Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?

Mutu 37

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?

Pamfundo zotsatirazi, chongani kuti zoona kapena zonama:

Ubatizo ndi wofunika kwa Mkhristu aliyense.

□ Zoona

□ Zonama

Cholinga chachikulu cha ubatizo ndicho kukutetezani kuti musachite tchimo.

□ Zoona

□ Zonama

Ubatizo umakuthandizani kuti mudzapulumuke.

□ Zoona

□ Zonama

Ngati simunabatizidwe, Mulungu sakuimbani mlandu pa zochita zanu.

□ Zoona

□ Zonama

Ngati anzanu akubatizidwa, ndiye kuti inunso mukhoza kubatizidwa.

□ Zoona

□ Zonama

NGATI mukutsatira mfundo za Mulungu, mukuchita zinthu zokuthandizani kukhala naye paubwenzi ndiponso mukuuza ena zimene mumakhulupirira, sizingakhale zachilendo kufuna kubatizidwa. Komano kodi mungadziwe bwanji ngati ndinu wokonzeka kubatizidwa? Kuti muyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane mfundo zimene zili pamwambazi.

Ubatizo ndi wofunika kwa Mkhristu aliyense.

Zoona. Yesu analamula kuti ophunzira ake azibatizidwa. (Mateyo 28:19, 20) Ndipotu, ngakhale Yesu mwiniwakeyo anabatizidwa. Kuti mukhale wotsatira wa Khristu, muyenera kubatizidwa ngati mwakula kufika pamsinkhu woti mungathe kusankha zoti mubatizidwe komanso ngati muli wofunitsitsa kutero.

Cholinga chachikulu cha ubatizo ndicho kukutetezani kuti musachite tchimo.

Zonama. Ubatizo ndi chizindikiro cha pagulu chosonyeza kuti munadzipereka kwa Yehova. Kudzipereka kwanu kwa Yehova si pangano limene lingakulepheretseni kuchita zinthu zimene mungakonde kuchita muli kwanokha. M’malo mwake, munthu amadzipereka kwa Yehova chifukwa choti akufunitsitsa kutsatira malamulo ake.

Ubatizo umakuthandizani kuti mudzapulumuke.

Zoona. Baibulo limati ubatizo ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene munthu ayenera kuchita kuti adzapulumuke. (1 Petulo 3:21) Komabe, izi sizikutanthauza kuti munthu akabatizidwa ndiye kuti basi, adzapulumuka. Chifukwa chimene muyenera kubatizidwira n’choti mumakonda Yehova ndipo mukufuna kumutumikira ndi mtima wanu wonse kwamuyaya.—Maliko 12:29, 30.

Ngati simunabatizidwe, Mulungu sakuimbani mlandu pa zochita zanu.

Zonama. Kaya munthu ndi wobatizidwa kapena ayi, Baibulo limati ngati “akudziwa kuchita chabwino koma sachita, akuchimwa.” (Yakobe 4:17) Choncho ngati mukudziwa zinthu zabwino zimene muyenera kuchita ndipo ndinu wamkulu ndithu moti mungathe kuganizira mofatsa zamoyo wanu, mwina ndi bwino kuti panopa mukambirane nkhaniyi ndi makolo anu kapena Mkhristu wolimba mwauzimu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudziwe zimene mungachite kuti mufike pobatizidwa.

Ngati anzanu akubatizidwa, ndiye kuti inunso mukhoza kubatizidwa.

Zonama. Munthu amayenera kusankha yekha kuti akufuna kubatizidwa. (Salmo 110:3) Muyenera kubatizidwa ngati mwadziwa zinthu zonse zimene muyenera kuchita monga wa Mboni za Yehova, ndiponso mukaona kuti mukhoza kukwanitsa kuchita zimenezo.—Mlaliki 5:4, 5.

Ubatizo Umasintha Moyo Wanu

Ubatizo umasintha moyo ndipo munthu akabatizidwa amadalitsidwa kwambiri. Komabe, munthu akabatizidwa amakhala ndi udindo waukulu wochita zinthu mogwirizana ndi lonjezo la kudzipereka kwake kwa Yehova.

Ndiyeno, kodi ndinu wokonzeka kubatizidwa? Ngati ndi choncho, muyenera kukhala wosangalala kwambiri. Mukabatizidwa, mudzakhala ndi mwayi wamtengo wapatali wotumikira Yehova ndiponso wokhala ndi moyo wosonyeza kuti munadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse.—Mateyo 22:36, 37.

M’MUTU WOTSATIRA

Onani zimene mungachite kuti mukhale ndi zolinga pamoyo wanu ndiponso kuti zinthu zizikuyenderani bwino.

LEMBA LOFUNIKA

“Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira.”—Aroma 12:1.

MFUNDO YOTHANDIZA

Mothandizidwa ndi makolo anu, pezani munthu wina mumpingo amene angakuthandizeni kuti mupite patsogolo mwauzimu.—Machitidwe 16:1-3.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ubatizo ndi mbali yofunika kwambiri ya “chizindikiro” chimene chimasonyeza kuti munthu ndi woyenera kudzapulumuka.—Ezekieli 9:4-6.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndifike pobatizidwa, ndiyesetsa kuti ndimvetse bwino mfundo za m’Baibulo zotsatirazi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani ubatizo si nkhani ya masewera?

● N’chiyani chingachititse wachinyamata kubatizidwa asanakonzekere?

● Kodi n’chiyani chingachititse wachinyamata kuzengereza kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa?

[Mawu Otsindika patsamba 306]

“Kukumbukira kuti ndine wobatizidwa kunandithandiza kusankha zinthu mwanzeru ndiponso kupewa zinthu zimene zikanandilowetsa m’mavuto aakulu.”—Anatero Holly

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 307]

Zimene Anthu Amafunsa Kawirikawiri Zokhudza Ubatizo

Kodi ubatizo umaimira chiyani? Kumizidwa ndi kuvuulidwa m’madzi kumatanthauza kuti mwasiya moyo wongochita zimene mukufuna ndipo tsopano mukuyamba moyo wochita chifuniro cha Yehova.

Kodi kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kupereka moyo wanu wonse kwa Mulungu ndi kulonjeza kuti muziika zofuna zake pamalo oyamba m’moyo wanu. (Mateyo 16:24) Choncho, muyenera kudzipereka kwa Yehova m’pemphero musanabatizidwe.

Kodi muyenera kumachita zotani musanabatizidwe? Muyenera kumachita zinthu zogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndiponso kuuza ena zimene mumakhulupirira. Muyeneranso kumapemphera ndiponso kuphunzira Mawu ake, zimene zingakuthandizeni kukhala naye paubwenzi. Komanso, muyenera kumatumikira Yehova chifukwa choti mwasankha nokha kuchita zimenezo, osati chifukwa chokakamizidwa ndi ena.

Kodi munthu ayenera kubatizidwa akafika zaka zingati? Zaka kapena kuti msinkhu wa munthu si zofunika kwenikweni kuti munthu abatizidwe. Komabe, muyenera kukhala wamkulu ndithu moti mukhoza kumvetsa tanthauzo la kudzipereka kwanu kwa Mulungu.

Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kubatizidwa koma makolo anu akukuuzani kuti mudikire kaye? Mwina iwo akuchita zimenezo n’cholinga choti mukule kaye mwauzimu. Mverani malangizo awowo, ndipo poyembekezera ubatizowo, gwiritsani ntchito nthawi imeneyo kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova.—1 Samueli 2:26.

[Bokosi pamasamba 308, 309]

Zimene Munalemba

Kodi Mukufuna Kubatizidwa?

Gwiritsani ntchito mafunso ndi mfundo zotsatirazi kuti muone ngati mwapita patsogolo mwauzimu moti n’kubatizidwa. Musanalembe mayankho anu, onetsetsani kuti mwawerenga malembawo.

Kodi panopa mukusonyeza m’njira ziti kuti mumadalira Yehova?Salmo 71:5. ․․․․․

Kodi mwachitapo zotani zimene zikusonyeza kuti muli ndi luntha la kuzindikira ndipo mumatha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika?Aheberi 5:14. ․․․․․

Kodi mumapemphera nthawi zonse? ․․․․․

Mukamapemphera, kodi mumatchula mwachindunji zimene mukufuna? Nanga mapemphero anuwo amasonyeza kuti mumakondadi Yehova?Salmo 17:6. ․․․․․

Lembani m’munsimu zolinga zilizonse zimene mukufuna kukhala nazo pankhani ya pemphero. ․․․․․

Kodi mumaphunzira Baibulo panokha nthawi zonse?Yoswa 1:8. ․․․․․

Kodi mumachita zinthu zotani paphunziro lanu laumwini? ․․․․․

Lembani m’munsimu zolinga zilizonse zimene mukufuna kukhala nazo pankhani ya phunziro laumwini. ․․․․․

Kodi mumachita utumiki wanu mogwira mtima? (Mwachitsanzo: Kodi mungakwanitse kufotokozera anthu ena mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Kodi mumachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi? Kodi mukuyesetsa kuti mukhale ndi phunziro la Baibulo lapanyumba?)

□ Inde □ Ayi

Kodi mumalowa mu utumiki ngakhale ngati makolo anu sanalowe?Machitidwe 5:42.

□ Inde □ Ayi

Lembani m’munsimu zolinga zilizonse zimene mukufuna kukhala nazo pankhani ya utumiki.2 Timoteyo 2:15.

Kodi mungati mumafika pamisonkhano nthawi zonse kapena ayi?Aheberi 10:25.

Kodi mumatenga mbali pamisonkhano m’njira ziti?

Kodi mumapita ku misonkhano ngakhale ngati makolo anu sanapite (ngati akulolezani kutero)?

□ Inde □ Ayi

Kodi mungati mumakondadi kuchita chifuniro cha Mulungu?Salmo 40:8.

□ Inde □ Ayi

Kodi ndi pazochitika zotani pamene munakana kutengera zochita za anzanu?Aroma 12:2. ․․․․․

Kodi mukukonza zotani kuti mupitirize kukonda kwambiri Yehova?Yuda 20, 21. ․․․․․

Kodi mungapitirize kutumikira Yehova ngakhale makolo anu ndiponso anzanu atasiya kum’tumikira?Mateyo 10:36, 37.

□ Inde □ Ayi

[Chithunzi patsamba 310]

Ubatizo uli ngati ukwati chifukwa umasintha moyo wa munthu. Choncho, ndi bwino kuganiza mofatsa musanabatizidwe