Kodi Ndiyenera Kuchita Masewera a Pakompyuta?
Mutu 30
Kodi Ndiyenera Kuchita Masewera a Pakompyuta?
MNYAMATA wina dzina lake Brian anati: “Masewera a pakompyuta ndi osangalatsa kwambiri chifukwa munthu umatha kuchita zinthu zomwe zitakhala kuti ndi zenizeni, zingakubweretsere mavuto aakulu.” Mtsikana wina dzina lake Deborah ananenanso kuti amakonda kuchita masewera amenewa. Komabe iye anati: “Masewera a pakompyuta amawonongetsa nthawi kwambiri. Ndipo ukayamba kuchita masewerawa, sufuna kusiya.”
Masewera a pakompyuta ndi otsogola kwambiri, amafuna luso, komanso amathandiza munthu kuti asasungulumwe. Masewerawa amathandizanso munthu kuti azichita zinthu mochangamuka, azidziwa masamu ndiponso kuti azitha kuwerenga bwino. Komanso, popeza kuti anthu ambiri kusukulu amakonda kukambirana za masewera a pakompyuta amene angotuluka kumene, ngati mukuwadziwa masewerawa, mumapeza nkhani yokambirana ndi anzanu.
Choncho, ngati mutasankha mwanzeru, mungathe kupeza masewera a pakompyuta abwino ndiponso osangalatsa. Komabe, kodi n’chifukwa chiyani mufunika kusamala?
Kuopsa kwa Masewera a Pakompyuta
Masewera ena a pakompyuta si abwino chifukwa amalimbikitsa makhalidwe amene Baibulo limati ndi “ntchito za thupi.” Makhalidwe amenewa ndi oipa ndipo Mulungu amadana nawo.—Agalatiya 5:19-21.
Mnyamata wina wazaka 18, dzina lake Adrian, pofotokoza masewera ena otchuka kwambiri a pakompyuta, anati: “Masewerawa amaonetsa anthu akumenyana, akugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, akuchita chiwerewere poyerayera, akutukwana, akuchita
zachiwawa ndiponso akuvulazana.” Masewera ena amalimbikitsa zamizimu. Ndiponso pakatuluka masewera atsopano, akale aja amakhala opanda ntchito. Munthu umatha kuchita masewera achiwawa amenewa ndi anthu ena pa Intaneti. Zimenezi zapangitsa kuti masewerawa apite patsogolo kwambiri. Mnyamata wina wazaka 19, dzina lake James, anati: “N’zotheka kumapikisana ndi anthu a ku mayiko ena pakompyuta yanu.”Masewera a pakompyuta omwe atchuka kwambiri masiku ano ndi a pa Intaneti. Pamasewerawa umasankha kuti ukhale munthu, nyama, kapena zonse ziwiri. Pa Intanetipo pamakhalanso anthu ena ambirimbiri omwe akusewera. Ndipo pamakhalanso masitolo, magalimoto, nyumba, malo a zisangalalo, ndi nyumba zosungiramo mahule, zomwe zimaoneka ngati zenizeni. Zidole za pakompyuta zikamalankhulana kapena kuchita zinthu zina, anthu amene akusewerawo amatumizirana mauthenga.
Zinthu zomwe anthu amachita pamasewerawa sangazichite n’komwe pamoyo wawo. M’masewera a pa Intaneti amenewa, mumakhala anthu achiwawa, zigawenga, anthu omwe amafufuza amuna oti agone ndi mahule, anthu akuba, achinyengo, ndiponso opha anzawo. Kungothabwanya mabatani ochepa, anthu ochita masewerawa angachititse zidole zawozo kuti zigonane, uku iwo akutumizirana mauthenga onena za kugonana. Masewera ena amaonetsa zidole zikugonana ndi tizidole tooneka ngati ana. Ichi n’chifukwa chake anthu ambiri akudandaula ndi zinthu zosaloleka zimene zimachitika m’masewerawa.
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusankha Mwanzeru?
Anthu amene amachita masewera osonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere amanena kuti: “Palibe cholakwika
chifukwa si zenizeni. Amenewa ndi masewera basi.” Koma maganizo amenewa asakupusitseni.Baibulo limanena kuti: “Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” (Miyambo 20:11) Kodi mungatchedwe woyera ndiponso wolungama ngati mumachita masewera a pakompyuta a zachiwawa ndi a zachiwerewere? Ofufuza apeza kuti anthu amene amaonerera zinthu zachiwawa amakhala aukali. Akatswiri ena akuti masewera a pakompyuta amasintha kwambiri khalidwe la munthu kusiyana ndi TV. Izi zili choncho chifukwa anthu amachita nawo masewerawo osati kungoonerera chabe.
Kuchita masewera osonyeza chiwawa ndi chiwerewere kuli ngati kusewera ndi zinyalala zotsalira popanga mabomba zomwe ndi za poizoni. Kuopsa kwa zinthu zimenezi sikuonekera msanga koma n’kosapeweka chifukwa poizoniyu akalowa m’mimba, amawononga matumbo. Mofanana ndi zimenezi, kuonera zinthu zachiwerewere ndi zachiwawa kungawononge Aefeso 4:19; Agalatiya 6:7, 8.
‘makhalidwe anu abwino,’ ndipo mungayambe kuganiza ndi kuchita zinthu zoipa.—Kodi Ndizichita Masewera Otani?
Ngati makolo anu sakukanizani kuchita masewera a pakompyuta, kodi mungadziwe bwanji masewera oyenera ndiponso nthawi imene mungathere posewera? Dzifunseni mafunso otsatirawa:
Kodi masewera amene ndikufuna kuchita angakwiyitse Yehova? Lemba la Salmo 11:5 limati: “Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” Mawu a Mulungu amachenjeza anthu amene amachita zamizimu, kuti: “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Ngati nanunso mukufuna kuti musakwiyitse Mulungu, muyenera kutsatira malangizo a pa Salmo 97:10 akuti: “Danani nacho choipa.”
Kodi masewerawa angawononge bwanji maganizo anga? Dzifunseni kuti, “Kodi ndikamachita masewera amenewa, ndingathe ‘kuthawa dama’?” (1 Akorinto 6:18) Dziwani kuti masewera amene amakhala ndi zithunzi kapena mawu oyambitsa chilakolako cha kugonana, sangakuthandizeni kuganizira zinthu zolungama, zoyera, ndi zabwino.—Afilipi 4:8.
Kodi ndizisewera nthawi yaitali bwanji? Ngakhale masewera abwino, angakudyereni nthawi yambiri. Choncho, lembani nthawi imene mumathera posewera ndipo yerekezerani ndi nthawi imene mumathera pochita zinthu zina zofunika kwambiri. Zimenezi zingakuthandizeni kuchita zinthu zofunika panthawi yake.—Aefeso 5:16.
Komabe, Baibulo silinena kuti tizingokhalira kuphunzira kapena kugwira ntchito. Limatiuza kuti pali “mphindi Mlaliki 3:4) Dziwani kuti mawu akuti ‘kuvina’ sakutanthauza kusewera kokha, koma kuchitanso zinthu zolimbitsa thupi. Choncho, yesetsani kupatula nthawi yochita masewera ena olimbitsa thupi m’malo mongokhala muli dwii pa TV kapena pakompyuta.
yakuseka. . . ndi mphindi yakuvina.” (Sankhani Mwanzeru
Masewera a pakompyuta angakhale osangalatsa kwambiri, makamaka ngati mukuwadziwa bwino. N’chifukwa chake muyenera kusankha mwanzeru. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimakhoza bwino maphunziro ati kusukulu?’ N’zosakayikitsa kuti maphunziro amene mumakhozawo ndi amene mumawakonda. Mukamakonda kwambiri phunziro linalake m’pamenenso mumalidziwa bwino kwambiri. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi masewera ati a pakompyuta amene ndimawakonda kwambiri? Ndipo kodi amandiphunzitsa makhalidwe otani?’
Onetsetsani kuti musamachite masewerawa chifukwa chongokopeka ndi anzanu. Koma muzisankha nokha masewera amene mukufuna kuchita. Chofunika kwambiri ndicho kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti cholandirika kwa Ambuye n’chiti.”—Aefeso 5:10.
Pafupifupi aliyense amakonda kumvetsera nyimbo. Koma kodi inuyo simutha kukhala osamvetsera nyimbo?
LEMBA LOFUNIKA
“Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.”—Salmo 97:10.
MFUNDO YOTHANDIZA
Lembani masewera angapo a pakompyuta amene mukufuna kuchita. Lembaninso cholinga cha masewerawo ndi zimene mungachite kuti mukwanitse cholingacho. Onani ngati zimenezi zikugwirizana ndi malangizo a m’Baibulo amene afotokozedwa m’mutu uno. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa ngati masewerawo ndi abwino kapena ayi.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Chipatala choyamba cha anthu amene ali ndi vuto lochita masewera a pakompyuta chinatsegulidwa ku Amsterdam, m’dziko la Netherlands, m’chaka cha 2006.
ZOTI NDICHITE
Mnzanga akandiuza kuti ndichite masewera a pakompyuta osonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere, ndizinena izi: ․․․․․
Ndizichita masewera a pakompyuta kwanthawi yosapitirira pamlungu, ndipo kuti ndikwanitse zimenezi, ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi masewera a pakompyuta angakhudze bwanji khalidwe ndi maganizo a munthu?
● Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a Yehova posankha masewera a pakompyuta?
● Kodi mungamuthandize bwanji mng’ono wanu amene amachita masewera oipa a pakompyuta?
[Chithunzi patsamba 249]
“Masewera ambiri amachititsa munthu kuona zinthu monga chiwawa, kutukwana ndi chiwerewere kuti si zoipa kwenikweni. Ndiponso angachititse munthu kugonja pa ziyeso zosiyanasiyana. Choncho tiyenera kukhala osamala kwambiri ndi masewera amene tasankha.”—Anatero Amy
[Chithunzi patsamba 250]
Kuchita masewera a zachiwawa ndi zachiwerewere kuli ngati kuseweretsa zinyalala zotsalira popanga mabomba zomwe ndi za poizoni. Kuopsa kwa zinthu zimenezi sikuonekera msanga koma n’kosapeweka