Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhoza Bwino Kusukulu?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhoza Bwino Kusukulu?

Mutu 13

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhoza Bwino Kusukulu?

TAYEREKEZERANI kuti mwasochera m’nkhalango yowirira kwambiri ndipo simukuonanso kuwala. Mukulephera kuyenda bwinobwino chifukwa chakuti m’nkhalangomo muli mitengo yothithikana ndi ziyangoyango zambirimbiri. Koma mutakhala ndi chikwanje mungathe kudula ziyangoyangozo n’kutuluka bwinobwino m’nkhalangomo.

Ena amaona kuti umu ndi mmene sukulu ilili. Zoonadi, sukulu ndi yovuta chifukwa tsiku lonse limatha uli m’kalasi ndipo usiku umangokhalira kuwerenga. Kodi inunso mumamva choncho? Lembani phunziro limene limakuvutani kwambiri pa mzere uwu.

․․․․․

Mwina makolo ndi aphunzitsi anu amakuuzani kuti muzilimbikira kwambiri phunziro limeneli. Cholinga chawo sikukuvutitsani ayi koma amafuna kuti inuyo muzikhoza bwino m’kalasi. Koma kodi mungatani ngati zimene akufunazo zili zovuta kwa inuyo? Pamenepa mungadzimve ngati muli m’nkhalango, koma ngati mutagwiritsira ntchito zipangizo zoyenera mungathe kutulukamo. Kodi tingati ndi zipangizo zotani zimene mungagwiritse ntchito?

Chipangizo Choyamba: Muzikonda maphunziro. N’zovuta kuti muzilimbikira sukulu ngati mumadana ndi maphunziro. Choncho ganizirani za kufunika kwake. Mtumwi Paulo anati: “Wolima ayenera kulima ndi chiyembekezo ndipo munthu wopuntha azipuntha ndi chiyembekezo chodzadya nawo.”—1 Akorinto 9:10.

Mwina simulimbikira maphunziro ena chifukwa chakuti mumaona kuti alibe phindu. Komabe maphunziro osiyanasiyana amakuthandizani kukhala munthu wodziwa zinthu. Angakuthandizeni kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana” ndipo mungamathe kukhala bwino ndi anthu osiyanasiyana. (1 Akorinto 9:22) Maphunzirowa angakuthandizeninso kuganiza bwino ndipo zimenezi zingadzakuthandizeni kwambiri m’tsogolo.

Chipangizo Chachiwiri: Musamadzikayikire. Dziwani kuti muli ndi luso limene ena alibe. Sukulu ingakuthandizeni kuti mudziwe luso limene muli nalo. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Ukolezere ngati moto mphatso ya Mulungu imene ili mwa iwe.” (2 Timoteyo 1:6) Nthawi imeneyi n’kuti Timoteyo atapatsidwa udindo wapadera mumpingo wachikhristu. Komabe, iye nthawi zonse anafunikira kugwiritsa ntchito “mphatso” kapena kuti luso limene Mulungu anam’patsa. Komabe, ngakhale kuti Mulungu anakupatsani nzeru, simungakhoze bwino m’kalasi popanda kulimbikira. Choncho m’pofunika kulimbikira kuti muzikhoza bwino komanso kuti mukulitse luso limene muli nalo.

Musalole kuti mulephere kuchita bwino pamaphunziro anu chifukwa cha kudzikayikira. Mukayamba kudzikayikira, yesetsani kuganizira zinthu zimene mungathe kuchita bwino. Mwachitsanzo, anthu atamunyoza Paulo kuti satha kulankhula, iye anayankha kuti: “Ngati ndilibe luso la kulankhula, si kuti ndine wosadziwanso zinthu.” (2 Akorinto 10:10; 11:6) Paulo ankadziwa kuti panali zinthu zina zimene ankachita bwino komanso zina zimene sankachita bwino.

Kodi inunso mumadziwa zinthu zimene mumachita bwino? Ngati simudziwa, funsani munthu wachikulire amene mumagwirizana naye. Munthu wotero angakuthandizeni kuti mudziwe ndiponso kugwiritsa ntchito zinthu zimene mumachita bwino.

Chipangizo Chachitatu: Muziwerenga. Simungachite bwino kusukulu ngati simulimbikira. Zivute zitani muyenera kuwerenga basi. Koma ena safuna kumva n’komwe mawu akuti kuwerenga. Komabe kuwerenga n’kofunika kwambiri. Mukalimbikira mudzaona kuti kuwerenga kumasangalatsa.

Muzionetsetsa kuti mukugwiritsa ntchito bwino nthawi imene mukuwerengayo. Dziwani kuti ngati muli pasukulu, kuwerenga n’kofunika kwambiri. Komabe, Baibulo limati pali “mphindi yakuseka,” ndiponso “mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4; 11:9) Choncho muyeneranso kukhala ndi nthawi yosangalala ngati mmene anzanu ena amachitira. * Koma lemba la Mlaliki 11:4 limati: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Muziyamba mwawerenga kaye musanayambe kucheza. Dziwani kuti n’zotheka kupeza nthawi yowerenga ndiponso yocheza.

Mfundo Zothandiza Powerenga

Kodi mungatani ngati muli ndi zinthu zambiri zoti muwerenge? Mwina mungamve ngati mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Sandrine, amene anati: “Usiku ulionse ndimawerenga kwa maola awiri kapena atatu ngakhalenso Loweruka ndi Lamlungu lomwe.” Kodi mungatani kuti muzitha kuwerenga maola ambiri? Tsatirani mfundo zimene zili patsamba 119.

Kodi Mungakwanitse Bwanji?

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti apite patsogolo mwauzimu pomuuza kuti: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” (1 Timoteyo 4:15) Choncho mukamalimbikira pamaphunziro anu, zidzadziwika kuti ndinu wanzeru.

Taganiziraninso chitsanzo chimene tafotokoza kumayambiriro kwa mutu uno. Kuti mutuluke m’nkhalango ija mufunika kugwiritsa ntchito chipangizo choyenerera monga chikwanje. N’chimodzimodzinso ndi sukulu. M’malo moona ngati makolo ndi aphunzitsi anu akukupanikizani kuchita zinthu zimene simungathe, yesani kugwiritsa ntchito zipangizo zitatu zimene takambiranazi. Mukayamba kuchita bwino pa maphunziro anu mudzakhala wosangalala kuti munagwiritsa ntchito zipangizo zimenezi.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 18

M’MUTU WOTSATIRA

Kuwonjezera pa kuvuta kwa maphunziro, anzanu angamakuvutitseni. Kodi mungatani pamenepa?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri, werengani Chigawo 8 cha buku lino.

LEMBA LOFUNIKA

“Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.”—Mlaliki 11:4.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musanayambe kuwerenga onani mwachidule nkhani imene mukufuna kuwerengayo. Ndiyeno dzifunseni mafunso pogwiritsa ntchito mitu ing’onoing’ono ya m’nkhaniyo. Kenako werengani nkhaniyo ndipo fufuzani mayankho a mafunso aja. Pomaliza yesani kukumbukira zimene mwawerenga.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu wobera mayeso amakhala wosadalirika ndiponso maphunziro ake sayenda bwino. Komanso Mulungu sasangalala ndi munthu wotero.—Miyambo 11:1.

ZOTI NDICHITE

Ndikufuna kuti ndidzakhoze ․․․․․ pa phunziro ili: ․․․․․

Ndiyesetsa kulimbikira kwambiri phunziro limeneli pochita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani muyenera kulimbikira kwambiri maphunziro?

● Kodi inuyo mungamawerenge bwino nthawi iti?

● Kodi ndi malo ati kunyumba kwanu amene ali abwino kuwerengera?

● Kodi mungatani kuti masewera ndiponso zosangalatsa zisamakulepheretseni kulimbikira sukulu?

[Mawu Otsindika patsamba 117]

“Ndimaona kuti anzanga amene ankakonda kuwerenga ali kusukulu amakondanso kuwerenga zinthu zauzimu. Koma amene sankakonda kuwerenga ali kusukulu safuna n’komwe kuphunzira Baibulo paokha.”—Anatero Sylvie

[Bokosi/Chithunzi patsamba 119]

Pezani malo abwino owerengera. Malowo akhale opanda zosokoneza. Gwiritsani ntchito tebulo ndi mpando ngati zilipo, ndipo musayatse TV.

Yambani ndi zinthu zofunika. Popeza kuti sukulu ndi yofunika kwambiri, onetsetsani kuti musayatse TV mpaka mutamaliza kuwerenga.

Musamadumphitse. Pangani ndandanda yowerengera ndipo muziitsatira nthawi zonse.

Konzeranitu zoti muchite. Sankhani maphunziro omwe mukufuna kuwerenga ndipo alembeni mu ndandanda papepala. Ndipo phunziro lililonse mulipatse nthawi yake. Mukamaliza kuwerenga phunziro lililonse, lichongeni.

Muzipumira. Mukaona kuti mwatopa ndipo simukumvetsa zimene mukuwerengazo, muzipuma kaye pang’ono n’kuyambiranso.

Musamadziderere. Dziwani kuti chimene chimachititsa kuti munthu azikhoza kapena kulephera m’kalasi ndi kulimbikira osati nzeru chabe ayi. Musamakayikire kuti mungachite bwino pa maphunziro anu. Ndiyetu, muzilimbikira ndipo mudzayamba kukhoza bwino m’kalasi.

[Chithunzi pamasamba 116]

Sukulu ili ngati nkhalango yowirira, kuti mutulukemo bwinobwino mumafunika kugwiritsa ntchito zipangizo zoyenera