Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Thupi Langali Latani?

Kodi Thupi Langali Latani?

Mutu 6

Kodi Thupi Langali Latani?

“Ndinangoyamba kutalika kwambiri ndipo zimenezi zinkachititsa kuti mapazi ndi miyendo yanga zizipweteka. N’zoona kuti ndinkafuna nditatalika, koma sindinkasangalala chifukwa cha kupwetekako.”—Anatero Paul.

“Thupi likamasintha, umafuna kuti ena asadziwe. Komabe umangomva munthu wina, amene mwina alibe cholinga chokukhumudwitsa, akukuuza kuti ‘mwayamba mahipitu.’ Ukangomva zimenezi umangolakalaka utalowa pansi.”—Anatero Chanelle.

KODI munayamba mwasamukirapo ku malo achilendo? Ngati munatero, muyenera kuti munasiya zinthu zonse zimene munazizolowera monga nyumba yanu, sukulu ndiponso anzanu. N’kutheka kuti zinakutengerani nthawi ndithu kuti muzolowere malo atsopanowo.

Mukamakula thupi lanu limasintha ndipo pali zinthu zinanso zimene zimasintha pamoyo wanu. Choncho mumakhala ngati mwasamukira kumalo achilendo ndipo zimatenga nthawi kuti muzolowere. Nthawi imeneyi imakhala yosangalatsa kwambiri koma ilinso ndi mavuto ake. Kodi n’chiyani kwenikweni chimachitika pa nthawi imeneyi?

Mtsikana Akamakula

Mtsikana akamakula thupi lake limasintha m’njira zambiri. Mwachitsanzo, tsitsi limamera malo ena. Amayamba kumera mabere, ndipo amakula ntchafu ndi matako. Pang’ono ndi pang’ono amasintha n’kuyamba kuoneka ngati mzimayi. Koma sayenera kuchita mantha chifukwa chimenechi ndi chizindikiro choti akukula ndipo wafika msinkhu woti angathe kukhala ndi mwana.

Kenako, amayamba kusamba. Ngati sakuzidziwa bwino, zimenezi zingamuchititse mantha. Mtsikana wina dzina lake Samantha, anati: “Pamene ndinkayamba kusamba sindinkadziwa kuti chikundichitikira n’chiyani. Ndinkaona kuti ndine wauve kwambiri. Ndinkadzinyula kwambiri posamba ndipo ndinkangoti ‘ndine wochititsa nyansi.’ Ndinachita mantha kwambiri nditadziwa kuti ndizisamba mwezi ndi mwezi.”

Komabe dziwani kuti kusamba ndi chizindikiro chakuti mwafika poti mutha kutenga mimba ngakhale kuti payenera kudutsa zaka zambiri kuti mudzakhale kholo. Koma kusamba kumabweretsa mavuto ena. Mtsikana wina dzina lake Kelli, anati: “Vuto langa lalikulu linali lakuti ndinkasinthasintha, pena kusangalala pena kukhumudwa. Zinkandikwiyitsa kwambiri chifukwa sindinkadziwa chimene chinkachititsa kuti masana onse ndikhale wosangalala koma usiku n’kuyamba kulira kwambiri.”

Ngati inunso mukumva choncho, musade nkhawa chifukwa muzolowera. Mtsikana wina wa zaka 20, dzina lake Annette, anati: “Pamapeto pake ndinavomereza kuti zimenezi ziyenera kundichitikira monga mkazi wina aliyense amene Yehova anam’patsa mphatso yobereka. Zimatenga nthawi kuti munthu avomereze zimenezi ndipo ndi zovuta kwa atsikana ena, komabe umafika pozizolowera.”

Kodi zina mwa zinthu zimene tafotokozazi zayamba kale kukuchitikirani? M’mizere ili m’munsiyi, lembani funso lililonse lokhudza zimene zikukuchitikirani.

․․․․․

Mnyamata Akamakula

Mnyamatanso akamakula thupi lake limasintha kwambiri. Ena khungu lawo limakhala ndi mafuta ambiri ndipo mafutawa amachititsa kuti azituluka ziphuphu. * Mnyamata wina wazaka 18, dzina lake Matt, anati: “Zimapsetsa mtima munthu ukatuluka ziphuphu zambirimbiri. Nthawi zonse umangoganiza za njira yothetsera ziphuphuzo. Umaona ngati sizidzatha kapena zidzakusiyira zipsera kapenanso anzako azingokunyoza chifukwa cha ziphuphuzo.”

Komabe nkhani yabwino ndi yakuti mukamakula mumakhala ndi mphamvu ndiponso mapewa anu amatambalala. Komanso, panthawi imeneyi mumamera tsitsi m’miyendo, pachifuwa, kumaso ndiponso m’khwapa. Komabe kukhala ndi tsitsi lochepa sikutanthauza kuti siinu mwamuna weniweni. Chibadwa ndi chimene chingachititse munthu kukhala ndi tsitsi lambiri kapena lochepa.

Nthawi zina mungafooke kwambiri chifukwa mbali zina za thupi lanu sizikula mwamsanga poyerekeza ndi zina. Dwayne anati: “Ndinkangomva ngati ndilibe mafupa. Ndikaganiza zoyenda, ndinkangoona ngati zinditengera chaka chathunthu kuti ndinyamule mwendo.”

Mukamafika zaka 14 kapena 15, pang’onopang’ono mawu anu amayamba kumveka besi. Kwa kanthawi mawu anuwo amamveka manzenene ndipo mungamachite manyazi kulankhula. Komabe musadandaule, chifukwa mawu anu adzasinthanso n’kuyamba kumveka bwinobwino. Imeneyi si nkhani yoti muzikwiya nayo muzingoona kuti n’zoseketsa basi.

Kenako maliseche amayamba kukula ndipo amamera tsitsi. Ndiyeno mumayamba kutuluka ubwamuna. Mwamuna akagona ndi mkazi, ubwamunawo umatha kukumana ndi dzira la mkaziyo n’kuyamba kupanga mwana.

Ubwamuna ukachuluka, nthawi zina umatuluka usiku mukagona. Limeneli si vuto ayi ndipo ngakhalenso m’Baibulo zimatchulidwa. (Levitiko 15:16, 17) Zimangosonyeza kuti mwafika msinkhu woti ngati mutagona ndi mkazi mutha kum’patsa mimba.

Kodi zina mwa zinthu zimene tafotokozazi zayamba kale kukuchitikirani? M’mizere imene ili m’munsiyi, lembani funso lililonse lokhudza zimene zikukuchitikiranizo.

․․․․․

Zimene Mungachite Thupi Lanu Likamasintha

Anyamata ndi atsikana akamakula, amayamba kusirirana. Matt anati: “Nditangoyamba kukula, ndinayamba kuona kuti kunja kuno kuli atsikana ambiri okongola. Zimenezi zinkandisokoneza kwambiri chifukwa ndinkadziwa kuti palibe chimene ndingapange mpaka nditafika nthawi yokwatira.” Mutu 29 wa buku lino ufotokoza zambiri za nkhani imeneyi. Komabe, mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti muyenera kudziletsa. (Akolose 3:5) Mungathe kudziletsa ngakhale kuti sizophweka.

Komanso pali zinthu zina zimene zingakuchitikireni mukamakula. Mwachitsanzo, mungayambe kudziona ngati ndinu wosafunika. Achinyamata ambiri amaona kuti palibe aliyense amene amawamvetsa ndiponso amavutika maganizo. Mukamamva choncho, ndi bwino kuuza makolo anu kapena munthu aliyense amene mumam’dalira. Lembani m’munsimu dzina la munthu wamkulu amene mukuona kuti mungamasuke kumuuza zakukhosi kwanu.

․․․․․

Kukula Kumene Kuli Kofunika Kwambiri

Kutalika, kusintha kwa thupi lanu kapena kaonekedwe ka nkhope yanu n’kofunika. Koma kukula kofunika kwambiri ndi kwa maganizo ndiponso kwauzimu. Mtumwi Paulo anati: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Pamenepa mfundo yaikulu ndi yakuti, kukhala munthu wamkulu kokha sikokwanira. Mufunika kulankhula, kuganiza ndiponso kuchita zinthu ngati munthu wamkulu. Musade nkhawa kwambiri ndi kusintha kwa thupi lanu mpaka kufika ponyalanyaza umunthu wanu wamkati.

Kumbukiraninso kuti Mulungu ‘amayang’ana mumtima.’ (1 Samueli 16:7) Baibulo limati Mfumu Sauli anali wamtali ndi wokongola, koma iye sanali munthu wabwino ndiponso anali mfumu yoipa. (1 Samueli 9:2) Limatinso Zakeyu “anali wamfupi” koma wodzichepetsa ndipo anasintha moyo wake n’kukhala wophunzira wa Yesu. (Luka 19:2-10) Choncho, umunthu wathu wamkati ndiwo wofunikira kwambiri.

Mfundo ndi yakuti: Simungathe kufulumizitsa kapena kuchedwetsa kukula kwa thupi lanu. Choncho m’malo mokwiya kapena kuchita mantha ndi mmene mukukulira, ingosangalalani kuti mukukula. Kukula si matenda ndipo sikungaphe munthu ayi. Komanso inuyo si munthu woyamba kukula. Mavuto onse omwe amakhalapo panthawiyi adzatha ndipo mudzakhala bwinobwino.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati simukusangalala ndi mmene mumaonekera mukadziyang’ana pa galasi? Kodi mungatani kuti musamakhumudwe ndi mmene mukuonekera?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Atsikananso amatuluka ziphuphu. Kusamalira bwino khungu kungathandize kuchepetsa vutoli.

LEMBA LOFUNIKA

‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.’—Salmo 139:14.

MFUNDO YOTHANDIZA

Thupi lanu likayamba kusintha, musamavale zovala zokopa anyamata kapena atsikana. Nthawi zonse muzivala “mwaulemu ndi mwanzeru.”—1 Timoteyo 2:9.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Thupi lanu lingathe kusintha kuyambira zaka 8 mpaka 14 kapenanso mutangodutsa zaka zimenezi.

ZOTI NDICHITE

Ndikamakula ndikufuna ndikhale munthu wakhalidwe lotere: ․․․․․

Kuti ndikhale wokonda Mulungu ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani munthu akamakula, amavutika ndi kusintha kwa thupi ndiponso maganizo ake?

N’chiyani chimene inuyo mukuvutika nacho kwambiri pa msinkhu wanu?

N’chiyani chimachititsa achinyamata ambiri kusiya kukonda Mulungu, ndipo mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?

[Mawu Otsindika patsamba 61]

“Pali mavuto ambiri amene amabwera ukamakula ndipo sudziwa kuti chikuchitikire n’chiyani. Koma kenako, umazizolowera.”—Anatero Annette

[Bokosi pamasamba 63, 64]

Kodi Ndingafunse Bwanji Bambo Kapena Mayi Anga Nkhani Zokhudza Kugonana?

“Nditakhala ndi funso lokhudza kugonana, sindingayerekeze dala kufunsa makolo anga.”—Anatero Beth.

“Sindingalimbe mtima kufunsa makolo anga.”—Anatero Dennis.

Ngati muli ndi maganizo ngati a Beth kapena Dennis, ndiye kuti zinthu sizili bwino. Makolo anu ndi amene angathe kukuyankhani ngati mutakhala ndi funso lililonse lokhudza kugonana. Koma ngati simumasuka nawo, mungade nkhawa kuti:

Kodi Ndikawafunsa Aganiza Chiyani?

“Ndikuopa kuti ndikawafunsa ayamba kundikayikira.”—Anatero Jessica.

“Ukangowafunsa za kugonana amayamba kuganiza kuti wayamba khalidwe loipa.”—Anatero Beth.

Kodi ndikawafunsa andiyankha bwanji?

“Ndimadziwa kuti ndikangoyerekeza kuwafunsa makolo anga ndiye kuti ndawapalamula dala malangizo.”—Anatero Gloria.

“Makolo anga sadziwa kulankhula monyengerera, choncho ndimachita mantha kuti ndikawafunsa akwiya kwambiri. Ndikudziwa kuti ndikangoyamba kulankhula, bambo akhala atayamba kale kuganizira malangizo oti andipatse.”—Anatero Pam.

Kodi andiganizira zolakwika ndikawafunsa?

“Angandikalipire ndi kuyamba kundifunsa kuti, ‘Ndiye kuti unagonanapo ndi winawake eti?’ kapena ‘Kodi alipo amene akukunyengerera kuti ugonane naye?’ Koma iweyo umakhala ukungofuna kudziwa basi.”—Anatero Lisa.

“Ndikangotchula za mnyamata bambo anga sasangalala. Nthawi yomweyo amangoyamba kundilangiza zokhudza kugonana. Mumtimamu ndimangoti, ‘Nanga ndalakwa chiyani? Inetu ndangonena kuti mnyamatayo ndi wooneka bwino, sindinanene kuti ndikufuna kukwatiwa kapena kugonana naye ayi.’”—Anatero Stacey.

Dziwani kuti makolo ena amachita manyazi kulankhula ndi ana awo nkhani zokhudza kugonana ndipo ana ena amachitanso manyazi kulankhula ndi makolo awo nkhani zimenezi. Ofufuza ena atsimikizira kuti zimenezi n’zoona. Iwo apeza kuti makolo 65 pa 100 alionse amene anawafunsa ananena kuti amalankhula ndi ana awo nkhani za kugonana. Koma zimene ananena makolozi sizoona kwenikweni chifukwa ndi ana 41 okha pa 100 alionse amene anavomereza kuti makolowo anakambirana nawodi zimenezi.

Mfundo ndi yakuti, makolo anu angachite manyazi kukambirana nanu nkhani zokhudza kugonana. Nthawi zambiri zimakhala kuti agogo anu sankakambirana zimenezi ndi makolo anuwo. Motero musachite kuwakakamiza. Komabe mwina mungalimbe mtima n’kupeza njira yabwino imene ingathandize nonsenu kuti mukambirane nkhaniyi.

Mungachite bwanji zimenezi?

Makolo anu amadziwa zambiri zokhudza nkhani za kugonana. Mungofunikira kupeza njira yoti muyambe kukambirana nawo. Yeserani izi:

1 Auzeni makolo anu kuti mukuchita mantha koma mukufunabe kukambirana nawo nkhaniyi, nenani kuti: “Ndikulephera kukuuzani nkhani inayake chifukwa ndikuopa muganiza kuti . . . ”

2 Kenako auzeni makolo anu zimene mukufuna kukambirana nawo, ponena kuti: “Ndili ndi funso limene sindikufuna kufunsa wina aliyense koma inuyo.”

3 Kenako ingonenani nkhaniyo motere: “Ndimafuna ndidziwe kuti, kodi . . . ”

4 Mukamaliza kukambiranako, apempheni kuti mudzakambirane nawonso m’tsogolo. Auzeni kuti: “Ndikadzakhala ndi funso lina, kodi ndingadzakufunseninso?”

Ngakhale mutadziwa kuti makolo anu avomera, ndi bwinobe kuwafunsa chifukwa akayankha okha kuti inde mudzakhala omasuka kwambiri kudzalankhula nawonso nthawi ina. Yeserani zimenezi. Mwina mungagwirizane ndi zimene ananena Trina amene tsopano ali ndi zaka 24. Iye anati: “Ndikulankhulana ndi mayi anga za nkhaniyi, iwo anandiuza chilichonse mosabisa mawu ndipo ndinayamba kuganiza kuti, ‘Kaya ndinaiyambitsiranji nkhani imeneyi?’ Koma panopa ndimasangalala kuti anatero chifukwa zandithandiza kwambiri.”

[Chithunzi patsamba 59]

Mukamakula mumakhala ngati mukusamukira ku dera lina, koma pakapita nthawi mumazolowera