Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuona Zithunzi Zolaula?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuona Zithunzi Zolaula?

Mutu 33

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupewa Kuona Zithunzi Zolaula?

Kodi zithunzi zolaula mumaziona kangati mwangozi?

□ Sindinazionepo

□ Mwa apo ndi apo

□ Nthawi zambiri

Kodi nthawi zambiri mumaziona kuti?

□ Pa Intaneti

□ Kusukulu

□ Pa TV

□ Kumalo ena

Mumachita chiyani mukaziona?

□ Ndimayang’ana kumbali nthawi yomweyo.

□ Ndimakhala ndi chidwi kuti ndioneko pang’ono.

□ Ndimayang’anitsitsa ndipo ndimafufuzanso zina.

MAKOLO anu ali achinyamata, zithunzi zolaula sizinkapezeka wambawamba. Koma masiku ano, zithunzi zolaula zangoti mbwee. Mtsikana wina wazaka 19 anati: “Nthawi zina ndikamafufuza zinthu pa Intaneti monga mitengo ya zinthu kapena ndalama zanga zimene zili kubanki, ndimangozindikira kuti patulukira chithunzi cholaula.” Zimenezi sizachilendo. Ofufuza ena anapeza kuti achinyamata 90 pa 100 alionse azaka za pakati pa 8 ndi 16 akamagwiritsa ntchito Intaneti, zithunzi zolaula zimangotulukira mwadzidzidzi, ndipo nthawi zambiri zimenezi zimachitika akamafufuza za kusukulu.

Popeza kuti masiku ano zithunzi zolaula zili paliponse, mwina mungaone kuti palibe vuto lililonse ndi kuona zithunzi zimenezi. Koma kodi zimenezi n’zoona? Ayi. Anthu amene amapanga komanso kuona zithunzi zolaula amadzichotsera ulemu ndipo nthawi zambiri amachita zachiwerewere. Koma palinso mavuto ena ambiri.

Munthu akazolowera kuona zithunzi zolaula safuna kusiya ndipo zotsatira zake zimakhala zoipa. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Jeff, ngakhale kuti anali atatha zaka 14 atasiya khalidweli, anati: “Mtima wofuna kuona zithunzi zolaula ndidakali nawobe. Ndipo tsiku lililonse ndimayesetsa kudzigwira kuti ndisaone zithunzizi. Koma ndimazionabe m’maganizo mwanga. Ndikanadziwa sindikanayamba n’komwe kuona zithunzizi. Poyamba ndinkaganiza kuti zilibe vuto lililonse. Koma panopo palibe angandinamize. Zithunzizi zimawononga munthu, n’zoipa kwambiri, ndipo zimachotsera ulemu anthu amene amazipanga komanso amene amaziona. Ngakhale kuti anthu amene amalimbikitsa khalidweli amanena kuti zithunzizi n’zabwino, zoona zake n’zakuti palibe chabwino chilichonse ndi zithunzi zimenezi.”

Iganizireni Bwino Nkhaniyi

Kodi mungatani kuti mupeweretu kuona zithunzi zolaula ngakhale mwangozi? Choyamba, iganizireni bwino nkhaniyi. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimachititsa kuti muone zithunzizi mwangozi? Taganizirani izi:

Kodi anzanu a kusukulu amakonda kukutumizirani zithunzi zolaula pakompyuta kapena pafoni yam’manja? Ngati ndi choncho, musamawerenge mauthenga awowo ndipo muzingowafufutiratu.

Kodi zithunzi zolaula zimabwera mukalemba mawu enaake pa Intaneti? Ngati ndi choncho, muzisamala pofufuza zinthu pa Intaneti, muzilemba mawu ogwirizana ndi zimene mukufufuzazo basi.

․․․․․

Lembani pansipa zinthu zina zimene zinakuchititsani kuti muone zithunzi zolaula.

․․․․․

Kodi mungatani kuti mupewe kuona mwangozi zithunzi zolaula? Lembani pansipa zimene mungachite.

Mungatani Ngati Mumakonda Kuona Zithunzi Zolaula?

Kuona zithunzi zolaula mwangozi ndi kosiyana ndi kuziona mwadala. Kodi inuyo mungatani ngati mwayamba kukonda kuona zithunzi zolaula? Dziwani kuti kusiya khalidweli n’kovuta. Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti akumangani manja ndi ulusi. N’zosavuta kuti mudule ulusiwo. Koma bwanji ngati ulusiwo atauzunguliza kambirimbiri? Zingakhale zovuta kuti muudule. N’chimodzimodzinso ndi anthu amene amakonda kuona zithunzi zolaula. Akamazionaona amayamba kuzikonda ndipo zimavuta kwambiri kuti asiye. Ngati zimenezi zikukuchitikirani, kodi mungatani kuti musiye khalidweli?

Dziwani kuti zithunzi zolaula n’zoipa. Satana ndi amene amafuna kuti tiziona zithunzi zolaula n’cholinga chofuna kunyoza zimene Yehova anazipanga kuti zikhale zolemekezeka. Mukadziwa kuti cholinga cha zithunzi zolaula n’chimenechi, mungathe kuyamba ‘kudana nacho choipa.’—Salmo 97:10.

Ganizirani kuipa kwake. Kuona zithunzi zolaula kumasokoneza mabanja ambiri. Anthu amene amajambulidwa mu zithunzi zimenezi amadzichotsera ulemu. Zimam’chotseranso ulemu munthu amene akuzionayo. N’chifukwa chaketu Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Lembani pansipa vuto limene mungakumane nalo chifukwa chokonda kuona zithunzi zolaula.

․․․․․

Tsimikizani mtima. Munthu wokhulupirika Yobu, ananena kuti: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Nanunso mungathe kutsimikiza mtima kuchita izi:

Sindidzagwiritsiranso ntchito Intaneti ndili pa malo obisika.

Pa Intaneti pakabwera chithunzi cholaula ndizitseka nthawi yomweyo.

Ndikayambiranso kuona zithunzi zolaula, ndiziuza munthu wina wachikulire amene ndimagwirizana naye.

Lembani chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene mwatsimikiza kuchita kuti zikuthandizeni kuthetsa vuto loona zithunzi zolaula.

․․․․․

Pemphererani nkhaniyi. Wamasalmo anapemphera kwa Yehova kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” (Salmo 119:37) Yehova Mulungu akufuna kuti zinthu zikuyendereni bwino, motero angathe kukuthandizani kuti muchite zabwino.—Afilipi 4:13.

Uzani munthu wina. Nthawi zambiri njira yothandiza kwambiri kuthetsera vuto limeneli ndiyo kukhala ndi munthu womuuza zakukhosi. (Miyambo 17:17) Lembani pansipa dzina la munthu amene mungamasuke kumuuza nkhaniyi.

․․․․․

Dziwani kuti mungathe kusiya kuona zithunzi zolaula. Ndipotu, nthawi iliyonse imene mwapewa kuona zithunzi zoterezi, ndiye kuti mwayamba kuthetsa vutolo. Mukachita zimenezi, muuzeni Yehova, ndipo muthokozeni pokupatsani mphamvu zochitira zimenezo. Nthawi zonse kumbukirani kuti mukapewa kuona zithunzi zolaula, mumasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.

LEMBA LOFUNIKA

Chititsani ziwalo za thupi lanu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.Akolose 3:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Onetsetsani kuti kompyuta yanu mwaichuna kuti isamalandire zithunzi zolaula. Komanso muzipewa kutsegula mauthenga a anthu amene simukuwadziwa.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Anthu amene amasangalala ndi zithunzi zolaula amafanana ndi angelo oipa a m’masiku a Nowa omwe anali ndi mtima wachiwerewere.—Genesis 6:2.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisamaone mwangozi zithunzi zolaula, ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi, ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi zithunzi zolaula zimanyozetsa bwanji zinthu zolemekezeka?

Kodi m’bale wanu amene ali ndi vuto loona zithunzi zolaula mungamuthandize bwanji?

[Mawu Otsindika patsamba 278]

“Ndisanayambe kuphunzira Baibulo, ndinkaona zithunzi zolaula ndiponso ndinkagwiritsira ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo osiyanasiyana. Koma pazinthu zonsezi, kuona zithunzi zolaula kunandivuta kwambiri kusiya. Yehova ndi amene anandithandiza kuti ndithetse vuto limeneli.”—Anatero Jeff

[Chithunzi patsamba 276]

Munthu akamaonaona zithunzi zolaula amayamba kuzikonda ndipo zimavuta kwambiri kuti asiye