Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 12

Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”

Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”

“Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa.”—AEFESO 4:29.

1-3. (a) Kodi Yehova anatipatsa mphatso iti, ndipo ingagwiritsidwe ntchito bwanji molakwika? (b) Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kulankhula kuti Mulungu apitirize kutikonda?

NGATI mwam’patsa mphatso munthu wina amene mumam’konda, kodi mungamve bwanji mutaona kuti sakuigwiritsa ntchito bwino? Yerekezerani kuti munamupatsa galimoto, ndiye mwadziwa kuti amayendetsa mosasamala, moti amavulaza nayo anzake. Kodi zimenezi zingakusangalatseni?

2 Luso lolankhula zinthu zomveka ndi mphatso yochokera kwa Yehova, amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yakobo 1:17) Mphatso imeneyi, yomwe imasiyanitsa anthu ndi nyama, imatithandiza kufotokoza maganizo athu komanso mmene tikumvera. Komabe mofanana ndi galimoto, mphatso ya kulankhula tingathenso kuigwiritsa ntchito molakwika. Ziyenera kuti zimam’khumudwitsa kwambiri Yehova tikamagwiritsira ntchito mphatso yathu molakwika polankhula zinthu zopweteketsa mtima anthu ena.

3 Kuti Mulungu apitirizebe kutikonda, tifunika kugwiritsa ntchito mphatso ya kulankhula imeneyi monga mmene wotipatsayo amafunira. Yehova amatiuza momveka bwino kalankhulidwe kamene kamam’sangalatsa. Mawu ake amati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire,  kuti asangalatse owamva.” (Aefeso 4:29) Tiyeni tikambirane chifukwa chake tiyenera kusamala polankhula komanso kalankhulidwe kamene tiyenera kupewa ndi zimene tingachite kuti tizilankhula zinthu ‘zolimbikitsa.’

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSAMALA POLANKHULA?

4, 5. Kodi miyambi ina ya m’Baibulo imafotokoza kuti mawu ali ndi mphamvu yotani?

4 Chifukwa chimodzi chofunika kwambiri chomwe tiyenera kukhalira osamala polankhula n’chakuti mawu ali ndi mphamvu. Lemba la Miyambo 15:4 limati: “Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo, koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.” * Mawu odekha amalimbikitsa ena monga mmene madzi amapangitsira mtengo umene unafota kusangalala. Mosiyana ndi zimenezo, mawu oipa a lilime lachinyengo amakhumudwitsa ena. Zoonadi, zolankhula zathu zingavulaze kapena kuchiritsa ena.—Miyambo 18:21.

5 Pofotokoza za mphamvu ya mawu, mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga.” (Miyambo 12:18) Kulankhula mosaganiza kumakhumudwitsa ena ndiponso kumadanitsa.  Kodi munayamba mwapwetekedwapo ndi mawu ngati kuti mwabayidwa ndi lupanga? Mwambi womwewu umanenanso za ubwino wa lilime. Umati: “Lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Munthu amene amalankhula moganizira ena komanso amene ali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, amalankhula mawu amene amachiritsa kapena kulimbikitsa munthu wokhumudwa ndiponso amakhazikitsa mtendere. Kodi mukukumbukira nthawi ina pamene munalimbikitsidwa ndi mawu abwino? (Werengani Miyambo 16:24.) Podziwa kuti zimene timalankhula zimakhudza anthu ena, tiyenera kumalankhula zinthu zochiritsa ena osati zowapweteka.

Mawu odekha amalimbikitsa ena

6. N’chifukwa chiyani n’zovuta kulamulira lilime lathu kuti tisalankhule zoipa?

6 Ngakhale titayesetsa bwanji, sitingathe kuletseratu lilime lathu kuti lisalankhule zinthu zoipa ngakhale pang’ono. Zimenezi zikutifikitsa pa chifukwa chachiwiri chimene tiyenera kukhalira osamala polankhula: Uchimo ndi kupanda ungwiro zimatilepheretsa kugwiritsa ntchito bwino lilime lathu. Zimene timalankhula zimachokera mumtima, ndipo “maganizo a anthu amakhala oipa.” (Genesis 8:21; Luka 6:45) Choncho, kulamulira lilime lathu kuti tisalankhule zoipa n’kovuta kwambiri. (Werengani Yakobo 3:2-4.) Ngakhale kuti sitingaletseretu lilime lathu kulankhula zoipa, komabe n’zotheka kuti tizilankhula bwino. Munthu amene akusambira molowera kumene madzi akuchokera amafunika kulimbikira kuti madziwo asamukokolole. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tiyenera kulimbikira kuti tipewe chizolowezi choipa chogwiritsa ntchito lilime molakwika.

7, 8. Kodi timakhala ndi mlandu wotani kwa Yehova ngati sitilankhula bwino?

7 Chifukwa chachitatu chimene tiyenera kukhalira osamala polankhula n’chakuti timakhala ndi mlandu kwa Yehova ngati sitilankhula bwino. Mmene timagwiritsira ntchito lilime lathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi anthu ena komanso ndi Yehova. Lemba la Yakobo 1:26  limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” * Monga tinaonera m’mutu wapitawu, zimene timalankhula zimakhudza kwambiri kulambira kwathu. Ngati sitilamulira lilime lathu ndipo timalankhula zopweteka komanso zovulaza ena, ndiye kuti zonse zimene timachita potumikira Mulungu zingakhale zopanda phindu. Ndithudi, m’pofunika kusamala kwambiri ndi kalankhulidwe kathu.—Yakobo 3:8-10.

8 Choncho tili ndi zifukwa zomveka zokhalira osamala kuti tisagwiritse ntchito molakwika mphatso ya kulankhula. Tisanakambirane kalankhulidwe kabwino kamene kamalimbikitsa, tiyeni tikambirane kalankhulidwe komwe Mkhristu woona ayenera kupewa.

KALANKHULIDWE KOSALIMBIKITSA

9, 10. (a) Kodi ndi kalankhulidwe kotani kamene kafala masiku ano? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa mawu otukwana? (Onaninso mawu am’munsi.)

9 Mawu otukwana. Masiku ano kutukwana, kunyoza ndiponso kulankhula mawu ena oipa n’zofala kwambiri. Anthu ambiri amagwiritsa ntchito mawu otukwana akakwiya. Anthu anthabwala kapena a zisudzo nthawi zambiri amalankhula mawu otukwana kapena olaula pofuna kuseketsa anthu. Komabe, kutukwana ndi nkhani yoopsa. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo anauziridwa kulangiza Akhristu a ku Kolose kuti ataye kutali “nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Paulo anauza mpingo wa ku Efeso kuti “nthabwala zotukwana” zili m’gulu la zinthu zimene siziyenera ‘kutchulidwa n’komwe pakati’ pa Akhristu oona.—Aefeso 5:3, 4.

10 Kutukwana kumam’nyansa Yehova ndi anthu amene amam’konda ndipo timapewa kutukwana chifukwa chakuti  timakonda Yehova. Potchula “ntchito za thupi,” Paulo anatchulapo “zinthu zodetsa,” ndipo chimodzi mwa zinthu zimenezi ndi kulankhula zinthu zonyansa. (Agalatiya 5:19-21) Imeneyi ndi nkhani yaikulu. Ngati munthu sakusintha atapatsidwa uphungu mobwerezabwereza kuti asiye kulankhula zinthu zoipa, zolaula ndi zochititsa manyazi, angathe kuchotsedwa mumpingo. *

11, 12. (a) Kodi kunena za ena kumaipa kukafika pati? (b) Kodi n’chifukwa chiyani olambira Yehova afunika kupewa miseche?

11 Miseche. Anthu amakonda kunena za ena. Kodi kunena za ena n’koipa nthawi zonse? Ayi, si koipa ngati tikunena zinthu zabwino kapena nkhani zothandiza, monga zakuti wina wabatizidwa kapena wina akufunika kumulimbikitsa. Akhristu oyambirira anali ndi chidwi chofuna kudziwa za moyo wa ena ndiponso ankauzana nkhani zokhudza okhulupirira anzawo. (Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:8, 9) Komabe, kunena za ena kungakhale koipa ngati sitikunena zoona kapenanso ngati tikuulula nkhani zachinsinsi. Choipa kwambiri n’chakuti, kunena za ena kumayambitsa miseche, imene nthawi zonse ndi yoipa kwambiri. Miseche ndi khalidwe lojeda kapena lonenera wina zoipa kuseri pofuna kumuipitsira mbiri. Mwachitsanzo, Afarisi ankanena mabodza n’cholinga chakuti anthu asamukhulupirire Yesu. (Mateyu 9:32-34; 12:22-24) Nthawi zambiri miseche imayambitsa mikangano.—Miyambo 26:20.

12 Yehova amadana ndi anthu amene amagwiritsa ntchito mphatso ya kulankhula kuipitsira mbiri ya anthu ena kapena kugawanitsa anthu. Iye amadana ndi munthu “woyambitsa mikangano pakati pa abale.” (Miyambo 6:16-19) Pa Chigiriki mawu otanthauza “wamiseche” ndi di·aʹbo·los, ndipo limeneli ndi dzina linanso la Satana. Iye  ndi “Mdyerekezi,” chifukwa amanenera Mulungu zabodza. (Chivumbulutso 12: 9, 10) Ndithudi, tiyenera kupewa kulankhula zinthu zimene zingatipangitse kukhala ngati Mdyerekezi. Miseche siloledwa mumpingo chifukwa imayambitsa ntchito za thupi monga “mikangano” ndi “kugawikana.” (Agalatiya 5:19-21) Choncho, musananene nkhani yokhudza wina imene mwamva, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona? Kodi chingakhale chikondi kuuzanso ena? Kodi ndikufunikadi kuuza ena nkhani imeneyi?’—Werengani 1 Atesalonika 4:11.

13, 14. (a) Kodi mawu achipongwe angakhudze bwanji anthu ena? (b) Kodi kulalata n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani munthu wolalata amaika moyo wake pa ngozi?

13 Mawu achipongwe. Monga taonera kale, mawu angathe kupweteka ena. Kunena zoona, nthawi zina chifukwa chopanda ungwiro, timanena zinthu zimene pamapeto pake timanong’oneza nazo bondo. Komabe, Baibulo limachenjeza za kalankhulidwe komwe si koyenera ngakhale pang’ono panyumba kapena mumpingo wachikhristu. Paulo analangiza Akhristu kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu.” (Aefeso 4:31) Mabaibulo ena amamasulira mawu akuti “mawu achipongwe” kuti “mawu oipa,” “mawu opweteka,” ndiponso “mawu onyoza.” Mawu achipongwe amaphatikizapo kutchulana mayina onyoza komanso kukonda kudzudzula mwaukali. Zimenezi zingachotsere ena ulemu ndi kuwapangitsa kudziona kukhala anthu osafunika. Makamaka ana sachedwa kukhumudwa ndi mawu achipongwe.—Akolose 3:21.

14 Baibulo limagwiritsa ntchito mawu amphamvu kwambiri poletsa kulalata. Kulalata kumatanthauza kunyoza anthu ena ndi mawu amwano, otukwana kapena achipongwe. Munthu amene amakonda kugwiritsa ntchito mawu amenewa amaika moyo wake pa ngozi, chifukwa wolalata angathe kuchotsedwa mumpingo ngati sakusintha atathandizidwa mobwerezabwereza. Ndipo ngati sasintha, akhoza  kutaya mwayi wake wodzalowa mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10) Ndithudi, Mulungu sangapitirize kutikonda ngati timalankhula zinthu zoipa, zonama ndiponso zosonyeza kusakomera ena mtima. Kalankhulidwe kameneka ndi kosalimbikitsa.

MAWU AMENE ‘AMALIMBIKITSA’

15. Kodi ndi kalankhulidwe kotani kamene ‘kamalimbikitsa’?

15 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mphatso ya kulankhula monga mmene Mulungu amafunira? Kumbukirani kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kulankhula mawu ‘alionse olimbikitsa.’ (Aefeso 4:29) Yehova amasangalala tikamalankhula mawu omangirira ndi olimbikitsa ena. Pamafunika kuganiza bwino kuti tilankhule mawu oterewa. Baibulo silipereka malamulo achindunji a kalankhulidwe komanso silitchula mndandanda wa ‘mawu oyenera.’ (Tito 2:8) Kuti tilankhule mawu ‘olimbikitsa,’ tingachite bwino kukumbukira mfundo zitatu zofunika zosavuta kuchita izi: Kulankhula zabwino, kulankhula zoona ndiponso kulankhula mokoma mtima. Tili ndi mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo za kalankhulidwe kolimbikitsa.—Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndimalankhula Zolimbikitsa?

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira ena? (b) Kodi tingayamikire ena pa zifukwa ziti mumpingo, nanga m’banja?

16 Kuyamikira ena ndi mtima wonse. Yehova ndi Yesu amaona kuti kuyamikira ena n’kofunika kwambiri. (Mateyu 3:17; 25:19-23; Yohane 1:47) Monga Akhristu, nafenso tingachite bwino kuyamikira ena kuchokera pansi pa mtima. Chifukwa chiyani? Lemba la Miyambo 15:23 limati: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamva bwanji anthu ena akandiyamikira kuchokera pansi pa mtima? Kodi ndimasangalala komanso ndimalimbikitsidwa?’ Ndithudi, mukayamikiridwa mochokera pansi pa mtima zimasonyeza kuti munthu wina amaona zomwe mumachita, amakuganizirani, ndiponso  kuti zimene munachita n’zaphindu. Kudziwa zimenezi kumakuthandizani kulimbikira kudzachita zoposa pamenepo m’tsogolo. Popeza kuti mumasangalala ena akakuyamikirani, inunso muyenera kuyesetsa kuti muziyamikira anthu ena.—Werengani Mateyu 7:12.

17 Phunzirani kuona zinthu zabwino mwa anthu ena, ndiyeno ayamikireni. Mumpingo, mungayamikire nkhani imene yakambidwa bwino kwambiri, mungaone wachinyamata akuyesetsa kuti akwaniritse zolinga zauzimu, kapenanso mungaone wachikulire amene amabwera kumisonkhano mokhulupirika ngakhale kuti amavutika ndi ukalamba. Kuyamikira anthu oterewa mochokera pansi pa mtima kungawakhudze ndipo kungawalimbikitse kuti apitirize kutumikira Yehova. M’banja, mwamuna ndi mkazi wake amafunika kuyamikirana mochokera pansi pa mtima. (Miyambo 31:10, 28) Makamaka ana amakula bwino akamaona kuti amayamikiridwa. Ana amafunika kuwayamikira monga momwe zomera zimafunikira dzuwa ndi madzi kuti zikule bwino. Choncho, makolo muziyesetsa kuyamikira ana anu chifukwa cha makhalidwe awo abwino ndiponso zimene amachita bwino. Kuwayamikira kungawathandize kukhala olimba mtima ndi odzidalira ndipo kungawalimbikitse kuyesetsa kwambiri kuchita bwino.

18, 19. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kutonthoza ndi kulimbikitsa okhulupirira anzathu, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

18 Mawu otonthoza ndi olimbikitsa. Yehova amaganizira kwambiri anthu ovutika ndi ‘opsinjika.’ (Yesaya 57:15) Mawu ake amatilimbikitsa ‘kupitiriza kutonthozana’ ndi ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni.’ (1 Atesalonika 5:11, 14) Tingakhale otsimikiza kuti Mulungu amaona ndipo amayamikira zimene timachita potonthoza ndi kulimbikitsa okhulupirira anzathu amene ali ndi chisoni.

Yehova amasangalala tikamalankhula mawu olimbikitsa anthu ena

19 Komabe, kodi munganene chiyani polimbikitsa Mkhristu mnzanu amene ali ndi chisoni? Musaganize kuti muyenera kuthetsa vuto lakelo. Nthawi zambiri, zimene zimathandiza kwambiri ndi kungonena mawu achidule.  Mutsimikizireni kuti mumamuganizira. Pempherani naye limodzi ndipo m’pempheni Yehova kuti muthandize kuona mmene anthu ena komanso Mulungu amamukondera. (Yakobo 5:14, 15) Mutsimikizireni kuti anthu mumpingo amamukonda kwambiri. (1 Akorinto 12:12-26) Muwerengereni lemba la m’Baibulo lomutsimikizira kuti Yehova amamukonda kwambiri monga munthu payekha. (Salimo 34:18; Mateyu 10:29-31) Kupeza nthawi yomuuza munthu amene ali ndi chisoni “mawu abwino” mochokera pansi pa mtima, kudzamuthandiza kudziwa kuti amakondedwa ndiponso kuti ndi wofunika.—Werengani Miyambo 12:25.

20, 21. Kodi ndi mfundo ziti zimene zimachititsa kuti uphungu ukhale wogwira mtima?

20 Malangizo ogwira mtima. Monga anthu opanda ungwiro nthawi zambiri timafunika kupatsidwa malangizo. Baibulo likutilimbikitsa kuti: “Mvera uphungu, ndipo utsatire malangizo kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.” (Miyambo 19:20) Kupereka uphungu si ntchito ya akulu okha. Makolo amafunika kupereka malangizo kwa ana awo. (Aefeso 6:4) Alongo achikulire angafunikenso kupereka malangizo kwa alongo achitsikana. (Tito 2:3-5) Kukonda ena kumatilimbikitsa kuwapatsa uphungu m’njira imene ingawapangitse kulandira uphunguwo popanda kukhumudwa. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kupereka uphungu kwa ena m’njira imeneyi? Ganizirani mfundo zitatu zimene  zimapangitsa uphungu kukhala wogwira mtima kwambiri: Maganizo ndi zolinga za wopereka uphunguyo, kumene kwachokera uphunguwo, ndiponso mmene uphunguwo ukuperekedwera.

21 Munthu amene akupereka uphungu ndi amene angachititse kuti uphunguwo ukhale wogwira mtima. Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimandithandiza kuti ndisavutike kulandira uphungu?’ Mukadziwa kuti munthu amene akukupatsani uphunguyo amakukondani, sakulankhula chifukwa chakuti wakukwiyirani, komanso alibe zolinga zoipa, uphunguwo suvuta kulandira. Inunso muyenera kutsatira zimenezi popatsa ena uphungu. Uphungu wabwino ndi umene umachokera m’Mawu a Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Kaya tachita kutchula lemba la m’Baibulo kapena ayi, koma uphungu wathu uzikhala wogwirizana ndi Malemba. Choncho, akulu ayenera kusamala kuti asanene maganizo awoawo, kapena kukhotetsa Malemba, n’cholinga chakuti zimene akunenazo zioneke ngati zikuchokera m’Baibulo. Uphungu umakhalanso wogwira mtima kwambiri ukaperekedwa m’njira yoyenera. Uphungu umene umaperekedwa mokoma mtima suvuta kuulandira ndipo umathandiza kuti tisachotsere ulemu munthu amene tikum’patsa uphunguyo.—Akolose 4:6.

22. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani pa nkhani yogwiritsa ntchito mphatso yolankhula?

22 Kunena zoona, kulankhula ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Kukonda kwathu Yehova kuyenera kutilimbikitsa kuti tisagwiritse ntchito mphatso imeneyi molakwika. Tizikumbukira kuti mawu amene timalankhula ali ndi mphamvu yolimbikitsa kapena kukhumudwitsa ena. Choncho, tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito mphatso imeneyi ‘polimbikitsa’ ena, monga mmene Yehova amafunira. Tikamatsatira zimenezi, mawu athu adzakhala olimbikitsa anthu ena ndipo zidzatithandiza kuti Mulungu apitirize kutikonda.

^ ndime 4 Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti ‘chinyengo’ pa Miyambo 15:4 angatanthauzenso ‘kukhota’ kapena ‘kupotoka.’

^ ndime 7 Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti ‘kupanda pake’ anamasuliridwanso kuti ‘chopanda ntchito.’—1 Akorinto 15:17.

^ ndime 10 M’Malemba, mawu akuti “zinthu zodetsa” amatanthauza machimo osiyanasiyana. Sikuti zodetsa zilizonse zimafunikira komiti ya chiweruzo, komabe munthu angathe kuchotsedwa mumpingo ngati akupitirizabe kuchita zonyansa.2 Akorinto 12:21; Aefeso 4:19; onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006.