Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga?
Mutu 38
Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga?
“Poyamba sindinkaganizako n’komwe za tsogolo langa. Koma nditatsala pang’ono kumaliza sukulu, ndinayamba kuzindikira kuti tsopano ndikukayamba moyo wina, wofunika kugwira ntchito mwakhama komanso wongokhalira kulipira mabilu.”—Anatero Alex.
TIYEREKEZERE kuti mukuganiza zoyenda ulendo winawake wautali kwambiri. N’zodziwikiratu kuti mungayambe mwaona kaye mapu kuti mudziwe njira yoyenera. N’chimodzimodzinso ndi kukonzekera tsogolo lanu. Mnyamata wina amene tsopano akutumikira pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova, dzina lake Michael, anati: “Pali zinthu zambirimbiri zimene aliyense angafunikire kusankhapo.” Koma kodi mungatani kuti musankhe mwanzeru? Michael anapitiriza kuti: “Nkhani yagona pa cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa.”
Cholinga chanu tingachiyerekezere ndi malo amene mukupita. N’zodziwikiratu kuti simungafikeko ngati mukungoyendayenda mwachisawawa. Choncho, mungachite bwino kwambiri kumaganizira zimene mukuchita kuti mukwaniritse cholinga chanucho, zimene zili ngati kuona mapu amene angakuthandizeni kudziwa njira yoyenera. Kuchita zimenezi kukugwirizana ndi malangizo omwe ali pa Miyambo 4:26 akuti: “Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako.” Pa lemba limeneli, Baibulo lina limati: “Dziwani kumene mukupita.”—Contemporary English Version.
M’zaka zikubwerazi, mudzafunikira kusankha zochita pankhani zikuluzikulu zokhudza kulambira, ntchito, kulowa m’banja, kukhala ndi ana komanso nkhani zina zofunika kwambiri. Pankhani zoterezi simudzavutika kusankha zinthu mwanzeru ngati mukudziwa cholinga chanu. Komabe, mukamaganiza zoti muchite pamoyo wanu, pali chinthu chofunika kwambiri chimene simuyenera kuchinyalanyaza.
‘Ukumbukire Mlengi Wako’
Kuti mukhaledi wosangalala, muyenera kutsatira zimene mfumu yanzeru Solomo ananena. Iye anati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 12:1) M’mawu ena, zinthu zimene mumasankha kuchita pamoyo wanu zizikhala zogwirizana ndi cholinga chanu chofuna kusangalatsa Mulungu.
N’chifukwa chiyani kukumbukira Mlengi wanu kuli kofunika kuposa china chilichonse? Pa Chivumbulutso 4:11, Baibulo limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Zolengedwa zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi pano zimayenera kulemekeza Mlengi. Kodi mumayamikira kuti anakupatsani “moyo, mpweya, ndi zinthu zonse”? (Machitidwe 17:25) Kodi simuona kuti ndi bwino kuti mum’chitire kenakake Yehova Mulungu poyamikira zinthu zonse zimene anakuchitirani?
Chifukwa chokumbukira Mlengi wawo, achinyamata ambiri a Mboni za Yehova ayamba utumiki wa nthawi zonse. Taonani mbali zina zosangalatsa kwambiri za utumiki woterewu zimene inuyo mungachite.
Upainiya. Apainiya okhazikika amathera nthawi yaitali muutumiki. Iwo amatha kuphunzitsa anthu Baibulo mwaluso kwambiri chifukwa cha zimene amaphunzitsidwa, chifukwa cholalikira kawirikawiri ndiponso zimene amakumana nazo muutumiki.
Kukatumikira kudera limene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Anthu ena amasamukira kudera limene kuli olalikira Ufumu ochepa kwambiri. Ena amaphunzira chinenero china ndipo amatha kutumikira m’mipingo ya chinenerocho yomwe ili kufupi ndi kwawo kapena kusamukira kudziko lina. *
Utumiki waumishonale. Apainiya oyenerera amene ali ndi thanzi labwino, amaphunzitsidwa mmene angakachitire utumiki waumishonale kumayiko ena. Amishonale amakhala ndi moyo wosangalala kwambiri.
Utumiki wa pa Beteli. Anthu a m’banja la Beteli amagwira ntchito m’maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. M’mayiko ena, zina mwa ntchito zimene amagwira ndi kupanga ndi kutumiza mabuku ofotokoza Baibulo.
Utumiki wa m’mayiko ena. Anthu otumikira m’mayiko ena amakathandiza pantchito yomanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano ndiponso maofesi a nthambi m’mayiko osiyanasiyana.
Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Akulu ndi atumiki othandiza osakwatira komanso oyenerera amakaphunzira ku sukuluyi mmene gulu limayendera ndiponso amaphunzira luso lolankhula pagulu. Ena akamaliza sukuluyi amatumizidwa kuti akatumikire ku mayiko ena.
Kukonzekera Zimene Mukufuna Kudzachita
Utumiki wa nthawi zonse ndi ntchito yabwino kwambiri ndipo umabweretsa madalitso osaneneka. Komabe, m’pofunika kuti muzikonzekereratu zimene mukufuna kudzachita. Mwachitsanzo, dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimene ndizidzachita kuti ndidzathe kudzisamalira ndekha?’
Mtsikana wina dzina lake Kelly anali ndi cholinga chodzakhala mpainiya, choncho anaganizira ntchito imene azidzagwira kuti adzathe kukwaniritsa
cholinga chakecho. Iye anati: “Ndinafunika kusankha ntchito imene ingamadzandithandize kudzisamalira ndekha pamene ndikuchita upainiya.”Panthawi imene anali ku sekondale, Kelly anachita maphunziro a ntchito inayake. Zimenezi zinam’thandiza kukwaniritsa cholinga chake chija. Iye anati: “Panalibenso china chilichonse chimene ndinkafunitsitsa kuchita kuposa utumiki wa nthawi zonse.” Kelly akusangalala kwambiri ndi zimene anasankha kuchita ndipo anati: “Ndimaona kuti ndinasankha bwino kwambiri.”
Muzipempha Malangizo
Mukamayenda m’dera lachilendo, n’zodziwikiratu kuti penapake mungafunike kufunsira njira. Mungachitenso chimodzimodzi pankhani yokonzekera tsogolo lanu. Choncho ndi bwino kuti muzipempha malangizo kwa anthu ena. Lemba la Miyambo 20:18 limati: “Uphungu utsimikiza zolingalira.”
Ena mwa anthu amene angakuthandizeni kwambiri ndi makolo
anu. Koma mungapemphenso malangizo kwa Akhristu ena okhwima mwauzimu amene moyo wawo umasonyeza kuti amatsatira mfundo za Mulungu. Mnyamata wina wazaka za m’ma 20 amene akutumikira pa Beteli, dzina lake Roberto anati: “Pemphani malangizo kwa anthu achikulire achitsanzo chabwino a mumpingo wanu kapena a m’mpingo yoyandikana ndi wanu.”Kuposa munthu wina aliyense, Yehova Mulungu amafuna kukuthandizani kuti musankhe zinthu zimene zingadzakupangitseni kukhala munthu wosangalala kwambiri. Choncho, m’pempheni kuti akuthandizeni ‘kupitiriza kuzindikira chifuniro chake’ pankhani yokhudza tsogolo lanu. (Aefeso 5:17) Pazochita zanu zonse, tsatirani malangizo a pa lemba la Miyambo 3:5, 6, akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”
Kuti mudziwe zambiri, onerani DVD yakuti “Young People Ask—What Will I Do With My Life?” DVD imeneyi ili m’zinenero zoposa 30
[Mawu a M’munsi]
LEMBA LOFUNIKA
“Mundiyese . . . , ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.”—Malaki 3:10.
MFUNDO YOTHANDIZA
Chezani ndi anthu amene achita utumiki wa nthawi zonse kwazaka zambiri. Afunseni chifukwa chake anasankha utumiki umenewo komanso madalitso amene apeza.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Mphamvu zamagetsi zimapangitsa kuti zipangizo zoyendera magetsi zizigwira ntchito yake. Mofanana ndi zimenezi, mzimu woyera wa Mulungu ungakuthandizeni kuchita zinthu zambiri pamene mukum’tumikira.—Machitidwe 1:8.
ZOTI NDICHITE
Kuti ndizisangalala kwambiri ndi utumiki, ndikambirana ndi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi mungadzagwire ntchito yotani kapena muli ndi luso lotani limene lingadzakuthandizeni kudzisamalira pochita utumiki wa nthawi zonse?
● Kodi luso lanu mungaligwiritse ntchito motani polemekeza Yehova?
● Pa mbali zosiyanasiyana za utumiki wa nthawi zonse zimene takambirana m’nkhaniyi, kodi ndi utumiki uti umene inuyo mukufunitsitsa kudzachita?
[Mawu Otsindika patsamba 313]
“Ndimalemekeza kwambiri makolo anga, chifukwa anali achangu kwambiri muutumiki, anapiririra mavuto azachuma ndiponso ankandilimbikitsa kuti ndichite utumiki wa nthawi zonse. Zimenezi zinandithandiza kwambiri.”—Anatero Jarrod
[Bokosi patsamba 314]
Zimene Munalemba
Zolinga Zanga
Chongani zolinga zimene mukufuna kukhala nazo. Lembani m’mipatamu zimene mukufuna kuchita mogwirizana ndi zolinga zanuzo kapena zolinga zina zimene mukufuna kukhala nazo.
Zolinga za mu Utumiki
□ Kuwonjezera nthawi imene ndimathera mu utumiki kufika pa ․․․․․ maola mwezi uliwonse
□ Kugawira zofalitsa ․․․․․ mwezi uliwonse
□ Kugwiritsa ntchito Baibulo ndikamalankhula ndi ena zimene ndimakhulupirira
□ Kupanga maulendo obwereza mwezi uliwonse
□ Kuyambitsa ․․․․․ phunziro la Baibulo
Zolinga zina: ․․․․․
Zolinga Zokhudza Kuphunzira
□ Kuwerenga masamba ․․․․․ a Baibulo tsiku lililonse
□ Kukonzekera misonkhano ya mlungu uliwonse
□ Kufufuza mozama nkhani za m’Baibulo zotsatirazi: ․․․․․
Zolinga za ku Mpingo
□ Kuyankhapo ngakhale kamodzi kokha pamsonkhano uliwonse
□ Kuyamba kukambirana ndi munthu wina wachikulire amene ndikufuna kum’dziwa bwino
□ Kuchezera munthu wachikulire kapena amene akudwala wa mumpingo mwathu
Zolinga zina: ․․․․․
Deti Lalero ․․․․․
Pakatha miyezi 6, onani zimene mwachita pokwaniritsa zolinga zanuzo. Mungasinthe kapena kuwonjezera zolingazo ngati pakufunika kutero.
[Chithunzi patsamba 312]
Kukhala ndi zolinga kungakuthandizeni kuti musamawonongere mphamvu zanu pa zinthu zopanda ntchito