Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Wokondedwa Bwenzi la Yehova:

Yesu anati: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:​32) Mawu amenewatu ndi olimbikitsa kwambiri. Tangoganizani, n’zotheka kudziwa choonadi ngakhale “m’masiku otsiriza” ovuta ano, pamene ziphunzitso zonyenga zafala kwambiri. (2 Timoteyo 3:1) Kodi mumakumbukira nthawi imene munayamba kudziwa choonadi cha m’Mawu a Mulungu? Muyenera kuti munasangalala kwambiri.

N’zoona kuti kudziwa choonadi cha m’Baibulo molondola komanso kuuza ena zimenezi nthawi zonse n’kofunika kwambiri. Komabe, chofunikanso kwambiri n’chakuti tizichita zogwirizana ndi choonadicho. Kuti tithe kuchita zimenezi, tiyenera kupitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kutikonda. Kodi zimenezi ndi zinthu ngati ziti? Zimene Yesu ananena usiku woti mawa lake aphedwa, zimayankha funs limeneli. Iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.”​—Yohane 15:10.

Onani kuti Yesu anapitiriza kukondedwa ndi Mulungu chifukwa chosunga malamulo a Atate wake. N’zimenenso tiyenera kuchita masiku ano. Kuti tipitirize kukondedwa ndi Mulungu, nthawi zonse tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi. Usiku womwewo, Yesu ananenanso kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”​—Yohane 13:17.

Sitikukayikira kuti buku lino likuthandizani kupitiriza kugwiritsa ntchito choonadi pa moyo wanu, ndipo zimenezi zikuthandizani kuti ‘muzichita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani . . . pamene mukuyembezera kuti . . . mulandire moyo wosatha.’​—Yuda 21.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova