Kusirira Mnyamata Kapena Mtsikana
Chigawo 1
Kusirira Mnyamata Kapena Mtsikana
Kusukulu kwanu, mukuona mnyamata ndi mtsikana atagwirana manja ndipo akuyenda pang’onopang’ono. Kodi mungamve bwanji?
□ Sindingavutike nazo
□ Ndingasirire pang’ono
□ Ndingasirire kwambiri
Mukuonera filimu ndi anzanu ndipo kenako mukuona kuti onse akhala awiriawiri, kupatulapo inuyo basi. Kodi mungamve bwanji?
□ Sindingavutike nazo
□ Ndingachite manyazi pang’ono
□ Ndingasirire kwambiri
Mnzanu wapamtima wayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana winawake ndipo chibwenzi chayambika. Kodi mungamve bwanji?
□ Ndingasangalale
□ Ndingasirire pang’ono
□ Ndingakhumudwe nazo
Kaya muli ku sukulu, mumsewu ngakhale kumsika mumaona anyamata ndi atsikana ali awiriawiri. Nthawi zonse mukawaona, mumasirira kwambiri moti mumafuna kuti nanunso mukhale ndi chibwenzi. Koma kodi ndinu wokonzekadi kukhala ndi chibwenzi? Ngati zili choncho, mungatani kuti mupeze munthu woyenerera? Mukam’peza, mungatani kuti chibwenzi chanucho chikhale chosadetsedwa? Mungapeze mayankho a mafunso amenewa m’Mitu 1 mpaka 5.
[Chithunzi chachikulu pamasamba 12, 13]