Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tikhale Oyera M’makhalidwe Athu Onse

Tikhale Oyera M’makhalidwe Athu Onse

“Khalani oyera m’makhalidwe anu onse.”—1 PET. 1:15.

1, 2. (a) Kodi anthu a Mulungu ayenera kukhala ndi makhalidwe otani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

MTUMWI PETULO anasonyeza kuti Akhristu ayeneranso kukhala oyera mogwirizana ndi zimene buku la Levitiko limanena. (Werengani 1 Petulo 1:14-16.) Yehova ndi “woyera,” choncho amafuna kuti odzozedwa komanso a “nkhosa zina” aziyesetsa kukhala oyera m’makhalidwe awo onse.Yoh. 10:16.

2 Tiyeni tsopano tikambirane mfundo zina za m’buku la Levitiko zimene zingatithandize kukhala oyera m’makhalidwe athu onse. Tikambirana mafunso awa: N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza mfundo za Yehova? Kodi buku la Levitiko lingatithandize bwanji kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova? Kodi tikuphunzira chiyani pa nsembe zimene Aisiraeli ankapereka?

MUSANYALANYAZE MFUNDO ZA YEHOVA

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kunyalanyaza malamulo ndiponso mfundo za Yehova? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kubwezera kapena kusungira anthu chakukhosi?

3 Kuti tisangalatse Yehova, tiyenera kukhala oyera n’kumatsatira malamulo ndi mfundo zake nthawi zonse. Ngakhale kuti sititsatira Chilamulo cha Mose, mfundo zake zimatithandiza  kudziwa zimene Mulungu amafuna ndiponso zimene safuna. Mwachitsanzo, Aisiraeli anauzidwa kuti: “Usabwezere choipa kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha. Ine ndine Yehova.”—Lev. 19:18.

4 Yehova safuna kuti tizibwezera kapena kusungira chakukhosi anthu amene atilakwira. (Aroma 12:19) Tikamanyalanyaza mfundo za Yehova ngati zimenezi, Mdyerekezi amasangalala kwambiri koma zimanyozetsa dzina la Mulungu. Baibulo limanena kuti ndife ziwiya “zonyamulira” chuma cha Mulungu chomwe ndi uthenga wabwino. (2 Akor. 4:1, 7) Choncho ngakhale munthu atatilakwira mwadala tisamusungire chakukhosi chifukwa tikatero tidzakhala ziwiya zonyamulira mkwiyo. Sitikufuna kuika mkwiyo m’ziwiya zonyamulira chuma cha Mulungu.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imene inachitikira banja la Aroni? (Onani chithunzi patsamba 13.)

5 Pa Levitiko 10:1-11 pali nkhani yomvetsa chisoni kwambiri imene inachitikira banja la Aroni. Anthu a m’banjali ayenera kuti anapwetekedwa mumtima pamene moto wochokera kumwamba unapha Nadabu ndi Abihu. Anthuwo ayeneranso kuti anavutika kwambiri atauzidwa kuti asalirire achibale awowo. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Tiyenera kukhala oyera n’kumapewa kucheza ndi achibale kapena anthu ena amene achotsedwa mumpingo.—Werengani 1 Akorinto 5:11.

6, 7. (a) Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize pa nkhani ya ukwati wochitikira m’tchalitchi? (Onani mawu a m’munsi.) (b) Kodi tingafotokozere bwanji achibale athu zimene tasankha pa nkhaniyi?

6 Koma kodi tingatani ngati taitanidwa ku ukwati wa wachibale wathu umene ukachitikira m’tchalitchi? Palibe malamulo a m’Baibulo okhudza nkhaniyi. Koma pali mfundo za m’Malemba zimene zingatithandize kusankha mwanzeru. *

7 Zimene tingasankhe pa nkhaniyi chifukwa chofuna kukhalabe oyera mwina sizingasangalatse achibale athu amene si Mboni. (1 Pet. 4:3, 4) N’zoona kuti sitifuna kuwakhumudwitsa, koma tiyenera kuwafotokozera mokoma mtima zimene tasankha. Ndi bwino kuchita zimenezi pasadakhale. Tingayambe ndi kuwayamikira potiitana ku ukwatiwo. Kenako tingawauze kuti tikapita mwina pali zinthu zina zokhudza chipembedzo chawo zimene sitingachite. Choncho sitikufuna kuwachititsa manyazi kapena kuwalepheretsa kusangalala pa tsiku lawo lapadera. Tikatero tidzasonyeza kuti sitikufuna kunyalanyaza mfundo za Yehova.

KHALANI KUMBALI YA ULAMULIRO WA YEHOVA

8. Kodi buku la Levitiko limatsindika bwanji za ulamuliro wa Yehova?

8 Buku la Levitiko limatsindika kwambiri za ulamuliro wa Yehova. Bukuli limanena maulendo oposa 30 kuti malamulo ake ndi ochokera kwa Yehova. Mose ankadziwa zimenezi ndipo ankachita zonse zimene Yehova anamulamula. (Lev. 8:4, 5) Nafenso tiyenera kuchita zimene Yehova amafuna. Ubwino wake ndi wakuti gulu lake limatithandiza kudziwa zoyenera kuchita. Komano kukhala omvera kungavute tikakhala kwatokha. Kumbukirani kuti ngakhale Yesu anayesedwa ali yekhayekha kuchipululu. (Luka 4:1-13) Ngati timaganizira kwambiri za ulamuliro wa Yehova n’kumamudalira, sitingasiye kumumvera ndipo sitingaope aliyense.—Miy. 29:25.

9. N’chifukwa chiyani timadedwa?

9 Akhristufe timazunzidwa m’mayiko ambiri. Paja Yesu anauza ophunzira ake kuti:  “Anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Ngakhale zili choncho, timapitiriza kulalikira komanso kukhala oyera pamaso pa Yehova. Kunena zoona timayesetsa kukhala oona mtima, oyera komanso omvera malamulo a m’dziko. Komano n’chifukwa chiyani timadedwa? (Aroma 13:1-7) Chifukwa chakuti timamvera Yehova n’kumaona kuti iye ndi Mfumu yathu. Timatumikira “iye yekha basi” ndipo sitidzasiya kutsatira malamulo ake komanso mfundo zake zolungama.—Mat. 4:10.

10. N’chiyani chinachitikira m’bale wina amene anafooka n’kulowa usilikali?

10 Akhristufe ‘sitilinso mbali ya dziko’ choncho sitilowerera nkhondo kapena ndale. (Werengani Yohane 15:18-21; Yesaya 2:4.) Anthu ena amene anadzipereka kwa Yehova anafooka pa nkhaniyi. Koma ambiri mwa iwo analapa n’kubwerera kwa Atate wathu wachifundo. (Sal. 51:17) Ngakhale zili choncho, ena sanalape. Zoterezi zinachitika pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Abale oposa 160 azaka zosapitirira 45, amene anatsekeredwa m’ndende zosiyanasiyana ku Hungary, anasonkhanitsidwa patauni ina. Ndiyeno anauzidwa kuti ayambe usilikali. Ambiri sanalole koma 9 okha analumbira kuti akhala asilikali ndipo analandira mayunifomu. Patangopita zaka ziwiri, mmodzi mwa anthu 9 aja anali m’gulu la asilikali amene anauzidwa kuti awombere Mboni zokhulupirika. Tsoka lake, anapeza kuti mchimwene wake anali m’gulu loti liwomberedwelo. Koma mwamwayi abalewo sanawomberedwe.

TIZIPATSA YEHOVA ZONSE ZIMENE TINGATHE

11, 12. Kodi tikuphunzira chiyani pa nsembe zimene Aisiraeli ankapereka?

11 Malinga ndi Chilamulo cha Mose, Aisiraeli ankayenera kupereka nsembe. (Lev. 9:1-4, 15-21) Nsembezo zinayenera kukhala zopanda chilema chilichonse chifukwa zinkaimira nsembe ya Yesu, yemwe ndi wangwiro. Panali malangizo oyenera kutsatira popereka nsembe iliyonse. Mwachitsanzo, ponena za mayi yemwe wabereka mwana, lemba la Levitiko 12:6 limati: “Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza. Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo.” Apa Mulungu anafotokoza bwinobwino zoyenera kuchita. Koma ankaganiziranso anthu ovutika. Tikutero chifukwa chakuti ngati mayiyo sakanakwanitsa kupereka nkhosa, ankatha kupereka nkhunda kapena njiwa ziwiri. (Lev. 12:8) Mulungu ankakonda munthu amene wapereka zinthu zochepa mofanana ndi amene wapereka zambiri. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi?

12 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti azitamanda Mulungu chifukwa zinali ngati kupereka nsembe. (Aheb. 13:15) Timachita zimenezi pouza ena za dzina la Yehova. Abale ndi alongo ena amagwiritsa ntchito chinenero chamanja potamanda Mulungu. Akhristu ena amene sangatuluke m’nyumba chifukwa chodwala amatamanda Mulungu polemba makalata, kulalikira pa foni ndiponso kulalikira kwa anthu odzawaona. Choncho chofunika ndi kuchita zonse zimene tingathe potamanda Yehova.—Aroma 12:1; 2 Tim. 2:15.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupereka lipoti la utumiki wathu?

13 Timatamanda Mulungu ndi mtima wonse chifukwa chomukonda. (Mat. 22:37, 38) Koma timauzidwa kuti tizilemba lipoti la  zimene tachita mu utumiki. Kodi tiyenera kuona bwanji nkhani imeneyi? Tikamapereka lipoti mwezi uliwonse timasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu. (2 Pet. 1:7) Koma sitiyenera kudzikakamiza kuchita zambiri mu utumiki chifukwa chongofuna kupereka maola ambiri. Ngati munthu sangachite zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba, akhoza kupereka lipoti la maminitsi 15. Yehova amayamikira kwambiri maminitsi ochepawo. Amaona kuti munthuyo wachita zonse zimene angathe posonyeza kuti amamukonda ndiponso kuyamikira mwayi wake womutumikira. Mofanana ndi Aisiraeli amene sankakwanitsa kupereka zinthu zodula, anthu a Yehova amene sangachite zambiri akhoza kuperekabe lipoti. Lipoti lililonse limaphatikizidwa mu lipoti la padziko lonse ndipo izi zimathandiza kuti gulu likonzekere bwino zam’tsogolo. Chifukwa cha zimenezi, tiyenera kupereka lipoti la utumiki wathu.

TIZICHITA KHAMA POPHUNZIRA MAWU A MULUNGU

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zimene timachita pophunzira Baibulo?

14 Mwina mfundo za m’buku la Levitiko zimene takambiranazi zakuchititsani kuona kuti Mulungu anachita bwino kuphatikiza bukuli m’Mawu ake. (2 Tim. 3:16) Taona kuti Yehova amatilamula kuti tikhale oyera komanso tizimupatsa zonse zimene tingathe. Kodi inuyo mumayesetsa kuchita zimenezi? Pajatu iye ndi woyenera kupatsidwa zinthu zabwino kwambiri. Mwina zimene takambirana m’buku la Levitiko zikukuchititsaninso kulakalaka kuphunzira mwakhama mabuku ena a m’Baibulo. (Werengani Miyambo 2:1-5.) Kodi panopa mumatani pophunzira Baibulo? Nkhani imeneyi ndi yofunika kuiganizira komanso kuipempherera n’cholinga choti tizipatsa Yehova zonse zimene tingathe. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimalephera kuphunzira Mawu a Mulungu chifukwa choonera TV, kuchita masewera enaake kapena kucheza?’ Ngati timalepheradi, ndi bwino kuganizira mfundo zina zimene Paulo analemba m’buku la Aheberi.

Kodi mumaona kuti kuphunzira Baibulo panokha komanso Kulambira kwa Pabanja n’kofunika kwambiri? (Onani ndime 14)

15, 16. N’chifukwa chiyani Paulo analankhula mosapita m’mbali kwa Akhristu achiheberi?

15 Paulo analankhula mosapita m’mbali kwa Akhristu achiheberi. (Werengani Aheberi 5:7, 11-14.) Iye ananena kuti Akhristuwo ‘ankachedwa kumvetsa zinthu.’ N’chifukwa chiyani Paulo analankhula mosanyengerera chonchi? Mofanana ndi Yehova, iye ankakonda Akhristuwo ndiponso kuwaganizira. Koma iwo ankangochita zinthu ngati ana odalira mkaka basi. M’malo mophunzira mwakhama mfundo zozama, zimene zili ngati “chakudya chotafuna,” iwo ankangodalira mfundo zoyambirira. N’zoona kuti kudziwa mfundo zoyambirira n’kofunika koma tiyenera kuphunziranso zinthu zozama kuti tikhale Akhristu olimba.

16 M’malo moti akhale aphunzitsi, Akhristu achiheberiwo ankafunikanso kuphunzitsidwa. Zinali choncho chifukwa choti sankadya  “chakudya chotafuna.” Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi inenso sindikonda kudya chakudya chotafuna? Kodi sindikonda kupemphera komanso kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo? Kodi mwina njira zimene ndimatsatira pophunzira n’zimene zili ndi vuto?’ Tiyenera kukumbukira kuti tili ndi udindo wophunzitsa anthu osati kungowalalikira basi.—Mat. 28:19, 20.

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani yomwa mowa tisanapite ku misonkhano?

17 Enafe timavutika kuphunzira Baibulo. N’zoona kuti Yehova safuna kuti tizikakamizika kuphunzira Baibulo chifukwa chodziimba mlandu. Koma kaya tinadzipereka kalekale kwa Yehova kapena posachedwapa, tonsefe tiyenera kuchita khama pophunzira mfundo zozama za m’Baibulo. Tiyenera kuchita zimenezi ngati tikufuna kukhalabe oyera.

18 Kuti tikhale oyera, tiyenera kufufuza m’Malemba kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna n’kumachita zimenezo. Kumbukirani zimene zinachitikira ana a Aroni. Iwo anaphedwa chifukwa chopereka zofukiza “pamoto wosaloledwa.” Mwina anachita zimenezi chifukwa choti anali ataledzera. (Lev. 10:1, 2) Tikutero chifukwa cha zimene Mulungu anauza Aroni pambuyo pake. (Werengani Levitiko 10:8-11.) Kodi izi zikutanthauza kuti munthu asayerekeze n’komwe kumwa mowa asanapite ku misonkhano? Kuti tiyankhe funsoli tiyenera kuganizira mfundo zina. Choyamba, Akhristu sayendera Chilamulo cha Mose. (Aroma 10:4) Chachiwiri, m’mayiko ena Akhristu amamwa pang’ono pa nthawi ya chakudya asanapite ku misonkhano. Chachitatu, pa mwambo wa Pasika ankagwiritsa ntchito makapu 4 a vinyo. Chinanso n’chakuti pamene ankayambitsa mwambo wa Chikumbutso, Yesu anapatsa atumwi ake vinyo amene ankaimira magazi ake. (Mat. 26:27) Komanso Baibulo limaletsa kumwa kwambiri ndiponso kuledzera. (1 Akor. 6:10; 1 Tim. 3:8) Tisaiwalenso kuti chikumbumtima cha Akhristu ambiri sichiwalola kumwa mowa ngakhale pang’ono asanapite kukachita chilichonse chokhudza kulambira Mulungu. Komabe tizikumbukira kuti zinthu zimasiyana malinga ndi kumene tikukhala. Chofunika kwambiri n’choti Akhristu azitha kusiyanitsa “pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa” n’cholinga choti akhale oyera pamaso pa Mulungu.

19. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira Baibulo patokha? (b) Kodi inuyo muyesetsa kuchita chiyani kuti mukhalebe oyera?

19 Mukamaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama mudzapeza mfundo zambiri zochititsa chidwi. Mukamachita Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo panokha, muzifufuza zinthu pogwiritsa ntchito mabuku ndi zinthu zina zimene tili nazo. Mukatero mudzadziwa bwino Yehova komanso zolinga zake. Mudzayambanso kugwirizana naye kwambiri. (Yak. 4:8) Muzipemphera kwa Yehova ngati wamasalimo amene anati: “Tsegulani maso anga kuti ndione zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.” (Sal. 119:18) Musamanyalanyaze malamulo kapena mfundo za m’Baibulo. Muzitsatira malamulo a Yehova yemwe ndi woyera ndipo muzigwira mwakhama “ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (1 Pet. 1:15; Aroma 15:16) Tiyeni tonse tiziyesetsa kukhala oyera m’makhalidwe athu onse m’masiku ovutawa. Tikatero tidzasonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Mulungu wathu woyera.

^ ndime 6 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002.