Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakonde Kupsa Mtima Ndiponso Kukhumudwa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakonde Kupsa Mtima Ndiponso Kukhumudwa?

Mutu 26

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakonde Kupsa Mtima Ndiponso Kukhumudwa?

KODI moto ndi wabwino kapena woipa? Funso limeneli ndi lovuta kuyankha chifukwa moto ndi wabwino koma nthawi zina ukhoza kukhala woipa. Mwachitsanzo, moto ndi wabwino m’nyengo yozizira chifukwa timawotha kuti titenthedwe. Komabe popanda kusamala, moto womwewo ungathe kuwotcha nyumba.

N’chimodzimodzinso ndi mtima wanu. Ngati mutadziletsa mungamakhale bwino ndi anzanu. Koma popanda kusamala, mungachite zinthu zimene zingabweretse mavuto aakulu kwa inuyo ndiponso anthu ena.

Koma nthawi zina achinyamatanu, mungalephere kuugwira mtima. Kodi mungatani kuti musamapse mtima kapena kukhumudwa kwambiri? Tiyeni tikambirane zimene mungachite.

Pewani Kupsa Mtima

N’zovuta kuugwira mtima anthu ena akakulakwirani. Baibulo limanena kuti anthu ena akaputidwa ‘amakwiya msanga’ ndiponso amakhala ‘aukali.’ (Miyambo 22:24; 29:22) Zimenezi n’zoopsa chifukwa munthu akapsa mtima kwambiri amatha kuchita zinthu zimene angadzanong’oneze nazo bondo. Ndiyeno kodi mungatani kuti muziugwira mtima ena akakulakwirani?

Choyamba ganizirani bwinobwino nkhaniyo, n’kuona ngati mukufunikira kungoinyalanyaza. * (Salmo 4:4) Dziwani kuti kubwezera “choipa pa choipa” kumangochititsa kuti zinthu ziipe kwambiri. (1 Atesalonika 5:15) Kuganizira bwinobwino nkhaniyo komanso kupemphera, kungakuthandizeni kuti musawawidwe mtima kwambiri.—Salmo 37:8.

Koma kodi mungatani ngati simungathe kungoiwala zimene munthu wina wakulakwirani? Baibulo limanena kuti pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Choncho, mwina mungafunike kulankhula ndi munthuyo. Koma ngati mukuona kuti zimenezi sizingathandize, mungachite bwino kuuza makolo anu kapena munthu wina wamkulu. Ngati mnzanu akukuputani dala, yesetsani kuti musamupsere mtima.  Bokosi limene lili patsamba 221 lingakuthandizeninso ngati pali zinthu zina zimene zimakupsetsani mtima.

Koma chofunika kwambiri ndi kupemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni kuti musamupsere mtima munthu amene wakuputaniyo. Muyenera kudziwa kuti simungathe kuletsa anzanu kuti asamakulakwireni, koma mungathe kudziletsa kuti musamapse mtima. Munthu akamapitirizabe kupsa mtima amakhala ngati nsomba imene yakoledwa ndi mbedza. Nsombayo imayendera zofuna za amene waikolayo. Munthu amene akupitirizabe kupsa mtima, nayenso amayendera zofuna za amene wamupsetsa mtimayo. Choncho, kodi inuyo mungalole kuti muzingochita zofuna za munthu amene wakupsetsani mtima?—Aroma 12:19.

Zimene Mungachite Mukakhumudwa

Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Laura, anati: “Ndimangokhalira kukhumudwa komanso kudziimba mlandu ndipo moyo sukusangalatsanso. Nthawi zambiri ndimangokhalira kulira.” Pali achinyamata ambiri amene amamva ngati Laura. Kodi inunso mumamva choncho? Achinyamata ena amakhumudwa chifukwa makolo awo, anzawo ndiponso aphunzitsi awo amayembekezera zambiri kwa iwo. Nthawi zinanso amakhumudwa chifukwa cha kusintha kwa thupi lawo komanso chifukwa choona kuti akulephera kuchita bwino zinthu zina.

Achinyamata ena amafika mpaka podzivulaza kuti mtima wawo uphwe. * Ngati nanunso mumachita zimenezi, yesetsani kudziwa chimene chimakuchititsani. Mwachitsanzo anthu ena amadzivulaza ngati pali chinachake chimene chikuwavutitsa maganizo. Kodi pali nkhani inayake yokhudza banja lanu kapena anzanu imene ikukusowetsani mtendere?

Njira yabwino kwambiri yothetsera mavuto anu ndiyo kuuza makolo kapena munthu wina wamkulu mumpingo mwanu kuti ‘akuthandizeni pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17) Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Liliana, ankauza alongo ena achikulire zakukhosi kwake. Iye ananena kuti: “Popeza anthu amenewa ndi achikulire, malangizo awo ndi othandiza. Panopo ndimagwirizana nawo kwambiri.” * Mtsikana winanso wazaka 15, dzina lake Dana, anafotokoza kuti atayamba kuthera nthawi yochuluka pantchito yolalikira, anasiya kumangokhalira kukhumudwa. Iye anati: “Ndinayamba kusangalala kwambiri, palibe chilichonse chikanandithandiza kuposa zimenezi.”

Pemphero lingakuthandizeni kwambiri mukakhumudwa, choncho musamanyalanyaze kupemphera. Wamasalmo Davide, yemwenso anakumana ndi mavuto ambiri pamoyo wake, anati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Yehova amadziwa bwino kwambiri mavuto amene mukukumana nawo. Ndiponso iye “amasamala za inu.” (1 Petulo 5:7) Mtima wanu ukamakutsutsani, kapena mukamadziimba mlandu, muzikumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:20) Iye amamvetsa bwino kwambiri zimene zikukuvutitsani ndipo angakuthandizeni.

Koma ngati mukupitirizabe kukhumudwa, mwina chingakhale chifukwa choti mukudwala. * Choncho mungachite bwino kukaonana ndi dokotala. Kunyalanyaza zimenezi kuli ngati kunyalanyaza phokoso la injini ya galimoto yanu losonyeza kuti chinachake chavuta. M’malo mokonza galimotoyo, kodi mungakweze wailesi ya m’galimotoyo kuti musamve phokosolo? Simungachite zimenezo. Choncho palibe chifukwa chochitira manyazi ngati mukudwala. Achinyamata ambiri amene akudwala matenda a maganizo amapeza bwino akalandira chithandizo cha mankhwala.

Kumbukirani kuti mtima wanu uli ngati moto. Nthawi zina ungakuthandizeni koma ngati simusamala ungakuchititseni zinthu zimene zingakubweretsereni mavuto aakulu. Choncho muziyesetsa kuugwira mtima. N’zoona kuti nthawi zina munganene kapena kuchita zinthu zimene mungadzanong’oneze nazo bondo. Komabe musamadandaule kwambiri ndi zimenezi chifukwa m’kupita kwanthawi mudzatha kumadziletsa kuti musamakwiye msanga kapena kukhumudwa kwambiri.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mumafuna kuti nthawi zonse muzingochita zinthu mosalakwitsa? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti musamakhumudwe kwambiri mukalakwitsa zinthu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ngati anzanu amakuvutitsani kapena kukumenyani, werengani Mutu 14 m’buku lino. Koma ngati mnzanu wakukwiyitsani, mungapeze mfundo zothandiza m’Mutu 10.

^ ndime 13 Anthu amadzivulaza m’njira zambiri monga kudzicheka, kudziotcha, kudzikalakala kapena kudzisupula.

^ ndime 14 Ngati mumachita manyazi kulankhula ndi anthu akuluakulu maso ndi maso, mungathe kungowalembera kalata kapena kuwaimbira foni. Nthawi zambiri kuuza ena mmene mukumvera ndi njira yabwino yokuthandizani kuti musamangokhalira kukhumudwa.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri zokhudza matenda ovutika maganizo, werengani Buku Loyamba, mutu 13.

LEMBA LOFUNIKA

Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.Aroma 12:21.

MFUNDO YOTHANDIZA

Tsiku lililonse muziuza makolo anu chinthu chimodzi chabwino chimene chakuchitikirani ngakhale chitakhala chaching’ono. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musadzavutike kuwauza mavuto aakulu amene mungadzakumane. Ndipo nawonso sadzadabwa ndi zimenezi, choncho adzakuthandizani.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu amene sagona ndiponso kudya mokwanira, sachedwa kukwiya komanso amangokhala wokhumudwa.

ZOTI NDICHITE

Vuto langa lalikulu ndi: ․․․․․

Kuti ndithetse vutoli ndichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani Mulungu sasangalala ndi munthu amene amapitirizabe kukwiya?

● Kodi kupsa mtima kungakubweretsereni mavuto otani?

● Kodi mungatani kuti musamakonde kukhala wokhumudwa?

[Mawu Otsindika patsamba 223]

“Chimene chinandithandiza kwambiri ndicho kudziwa kuti pali ena amene amandikonda, amenenso ndingathe kuwauza zakukhosi kwanga.”—Anatero Jennifer

[Tchati/​Zithunzi patsamba 221]

 Zimene Munalemba

Yesetsani kuti musapse lembani maganizo

mtima kwambiri anu m’bokosili

vuto zosayenera zoyenera

kuchita kuchita

Mnzanga wa Ndimuyankha Ndingangozinyalanyaza

m’kalasi mwamwano kuti adziwe kuti

akandigemula sangathe

kundipsetsa mtima

Mchemwali wanga Inenso ․․․․․

akavala nsapato ndizitenga

zanga zimene zinthu zake

ndimazikonda osapempha

kwambiri popanda

kundipempha

Makolo anga ․․․․․ ․․․․․

akandiletsa

kupita kokacheza

[Chithunzi patsamba 220]

Munthu wokonda kupsa mtima amakhala kapolo wa munthu amene wamukwiyitsa, ngati nsomba imene yakoledwa ndi mbedza