Kodi Ndizichita Zosangalatsa Zotani?
Mutu 32
Kodi Ndizichita Zosangalatsa Zotani?
Chongani ziganizo zili m’munsimu kuti zoona kapena zonama.
Baibulo limati . . .
Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kulakwa.
□ Zoona □ Zonama
Kuonera mafilimu ndi TV n’kulakwa.
□ Zoona □ Zonama
Kuvina n’kulakwa.
□ Zoona □ Zonama
Miyambo 20:29) Ndipo mukufuna kuchita zosangalatsa.
MLUNGU wonse mwakhala mukulimbikira sukulu. Kunyumbanso mwamaliza ntchito zanu zonse. Komabe chifukwa choti ndinu wachinyamata mudakali ndi mphamvu zochitira zinthu zina. (Achinyamata ena amaganiza kuti Baibulo limaletsa kuchita zosangalatsa. Kodi zimenezi ndi zoona? Tiyeni tione mayankho olondola a ziganizo zomwe zili pa tsamba 263 ndiponso zimene Baibulo limanena pankhani ya zosangalatsa.
● Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kulakwa.
Zonama. Baibulo limati: ‘Masewero olimbitsa thupi amapindulitsa.’ (1 Timoteyo 4:8) Mawu achigiriki akuti “masewero” amene Paulo anagwiritsira ntchito mu lembali amanena za ‘kunyamula zitsulo’ ndipo amatanthauza kuchita zolimbitsa thupi. Masiku ano kuli masewera ambiri olimbitsa thupi komanso osangalatsa monga mpira wamiyendo ndi wamanja, kuthamanga, kukwera njinga ndi ena ambiri.
Komabe tifunikira kusamala. Taonani mawu onse a mu lembali. Mtumwi Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Pakuti chizolowezi chochita masewero olimbitsa thupi chipindulitsa pang’ono; koma kudzipereka kwa Mulungu n’kopindulitsa m’zonse, chifukwa kuli ndi lonjezo la moyo uno ndi umene ukubwerawo.” Mawu a Paulo amasonyeza kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kukondweretsa Mulungu. Mungasonyeze kuti ndinu wodzipereka kwa Mulungu, ngakhale posankha masewera, mwa kudzifunsa mafunso atatu otsatirawa:
1. Kodi ndi anthu ambiri bwanji amene amavulala pa masewerawo? Kuti mudziwe zolondola, musangokhulupirira zonena za ena kapena zimene anzanu omwe amakonda masewerawa anganene. Fufuzani zoona zake. Mwachitsanzo,
fufuzani izi: Kodi ndi anthu angati amene amavulala pa masewerawo? Kodi anthu amadziteteza bwanji akamachita masewerawo? Kodi mukufunikira kuphunzira chiyani komanso kukhala ndi zida zotani kuti muzichita masewerawo? Ngakhale kuti pa masewera aliwonse anthu amavulala, muyenerabe kufufuza kuti mudziwe ngati masewerawo ndi oika moyo pangozi.Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo m’Chilamulo chimene anapatsa Aisiraeli, Mulungu ananena kuti munthu wopha mnzake mwangozi azilandira chilango choopsa. (Eksodo 21:29; Numeri 35:22-25) Choncho Aisiraeli anauzidwa kuti azipewa ngozi. (Deuteronomo 22:8) Masiku anonso Akhristu afunikira kulemekeza moyo.
2. Kodi mukasewera ndi anthu otani? Ngati muli ndi luso pa masewera enaake, anzanu ndi aphunzitsi anu angakuumirizeni kuti mulowe timu ya sukulu. Mwina zingakuvuteni kukana. Mnyamata wina wachikhristu dzina lake Mark anati: “Ndikuona ngati makolo anga sachita bwino, iwo amandikaniza kulowa timu ya sukulu.” M’malo mokakamiza makolo anu kuti akulolezeni kuchita zimene mukufuna, ganizirani mfundo izi: Nthawi zambiri timu ya sukulu imakonzekera masewera ana ataweruka. Mukamasewera bwino,
amakulimbikitsani kuti muwonjezere nthawi yochita masewerawo. Ngati simukusewera bwino, mumafunitsitsa kuti muzikonzekera masewerawo nthawi yaitali. Komanso osewera timu imodzi amayamba kugwirizana kwambiri akapambana mpikisano kapena akalephera.Ndiye mudzifunse kuti: ‘Kodi kusewera nthawi yaitali ndi a zipembedzo zina sikungachititse kuti ndiyambe kuchita makhalidwe oipa?’ (1 Akorinto 15:33) ‘Kodi kusewera mu timu imeneyi kungandiwonongetse zinthu zochuluka bwanji?’
3. Kodi ndingawononge nthawi ndi ndalama zochuluka bwanji pa masewera amenewa? Baibulo limalimbikitsa kuti “mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Kuti mugwiritsire ntchito malangizo amenewa, dzifunseni kuti: ‘Kodi kuchita masewera amenewa kumandithera nthawi imene ndikanaigwiritsa ntchito kuwerenga za kusukulu kapena kuchita zinthu zauzimu? Kodi masewera amenewa andiwonongera ndalama zingati? Kodi ndingakwanitse kupeza ndalama zimenezi?’ Kuyankha mafunso amenewa, kukuthandizani kuika patsogolo zinthu zofunika kwambiri.
● Kuonera mafilimu ndi TV n’kulakwa.
Zonama. Baibulo limauza Akhristu kuti: “Gwirani zolimba chimene chili chabwino.” Ndiponso kuti: “Pewani zoipa za mtundu uliwonse.” (1 Atesalonika 5:21, 22) Lemba limeneli silikuletsa mafilimu ndi mapulogalamu onse a pa TV. *
Kunena zoona, kuonera filimu ndi anzako n’kosangalatsa. Mwachitsanzo, mtsikana wina wa ku South Africa, dzina lake Leigh anati, “Ndikafuna kuonera filimu inayake, ndimaitana anzanga.” Nthawi zambiri atsikanawa amamaliza kuonera filimuyo kusanade. Filimuyo ikatha, makolo awo amadzawatenga ndipo amapita kukadya ku lesitanti.
Kale anthu ankangomvetsera nthano chifukwa kunalibe mafilimu ndiponso TV. Yesu ankaphunzitsa anthu mogwira mtima pogwiritsa ntchito mafanizo. Mwachitsanzo, fanizo lake la Msamariya wachifundo limaphunzitsa anthu za chifundo ndi makhalidwe ena abwino.—Luka 10:29-37.
Masiku anonso mafilimu amaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana zimene zimasintha maganizo a anthu. Anthu opanga mafilimuwa amayesetsa kukopa oonera kuti azikonda anthu a mu filumuwo, ngakhale atakhala oipa. Ngati simusamala, mungayambe kuchemerera munthu woipa amene akusonyezedwa mu filimuyo, n’kumaona ngati palibe vuto ndi zimene akuchitazo. Kodi mungapewe bwanji zimenezi?
Mukamasankha filimu kapena pulogalamu ya pa TV, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi filimu kapena pulogalamu imeneyi, Aefeso 4:32) ‘Kapena kodi indichititsa kuti ndizisangalala ndi tsoka la wina?’ (Miyambo 17:5) ‘Kodi indichititsa kuti ndizikonda zinthu zoipa?’ (Salmo 97:10) ‘Kodi kapena ndikhala m’gulu la anthu “ochita zoipa”?’—Salmo 26:4, 5.
indithandiza kukhala wokoma mtima?’ (Mawu ndi zithunzi zoyambirira zonenerera filimu, zingakuthandizeni kudziwa kuti filimuyo ndi yotani. Koma ‘musamangokhulupirira mawu onse.’ (Miyambo 14:15) Amenewa amakhala maganizo a anthu ena osati a inuyo ayi. Komanso onenerera mafilimu amabisa zinthu zina zoipa za m’filimuyo. Wachinyamata wina dzina lake Connie anati: “Ndaona kuti ukadziwa anthu amene ali mu filimuyo, umatha kudziwa kuti filimuyo ndi yotani.”
Akhristu anzanu angathe kukuuzani ngati filimu inayake
ndi yabwino kapena ayi. Komabe, dziwani kuti anthu amakonda kungonena zimene zawasangalatsa mu filimuyo. Choncho, afunseninso zoipa zimene aona m’filimuyo. Afunseni ngati muli zachiwawa, zachiwerewere, kapena zamizimu. Mungachitenso bwino kufunsa makolo anu. Mtsikana wina dzina lake Vanessa anati: “Ine ndimafunsa makolo anga ndipo akandiuza kuti filimuyo ndi yabwino, ndimaionera.”Musaone ngati kusankha filimu kapena pulogalamu ya pa TV ndi nkhani yaing’ono. Iyi ndi nkhani yaikulu chifukwa zimene mumaonera zimasonyeza kuti mtima wanu ndi wotani. (Luka 6:45) Zimene mumaonera zimasonyezanso kuti mumakonda kucheza ndi anthu otani, mumakonda kulankhula zotani, komanso mumaganiza zotani pankhani yogonana. Choncho, muzisankha bwino zinthu zimene mumaonera.
● Kuvina n’kulakwa.
Zonama. Aisiraeli atapulumutsidwa pa Nyanja Yofiira, Miriamu ndi akazi onse anayamba “kuvina” chifukwa cha chisangalalo. (Eksodo 15:20, NW) Komanso paphwando la m’fanizo la Yesu la mwana wolowerera, panali ‘kuimba ndi kuvina.’—Luka 15:25.
Agalatiya 5:19-21) Mneneri Yesaya analemba kuti: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mgoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m’maphwando awo; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang’ana pa machitidwe a manja ake.”—Yesaya 5:11, 12.
Zimenezi zimachitikanso masiku ano. M’mayiko ambiri, anthu amapanga maphwando ndipo achinyamata ndi achikulire omwe amavina. Komabe, tiyenera kusamala. Baibulo sililetsa maphwando, koma limaletsa “maphwando aphokoso.” (Pamaphwando amenewa pankakhala “zakumwa zoledzeletsa” ndi nyimbo zaphokoso. Ankayamba m’mamawa ndipo ankatha usiku kwambiri. Onaninso kuti anthu amene ankapezeka m’maphwando amenewa ankachita zinthu zosonyeza ngati kulibe Mulungu. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Mulungu analetsa maphwando amenewa.
Ngati mwaitanidwa ku phwando kumene anthu azikavina, dzifunseni mafunso awa: ‘Kodi kukakhala ndani ndi ndani? Kodi anthu amenewa ali ndi makhalidwe otani? Kodi ndani akayang’anire phwando limeneli? Kodi akayang’anira bwanji? Kodi makolo anga avomereza kuti ndipite ku phwandoli? Kodi azikavina motani?’ Mavinidwe ambiri amachititsa anthu kuti akhale ndi chilakolako chogonana. Kodi ‘mungathawe dama’ ngati muvina nawo kapena muonerera mavinidwe amenewa?—Nanga kodi mungatani ngati mwaitanidwa ku malo achisangalalo komwe anthu amachezera kuvina usiku wonse? Mnyamata wina dzina lake Shawn, asanakhale Mkhristu ankapita kukavina kumalo amenewa. Ndipo iye anati: “Nyimbo zake zimakhala zoipa. Kavinidwe kake kamakhala konyanyula, ndipo ambiri amene amapita kumeneko amakhala ndi cholinga.” Shawn ananena kuti cholinga chawo chimakhala choti apeze munthu woti akagonane naye. Koma Shawn ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anasiya kupita ku malo amenewa. N’chifukwa chiyani? Iye anati: “Amenewa si malo oti Akhristu azipitako.”
Muyenera Kusamala
Kodi mukuganiza kuti ndi nthawi iti imene msilikali amakhala wosatetezeka? Ndi nthawi imene ali ku nkhondo kapena pamene akucheza ndi anzake? Akamacheza, chifukwa amakhala atasiya zida zake. N’chimodzimodzinso mukakhala kusukulu kapena kuntchito, mumayesetsa kudziteteza. Mumakhala tcheru kuti musachite chilichonse chimene chingasokoneze moyo wanu wauzimu. Koma mukamasangalala ndi anzanu, m’pamene mumakhala pangozi yoti mutha kuchita chilichonse choipa.
Anzanu ena angakunyozeni kuti simungasangalale ngati mukutsatira kwambiri Baibulo. Ngakhale achinyamata amene akulira m’banja lachikhristu angakunyozeni chonchi. Koma dziwani kuti achinyamata amenewa chikumbumtima chawo chinafa. (1 Timoteyo 4:2) Iwo anganene kuti mumachita zinthu monyanyira kapena mumafuna kudzionetsa ngati wolungama. Musafooke ndi zimenezi, koma “khalani ndi chikumbumtima chabwino.”—1 Petulo 3:16.
Chofunika kwambiri ndi kusangalatsa Yehova osati anzanu. Ndipo ngati anzanu akukuvutitsani chifukwa chochita zimene mukuona kuti n’zabwino, siyani kucheza nawo n’kupeza anzanu ena. (Miyambo 13:20) Dziwani kuti udindo wonse wodziletsa kuchita zoipa, ngakhale pamene muli kosangalala, uli m’manja mwanu.—Miyambo 4:23.
WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 37
Masiku ano zithunzi zolaula zili paliponse. Kodi mungazipewe bwanji?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 22 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 36 m’Buku Loyamba.
LEMBA LOFUNIKA
“Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe . . . nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.”—Mlaliki 11:9.
MFUNDO YOTHANDIZA
Pemphani makolo anu kuti mwezi uliwonse muzikhala ndi nthawi yosangalala pabanja panu ndipo panthawiyi musamaonere TV.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Kale Aisiraeli akamalambira Mulungu ankaimba ndi kuvina.—Salmo 150:4.
ZOTI NDICHITE
Anzanga akandiuza kuti ndizisewera mu timu ya sukulu, ndizinena izi: ․․․․․
Ngati ndaona kuti filimu imene ndikuonera ndi anzanga ndi yokayikitsa, ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani Akhristu amapewa masewera oika moyo pangozi?
● Kodi filimu yabwino mungaidziwe bwanji?
● Kodi kuvina koyenera n’kotani?
[Mawu Otsindika patsamba 269]
“Ndimakonda kwambiri kuvina, koma ndaona kuti ndi bwino kumvera makolo. Sindifuna kuti kuvina kuzindilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri pamoyo wanga.”—Anatero Tina
[Chithunzi patsamba 268]
Msilikali amakhala wosatetezeka akasiya zida zake n’kumacheza. Inunso mukakhala pachisangalalo, n’zosavuta kuti muchite makhalidwe oipa