Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?

Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?

Mutu 15

Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?

“Kusukulu kumachitika zinthu zambiri monga kusuta fodya, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndi zachiwerewere. Munthu umadziwa kuti zimene anzako akufuna kuti uchite ndi zoipa, koma nthawi zina umalephera kukana.”—Anatero Eve.

ALIYENSE amafuna kuti anzake azimukonda. N’chifukwa chake anzanu ena amapezerapo mwayi pa zimenezi kuti muzichita nawo zoipa. Mwachitsanzo, ngati mwakulira m’banja lachikhristu mumadziwa kuti chiwerewere ndiponso kuledzera n’zolakwika. (Agalatiya 5:19-21) Komabe, anzanu angakukakamizeni kuti muzichita zimenezi. Kodi iwowo anayamba bwanji khalidwe loipali? Ambiri amachita zimenezi chifukwa chotengera anzawo. Amafuna kuti anzawo aziwakonda, choncho amangochita zimene anzawowo akufuna. Kodi inunso mumatero kapena mumakana molimba mtima?

Nthawi inayake, Aroni, mchimwene wake wa Mose anagonjera zofuna za anthu. Aisiraeli atamuunjirira n’kumuumiriza kuti awapangire fano, iye anagonja n’kupanga zimene iwo amafunazo. (Eksodo 32:1-4) N’zodabwitsa kuti munthu amene anauza Farao molimba mtima uthenga wochokera kwa Mulungu, anagonja kwa Aisiraeli anzakewo. (Eksodo 7:1, 2, 16) Ngakhale kuti Aroni analankhulana ndi mfumu ya Aiguputo mopanda mantha, iye analephera kulankhula molimba mtima kwa Aisiraeli anzake.

Kodi inunso zimakuvutani kukana, ena akamakuumirizani kuchita zinthu zoipa? Inunso mutha kukana molimba mtima, anzanu akakuumirizani kuchita zimene iwo akufuna. Kuganiziratu zinthu zimene anzanu angakukakamizeni kungakuthandizeni kwambiri. Mfundo zinayi zotsatirazi zikuthandizani kuchita zimenezi.

1. Konzekerani. (Miyambo 22:3) N’zosavuta kudziwiratu zinthu zimene anzanu angakuumirizeni kuchita. Mwachitsanzo, mukhoza kuona anzanu a kusukulu akubwera patsogolo panu akusuta fodya. Mukhoza kudziwiratu kuti akukakamizani kusuta. Koma mutakonzekereratu, sizingakuvuteni kukana.

2. Dzifunseni. (Aheberi 5:14) Mungadzifunse kuti, ‘Ndikachita zimene anzangawa akuchita, kodi mumtima mwanga ndimva bwanji?’ Mukachita nawo zimenezo, anzanuwo angakukondeni koma kodi kenako mungamve bwanji mukakhala ndi makolo anu kapena Akhristu anzanu? Kodi mungakonde kusangalatsa anzanu a kusukulu m’malo mosangalatsa Mulungu?

3. Sankhani zochita. (Deuteronomo 30:19) Mtumiki wa Mulungu aliyense ayenera kusankha kukhala wokhulupirika n’kupeza madalitso kapena kukhala wosakhulupirika n’kukumana ndi mavuto. Anthu monga Yosefe, Yobu ndi Yesu anasankha mwanzeru pomwe Kaini, Esau ndi Yudasi sanasankhe bwino. Inunso muyenera kusankha zoyenera kuchita.

4. Nenani maganizo anu. Mwina mungaganize kuti kunena maganizo anu n’kovuta, komatu n’kosavuta. Ngati mwaganizira kale kuipa kwake ndipo mwasankha kale zochita, simungavutike kunena maganizo anu. (Miyambo 15:23) Sikuti mukuchita kufunikira kulalikira anzanuwo ayi. Kungonena kuti ayi kungakhale kokwanira. Kapena ngati mukufuna kuwatsimikizira kuti simusintha maganizo anu, munganene kuti:

“Sindikufuna kuti zimenezo zindikhudze.”

“Sindingachite zimenezo.”

“Inunso mukudziwa kuti sindingachite zimenezo.”

Kuyankha mwamphamvu ndiponso molimba mtima kungachititse kuti anzanu asiye kukuvutitsani. Komabe, kodi mungatani ngati anzanu akukunyozani? Bwanji ngati atakunenani kuti, “Ndiwe wamantha eti?” Akanena zimenezi musadabwe, chifukwa iwo akungofuna kukunyengererani. Koma kodi mungawayankhe bwanji? Pali njira zitatu zimene mungawayankhire.

● Vomerezani zimene akunenazo. (“Simukunama, ndinedi wamantha.” Kenako fotokozani mwachidule chifukwa chimene mukuchitira mantha.)

● Ingokanani kuti simungachite zimenezo koma osanena zambiri.

● Apanikizeni. Fotokozani chifukwa chimene mukukanira, ndipo asonyezeni kuti zimene akuchitazo n’zopanda nzeru. (“Ndimakuonani ngati anthu ozindikira oti simungasute fodya.”)

Anzanuwo akapitiriza kukuvutitsani, ingochokani chifukwa mukakhalabe pomwepo zinthu zikhoza kuipa kwambiri. Dziwani kuti ngakhale mwachokapo, simunagonje chifukwa simunalole kuchita zimene iwo akufuna.

Anzanu ena angakunyozeni kuti simutha kusankha nokha zochita. Koma zimenezo si zoona chifukwa Yehova amafuna muzindikire kuti kuchita chifuniro chake n’kofunika kwambiri. (Aroma 12:2) Ndipo musalole kuti anzanu akusandutseni kachidole. (Aroma 6:16) Choncho, yesetsani kuchita zimene mukudziwa kuti n’zolondola.

Kunena zoona n’zosatheka kupeweratu kuvutitsidwa ndi anzanu. Komabe mutha kusankha zimene mukufuna kuchita. Muthanso kunena maganizo anu kapena kuchita zilizonse zimene mungathe kuti anzanu asamakuvutitseni. Ndipo dziwani kuti ndi udindo wanu kusankha zochita.—Yoswa 24:15.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 9

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mumachita zinthu zinazake mwamseri? Kodi mukuganiza ndi bwino kuti makolo anu adziwe zimene mumachita mseri?

LEMBA LOFUNIKA

“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.

MFUNDO YOTHANDIZA

Kuti mukhale wolimba mtima, werengani nkhani za atumiki a Yehova a masiku ano amene akhalabe okhulupirika povutitsidwa.

KODI MUKUDZIWA  . . . ?

Anzanu ambiri amene mumaphunzira nawo mudzasiyana nawo mukadzamaliza sukulu. Mwinanso ena adzakuiwalani ndi dzina lomwe. Koma makolo ndi abale anu komanso Yehova Mulungu, sadzakuiwalani mpaka kalekale.—Salmo 37:23-25.

ZOTI NDICHITE

Pokonzekera kukana zimene anzanga akufuna kuti ndichite, ndizichita izi: ․․․․․

Anzanga akandikakamiza kuti ndichite zinthu zoipa, ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi njira zinayi zimene zafotokozedwa m’mutu uno, zingakuthandizeni bwanji?

Kodi chingachitike n’chiyani ngati mutalolera zimene anzanu akufuna kuti muchite?

Kodi mungakane bwanji ngati anzanu akukuumirizani kuchita zinthu zoipa?

[Mawu Otsindika patsamba 131]

“Anzanga ambiri amadziwa kuti ndine wa Mboni ndipo amandipatsa ulemu. Akafuna kukambirana zinthu zosayenera, amandiuza kuti, ‘Mike tikufuna kuyamba kukambirana zathu, ndiye ngati ukufuna, utha kuchoka.”—Anatero Mike

[Tchati pamasamba 132, 133]

Zimene Munalemba

mmene mungakonzekerere Chitsanzo cha

konzekerani

Kodi anzanga angandikakamize kuchita chiyani? Kusuta fodya.

Kodi zimenezi zingachitikire kuti? Kubwalo la mpira.

↓ ↓

Kodi nditalola ← dzifunseni → Kodi nditakana,

kusuta fodya, chingachitike

chingachitike n’chiyani?

n’chiyani?

Yehova ndiponso makolo anga Anzanga angandigemule

sangasangalale nazo. kapena kundinyoza.

Ndingawononge chikumbumtima Ena sangafune kucheza nane.

changa. Zingadzandivute Koma ndingasangalatse Yehova

kukana nthawi ina. ndiponso ndingapitirize kukhala

munthu wamakhalidwe abwino.

↓ ↓

Ngati ← 3 Sankhani Zochita → Ndidzakana

ndidzasute fodya, kusuta fodya

chidzakhala chifukwa chifukwa chakuti:

chakuti:

Sindikukonzekera choti Ndikudziwa kuti Yehova

ndidzachite anzanga amadana nazo ndiponso

akadzandikakamiza kusuta kusuta kukhoza

fodya. Kapena chifukwa kundidwalitsa.

choti ndimaona kuti

kukondweretsa anzanga

n’kofunika kwambiri kuposa

kukondweretsa Yehova.

↓ ↓

← 4 Nenani Maganizo Anu → Ndidzachita izi:

Kukana kenako

n’kuchokapo.

Anzanu akamakunenani

Anzanga akanena kuti: “Sutako pang’ono.

Kapena ukuchita mantha eti?”

Ndingachite izi:

kuvomereza kukana koma kuwapanikiza

osanena zambiri

“Simukunama, “Musavutike kundipatsa “Sindikufuna, inetu

sindifuna kusuta ine fodyayo.” ndimakutengani ngati

fodya chifukwa ndinu ozindikira oti

ndimaopa matenda simungasute fodya.”

a khansa.”

DZIWANI IZI: Chokani pamalopo mwamsanga. Mukakhalabe pomwepo, n’zosavuta kuti muyambe kuchita zimene iwo akufunazo. Tsopano, lembani zimene mungachite pa pepala limene lili patsamba lotsatirali.

mmene mungakonzekerere Koperani izi:

1 Konzekerani

Kodi anzanga angandikakamize kuchita chiyani? ․․․․․

Kodi zimenezi zingachitikire kuti? ․․․․․

↓ ↓

Kodi nditalola, ← 2 Dzifunseni → Kodi nditakana,

chingachitike chingachitike

n’chiyani? n’chiyani?

․․․․․ ․․․․․

↓ ↓

Ndikadzalolera, ← 3 Sankhani Zochita → Ndidzakana

chidzakhala chifukwa chakuti:

chifukwa chakuti:

․․․․․ ․․․․․

↓ ↓

← 4 Nenani Maganizo Anu Ndidzachita izi: →

․․․․․ ․․․․․

Anzanu akamakunenani

Mnzanga akanena kuti: ․․․․․

Ndingachite izi:

kuvomereza kukana koma kuwapanikiza

osanena zambiri

․․․․․ ․․․․․ ․․․․․

Yeserani ndi makolo anu kapena munthu wina wamkulu zimene mungachite.

[Chithunzi patsamba 135]

Mukamalolera kuchita zimene anzanu akufuna, mumakhala ngati kachidole kawo