Nkhani Zokhudza Ndalama
Chigawo 5
Nkhani Zokhudza Ndalama
Kodi mumaona kuti ndalama n’zofunika kuti mukhale wosangalala?
□ N’zosafunika
□ N’zofunika pang’ono
□ N’zofunika kwambiri
Kodi mumakonda kulankhula za ndalama ndiponso zinthu zimene mungagule?
□ Ayi
□ Nthawi zina
□ Nthawi zambiri
N’kutheka kuti makolo anu akuuzanipo mobwerezabwereza kuti ndalama zimafunika kukhetsera thukuta. Zimenezo n’zoona, ndipo n’chifukwa chake muyenera kuzigwiritsa ntchito mosamala. Ngakhale kuti ndalama n’zofunika, zikhoza kukusokonezani maganizo, kukudanitsani ndi anthu ena, ndiponso zingawonongetse ubwenzi wanu ndi Mulungu. Ndipotu moyo wanu ungakhudzidwe kwambiri ndi mmene mumaonera ndalama. Werengani Mitu 18 mpaka 20 kuti muziona ndalama m’njira yoyenera.
[Chithunzi chachikulu pamasamba 148, 149]