana naye. (Mateyu 19:9) Choncho, ngati munthu wosalakwayo wasankha kusiyana ndi mnzakeyo, sanalakwe. Komabe, mpingo wachikhristu sulimbikitsa munthu aliyense kuthetsa banja. Ndipotu, nthawi zina munthu wosalakwayo angasankhe zokhalabe ndi mwamuna kapena mkazi wake amene wachita chigololo, makamaka ngati walapa moona mtima. Komabe, anthu amene ali ndi chifukwa cha m’Malemba chothetsera banja, ayenera kusankha okha zochita pa nkhaniyi ndipo ayenera kuvomereza zilizonse zimene zingachitike chifukwa cha zosankha zawozo.​—Agalatiya 6:5.

Pa mavuto ena aakulu, Akhristu ena asankha kupatukana kapena kuthetsa banja ngakhale kuti mwamuna kapena mkazi wawoyo sanachite chigololo. Zikakhala choncho, Baibulo limanena kuti wochokayo “akhale choncho wosakwatiwa [kapena wosakwatira]. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna [kapena mkazi] wakeyo.” (1 Akorinto 7:11) Mkhristu amene wachita zimenezi sayenera kufunafuna wina woti akwatirane naye. (Mateyu 5:32) Onani mavuto aakulu angapo amene angapangitse anthu ena kusankha kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wawo.

Kusathandiza banjalo mwadala. Banja lingamavutike kwambiri, lingamasowe zinthu zofunika kwambiri pa moyo, chifukwa chakuti mwamuna akulephera kupezera banjalo zinthuzo ngakhale kuti akhoza kuzipeza. Baibulo limati: “Ngati munthu sasamalira . . . a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Timoteyo 5:8) Ngati mwamuna ameneyu akukana kusintha khalidwe lakeli, mkazi angasankhe kupatukana naye mogwirizana ndi malamulo a boma pofuna kuteteza moyo wake komanso wa ana ake. Komabe, ngati mkazi wadandaula kuti mwamuna wake wachikhristu akukana  kusamalira banja lake, akulu achikhristu ayenera kusamalira nkhaniyi mosamala. Munthu angachotsedwe mumpingo ngati akukana kusamalira banja lake.

Nkhanza. Munthu wankhanza amachita zinthu mwachiwawa kwambiri moti angathe kuvulaza kapena kupha kumene mkazi kapena mwamuna wake. Ngati wankhanzayo ndi Mkhristu, akulu mumpingo ayenera kufufuza nkhaniyi. Munthu angathe kuchotsedwa mumpingo ngati ndi waukali kwambiri ndiponso amachita zinthu mwachiwawa.​—Agalatiya 5:​19-21.

Kukaniza mwamuna kapena mkazi kuchita zinthu zauzimu. Nthawi zina munthu angamalepheretse mkazi kapena mwamuna wake kulambira Mulungu woona kapena kumukakamiza kuti asamvere lamulo linalake la Mulungu. Ngati zili choncho, munthu amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa angasankhe kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wake mogwirizana ndi malamulo a boma kuti asonyeze “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Ngati pali mavuto aakulu ngati amene takambiranawa, munthu aliyense sayenera kukakamiza munthu wosalakwayo kupatukana kapena kukhalabe ndi mwamuna kapena mkazi wakeyo. Ngakhale kuti Akhristu anzathu achikulire mwauzimu ndiponso akulu mumpingo angathe kutithandiza ndi kutipatsa malangizo a m’Baibulo, iwo sangadziwe zonse zimene zikuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Ndi Yehova yekha amene amadziwa zimenezi. Sikungakhale kulemekeza Mulungu kapena ukwati ngati mwamuna kapena mkazi wachikhristu akukokomeza mavuto amene akukumana nawo m’banja n’cholinga choti apatukane. Yehova amakhala akudziwa zifukwa zenizeni zimene mwamuna ndi mkazi akupatukirana, ngakhale atabisa bwanji. Ndipotu, “zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.” (Aheberi 4:13) Koma ngati mavuto aakulu ngati amenewa akupitirirabe, munthu aliyense sayenera kudzudzula Mkhristu amene wasankha kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wake. Tiyenera kukumbukira kuti “tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu wa Mulungu.”​—Aroma 14:​10-12.