Moyo wa Kusukulu
Chigawo 4
Moyo wa Kusukulu
Kodi pali maphunziro ena amene amakuvutani kwambiri?
□ Inde
□ Ayi
Kodi munayamba mwavutitsidwapo kapena kuchitiridwa zachipongwe ndi anzanu a kusukulu?
□ Inde
□ Ayi
Kodi nthawi zina mumatengeka ndi makhalidwe a anzanu a kusukulu?
□ Inde
□ Ayi
Mwina mungaganize kuti: ‘Ngati nditakwanitsa kumaliza sukulu bwinobwino ndiye kuti palibenso china chilichonse chimene chingandivute.’ Zimenezi zikhoza kukhala zoona chifukwa kusukulu n’kumene kumavuta kwambiri kuti munthu asonyeze kuti ndi wanzeru, wosakwiya msanga ndiponso wokonda Mulungu. Kodi mungatani kuti muphunzire bwinobwino popanda kutengera makhalidwe oipa a anzanu a kusukulu? Mitu 13 mpaka 17 ikuthandizani kwambiri pankhani zimenezi.
[Chithunzi chachikulu pamasamba 112,
113]