Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 16

Tsutsani Mdyerekezi ndi Njira Zake

Tsutsani Mdyerekezi ndi Njira Zake

“Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”—YAKOBO 4:7.

1, 2. Kodi ndani amasangalala ndi ubatizo?

NGATI mwakhala mukutumikira Yehova kwa zaka zambiri, mosakayikira mwamvetsera nkhani za ubatizo zambiri pamisonkhano yathu yadera ndi yachigawo. Komabe, kaya mwapezekapo kangati pamisonkhano imeneyi, nthawi iliyonse mumasangalala mukaona anthu amene amakhala pamipando yakutsogolo akuimirira kupita kukabatizidwa. Panthawi imeneyi, anthu opezeka pamsonkhanopo amasangalala ndipo amawomba m’manja mosangalala. Misozi ingalengeze m’maso anu poona gulu la abale ndi alongo okondedwa amene asankha kukhala kumbali ya Yehova. Imakhaladi nthawi yosangalatsa kwambiri.

2 Ife tingaonere ubatizo m’dera lathu mwa apo ndi apo, koma angelo ndi amene amaonerera ubatizo pafupipafupi. Taganizirani chisangalalo chimene chimakhalapo kumwamba angelo akamaona anthu ambirimbiri padziko lonse akuwonjezereka m’gulu la Yehova mlungu uliwonse. (Luka 15:7, 10) Ndithudi, angelo amasangalala kwambiri akamaona kuti anthu ambiri akubwerabe m’gulu la Yehova.—Hagai 2:7.

MDYEREKEZI “AKUYENDAYENDA UKU NDI UKU NGATI MKANGO WOBANGULA”

3. N’chifukwa chiyani Satana akuyendayenda uku ndi uku “ngati mkango wobangula,” nanga akufuna chiyani?

3 Komabe, pali zolengedwa zina zauzimu zimene zimakwiya zikamaona anthu akubatizidwa. Satana ndi ziwanda zake amakwiya kwambiri akaona anthu ambiri akusiya zochitika  za dziko loipali. Ndipotu, Satana ananena mwamatama kuti palibe munthu amene amatumikira Yehova chifukwa chomukonda ndiponso kuti palibe amene angakhalebe wokhulupirika ngati atayesedwa kwambiri. (Werengani Yobu 2:4, 5.) Choncho, nthawi iliyonse imene munthu wadzipereka kwa Yehova, zimatsimikizira kuti Satana ndi wabodza. Zimakhala ngati kuti mlungu uliwonse pachaka anthu ambirimbiri akumuwomba Satana makofi. N’chifukwa chake “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) “Mkango” umenewu ndi wofunitsitsa kutidya mwauzimu, kutiwononga kapenanso kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Mulungu.—Salimo 7:1, 2; 2 Timoteyo 3:12.

Lolani kuti Yehova akuthandizeni pamene mukudwala

4, 5. (a) Kodi Yehova wasonyeza kuti wachepetsa mphamvu za Satana m’njira zikuluzikulu ziti? (b) Kodi Mkhristu woona sayenera kukayikira za chiyani?

 4 Ngakhale kuti tili ndi mdani wolusa kwambiri, palibe chifukwa choopera. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Yehova watitsimikizira kuti wachepetsa mphamvu za “mkango wobangula” umenewu m’njira zikuluzikulu ziwiri. Yoyamba, Yehova ananeneratu kuti “khamu lalikulu” la Akhristu oona lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chikubwerachi. (Chivumbulutso 7:9, 14) Zimene Mulungu amalosera sizimalephereka. Choncho, ngakhale Satana amadziwa kuti sangathe kusocheretsa anthu onse a Mulungu.

5 Njira yachiwiri ikupezeka pa mfundo yaikulu imene munthu wina wakale amene anali wokhulupirika kwa Mulungu ananena. Munthuyu ndi mneneri Azariya ndipo anauza Mfumu Asa kuti: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.” (2 Mbiri 15:2; Werengani 1 Akorinto 10:13.) Zitsanzo zambiri za m’Baibulo zimasonyeza kuti m’mbuyomo, Satana analephera kunyenga mtumiki wa Mulungu aliyense amene anakhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. (Aheberi 11:4-40) Masiku anonso, Mkhristu amene amakhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, angathe kutsutsa Mdyerekezi ngakhalenso kumugonjetsa kumene. Ndipotu, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”—Yakobo 4:7.

‘TIKULIMBANA NDI MAKAMU A MIZIMU YOIPA’

6. Kodi n’chiyani chimene Satana amachita kuti agonjetse Mkhristu aliyense payekha?

6 Satana sangapambane pankhondoyi, komabe ngati sitingasamale angathe kutigonjetsa. Satana amadziwa kuti angathe kutimeza mosavuta ngati atasokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi Satana amachita chiyani pofuna kukwaniritsa cholinga chakechi? Iye amaukira gulu lonse la atumiki a Mulungu, amaukiranso Mkhristu aliyense payekha ndiponso amagwiritsa ntchito njira zake zachinyengo. Tiyeni tikambirane njira zikuluzikulu zimenezi, zomwe Satana amagwiritsa ntchito.

7. N’chifukwa chiyani Satana akuukira kwambiri anthu a Yehova?

 7 Amaukira gulu lonse. Mtumwi Yohane ananena kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mawu amenewa ndi chenjezo kwa Akhristu onse oona. Popeza Satana wameza kale dziko lonse la anthu osaopa Mulungu, tsopano maso ake ali pa anthu a Yehova amene akhala akukana njira zake zachinyengo ndipo akuyesetsa kuchita chilichonse chimene angathe kuti awagonjetse. (Mika 4:1; Yohane 15:19; Chivumbulutso 12:12, 17) Iye ndi okwiya kwambiri ndipo akulimbikira kutiukira chifukwa akudziwa kuti watsala ndi kanthawi kochepa. Masiku ano, Satana akulimbana nafe kwambiri pofuna kuwononga ubwenzi wathu ndi Mulungu.

8. Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ‘tikulimbana’ ndi mizimu yoipa?

8 Amaukira munthu aliyense payekha. Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake kuti: ‘Tikulimbana ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’ (Aefeso 6:12) N’chifukwa chiyani Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘kulimbana’? Chifukwa chakuti mawu amenewa amatanthauza kumenyana moyandikana. Choncho, pogwiritsa ntchito mawu amenewa, Paulo anatsindika mfundo yakuti aliyense payekha amalimbana ndi mizimu yoipa. Kaya tikukhala m’dziko limene anthu amakhulupirira za mizimu yoipa kapena ayi, tiyenera kukumbukira kuti pamene tinadzipereka kwa Yehova, tinakhala ngati talowa m’bwalo lomenyanirana. Mkhristu akangodzipereka kwa Mulungu, amakhala kuti wayamba kumenya nkhondo imeneyi. N’chifukwa chake Paulo anauza Akhristu a ku Efeso katatu konse kuti “khalani olimba.”—Aefeso 6:11, 13, 14.

9. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Satana ndi ziwanda amagwiritsa ntchito “zochita zachinyengo” zosiyanasiyana? (b) N’chifukwa chiyani Satana amafuna kuwononga maganizo athu, nanga tingalepheretse bwanji zolinga zake? (Onani bokosi “ Samalani ndi Njira Zachinyengo za Satana.”) (c) Kodi tikambirana njira ina iti imene Satana amagwiritsa ntchito?

9 Amagwiritsa ntchito njira zachinyengo. Paulo anauza Akhristu kuti achite khama polimbana ndi “zochita zachinyengo” za Satana. (Aefeso 6:11) Onani kuti Paulo anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti akunena zinthu zambiri. Mizimu  yoipa siigwiritsa ntchito njira imodzi koma njira zosiyanasiyana ndipo pali zifukwa zimene imachitira zimenezi. Iyo imadziwa kuti Akhristu ena amene angathe kulimba pa mayesero enaake, angathe kugonja akakumana ndi mayesero a mtundu wina. Choncho, Mdyerekezi ndi ziwanda amayang’anitsitsa zimene timachita kuti adziwe mbali imene tili ofooka mwauzimu. Ndiyeno amapezerapo mwayi kuti awononge ubwenzi wathu ndi Mulungu. Koma ubwino wake ndi wakuti timadziwa njira zimene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito, chifukwa zinalembedwa m’Baibulo. (2 Akorinto 2:11) Kumayambiriro kwa buku lino, tinakambirana zina mwa njira zimenezi, monga kukonda kwambiri chuma, kugwirizana ndi anthu oipa, ndiponso chiwerewere. Tiyeni tsopano tikambirane njira inanso imene Satana amagwiritsa ntchito, yomwe ndi kukhulupirira mizimu.

KUCHITA ZAMIZIMU N’KUSAKHULUPIRIKA

10. (a) Kodi kukhulupirira mizimu n’kutani? (b) Kodi kukhulupirira mizimu Yehova amakuona bwanji, nanga inuyo muyenera kukuona bwanji?

10 Anthu amene amachita zamizimu, kapena kuti zaziwanda, amagwirizana ndi mizimu yoipa. Mitundu ina yokhulupirira mizimu ndi kulosera, kuchita zamatsenga, kutsirika ndiponso kulankhula ndi anthu akufa. Timadziwa kuti Yehova ‘amanyansidwa’ ndi kukhulupirira mizimu. (Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8) Popeza nafenso tiyenera ‘kunyansidwa ndi choipa,’ tiyenera kupewa kugwirizana ndi mizimu yoipa. (Aroma 12:9) Ndipotu, kuchita zamizimu n’kusakhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova.

11. N’chifukwa chiyani Satana angasangalale kwambiri ngati atakwanitsa kutikopa kuti tizikhulupirira mizimu? Perekani chitsanzo.

11 Komabe, Satana amafuna kuti tizichita zamizimu chifukwa amadziwa kuti kuchita zimenezi n’kusakhulupirika kwa Yehova. Satana amasangalala kwambiri akakwanitsa kukopa Mkhristu kuti azichita zamizimu. Chifukwa chiyani tikutero? Yerekezerani izi: Ngati msilikali wakopeka ndi adani ake mpaka kuchoka m’gulu lake n’kulowa la adaniwo, mkulu wa gulu la adanilo amasangalala kwambiri. Akhoza kufika poguba ndi  munthu woukirayo pachionetsero, kuti zipweteketse mtima mkulu wa gulu la asilikali limene woukirayo anali. Mofanana ndi zimenezi, ngati Mkhristu wayamba kukhulupirira mizimu, amakhala atasiya Yehova mwakufuna kwake ndiponso amakhala kuti wadzipereka yekha kuti azilamuliridwa ndi Satana. Tangoganizirani chisangalalo chimene Satana angakhale nacho poyenda ndi munthu amene wasiya Yehova. Kodi ifeyo tingafune kuthandiza Mdyerekezi kuti apambane? Ayi, sitingachite zimenezo chifukwa sitingafune kukhala oukira.

AMAGWIRITSA NTCHITO MAFUNSO KUTI TIZIKAYIKIRA ZINTHU ZINA

12. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira iti pofuna kusokoneza maganizo athu?

12 Ngati timadana ndi zamizimu, Satana amadziwa kuti sangatigonjetse ndi njira imeneyi. Choncho, amasankha njira ina. Njira yake ndi kupotoza maganizo athu. Kodi amachita bwanji zimenezi? Iye amayesetsa kusokoneza maganizo a Akhristu moti ena amafika poyamba kuganiza kuti ‘zoipa ndi zabwino, ndipo zabwino ndi zoipa.’ (Yesaya 5:20) Kuti athe kuchita zimenezi, nthawi zambiri Satana amagwiritsa ntchito njira imene wakhala akugwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali. Njira imeneyi ndi kufunsa mafunso ochititsa munthu kuyamba kukayikira zinthu zina.

13. Kodi Satana wagwiritsa ntchito bwanji mafunso pofuna kuchititsa anthu kuyamba kukayikira zinthu zina?

13 Taonani mmene Satana anagwiritsira ntchito njira imeneyi m’mbuyomu. M’munda wa Edeni, iye anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” M’nthawi ya Yobu, pamsonkhano wa angelo kumwamba, Satana anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?” Ndipo pamene Yesu ankayamba utumiki wake padziko lapansi, Satana anakayikira zoti Khristu ndi mwana wa Mulungu ponena kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.” Apatu Satana ankanyoza Yehova pogwiritsa ntchito mawu amene Yehova yemweyo anali atanena milungu 6 m’mbuyomo. Iye anati:  “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”—Genesis 3:1; Yobu 1:9; Mateyu 3:17; 4:3.

14. (a) Kodi Satana amachititsa bwanji anthu kukayikira zoti kukhulupirira mizimu n’koipa? (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

14 Masiku ano, Mdyerekezi amagwiritsanso ntchito njira imeneyi pofuna kuti tizikayikira zoti kukhulupirira mizimu ndi koipa. Zomvetsa chisoni n’zakuti, iye wapambana popangitsa Akhristu ena kukayikira zimenezi. Iwo ayamba kukayikira ngati mitundu ina yokhulupirira mizimu ili yoipadi. (2 Akorinto 11:3) Kodi mungawathandize bwanji anthu oterewa kusintha maganizo awo? Kodi tingatani kuti Satana asatikope ndi njira imeneyi? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane mbali ziwiri za moyo wathu zimene Satana akuzigwiritsa ntchito pofuna kutikopa kuti tiyambe kuchita zinthu zokhulupirira mizimu. Mbali zimenezi ndi zosangalatsa ndiponso kusamalira thanzi lathu.

AMAPEZERAPO MWAYI PA ZIMENE TIMAKONDA NDI ZOFUNIKIRA PA MOYO WATHU

15. (a) Kodi anthu ambiri a kumayiko a azungu amaiona bwanji nkhani yokhulupirira mizimu? (b) Kodi Akhristu ena atengera bwanji maganizo a dzikoli okhudza kukhulupirira mizimu?

15 Anthu ambiri makamaka akumayiko a azungu, amapeputsa kwambiri nkhani zamatsenga, zaufiti komanso zinthu zina zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. Nthawi zambiri mafilimu, mabuku, mapulogalamu a pa TV, ndiponso masewera a pakompyuta amasonyeza kuti zochita za ziwanda n’zosangalatsa komanso zilibe vuto lililonse. Mafilimu ndi mabuku ena okhudza zamatsenga ndi ofala kwambiri moti anthu amapita kukawerenga ndi kukaonera zimenezi m’malo osiyanasiyana. Ndithudi, ziwanda zapambana popusitsa anthu kuti zamatsenga zilibe vuto. Kodi Akhristu ena ayamba kutengera maganizo amenewa? Inde, Akhristu ena apusitsidwa. Motani? Chitsanzo cha zimenezi ndi cha Mkhristu wina amene ataonera filimu ya zamatsenga ananena kuti, “Ndinaoneradi filimuyo, koma sikuti ndinachita zamizimu.” N’chifukwa chiyani maganizo oterewa ali oopsa?

16. Kodi n’chifukwa chiyani kukonda zosangalatsa zokhudza matsenga kuli koopsa?

 16 Ngakhale kuti palidi kusiyana pakati pa kuchita zamizimu ndi kuonera, koma sizikutanthauza kuti kuonera zamatsenga kulibe vuto lililonse. Chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani mfundo iyi: Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Satana ndi ziwanda zake sadziwa zimene timaganiza. * Choncho, monga taonera kale, kuti mizimu yoipa idziwe zimene tikuganiza ndiponso zofooka zathu zauzimu, imayang’anitsitsa zochita zathu ndi zosangalatsa zimene timakonda. Ngati Mkhristu amakonda mafilimu kapena mabuku ofotokoza za olankhula ndi mizimu, zamatsenga, za anthu ogwidwa ndi ziwanda kapena nkhani zina zokhudza ziwanda, amakhala akuzitumizira uthenga ziwandazo. Ndiye kuti akuziuza mbali imene iyeyo ali wofooka. Ndiyeno ziwandazo zingalimbikire kulimbana ndi Mkhristuyo pogwiritsa ntchito mbali imene zaona kuti ndi wofooka mpaka zitamugonjetsa. Ndipotu, anthu ena ayamba kuchita zinthu zokhulupirira mizimu chifukwa chokonda kuwerenga ndi kuonera zinthu zokhudza matsenga.—Werengani Agalatiya 6:7.

Munthu aliyense akadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa, amatsimikizira kuti Satana ndi wabodza

17. Kodi Satana angagwiritse ntchito njira iti pofuna kupezerera anthu odwala?

17 Kuwonjezera pa zosangalatsa, Satana amapezeraponso mwayi pa zimene timachita tikadwala. Kodi amachita bwanji zimenezi? Mkhristu amene wadwala kwanthawi yaitali angakhumudwe ngati sakuchira ngakhale kuti wakhala akupita kuzipatala zosiyanasiyana. (Maliko 5:25, 26) Pofuna kupangitsa Mkhristu amene wathedwa nzeruyu kuswa malamulo a Mulungu, ziwanda zingam’chititse kupita kwa asing’anga, kulandira chithandizo kapena njira zina zochiritsira matenda zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. (Yesaya 1:13) Munthu wodwalayo akakopeka ndi njira ya ziwanda imeneyi, ubwenzi  wake ndi Mulungu umawonongeka. Kodi umawonongeka chifukwa chiyani?

18. Kodi ndi njira zotani zodziwira kapena kuchizira matenda zimene Mkhristu ayenera kukana, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Yehova amachenjeza anthu amene samvera malamulo ake kuti: “Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.” (Miyambo 28:9) Nthawi zonse tiyenera kupewa kuchita chilichonse chimene chingachititse kuti Yehova asamamve mapemphero athu ndi kusiya kutithandiza, makamaka pa nthawi imene tikudwala. (Salimo 41:3) Choncho, ngati zikuoneka kuti njira ina yodziwira kapena kuchizira matenda ndi yokhudzana ndi kukhulupirira mizimu, Mkhristu woona ayenera kuikana. * (Mateyu 6:13) Tikatsatira malangizo amenewa, Yehova adzatithandiza.—Onani bokosi lakuti, “ Kodi Zimenezi N’zokhudzanadi ndi Kukhulupirira Mizimu?

NGATI NKHANI ZA ZIWANDA ZILI ZOFALA

19. (a) Kodi Mdyerekezi wapusitsa anthu ambiri kukhulupirira kuti ali ndi mphamvu zotani? (b) Kodi Akhristu oona ayenera kupewa nkhani zotani?

19 Anthu ambiri m’mayiko a azungu saopa mphamvu za Satana, pamene anthu a m’madera ena amaopa kwambiri mphamvu za Satana. M’madera amenewa Mdyerekezi wapusitsa anthu ambiri kukhulupirira kuti iye ali ndi mphamvu zambiri  kuposa zimene ali nazo. Anthu ena amaopa kwambiri mizimu yoipa moti amakhala mwamantha akamadya, akamagwira ntchito kapenanso akamagona. Nkhani zokhudza zinthu zodabwitsa zimene ziwanda zimachita n’zofala kwambiri. Nthawi zambiri anthu amakamba nkhani zimenezi mokokomeza moti anthu ambiri amakopeka nazo. Kodi ndi bwino kuti tizifalitsa nawo nkhani ngati zimenezi? Ayi. Atumiki a Mulungu oona amapewa kufalitsa nkhani zimenezi pa zifukwa zikuluzikulu ziwiri.

20. Kodi munthu angafalitse bwanji mabodza a Satana mosadziwa?

20 Choyamba, munthu akamafalitsa nkhani za ziwanda, amakhala akuthandiza Satana pa ntchito yake. N’chifukwa chiyani zili choncho? Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Satana amatha kuchita zozizwitsa, koma amatichenjezanso kuti iye amagwiritsa ntchito “zizindikiro zabodza” ndi “zodabwitsa.” (2 Atesalonika 2:9, 10) Popeza kuti Satana ndi wonyenga wamkulu, iye amadziwa mmene angapotozere maganizo a  anthu amene amakonda zamizimu. Ndiponso amadziwa zimene angachite kuti anthuwa akhulupirire zinthu zonama. Anthu oterewa angakhulupiriredi kuti aona ndi kumva zinthu zina ndipo angamafotokozere ena kuti zimenezi zinachitikadi. Chifukwa chofotokoza mobwerezabwereza nkhanizi, anthu amayamba kuzikokomeza. Mkhristu akamafalitsa nkhani ngati zimenezi, amakhala akuchita chifuniro cha Mdyerekezi yemwe ndi “tate wake wa bodza.” Iye amakhala akufalitsa mabodza a Satana.—Yohane 8:44; 2 Timoteyo 2:16.

21. Kodi nthawi zonse tiyenera kumakamba nkhani zotani?

21 Chachiwiri, ngakhale zitakhala kuti Mkhristu ankavutitsidwadi ndi mizimu yoipa m’mbuyomo, ayenera kupewa chizolowezi chofotokozera okhulupirira anzake nkhani zimenezi. Chifukwa chiyani? Chifukwa timalangizidwa kuti tiyenera ‘kuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu.’ (Aheberi 12:2) Inde, nthawi zonse tiyenera kuganizira za Khristu, osati za Satana. N’zochititsa chidwi kuti Yesu ali padziko pano, sankawafotokozera ophunzira ake nkhani za mizimu yoipa, ngakhale kuti iye akanatha kunena zambiri zimene Satana angathe kuchita kapenanso zimene sangathe. M’malomwake, Yesu ankakonda kunena za uthenga wa Ufumu. Choncho, potengera chitsanzo cha Yesu ndi atumwi, nthawi zonse zolankhula zathu zizikhala zokhudza “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Machitidwe 2:11; Luka 8:1; Aroma 1:11, 12.

22. Kodi tingatani kuti tipitirize kuthandizira kuti ‘kumwamba kukhale chisangalalo’?

22 N’zoona kuti Satana akafuna kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova, amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana, monga kuchititsa anthu kukhulupirira mizimu. Komabe tikamanyansidwa ndi choipa ndi kugwiritsitsa chabwino, Mdyerekezi sangapeze mpata wotifooketsa n’kutilepheretsa kutsatira zimene tinatsimikiza mumtima mwathu, zoti sitidzalola kuchita chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. (Werengani Aefeso 4:27.) Tangoganizani mmene kumwamba kudzakhalire “chisangalalo chochuluka” tikapitiriza kukhala ‘osasunthika polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi’ mpaka pamene adzawonongedwe.—Luka 15:7; Aefeso 6:11.

^ ndime 16 Mayina ofotokoza ntchito za Satana monga akuti (Wotsutsa, Woneneza, Wonyenga, Woyesa, Wabodza) samasonyeza kuti iye ali ndi mphamvu zotha kudziwa za mu mtima ndi m’maganizo mwathu. Koma mosiyana ndi Satana, Malemba amafotokoza kuti Yehova “amayesa mitima,” ndipo amati Yesu, ‘amafufuza impso ndi mitima.’—Miyambo 17:3; Chivumbulutso 2:23.

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani nkhani yakuti, “Kodi Kupima Matenda Kumeneko N’koyenera kwa Inu?” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1994, patsamba 19 mpaka 22, ndiponso yakuti, “Lingaliro la Baibulo: Kusankha Chithandizo cha Mankhwala—Kodi N’kofunikira?” mu Galamukani! ya January 8, 2001.