Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi kuchita Chibwenzi Mobisa N’koopsa Motani?

Kodi kuchita Chibwenzi Mobisa N’koopsa Motani?

Mutu 2

Kodi kuchita Chibwenzi Mobisa N’koopsa Motani?

Jessica anathedwa nzeru mnyamata wina wa m’kalasi mwake, dzina lake Jeremy, atayamba kusonyeza kuti akum’funa. Ponena za Jeremy, Jessica anati: “Anali mnyamata wooneka bwino kwambiri, ndipo anzanga ankandiuza kuti sindidzapezanso mnyamata wakhalidwe labwino ngati ameneyu. Panali atsikana angapo amene ankamusirira koma iye sankawafuna. Ankangofuna ineyo basi.”

Pasanapite nthawi yaitali, Jeremy anafunsira Jessica. Jessica anauza Jeremy kuti iye ndi wa Mboni za Yehova, motero sangaloledwe kukhala pachibwenzi ndi mnyamata yemwe si wa Mboni. Jessica anati: “Nditamuuza zimenezi, Jeremy anatulukira nzeru inayake. Iye anati, ‘Tingathe kumangoyendetsa chibwenzi chathucho makolo ako osadziwa.’”

KODI inuyo mungatani ngati munthu amene amakudololani atakuuzani nzeru yotereyi? Mwina mudabwa kumva kuti Jessica anamvera maganizo a Jeremy aja. Iye anati: “Ndinkaganiza kuti nditakhala naye pachibwenzi ndingathe kumuphunzitsa kuti ayambe kukonda Yehova.” Koma kodi zinaterodi? Chakumapeto kwa nkhaniyi tiona zimene zinachitika, koma choyamba tiyeni tione zimene zimachititsa ena kuchita chibwenzi mobisa.

N’chifukwa Chiyani Amachita Zimenezi?

Kodi achinyamata ena amachitiranji chibwenzi mobisa? Mnyamata wina dzina lake David ananena mwachidule kuti: “Iwowa amadziwa kuti makolo awo sangasangalale nazo.” Mtsikana wina dzina lake Jane anatchula chifukwa chinanso. Iye anati: “Ena amachita zibwenzi mobisa pofuna kutsimikizira kuti angathe kuchita zinthu paokha, popanda kuuzidwa zochita. Akamaona kuti sakupatsidwa ufulu wochita zinthu ngati munthu wamkulu, amaona kuti ndi bwino kungochita zimene akufuna popanda kuuza makolo awo.”

Kodi mungaganizire zifukwa zina zimene zimapangitsa ena kuchita chibwenzi mobisa? Lembani m’munsimu zifukwazo.

․․․․․

Mosakayikira, mukudziwa kuti Baibulo limati muyenera kumvera makolo anu. (Aefeso 6:1) Ndipotu ngati makolo anu akukuletsani kukhala pachibwenzi, ayenera kuti ali ndi zifukwa zomveka. Komabe musadabwe ngati mutakhala ndi maganizo otsatirawa:

 Ndimaona kuti ndine wotsalira chifukwa aliyense ali ndi chibwenzi kupatulapo ineyo.

Munthu amene si wachipembedzo changa wandidolola.

Ndimafuna kukhala pachibwenzi ndi Mkhristu mnzanga ngakhale kuti sindinafike pamsinkhu wolowa m’banja.

N’kutheka kuti mukudziwiratu zimene makolo anu anganene pa maganizo amenewa. Ndipo pansi pamtima mungavomereze kuti makolo anuwo akunena zoona. Komabe, mwina mumamva ngati mmene ankamvera mtsikana wina dzina lake Manami, yemwe anati: “Ndimafuna kwambiri kukhala ndi chibwenzi moti nthawi zina ndimakayikira ngati ndi bwino kukhalabe wopanda chibwenzi. Achinyamata ambiri masiku ano, amaona kuti kukhala wopanda chibwenzi n’kutsalira kwambiri. Ndiponso palibe amene angafune kukhala yekhayekha.” Motero ena amachita chibwenzi mobisira makolo awo. Kodi amachita zimenezi motani?

“Anatiuza Kuti Tisaulule”

Mawu akuti “chibwenzi chobisa,” akusonyezeratu kuti pali zinazake zachinyengo. Ena amayendetsa chibwenzi chotere polankhulana pafoni kapena pa Intaneti. Akakhala pagulu, amangoonetsa ngati palibe chilichonse, koma mungadabwe kwambiri mutadziwa zimene amauzana pa Intaneti ndiponso pafoni.

Njira inanso yobisira chibwenzi choterechi ndi yoti iwowa amaitana gulu la anzawo kuti akachite zinazake pamodzi, koma kenaka amene ali pachibwenziwo amangocheza awiri basi. James anati: “Nthawi ina, tinaitanidwa kuti tikacheze kwinakwake monga gulu, osadziwa kuti imeneyi inali njira yoti mnyamata ndi mtsikana winawake akacheze awiri, ndipo anatiuza kuti tisaulule.”

Monga mmene James ananenera, nthawi zambiri anthu amathandizidwa ndi anzawo poyendetsa chibwenzi mobisa. Carol anati: “Mwina pamakhala mnzako mmodzi kapena awiri amene amadziwa za chibwenzicho koma sanena chilichonse chifukwa safuna kutchedwa kuti ndi apakamwa.” Nthawi zina, ena amachita kunena bodza lamkunkhuniza. Beth, wazaka 17, anati: “Ambiri amabisa zoti ali pachibwenzi ponamiza makolo awo za kumene akupita.” Misaki, mtsikana wazaka 19, anachita zimenezo. Iye anati: “Ndinkangopeka zoti ndiwauze. Komano pofuna kuti makolo anga asasiye kundikhulupirira, ndinkayesetsa kuti ndisamaname pa china chilichonse kupatulapo za chibwenzicho basi.”

Kuopsa Kochita Chibwenzi Mobisa

Ngati mukufuna kukhala ndi chibwenzi chobisa kapena ngati muli nacho kale, m’pofunika kuti muganizire mafunso awiri otsatirawa:

Kodi khalidwe langali likandifikitsa kuti? Kodi muli ndi cholinga chokwatirana ndi munthuyo posachedwapa? Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake Evan, anati: “Kukhala pachibwenzi popanda cholinga chomanga banja n’kofanana ndi kutsatsa malonda chinthu chinachake chimene sukuchigulitsa.” Mukatero, n’chiyani chingachitike? Lemba la Miyambo 13:12 limati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Kodi mungafune kuti munthu amene mumam’kondadi adwale mtima? Taonani chenjezo linanso: Kuchita chibwenzi mobisa kumakumanitsani mwayi woti makolo anu kapena achikulire ena okukondani akuthandizeni. Choncho, m’posavuta kuti muchite chiwerewere.—Agalatiya 6:7.

Kodi Yehova Mulungu akumva bwanji ndi zimene ndikuchitazi? Baibulo limati: “Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso . . . pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (Aheberi 4:13) Motero musadzinamize kuti mukubisa chibwenzi chanu kapena cha mnzanu, chifukwatu Yehova akuzidziwa kale zimenezo. Choncho, ngati mukuchita zachinyengo, dziwani kuti mukusewera paulimbo. Ndipotu, Yehova Mulungu amadana kwambiri ndi bodza. Moti “lilime lonama” lili m’gulu la zinthu zimene Baibulo linachita kuneneratu kuti iye amadana nazo.—Miyambo 6:16-19.

Ululani

N’chinthu chanzeru kuuza makolo anu kapena Mkhristu wamkulu wokhwima mwauzimu za chibwenzi chilichonse chimene mukuyendetsa mobisa. Ndipo ngati muli ndi mnzanu amene akuchita chibwenzi mobisa, musam’thandize chinyengo chakecho pomusungira chinsinsi. (1 Timoteyo 5:22) Komanso, kodi mungamve bwanji ngati mnzanuyo atagwa m’vuto chifukwa cha chibwenzicho? Kodi sitinganene kuti inuyo mwachititsa nawo vutolo?

Tiyerekeze kuti muli ndi mnzanu amene amadwala matenda a shuga ndiyeno akudya zinthu zotsekemera kwambiri mobisa. Inuyo mutadziwa zimenezi, mnzanuyo akukupemphani kuti musaulule. Kodi mungatani? Kodi nkhawa yanu ingakhale pa kupulumutsa moyo wake kapena kumusungira chinsinsi?

N’chimodzimodzinso ngati mukudziwa kuti mnzanu winawake akuchita chibwenzi mobisa. Musaope kuti mudana naye, muululeni. Ngati ali mnzanu weniwenidi, patsogolo pake adzazindikira kuti munatero chifukwa chomufunira zabwino.—Salmo 141:5.

Mobisa Kapena Mosaonetsera?

Sikuti nthawi zonse anthu akakhala pachibwenzi chimene anthu ena sakuchidziwa ndiye kuti akuchita zolakwika. Tayerekezerani kuti mnyamata ndi mtsikana akufuna kudziwana bwino, komano sakufuna kudzionetsera kwa kanthawi ndithu. N’kutheka kuti akutero pa chifukwa chofanana ndi chimene mnyamata wina dzina lake Thomas, ananena. Iye anati: “Iwo safuna kuti anthu aziwavutitsa ndi mafunso monga akuti: ‘Kodi mukwatirana liti?’”

N’zoona kuti zonena za anthu ena zingathe kukulowetsani m’mavuto. (Nyimbo ya Solomo 2:7) Motero, anyamata ndi atsikana ena amaona kuti ndi bwino kusaonetsera akangoyamba kumene chibwenzi mpaka patapita nthawi ndithu. (Miyambo 10:19) Anna, yemwe ali ndi zaka 20, anati: “Kusaonetsera kumathandiza anthuwo kuti akhale ndi nthawi yokwanira yoona bwinobwino ngati onse atsimikizadi kumanga banja. Ndiyeno akatsimikizira zimenezi, m’pamene angayambe kuonetsera kwa anthu.”

Komabe, dziwani kuti n’kulakwa kuwabisira anthu amene ayenera kudziwa za chibwenzicho, monga makolo anu komanso makolo a mnzanuyo. Ngati mukuona kuti simungauze munthu wina aliyense, dzifunseni chifukwa chake. Kodi n’kutheka kuti mukudziwa kuti makolo anu ali ndi zifukwa zomveka zokuletsani kutero?

“Ndinadziwa Zoyenera Kuchita”

Jessica, amene tam’tchula poyamba uja, anaganiza zothetsa chibwenzi chobisa ndi Jeremy atamva zimene zinachitikira mtsikana wina wachikhristu amenenso anachita chibwenzi mobisa. Jessica anati: “Nditamva mmene iye anathetsera chibwenzicho ndinadziwa zoyenera kuchita.” Kodi zinali zosavuta kuti Jessica athetse chibwenzi chakecho? Ayi. Jessica anati: “Uyutu anali mnyamata yekhayo amene ndinam’kondadi. Ndinkalira tsiku lililonse kwa milungu ingapo.”

Komabe, Jessica ankadziwa kuti amakonda Yehova. Motero, ngakhale kuti anasokonezeka pang’ono, ankafunitsitsa kuchita zoyenera. Ndipo patapita nthawi, iye anasiya kuganiza za chibwenzicho. Jessica anati: “Tsopano ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri. Ndikuyamikira kwambiri kuti iye amatipatsa malangizo ofunika panthawi yoyenera.”

M’MUTU WOTSATIRA

Tiyerekezere kuti mwafika poti n’kukhala ndi chibwenzi ndipo mwapeza munthu yemwe wakudololani. Kodi mungadziwe bwanji ngati munthuyo ndi wokuyenererani?

LEMBA LOFUNIKA

Timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.Aheberi 13:18.

MFUNDO YOTHANDIZA

M’posafunika kuti muzingouza aliyense kuti muli pachibwenzi. Koma mufunikira kuuza anthu amene ali oyenera kudziwa. Anthu amenewa angakhale makolo anu ndiponso makolo a mnzanuyo.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Pamafunika kukhulupirirana kuti anthu akhale pa ubwenzi wokhalitsa. Kuchita chibwenzi mobisa kumachititsa kuti makolo anu asamakukhulupirireni, ndiponso chibwenzi choterocho chimakhala chopanda maziko abwino.

ZOTI NDICHITE

Ngati ndikuchita chibwenzi mobisa ndi Mkhristu mnzanga, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Ngati mnzanga akuchita chibwenzi mobisa, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Taonani mawu omwe ali  m’zilembo zakuda kwambiri patsamba 22 m’buku lino. Kodi ndi mawu ati omwe akufotokoza mmene inuyo mumamvera nthawi zina?

● Kodi mungathane bwanji ndi maganizo anuwo popanda kuchita chibwenzi mobisa?

● Kodi mungatani mutadziwa kuti mnzanu akuchita chibwenzi mobisa, ndipo n’chifukwa chiyani mungasankhe kuchita zimenezo?

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Ndinathetsa chibwenzi chomwe ndinkachita mobisa. N’zoona kuti zinali zovuta kwambiri kuchita zimenezi chifukwa tsiku lililonse ndikapita ku sukulu ndinkamuona mnyamatayo. Koma Yehova Mulungu amadziwa zonse ndipo amaona zimene ifeyo sitingathe kuona. Choncho, tiyenera kumudalira.’’—Anatero Jessica”

[Chithunzi pamasamba 25]

Kusaulula mnzanu amene akuchita chibwenzi mobisa kuli ngati kusaulula munthu wodwala matenda a shuga amene akudya zotsekemera kwambiri mobisa