Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?

Mutu 22

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?

Tchulani ena mwa malamulo amene makolo anu anakuikirani. ․․․․․

Kodi nthawi zonse mumaona kuti malamulo amene makolo anu anakuikirani ndi abwino?

□ Inde □ Ayi

Kodi ndi lamulo liti limene limakuvutani kwambiri kulitsatira? ․․․․․

N’ZODZIWIKIRATU kuti makolo anu anakuikirani malamulo a zimene muyenera kuchita ndi zimene simuyenera kuchita. Malamulowo angakhale okhudza ntchito ya kusukulu yoti muchitire panyumba, ntchito zapakhomo, nthawi yofikira panyumba komanso nthawi imene mungagwiritse ntchito foni ndiponso kompyuta, kapena kuonera TV. Malamulo ena angakhudzenso khalidwe lanu la kusukulu ndiponso mmene mungasankhire anzanu.

Kodi mumaona kuti malamulo amene anakuikiraniwo akukuphwanyirani ufulu? Mwina mungaganize mofanana ndi achinyamata awa:

“Sindinkasangalala ndi nthawi imene anandiikira kuti ndizifika panyumba. Zinkandiwawa chifukwa chakuti anzanga ankaloledwa kufika panyumba mochedwa, koma ine ayi.”Anatero Allen.

“Sizindisangalatsa kuti azindifunsa za aliyense amene ndalankhula naye pafoni. Ndimaona kuti amanditenga ngati mwana.”Anatero Elizabeth.

“Ndinkaona kuti makolo anga akundipondereza kwambiri ndipo safuna kuti ndizicheza ndi anthu ena.”Anatero Nicole.

Nthawi zambiri achinyamata amaswa malamulo a makolo awo. Ngakhale zili choncho, ambiri mwa achinyamatawa amavomereza kuti malamulo ena ndi ofunika kuti zinthu ziziyenda bwino panyumba. Koma ngati malamulo a panyumba ali ofunikadi, n’chifukwa chiyani ena mwa iwo amavuta kuwatsatira?

“Siinenso Mwana Tsopano”

Mwina simusangalala ndi malamulo amene anakuikirani chifukwa mumaganiza kuti makolo anu amakuonani ngati mwana. Ndipo nthawi zina mungakwiye n’kunena kuti, “Siinenso mwana tsopano.” Koma mwina makolo anu amaona kuti malamulo awo ndi ofunika kuti mukhale wotetezedwa, ndiponso kuti mukonzekere udindo umene mungadzakhale nawo mukadzakula.

Komabe, mukamakula mwina mungaone kuti makolo anu sakusintha malamulo awo kuti azigwirizana ndi msinkhu wanu. N’kutheka kuti mungamve ngati mmene anamvera mtsikana wina dzina lake Brielle. Pofotokoza za makolo ake, iye anati: “Iwo amandionabe ngati mwana. Safuna kuti ndizinena maganizo anga pankhani zina, ndizisankha ndekha zochita ndiponso kuti ndizichita zinthu ngati munthu wamkulu.” Umu ndi mmene mtsikana winanso dzina lake Allison anamvera. Iye anati: “Ngakhale kuti ndili ndi zaka 18, makolo anga amaonabe ngati ndili ndi zaka 10 ndipo sandikhulupirira.”

Zingakhale zovuta kwambiri kutsatira malamulo a panyumba makamaka ngati mukuona kuti malamulo amene azikulu anu kapena azing’ono anu anapatsidwa si okhwima kwambiri poyerekezera ndi anu. Mwachitsanzo, pokumbukira zimene zinkachitika asanafike zaka 20, mnyamata wina dzina lake Matthew anati: “Mchemwali wanga ndiponso azibale anga ena ankawalekerera kwambiri ngakhale alakwe chotani.”

Kodi Zinthu Zingakuyendereni Bwino Popanda Malamulo?

Sizachilendo kufuna kukhala ndi moyo wosayendera malamulo a makolo anu. Koma kodi zinthu zingakuyenderenidi bwino popanda malamulo awo? Mwina mukudziwako achinyamata anzanu amene amachita zinthu mmene angafunire. Iwo amafika panyumba nthawi iliyonse, kuvala zilizonse, ndiponso panthawi iliyonse imene iwo angafune amatha kupita kulikonse ndi anzawo. Amachita zimenezi mwina chifukwa choti makolo awo amakhala otanganidwa kwambiri moti sadziwa zimene ana awo akuchita. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti ana sakula bwino akamaleredwa mwanjira imeneyi. (Miyambo 29:15) Masiku ano, chikondi n’chosowa chifukwa choti m’dzikoli mwachuluka anthu odzikonda, ndipo ambiri mwa anthu amenewa anakulira m’mabanja opanda malamulo alionse.—2 Timoteyo 3:1-5.

M’malo mosirira achinyamata anzanu amene amaloledwa kuchita chilichonse chimene akufuna, yesani kuona kuti makolo anu anakuikirani malamulowo chifukwa choti amakukondani kwambiri. Iwo anachita zimenezi potsanzira Yehova Mulungu amene anauza anthu ake kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa la kuyang’ana iwe.”—Salmo 32:8.

Komabe, nthawi zina mungaone ngati mukupanikizika kwambiri ndi malamulo a makolo anu. Kodi mungatani kuti mupezeko ufulu?

Kulankhulana Kwabwino

Ngati mukufuna kuti akufewetsereni malamulo ena kuti mukhale ndi ufulu wochulukirapo, muyenera kulankhulana bwino ndi makolo anu za nkhaniyi. Koma ena anganene kuti, ‘Ndayesetsa kulankhula nawo koma sizikuthandiza.’ Ngati mukuona choncho, dzifunseni kuti, ‘Kodi njira yabwino yolankhulira ndi makolo anga ingakhale yotani?’ Kulankhulana n’kofunika kwambiri chifukwa (1) kungathandize anthu ena kuti akumvetseni, kapena (2) kungakuthandizeni kudziwa chifukwa chimene akukuletserani zimene mukufuna. Kunena zoona, ngati mukufuna kupatsidwa ufulu wochita zinthu monga munthu wamkulu, muyenera kulankhula ndi makolo anu, ndipo zimene mungalankhulezo zisonyeze kuti ndinu munthu wamkulu. Kodi mungachite motani zimenezi?

Phunzirani kuugwira mtima. Kuti muzilankhulana bwino ndi ena, muyenera kukhala wodziletsa. Baibulo limati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.” (Miyambo 29:11) Choncho pewani kunyinyirika, kukhumudwa ndiponso kukwiya msanga ngati mwana. N’zomveka kuti akakuletsani kuchita chinachake, mungaganize zochita zinthu zosonyeza kuti mwakhumudwa monga kumenyetsa zitseko. Komabe, zimenezi zingangochititsa kuti makolo anuwo akuwonjezereni malamulo ena m’malo mokupatsani ufulu wochuluka.

Yesetsani kumvetsa cholinga cha makolo anu. Mtsikana wina wa Mboni dzina lake Tracy, yemwe analeredwa ndi mayi ake okha anati: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi cholinga cha mayi anga pondiikira malamulo amenewa n’chiyani?’” Yankho limene iye amapeza pa funso limeneli n’lakuti: “Iwo akufuna kundiphunzitsa kuti ndikhale munthu wabwino.” (Miyambo 3:1, 2) Kumvetsa zinthu kotereku kungakuthandizeni kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu.

Mwachitsanzo, makolo anu angakuletseni kupita kwinakwake kokacheza. M’malo moumirira kuti mupite, mungachite bwino kuwafunsa kuti, “Kodi mungandilole ngati nditapita ndi mnzanga wamkulu komanso wodalirika?” Ngakhale mutatero, mwina makolo anuwo sangakulolenibe kupita. Koma mukamvetsa zimene zikuwadetsa nkhawa, mungaganizire zinthu zina zabwino zoyenera kuchita.

Muzichita zinthu zoti makolo anu azikukhulupirirani. Taganizirani za munthu amene ali ndi ngongole kubanki yoti azibweza pang’onopang’ono. Ngati atamabweza ngongoleyo mokhulupirika, abanki angayambe kumukhulupirira ndipo angam’patse mwayi wotenganso ngongole ina yaikulu m’tsogolo. N’chimodzimodzinso panyumba. Muyenera kumvera makolo anu. Mukakhala wokhulupirika ngakhale pazinthu zing’onozing’ono, makolo anu angayambe kumakukhulupirirani kwambiri. Koma ngati simuwamvera, musadabwe ngati atakuchepetserani ufulu wanu, kapena kukulandani kumene.

Mukaphwanya Lamulo Linalake

Panthawi inayake mwina mungaphwanye malamulo amene anakuikirani, monga kulephera kugwira ntchito zapakhomo, kulankhula nthawi yaitali pafoni kapena kufika mochedwa panyumba. (Salmo 130:3) Zikatero, mungafunike kufotokozera makolo anu zimene zachititsa. Kodi mungatani kuti zinthu zisaipe kwambiri?

Nenani zoona. Mukamafotokoza zimene zachitika, nenani zoona. Makolo anu angasiyiretu kukukhulupirirani mukawanamiza. Choncho lankhulani zoona ndipo musachulutse gaga m’diwa. (Miyambo 28:13) Pewani kudzilungamitsa kapena kuchepetsa zimene mwachitazo. Ndipo nthawi zonse muzikumbukira kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

Pepesani. Ndi bwino kupepesa makolo anu mukachita zinthu zimene zawadetsa nkhawa, kuwakhumudwitsa kapena kuwaonjezera ntchito. Kupepesa kungathandize kuti akuchepetsereni chilango chimene angakupatseni. Koma muyenera kuchita zimenezi moona mtima.

Vomerezani chilango. (Agalatiya 6:7) Nthawi zambiri, chinthu choyamba chimene achinyamata amachita akalakwa ndi kuyesa kukana chilango makamaka ngati chikuoneka kuti sichoyenera. Koma kuvomereza kuti mwalakwa kumasonyeza kuti ndinu wokhwima maganizo. Chinthu chabwino kwambiri chimene mungachite mukalakwa, ndicho kuyesetsa kuchita zinthu zoti makolo anu ayambirenso kukukhulupirirani.

Pamfundo zitatu zimene taonazi, lembani pamzera uwu mfundo imodzi imene mukufunika kumaigwiritsa ntchito kwambiri. ․․․․․

Kumbukirani kuti makolo anu ali ndi udindo woika malamulo pa zimene muyenera kuchita ndiponso zimene simuyenera kuchita. N’chifukwa chake Baibulo limatchula za “malangizo a atate wako” ndiponso ‘malamulo a amayi ako.’ (Miyambo 6:20) Komabe, musamaganize kuti malamulo a panyumba panu amakuphwanyirani ufulu. Ndipo Yehova akukulonjezani kuti ‘zinthu zidzakuyenderani bwino,’ mukamamvera malamulo a makolo anu.—Aefeso 6:1-3.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 3

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi bambo kapena mayi anu amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapenanso kumwa mowa mwauchidakwa? Onani zimene mungachite.

LEMBA LOFUNIKA

Lemekeza atate wako ndi amayi wako . . . kuti zinthu zikuyendere bwino.Aefeso 6:2, 3.

MFUNDO YOTHANDIZA

Muzimvera malamulo a makolo anu ngati mukufuna kuti akupatseni ufulu wochuluka. Akaona kuti ndinu munthu womvera, sizingavute kuti akuloleni kuchita zimene mukufuna.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata amene makolo awo anawaikira malamulo abwino, nthawi zambiri amakhoza bwino kusukulu, amatha kukhala bwino ndi anthu ena ndiponso amakhala osangalala.

ZOTI NDICHITE

Nditaphwanya lamulo linalake la panyumba pathu, ndinganene izi: ․․․․․

Kuti makolo anga azindikhulupirira kwambiri ndingachite izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani nthawi zina mungaone ngati makolo anu akukukhwimitsirani zinthu kwambiri?

N’chifukwa chiyani nthawi zina mungakhumudwe chifukwa cha malamulo a panyumba panu?

Kodi mungatani kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu?

[Mawu Otsindika patsamba 183]

“Achinyamata amaganiza kuti amadziwa chilichonse. Choncho nthawi zambiri angathe kukhumudwa makolo awo akawaletsa chinachake. Koma makolo amachita zimenezi chifukwa choti amakonda ana awo.”—Anatero Megan

[Bokosi patsamba 186]

Kodi Kumakhaladi Kukondera?

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani makolo sachita zinthu mofanana kwa mwana aliyense?’ Ngati ndi choncho, taganizirani mfundo iyi: Sizingakhale bwino kuti nthawi zonse makolo anu azichita zinthu zofanana kwa inuyo ndi azibale anu. Choncho, funso lofunika kuliganizira n’lakuti, Kodi makolo anuwo amakunyalanyazani? Mwachitsanzo, kodi iwo amakuthandizani mukafuna malangizo awo? Ngati amatero, kodi munganene moona mtima kuti iwo amakondera? Sizingatheke kuti nthawi zonse makolo anu azichita zinthu zofanana kwa inuyo ndi azibale anu, popeza kuti simufunikira zinthu zofanana. Mfundo imeneyi ndi imene mtsikana wina dzina lake Beth anazindikira. Iye tsopano ali ndi zaka 18 ndipo anati: “Ine ndi mchimwene wanga ndife anthu osiyana ndipo sitingafunikire zinthu zofanana. Koma ndili mwana sindinkamvetsa mfundo imeneyi.”

[Bokosi​/Chithunzi patsamba 189]

Zimene Munalemba

Kambiranani ndi Makolo Anu

M’mitu iwiri yapitayi mwaona zimene mungachite ndi malamulo a panyumba panu ndiponso makolo anu akamakudzudzulani. Kodi mungatani ngati mukuona kuti makolo anu amangokhalira kukudzudzulani kapena akukukhwimitsirani malamulo kwambiri? Kodi n’chiyani chomwe mungachite kuti muyambe kukambirana nawo zimenezi?

Sankhani nthawi yabwino kwa inuyo komanso kwa makolo anu.

Lankhulani zakukhosi kwanu mwaulemu, osati mokalipa.

Ngati mukuona kuti makolo anu amangokhalira kukudzudzulani, munganene kuti: “Ndikuyesetsa kuti ndizichita zinthu molondola, koma zikundivuta chifukwa ndimangokhalira kudzudzulidwa. Kodi tingakambirane nkhani imeneyi?”

Lembani pa mzere uwu zimene mungachite kuti muyambe kukambirana nawo nkhaniyi.

․․․․․

MFUNDO YOTHANDIZA: Gwiritsani ntchito mutu 21 kuti muyambe kukambirana nkhaniyi. Mwina makolo anu angafune kuti mukambirane mutu umenewu.

Ngati mukuona kuti makolo anu sakukupatsani ufulu wokwanira, munganene kuti: “Ndikufuna kuti ndizichita zinthu monga munthu wamkulu, kuti m’tsogolo muno mudzandipatse ufulu wochuluka. Kuti zimenezi zidzatheke, kodi ndiyenera kumachita zinthu ziti?”

Lembani pa mzere uwu zimene mungachite kuti muyambe kukambirana nawo nkhaniyi.

․․․․․

MFUNDO YOTHANDIZA: Werengani mutu 3 m’buku loyamba. Mutuwu ndi wakuti: “Kodi Ndingachititse Motani Makolo Anga Kundipatsa Ufulu Wowonjezereka?” Ndiyeno lembani funso lililonse limene mungakhale nalo pa zimene mwawerengazo.

[Chithunzi pamasamba 184, 185]

Kumvera malamulo a makolo anu kuli ngati kubweza ngongole kubanki. Mukamatsatira malamulo awo mokhulupirika, iwo angayambe kukukhulupirirani kwambiri