Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kusonyezana Chikondi Mpaka Pati?

Kodi Tiyenera Kusonyezana Chikondi Mpaka Pati?

Mutu 4

Kodi Tiyenera Kusonyezana Chikondi Mpaka Pati?

Chongani kuti zoona kapena zonama:

Nthawi zonse n’kosayenera kuti anthu amene ali pachibwenzi azigwirana.

□ Zoona

□ Zonama

Anthu amene ali pachibwenzi akhoza kukhalabe ndi mlandu wa dama ngakhale atapewa kugonana.

□ Zoona

□ Zonama

Ngati anthu amene ali pachibwenzi sagwiranagwirana kapena kupsompsonana ndiye kuti sakondana.

□ Zoona

□ Zonama

N’ZODZIWIKIRATU kuti munaganizirapo kwambiri nkhani imeneyi. Ndipotu, ngati muli pachibwenzi zingakhale zovuta kudziwa malire pankhani yosonyezana chikondi. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu zili pamwambazi kuti tione mmene Mawu a Mulungu angatithandizire kuyankha funso lakuti: “Kodi tiyenera kusonyezana chikondi mpaka pati?”

Nthawi zonse n’kosayenera kuti anthu amene ali pachibwenzi azigwirana.

Zonama. Baibulo sililetsa kusonyezana chikondi m’njira yoyenera. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza nkhani ya mtsikana wachisulami ndi m’busa wachinyamata amene anali pachibwenzi. Iwo anadzisunga nthawi yonse imene anali pachibwenzi. Komabe, zikuoneka kuti asanakwatirane, nthawi zina ankagwirana ndiponso kupsompsonana posonyezana chikondi. (Nyimbo ya Solomo 1:2; 2:6; 8:5) Masiku anonso, anthu ena amene ali pachibwenzi ndipo atsimikiza kuti adzakwatirana angaone kuti n’zoyenera kusonyezana chikondi m’njira yoyenera. *

Komabe anthu amene ali pachibwenzi ayenera kusamala kwambiri. Kupsompsonana, kukumbatirana, kapena kuchita chilichonse chimene chingadzutse chilakolako chogonana kungawapangitse kuchita chiwerewere. N’zosavuta kwa anthu amene ali pachibwenzi kuti agonane, ngakhale kuti analibe cholinga chochita zimenezi.—Akolose 3:5.

Anthu amene ali pachibwenzi akhoza kukhalabe ndi mlandu wa dama ngakhale atapewa kugonana.

Zoona. Mawu a Chigiriki choyambirira amene anamasuliridwa kuti “dama” (por·neiʹa) amatanthauza zinthu zambiri. Amatanthauza kugonana kwa mtundu wina uliwonse kwa anthu osakwatirana komanso kugwiritsa ntchito ziwalo zogonanira m’njira yolakwika. Choncho, mawu oti dama samangotanthauza kugonana kwenikweni kokha koma amatanthauzanso kuseweretsa ziwalo zogonanira za munthu wina ndiponso kugonana m’kamwa kapena kumatako.

Ndiponso Baibulo silimangoletsa dama lokha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ntchito za thupi zimaonekera, ndizo dama, chonyansa, khalidwe lotayirira.” Ndipo anapitiriza kuti: “Anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21.

Kodi “chonyansa” chimene chikutchulidwa palembali n’chiyani? Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “chonyansa” amatanthauza chodetsa chilichonse, kaya zimene timalankhula kapena kuchita. N’zoona kuti zingakhaledi zonyansa kuti munthu wina apise dzanja lake m’kati mwa chovala cha munthu wina, kum’vula, kapena kusisita mbali zobisika za thupi lake monga mabere ake. Baibulo limasonyeza kuti kusisita mabere ndi mbali yosangalatsa imene angachite anthu okwatirana basi.—Miyambo 5:18, 19.

Achinyamata ena amanyalanyaza mfundo za Mulungu mopanda manyazi. Iwo amapitirira malire mwadala, kapenanso amakhala ndi zibwenzi zambirimbiri kuti azigonana ndiponso kuchita zinthu zina zonyansa. Achinyamata amenewa angakhale ndi mlandu wochita zimene mtumwi Paulo anati ndi “khalidwe lotayirira.” Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “khalidwe lotayirira” amatanthauza ‘kuchita zinthu mopandiratu manyazi, mopitirira kwambiri malire, mopanda ulemu, ndiponso mosadziletsa ngakhale pang’ono.’ Kunena zoona, inuyo simungafune kukhala munthu yemwe “sangathenso kuzindikira makhalidwe abwino” chifukwa chodzipereka yekha ku “khalidwe lotayirira kuti achite zonyansa zonse mwadyera.”—Aefeso 4:17-19.

Ngati anthu amene ali pachibwenzi sagwiranagwirana kapena kupsompsonana ndiye kuti sakondana.

Zonama. Mosiyana ndi zimene anthu ena amaganiza, kusonyezana chikondi m’njira zosayenera sikuti kumalimbitsa chibwenzi. M’malo mwake, kumachititsa anthuwo kuti asiye kulemekezana ndi kukhulupirirana. Taganizirani zimene zinachitikira Laura. Iye anati: “Tsiku lina mayi anga atachoka, mnyamata yemwe ndinali naye pachibwenzi anabwera ku nyumba kwathu ngati akudzangoonera TV. Poyamba, anangondigwira dzanja. Kenako anayamba kundigwiragwira. Ndinaopa kumuuza kuti asiye poganiza kuti angakhumudwe n’kuchoka.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mnyamatayo ankam’kondadi Laura, kapena ankafuna kungodzisangalatsa basi? Kodi munthu amene akukunyengererani kuti muchite zolakwika amakukondanidi?

Mnyamata akamakakamiza mtsikana kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo zachikhristu ndiponso chikumbumtima chake, amakhala akuswa malamulo a Mulungu ndipo amasonyeza kuti samukondadi mtsikanayo. Ndiponso, mtsikana amadzichotsera ulemu wake akalolera zimenezi. Komanso akatero, amakhala atachita chinthu chonyansa kwambiri, mwinanso dama limene. *1 Akorinto 6:9, 10.

Dziikireni Malire

Ngati muli pachibwenzi, kodi mungatani kuti mupewe kupitirira malire pankhani yosonyezana chikondi? Njira yanzeru ndiyo kudziikira malire mukangoyamba kumene chibwenzicho. Lemba la Miyambo 13:10 limati: “Omwe [amakambirana, NW] ali ndi nzeru.” Choncho, kambiranani ndi chibwenzi chanucho njira zoyenera zosonyezerana chikondi. Kunyalanyaza kudziikira malire mpaka mutayamba kusonyezana chikondi kwambiri kuli ngati kudikira kuti nyumba yanu iyambe kupsa ndiyeno n’kumaika alamu yochenjeza za moto.

N’zoona kuti kukambirana nkhani ngati imeneyi kungakhale kovuta ngakhalenso kochititsa manyazi makamaka chibwenzi chikangoyamba kumene. Koma kudziikira malire kungakuthandizeni kwambiri kuti mupewe mavuto amene angadzayambe m’tsogolo. Malire abwino angakhale ngati alamu yochenjeza za moto imene imalira moto utangoyamba kumene. Ndiponso, mukamakambirana bwino nkhani imeneyi ndiye kuti chibwenzi chanucho chingayende bwino. Ndipotu, kukhala wodziletsa, woleza mtima ndiponso wosadzikonda n’kofunika kwambiri kuti mudzasangalale ndi mphatso ya kugonana mukadzakwatirana.—1 Akorinto 7:3, 4.

N’zoona kuti kutsatira mfundo za Mulungu kumafuna khama. Koma dalirani malangizo a Yehova. Ndipo palemba la Yesaya 48:17, Yehova anadzilongosola kuti ndi ‘amene amatiphunzitsa kupindula, amene amatitsogolera m’njira yoyenera ife kupitamo.’ Ndipotu iye amakufunirani zabwino nthawi zonse.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 24

M’MUTU WOTSATIRA

Ngati mukhalabe wosagonana ndi munthu mpaka mutalowa m’banja, sindiye kuti muli ndi vuto. M’malo mwake, zimenezi zimasonyeza kuti ndinu wanzeru. Onani zifukwa zake.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 M’madera ena, kusonyezana chikondi mwa njira imeneyi kwa anthu osakwatirana n’kosayenera ndipo kukhoza kukhumudwitsa anthu ena. Akhristu amayesetsa kupewa kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse ena.—2 Akorinto 6:3.

^ ndime 25 Nkhani imene ili m’ndimeyi ikukhudza anyamata ndi atsikana omwe.

LEMBA LOFUNIKA

“Chikondi . . . sichichita zosayenera.”—1 Akorinto 13:4, 5.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati muli pachibwenzi, muyenera kukambirana zinthu zina zokhudza nkhani ya kugonana. Komabe, n’kulakwa kukambirana nkhaniyi n’cholinga choti mudzutse chilakolako chogonana, ngakhale mutagwiritsa ntchito foni.

MFUNDO YOTHANDIZA

Muzicheza pagulu ndi chibwenzi chanu kapena muzionetsetsa kuti muli ndi munthu wina wokuperekezani. Pewani kukhala awiriwiri m’malo monga m’galimoto yoimikidwa kapena m’nyumba.

ZOTI NDICHITE

Ndingapewe kukodwa mu msampha wochita zosayenera mwa kuchita izi: ․․․․․

Ngati chibwenzi changa chitandikakamiza kuchita zosayenera, ndingachite izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi mungadziikire malire otani pankhani yogwirana ndi munthu yemwe si mnyamata kapena mtsikana mnzanu?

Kodi pali kusiyana kotani pakati pa dama, chonyansa, ndi khalidwe lotayirira?

[Mawu Otsindika patsamba 46]

“Ine ndi chibwenzi changa tinkawerengera limodzi m’mabuku ofotokoza za Baibulo nkhani zotithandiza kuti tikhale odziletsa pachibwenzi chathu. Tikuyamikira kuti nkhanizo zinatithandiza kukhalabe ndi chikumbumtima choyera.”—Anatero Leticia

[Chithunzi patsamba 44]

Kodi Tingatani Ngati Tapitirira Malire?

Nanga bwanji ngati mwachita zosayenera? Musadzinamize kuti vutolo mungalithetse nokha. Mtsikana wina anati: “Ndinkapemphera kuti, ‘Tithandizeni kuti tisadzachitenso zimenezi.’ Nthawi zina tinkasiyadi kuchita zosayenerazo, koma nthawi zina sizinkatheka.” Choncho, uzani makolo anu. Baibulo limaperekanso malangizo abwino awa: ‘Itanani akulu a mpingo.’ (Yakobe 5:14) Abusa achikhristu amenewa angapereke malangizo, uphungu ndi chidzudzulo, zomwe zingakuthandizeni kuti mukonze ubwenzi wanu ndi Mulungu.

[Chithunzi patsamba 47]

Kodi mungadikire kuti nyumba yanu iyambe kupsa ndi moto ndiyeno n’kuika alamu? Choncho, musadikire kuti chilakolako chanu cha kugonana chikule kwambiri ndiyeno n’kumadziikira malire