Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Malangizo Abwino Ndingawapeze Kuti?

Kodi Malangizo Abwino Ndingawapeze Kuti?

Mawu Oyamba

Kodi Malangizo Abwino Ndingawapeze Kuti?

Atsikana

M’kalasi mwanu mwabwera mnyamata wina wooneka bwino. Ndipo mwayamba kumangoganiza za iyeyo. Mwina mumtima munganene kuti: ‘Sindikuona kuti pali vuto kumuganizira, ndiponso iyeyo sakudziwa n’komwe kuti ndikumuganizira.’ Mwinanso si inu nokha amene mumamufuna. Mwamvaponso atsikana ena akukamba za mnyamatayo.

Nthawi ina mwapezeka kuti mwakumana ndi mnyamatayo ndipo mukumwetulirana. Kenako mukuyamba kulankhulitsana.

Akukupatsani moni mwamanyazi kuti: “Uli bwanji?”

Ndipo inu mukumuyankha kuti:“Ndili bwino.”

Kenako akukuuzani kuti: “Dzina langa ndine Brett.”

Inuyo mukumufunsa kuti: “Paja wabwera kumene kunoko eti?”

Iye akuyankha kuti: “Inde tangosamukira kumene kunoko milungu yapitayi.”

Mukusangalala kwambiri kuti mwapeza mwayi wolankhulana ndi Brett. Kenako iye akukuuzani kuti:

“Ukudziwa, lero madzulo ano kwathu kuli phwando. Ubwera?”

Ndipo monong’ona akunenanso kuti:

“Makolo anga sadzakhalako, komanso kudzakhala mowa wambiri?”

Brett akuyembekezera kuti mumuyankhe. Ndipo mukudziwa kuti palibe mtsikana amene angamukane mnyamatayu.

Kodi pamenepa mungamuyankhe kuti chiyani?

Anyamata

Mukuona anyamata awiri a pasukulu panu akubwera poteropo. Ndipo mukuda nkhawa chifukwa mlungu wokha uno anyamatawa akukakamizani kawiri konse kuti musute fodya.

Mnyamata woyamba akunena kuti: “N’chifukwa chiyani umakonda kuyenda wekhawekha? Ndakupezera mnzako, ‘mnzako’ woti uzicheza naye.” Kenako akupisa m’thumba n’kutulutsa chinthu chinachake ndipo akukupatsani.

Inuyo mukuona kuti ndi ndudu ya fodya, ndipo mwayamba kuchita mantha choncho mukuyankha kuti:

“Ine zimenezo ayi. Ndinakuuzani kale kuti sindi . . . ”

Mnyamata wachiwiri uja akukudulani mawu, ndipo akunena kuti: “Kapena kutchalitchi kwanu sakulolani kusangalala eti?”

Mnyamata woyamba uja akukunyozani kuti: “Iwe ndiye khwangwala basi.”

Inuyo mukumuyankha molimba mtima kuti: “Ayi, sindine khwangwala.”

Kenako mnyamata wachiwiri uja akukolekera dzanja lake m’nkhosi mwanu, n’kunena kuti: “Eko, tasuta.”

Mnyamata woyamba akuyandikizitsa ndudu pakamwa panu ndipo monong’ona akukuuzani kuti: “Sitiuza aliyense.”

Kodi pamenepa mungatani?

ZOTEREZI zimachitika tsiku lililonse padziko lonse. Achinyamata ena amakonzekera kukana ngati anzawo atawauza kuchita zoipa. Achinyamata ena akakakamizidwa kuti asute fodya, amaganiza kuti: “Ndingosuta chifukwa sindikufuna kuti azindivutitsa. Ndiponso sindikufuna kuti aganize kuti ndine wotsalira.” Kapena mtsikana amene mnyamata wina akufuna kuti apite naye kwinakwake angaganize kuti: ‘Mnyamata uja ndi wooneka bwino. Kano kokha ndingomuvomera.’

Komabe, achinyamata ena anaphunzitsidwa kukana kuchita zinthu zoipa. Choncho iwo sagonja anthu ena akawakakamiza kuchita zoipa. Inunso mungathe kuchita zimenezi.

Baibulo lingakuthandizeni kuthana ndi mavuto amene achinyamatanu mumakumana nawo. Lili ndi malangizo abwino kwambiri chifukwa ndi Mawu a Mulungu. (2 Timoteyo 3:16, 17) Onani nkhani zimene zili m’munsizi ndipo muchonge zimene mukuona kuti zikukukhudzani.

Kusirira mnyamata kapena mtsikana

Kusintha kwa thupi

Anzanu ocheza nawo

Moyo wa kusukulu

Nkhani zokhudza ndalama

Makolo anu

Mtima wanu

Kusankha zosangalatsa

Kukula mwauzimu

Nkhani zimenezi zikupezeka m’zigawo 9 za buku lino monga mmene tasonyezera patsamba 4 ndi 5. Kodi inuyo mwachonga mitu iti? Mungachite bwino kuyamba kuwerenga zigawo zimenezo. Buku lino likuthandizani kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pankhani zimenezi. *

Mungathenso kulemba maganizo anu m’bukuli. Mwachitsanzo, chakumapeto kwa mutu uliwonse muzipeza bokosi lakuti “Zoti Ndichite.” M’bokosili muzilembamo mfundo zimene mukufuna kuzigwiritsira ntchito. Patsamba 132 ndi 133 pali bokosi lakuti “Mmene Mungakonzekerere.” Bokosi limeneli likuthandizani kuganizira mavuto amene mungakumane nawo ndi kupeza njira zowathetsera. Ndiponso kumapeto kwa chigawo chilichonse kuli tsamba lakuti “Mfundo Zanga.” Patsambali muzilembapo mmene nkhani iliyonse yakukhudzirani. M’chigawo chilichonse cha bukuli muzipezamo nkhani yakuti “Chitsanzo Chabwino.” Nkhani imeneyi izifotokoza za anthu otchulidwa m’Baibulo amene anasonyeza chitsanzo chabwino.

Baibulo limati: “Tenga nzeru, tenga luntha.” (Miyambo 4:5) Mawu akuti “nzeru” ndiponso “luntha” amatanthauza kudziwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Komanso munthu wanzeru ndi waluntha amatha kudziwiratu mapeto a chinthu chimene akufuna kuchita. Mwachitsanzo, anzanu akakukakamizani kuchita zinthu zoipa, mungathe kukana ngati mwadziwiratu mapeto ake.

Dziwani kuti si inu nokha amene mukukumana ndi mavuto. Pali achinyamata ambiri amene agonjetsa mavuto angati amene mukukumana nawowo. Inunso mungathe kuwagonjetsa. Liwerengeni bwinobwino bukuli. Zimenezi zikuthandizani kuona kuti Baibulo lili ndi malangizo abwino kwambiri omwe simungawapeze kwina kulikonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 40 Nkhani zambiri m’buku lino zatengedwa m’nkhani za mu Galamukani! zakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa.” Magaziniyi imafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.