Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Amandidzudzula Pachilichonse?

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Amandidzudzula Pachilichonse?

Mutu 21

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Amandidzudzula Pachilichonse?

“Amayi anga ankangokhala ngati wapolisi wofufuza milandu, nthawi zonse ankangofuna kundipezera zifukwa. Ndisanamalize n’komwe ntchito imene andipatsa, ankayendera kuti aone chimene ndalakwitsa.”—Anatero Craig.

“Makolo anga ankandikalipira nthawi zonse. Iwo ankati palibe chilichonse chimene ndikuchita bwino kaya kusukulu, kunyumba ngakhalenso kumpingo.”—Anatero James.

KODI mukuganiza kuti makolo anu amaona kuti palibe chilichonse chimene mumachita bwino? Kapena mumaona kuti makolo anu amakonda kufufuza chilichonse chimene mwachita kuti aone ngati chili bwino, koma palibe chomwe amakhutira nacho?

Pazinthu zotsatirazi, kodi ndi ziti zimene amakuuzani kawirikawiri?

□ Nthawi zonse zinthu zimakhala zili mbwee m’chipinda mwako.

□ Umaonera kwambiri TV.

□ Umagona mochedwa kwambiri.

□ Umadzuka mochedwa nthawi zonse.

Pamzere umene uli m’munsiwu, lembani chinthu chimodzi chimene chimakuipirani kwambiri makolo anu akamakukumbutsani kapena kukudzudzulani.

․․․․․

N’zoona kuti mungakwiye ngati makolo anu amangokhalira kukulamulani komanso kukudzudzulani. Koma taganizirani izi: Makolo anu akanakhala kuti sakulangizani kapena kukudzudzulani, kodi munganene kuti amakukondanidi? (Aheberi 12:8) Dziwani kuti iwo amakulangizani chifukwa choti amakukondani. Ndipotu Baibulo limati atate amadzudzula “mwana amene akondwera naye.”—Miyambo 3:12.

Motero makolo anu akamakudzudzulani, muyenera kuyamikira kuti amakukondani. Ndipotu inuyo ndinu mwana ndipo simukudziwa zambiri, choncho nthawi ina iliyonse mungafunike kupatsidwa malangizo. Popanda kupatsidwa malangizo alionse, zingakhale zosavuta kuti musokonezedwe ndi “zilakolako za unyamata.”—2 Timoteyo 2:22.

Komatu Zimandiwawa

N’zoona kuti “palibe kulanga kumene kumamveka kosangalatsa panthawiyo.” (Aheberi 12:11) Nthawi zambiri achinyamata ndi amene sasangalala akamalangizidwa. Ndipotu zimenezi n’zomveka chifukwa chakuti panthawi imeneyi mumakhala mukukula ndipo maganizo anu amasinthasintha. Choncho, nthawi zina mungakhumudwe ngakhale mutadzudzulidwa mwachikondi.

Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa chakuti mmene ena amakuonerani zimakhudza mmene mumachitira zinthu. Ndipo zimene makolo anu anganene zingakhudze kwambiri mmene mumadzionera. Motero mungakhumudwe kwambiri makolo anu atakudzudzulani kapena kudandaula ndi zomwe mukuchita.

Makolo anu akakudzudzulani chifukwa cha zinthu zina zimene mwalakwitsa, kodi zikutanthauza kuti palibe chilichonse chimene mungachite bwino kapena kuti ndinu wolephereratu? Ayi. Tonsefe timaphonyetsa zinthu zambirimbiri chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro. (Mlaliki 7:20) Ndipo munthu akamaphunzira sangalephere kulakwitsa. (Yobu 6:24) Nanga bwanji ngati makolo anu amakonda kukukalipirani mukalakwitsa chinachake, koma osakuyamikirani mukachita bwino? Zimenezo zingakhale zowawa, komatu sizitanthauza kuti ndinu wolephereratu.

Dziwani Zifukwa Zake

Nthawi zina mayi kapena bambo anu angathe kumangokukalipirani chifukwa choti sikunawachere bwino, osati chifukwa chakuti mwalakwitsa chinthu chinachake. Kodi pali chilichonse chimene chasokoneza maganizo mayi anu patsikulo? Kodi akuvutika ndi matenda enaake? Ngati zili choncho, iwo angathe kungokukalipirani ngati simunakonze m’chipinda mwanu mmene iwowo amafunira. Kodi bambo anu ndi okhumudwa chifukwa cha mavuto azachuma? Ngati zili choncho, angalankhule mosaganizira “ngati kupyoza kwa lupanga.” (Miyambo 12:18) N’zoona kuti simungasangalale kukalipiridwa popanda chifukwa chomveka. Ndipo kumangoganizira zakuti akulakwirani kungakupangitseni kuti mukwiye kwambiri, koma ndi bwino kuyesetsa kuwakhululukira zolakwa zawo. Kumbukirani kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri. Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.”—Yakobe 3:2.

Popeza kuti makolo anu ndi opanda ungwiro, nawonso angamavutike maganizo podziona ngati akulephera kukwaniritsa udindo wawo. Inuyo mukalephera chinachake, makolo anu angadzimve kuti iwowo ndi amene alephera. Mwachitsanzo, mayi angakalipire mwana wake akalephera mayeso. Koma n’kutheka kuti zimene mayiyo akuganiza zingakhale zakuti, ‘Ndikuona kuti monga mayi, ndikulephera kulimbikitsa mwana wangayu kuti azikhoza bwino kusukulu.’

Muzikhala Wodekha Akamakudzudzulani

Kaya akukudzudzulani pazifukwa zotani, koma funso lofunika kuliganizira ndi lakuti: Kodi mungatani akamakudzudzulani? Choyamba, musafulumire kuwayankha. Lemba la Miyambo 17:27 limati: “Wopanda chikamwakamwa [kapena kuti wokhala chete] apambana kudziwa; ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.” Kodi mungatani kuti mukhale ndi ‘mtima wofatsa’ akamakudzudzulani? Yesani kuchita zotsatirazi:

Mvetserani. M’malo mofulumira kuyankha kapena kunena kuti simunalakwe, yesetsani kukhala chete ndi kumvetsera zimene makolo anu akunena. Wophunzira Yakobe anauza Akhristu kuti akhale ‘ofulumira kumva, odekha polankhula, osafulumira kukwiya.’ (Yakobe 1:19) Mukafulumira kuyankha mwaukali makolo anu akamakulankhulani, iwo angaganize kuti simukuwamvetsera. Zimenezi zingawakwiyitse ndipo m’malo moti asiye kukudzudzulani, mwina zingachititse kuti akudzudzuleni kwambiri.

Ganizirani zimene akunenazo. Nthawi zina mungaone kuti makolo anu sanakulankhuleni bwino pokudzudzulani. Komabe, m’malo moganizira kwambiri mmene alankhulira, ndi bwino kuganizira zimene anenazo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi zoona kuti akungondidzudzula koma sindinalakwitse chilichonse? Kodi anayamba andidzudzulapo kale pankhani imeneyi? Kodi ndikamvera zimene iwo akunena ndioneka ngati wotsika?’ Ngakhale kuti sizingakusangalatseni akamakudzudzulani, kumbukirani kuti makolo anu amachita zimenezo chifukwa chokukondani. Akanakhala kuti sakukondani, akanangokusiyani osamakudzudzulani n’komwe.—Miyambo 13:24.

Bwerezani. Kunenanso mwaulemu zimene makolo anu akuuzani, kumasonyeza kuti mwawamvetsa bwino. Mwachitsanzo, iwo angakuuzeni kuti: “Nthawi zonse umasiya m’chipinda mwako muli mwauve. Ukapanda kukonzamo, ndikukhaulitsa.” Mwina panthawi imeneyi inuyo mukuona kuti m’chipindamo muli bwinobwino. Koma kuwauza zimenezi sikungathandize. Choncho, yesani kuona zinthu mmene iwo akuonera. Mungachite bwino kuwayankha mwaulemu kuti: “Mukunena zoona, m’chipinda mwangadi ndi mwauve. Kodi ndikonzemo panopa kapena tikamaliza kudya?” Kuyankha m’njira imeneyi kungawachititse kuti asakukalipireni kwambiri chifukwa angaone kuti mwawamvetsa. Komabe, muzionetsetsa kuti mwachita zimene makolo anu akuuzani.—Aefeso 6:1.

Dikirani kaye. Musafulumire kuuza makolo anu kuti simunalakwitse mpaka mutachita zimene iwo akukuuzani. Baibulo limati: “Wokhala chete achita mwanzeru.” (Miyambo 10:19) Iwo akaona kuti mumamvetseradi akamakulankhulani, nawonso angamakumvetsereni kwambiri mukamalankhula nawo.

Pamfundo zinayi zimene taonazi, lembani pamzera uwu mfundo imodzi imene mukufunikira kuigwiritsa ntchito kwambiri. ․․․․․

M’pofunikadi Khama

Kodi simungalolere kuvutika n’cholinga choti mupeze golide? Baibulo limanena kuti nzeru ndi yamtengo wapatali kwambiri kuposa chuma china chilichonse. (Miyambo 3:13, 14) Kodi mungatani kuti mukhale wanzeru? Lemba la Miyambo 19:20 limati: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pachimaliziro chako.” N’zoona kuti nthawi zina uphungu sungakusangalatseni. Koma mukapatsidwa uphungu, n’kusankhapo mfundo zothandiza zoti muzigwiritse ntchito, mudzapeza chuma chamtengo wapatali kwambiri kuposa golide.

Kunena zoona, munthu aliyense salephera kudzudzulidwa. Panopa muyenera kumapirira, makolo komanso aphunzitsi anu akamakudzudzulani. M’tsogolo muno, mudzakumananso ndi mabwana komanso anthu ena ndipo mudzafunika kumapirira. Mukadziwa panopa zimene muyenera kuchita wina akamakudzudzulani, maphunziro anu kusukulu aziyenda bwino, mudzakhala munthu wodalirika pantchito, komanso mudzakhala munthu wodzidalira m’zochita zanu zonse. Mosakayikira, kuti zimenezi zitheke, m’pofunika kuti muzipirira mukamadzudzulidwa.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mumaona kuti malamulo a panyumba panu akukuphwanyirani ufulu? Onani zimene zingakuthandizeni kukhala wokhutira ndi ufulu umene muli nawo, komanso zimene mungachite kuti mupeze ufulu wowonjezereka.

LEMBA LOFUNIKA

“Wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira.”—Miyambo 1:5.

MFUNDO ZOTHANDIZA

Kuti musamavutike kulandira uphungu wochokera kwa makolo anu . . .

muzisangalala ndi mfundo iliyonse yokuyamikirani imene angatchule pamene akukupatsani uphungu.

muzifunsa ngati simunamvetse zimene iwo akunena kuti mwalakwitsa kapena zimene akufuna kuti muchite.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Makolo ena zimawavuta kusonyeza ana awo chikondi chifukwa chakuti panthawi imene iwo anali ana sankakondedwa ndi makolo awo.

ZOTI NDICHITE

Makolo anga akamandidzudzula, ndizichita izi: ․․․․․

Ndikaona kuti makolo anga akungondidzudzula pachilichonse, ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuvomereza makolo anu akamakudzudzulani?

Kodi makolo anu angakudzudzuleni chifukwa chiyani?

Kodi mungatani kuti mupindule ndi uphungu uliwonse umene mungapatsidwe?

[Mawu Otsindika patsamba 177]

M’mbuyomu mayi anga akamandikalipira, ine ndinkawayankha mwamwano. Koma panopa ndimayesetsa kugwiritsa ntchito malangizo a m’Mawu a Mulungu ndipo akundithandiza kwambiri. Mayi anganso ayamba kusintha. Kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kwandithandiza kuti ndiziwamvetsa bwino kwambiri mayi angawo. Ndipo panopa timakondana kwambiri.’’—Anatero Marleen

[Chithunzi patsamba 180]

Pauphungu uliwonse umene mwapatsidwa mukasankhapo mfundo zothandiza n’kuzigwiritsa ntchito, mudzapeza chuma chamtengo wapatali kwambiri kuposa golide