Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganiza za Anyamata Kapena Atsikana?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganiza za Anyamata Kapena Atsikana?

Mutu 29

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganiza za Anyamata Kapena Atsikana?

MNYAMATA wina, dzina lake Michael, anati: “Nthawi zonse ndimangokhalira kuganiza za atsikana. Zimenezi zimandikhumudwitsa kwambiri chifukwa nthawi zina ndimalephera kuchita zinthu zina bwinobwino.”

Kodi nanunso muli ndi vuto ngati la Michael, moti mumangokhalira kuganiza za atsikana kapena anyamata? Ngati ndi choncho, mungavomereze kuti zimenezi n’zovutitsa maganizo. Michael ananenanso kuti: “Nthawi zina umati ukayamba kuganizira za mtsikana, umalephera kuchita zinthu zina. Nthawi zinanso munthu umatha kusintha njira imene umafunika kudutsa ndi cholinga choti ukumane ndi mtsikana winawake wokongola. Kapenanso ukhoza kukalowa m’sitolo usakufuna kugulamo chilichonse, koma n’cholinga choti ukaonemo kamkazi kenakake.”

Dziwani kuti chilakolako chofuna kugonana pachokha sicholakwika. Ndipotu Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi ndi mtima woti azifunana, koma ndi anthu okwatirana okha amene ayenera kugonana. Koma ngakhale musanakwatire, nthawi zina mungakhale ndi chilakolako chofuna kugonana. Zimenezi zikachitika, musaganize kuti ndinu wakhalidwe loipa kapena kuti simungathe kudzisunga. Dziwani kuti ngati mukufuna, mungathe kudzisunga. Koma kuti mugonjetse vuto lomangoganiza za atsikana kapena anyamata, muyenera kudziletsa. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Muzisamala ndi ocheza nawo. Anzanu akusukulu akayamba kukambirana nkhani zosayenera zokhudza kugonana, mwina mungakopeke nazo n’kuyamba kuyankhira n’cholinga choti musaoneke ngati wotsalira. Komatu zimenezi zingakulepheretseni kudziletsa. Nanga kodi muyenera kuchita chiyani? Kungochokapo basi. Ndipo musadzione ngati ndinu wopusa. Koma m’pofunika kupeza njira yabwino yochokera pamalopo, kuti musadzionetse ngati wolungama kwambiri. Zimenezi zingachititse kuti anzanuwo asakusekeni.

Pewani zosangalatsa zolimbikitsa chiwerewere. Sikuti mafilimu ndi nyimbo zonse n’zoipa ayi. Komabe zosangalatsa zambiri masiku ano zimachititsa anthu kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana. Koma kodi Baibulo limati chiyani pankhani imeneyi? Limanena kuti: “Tiyeni tidziyeretse kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu, tikumakwaniritsa chiyero chathu poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Muzipeweratu zosangalatsa zilizonse zimene zingakuchititseni kuti mukhale ndi chilakolako chogonana. *

Pewani Kuseweretsa Maliseche

Achinyamata ena amaseweretsa maliseche kuti azimva ngati akugonana ndi munthu wina. Koma zimenezi zimabweretsa mavuto aakulu. Baibulo limalangiza Akhristu kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.” (Akolose 3:5) Munthu amene amaseweretsa maliseche ‘sachititsa ziwalo za thupi lake kukhala zakufa’ koma amangowonjezera chilakolako.

Munthu amene amaseweretsa maliseche amakhala kapolo wa chilakolako chake. (Tito 3:3) Koma njira imodzi yomwe mungathetsere vutoli ndiyo kuuza munthu wina. Mkhristu wina amene anali ndi vutoli kwazaka zambiri, anati: “Zikanakhala bwino ndikanalimba mtima n’kuuza munthu wina za vuto langalo. Kwazaka zambiri ndinakhala ndikudziimba mlandu ndipo zimenezi zinasokoneza kwambiri ubwenzi wanga ndi anthu ena ndiponso Yehova.”

Kodi muyenera kuuza ndani? Mungachite bwino kwambiri kuuza makolo anu kapena Mkhristu wodalirika wa mumpingo mwanu. Mwina mungayambe ndi mawu akuti: “Ndikufuna ndikuuzeni vuto linalake limene likundivutitsa maganizo kwambiri.”

Mnyamata wina dzina lake André anauza mkulu wa mumpingo wake za vutoli, ndipo akuona kuti anachita bwino. Iye ananena kuti: “Nthawi imene ndinkamufotokozera, mkuluyo anagwetsa misozi. Nditamaliza kumufotokozera, iye ananditsimikizira kuti Yehova amandikonda. Anandiuzanso kuti si ine ndekha amene ndikukumana ndi vuto ngati limeneli. Anandiuza kuti iye aziona mmene ndikuchitira ndiponso azindipatsa malangizo opezeka m’mabuku ofotokoza Baibulo. Malangizo amene mkuluyo anandipatsa anandithandiza kwambiri ndipo ndinali wokonzeka kugonjetsa vutoli ngati litayambiranso.”

Mário anauza bambo ake za vuto lake ndipo iwo anamuthandiza mokoma mtima. Iwo anamuuza kuti nawonso anali ndi vuto limeneli ali mnyamata ndipo zinkawavuta kulithetsa. Mário anati: “Bambo anga anandilimbikitsa kwambiri chifukwa sanandibisire kanthu. Ndinaona kuti ngati iwo anagonjetsa vutoli ndiye kuti nanenso ndingathe kuligonjetsa. Ndinakhudzidwa kwambiri ndi mmene bambo anga anandithandizira mpaka ndinalira.”

Monga mmene zinalili ndi André ndiponso Mário, inunso mungathandizidwe kuti muthetse khalidwe loseweretsa maliseche. Ngakhale kuti nthawi zina mungayambirenso khalidweli, musagonje ndipo musakayike kuti inunso mungathe kuthetsa chizolowezi chimenechi. *

Muziganizira Zinthu Zoyenera

Mtumwi Paulo anati: “Ndipumphuntha thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.” (1 Akorinto 9:27) Inunso muyenera kudziletsa ngati mwayamba kuganiza za mnyamata kapena mtsikana winawake. Koma ngati mukulephera kudziletsa, yesani kuchita masewera olimbitsa thupi. Baibulo limati: “Chizolowezi chochita masewero olimbitsa thupi chipindulitsa pang’ono.” (1 Timoteyo 4:8) Kuchita masewera olimbitsa thupi kapena kuwongola miyendo kungakuthandizeni kuiwala maganizo olakwika.

Koma chofunika kwambiri ndi kukumbukira malangizo a Atate wanu wakumwamba. Mkhristu wina wosakwatira anati: “Chilakolako chofuna kugonana chikangoyamba, ndimapemphera kwambiri.” Musaganize kuti Mulungu angachititse kuti musiyiretu kuganiza za anyamata kapena atsikana. Komabe iye angakuthandizeni kuzindikira kuti pali zinthu zambiri zofunika kuti muziziganizira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Nkhani yonena za zosangalatsa yafotokozedwa bwino mu Chigawo 8 cha buku lino.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kuseweretsa maliseche, werengani Buku Loyamba, mutu 25.

LEMBA LOFUNIKA

“Khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu amachita zimene amakonda kuganiza.—Yakobe 1:14, 15.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati mwayambiranso khalidwe loseweretsa maliseche, musagonje. Ganizirani zimene zachititsa kuti muyambirenso khalidweli ndipo musazibwerezenso.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisiye kumangoganiza za anyamata kapena atsikana, ndizichita izi: ․․․․․

Anzanga akusukulu akayamba kunena nkhani zogonana, ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani simuyenera kuganiza kuti muli ndi vuto ngati nthawi zina mumakhala ndi chilakolako cha kugonana?

● N’chifukwa chiyani muyenera kudziletsa mukamalakalaka kugonana ndi winawake?

● Kodi ndi zosangalatsa ziti zimene zingachititse kuti muziganiza kwambiri za anyamata kapena atsikana?

● Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwino kuchokapo anzanu akayamba kulankhula nkhani zogonana?

[Mawu Otsindika patsamba 240]

“Ndikangoyamba kuganizira zogonana, ndimasintha zimene ndikuganizazo n’kuyamba kuganizira zinthu zina. Ndipo ndimadziwa kuti pakapita nthawi chilakolakocho chitha.”—Anatero Scott

[Chithunzi patsamba 239]

Kodi mungalole kuti mu kompyuta mwanu mulowe mapologalamu oipa? Ngati simungalole, musalolenso kuti m’maganizo mwanu mulowe zinthu zolakwika