Anzanu
Chigawo 3
Anzanu
Kodi mumaona kuti kukhala ndi anzanu n’kofunika?
□ N’kosafunika
□ N’kosafunika kwenikweni
□ N’kofunika kwambiri
Kodi mumavutika kupeza anthu ocheza nawo?
□ Inde
□ Ayi
Kodi muli ndi mnzanu wapamtima?
□ Inde
□ Ayi
Kodi mumafuna kuti mnzanu akhale ndi khalidwe lotani?
Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Aliyense amafuna kukhala ndi mnzake wotere. Koma kupeza anzanu abwino n’kovuta. Kodi mungatani kuti mupeze anzanu abwino ndiponso kuti muzigwirizana nawo bwinobwino? Onani malangizo amene ali m’Mitu 9 mpaka 12.
[Chithunzi chachikulu pamasamba 84, 85]