Kodi Ndi Bwino Kucheza pa Intaneti?
Mutu 11
Kodi Ndi Bwino Kucheza pa Intaneti?
Kodi mumakonda kucheza motani ndi anzanu?
□ Pamasom’pamaso
□ Pafoni
□ Pa Intaneti
Kodi ndani amene mumacheza naye momasuka?
□ Anzanga a kusukulu
□ Abale anga
□ Akhristu anzanga
Kodi n’kuti kumene mumacheza momasuka?
□ Kusukulu
□ Kunyumba
□ Kumisonkhano ya mpingo
KODI mwayankha bwanji funso loyambali? Kodi mwayankha kuti mumakonda kucheza ndi anthu pa Intaneti kuposa kucheza nawo pamasom’pamaso? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha, chifukwa pali achinyamata ambiri amene amakonda kucheza ndi anzawo pa Intaneti. Mtsikana wina, dzina lake Elaine, anati: “Zimasangalatsa kucheza ndi anthu a m’mayiko osiyanasiyana, amene sungathe kukumana nawo.” Mtsikana winanso wazaka 19, dzina lake Tammy, ananena kuti: “Pa Intaneti umatha kucheza ndi aliyense, koma zimavuta kucheza ndi anthu pamasom’pamaso ngati anthuwo sakufuna kucheza nawe.”
Tsopano onani zimene mwayankha pa funso lachiwiri ndi lachitatu. Musaone ngati zachilendo ngati mumakonda kucheza kwambiri ndi anzanu a kusukulu kusiyana ndi Akhristu anzanu kumpingo. Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Jasmine, anati: “Ukakhala kusukulu sulephera kupeza anthu amsinkhu wako amene umagwirizana nawo zochita. Ndipo sizivuta kuti uyambe kucheza nawo momasuka.”
* Mtsikana winanso wazaka 20, dzina lake Natalie, ankakonda kucheza ndi anzake pa Intaneti. Iye anati: “Intaneti ndi imodzi mwa njira zamakono zolankhulirana, ndipo ndimaikonda kwambiri.”
Chifukwa cha zinthu zimene tafotokozazi, zingaoneke ngati palibe vuto lililonse kucheza pa Intaneti ndi anzanu a kusukulu. Tammy ananenanso kuti: “Anzanga onse a kusukulu ankacheza pa Intaneti, choncho ine sindinkafuna kukhala wotsalira.”Ganizirani Kuopsa Kwake
N’zoona kuti anthu ambiri savutika kupeza anthu ocheza nawo pa Intaneti. Natalie anati: “Pa Intaneti umacheza ndi anthu momasuka kwambiri kusiyana ndi mmene ungachitire pocheza ndi anthu pamasom’pamaso.” Nayenso Tammy anavomereza zimenezi kuti: “Ngakhale utakhala wamanyazi, pa Intaneti umakhala ndi nthawi yokwanira yoganizira zoti unene.”
Komano dziwani kuti kucheza ndi anthu pa Intaneti kuli ndi vuto lake ndipo kunyalanyaza mfundo imeneyi n’kupusa. Kuti mumvetse, taganizirani izi: Kodi mungadutse pa malo oopsa mutamanga nsalu m’maso? Ngati simungachite zimenezi, kuli bwanji kucheza pa Intaneti?
Taganizirani za kuopsa kwake. Elaine, yemwe ankakonda kucheza ndi anthu osawadziwa pa Intaneti, anati: “N’zosavuta kuti uyambe kucheza ndi anthu achinyengo.” Iye anatinso: “Nthawi zina sizitenga nthawi kuti anthu ayambe kulankhula zotukwana kapena kukufunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi unayamba wagonanapo ndi munthu wina aliyense? Kodi umagonana m’kamwa ndi wina aliyense?’
Ena amayamba kukuuza kuti muzikambirana nkhani pa Intaneti ngati kuti mukugonana.”Koma bwanji ngati mukungocheza ndi mnzanu amene mumam’khulupirira? Ngakhale zili choncho, m’pofunikabe kusamala kwambiri. Mtsikana wina dzina lake Joan, anati: “Umawononga nthawi yambiri ukamacheza ndi mnyamata kapena mtsikana pa Intaneti ngakhale ali mnzako chabe. Mukamakonda kutumizirana mauthenga pa Intaneti, mumayamba kukondana kwambiri ndipo kenako mumayamba kukambirana zogonana.”
Ena Amabisa Khalidwe Lawo
Mfumu Davide ankadziwa bwino kufunika kopeza anthu abwino ocheza nawo. Iye anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika,” kapena kuti obisa khalidwe lawo.—Salmo 26:4.
Kodi munayamba mwachezapo ndi anthu otere pa Intaneti? Kodi n’chifukwa chiyani anthu amabisa khalidwe lawo pa Intaneti? ․․․․․
Kodi mwina inunso mumabisa khalidwe lanu mukakhala pa Intaneti? Mtsikana wina dzina lake Abigail, amene amakonda kupita kumalo okhala ndi makompyuta amene anthu amagwiritsira ntchito pocheza pa Intaneti, anati:
“Ndikamacheza ndi anthu pa Intaneti ndimasintha n’kukhala ngati ndimachitadi zimene tikuchezazo.”Mtsikana wina dzina lake Leanne, ankapusitsa anthu pa Intaneti. Iye anati: “Ndinkakonda kucheza kwambiri pa Intaneti ndi mnyamata wina wa mumpingo woyandikana nawo. Pasanapite nthawi, tinayamba kukambirana zachikondi. Makolo anga akamadutsa ndinkabisa zimene tikulemberanazo, kuti asadziwe. Poti ndinali ndi zaka 13 zokha, iwo sankaganiza n’komwe kuti ndingamalemberane ndakatulo za chikondi ndi mnyamata wazaka 14.”
Zimene Muyenera Kuchita
Nthawi zina kucheza ndi anthu pa Intaneti ndi kofunika kwambiri. Anthu ambirimbiri ngakhalenso akuluakulu, amacheza ndi anzawo pa Intaneti. Ngati inunso mumacheza ndi anzanu pa Intaneti, kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kusamala nazo? Onani mfundo zotsatirazi.
● Muziona nthawi imene mumawononga mukakhala pa Intaneti, ndipo musalole kuti Intaneti izikulepheretsani kuchita zinthu zofunika kwambiri, monga kugona. Mnyamata wina dzina lake Brian anati: “Ana ena kusukulu amati amakhala ali pa Intaneti mpaka 3 koloko m’mamawa.”—Aefeso 5:15, 16.
● Muzicheza ndi anthu amene mukuwadziwa bwino. Anthu ena amakhalidwe oipa amafufuza pa Intaneti kuti apeze achinyamata oti awanyengerere kuchita zinthu zoipa.—Aroma 16:18.
● Muzisamala pa nkhani zokhudza ndalama. Mukhala pa Intaneti musamangouza anthu china chilichonse chokhudza inuyo chifukwa angathe kukuberani kapena kuchitirani zilizonse zoopsa.—● Mukamatumizira anzanu zithunzi pa Intaneti, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi zithunzizi zikusonyeza kuti ndine mtumiki wa Mulungu?’—Tito 2:7, 8.
● Muzichita ngati mukulankhulana pamasom’pamaso. Ngati mukulankhulana ndi munthu pa Intaneti ndiye mwazindikira kuti mwayamba kulankhulana “zinthu zosayenera” muyenera kusiya kulankhulanako.—Aefeso 5:3, 4.
● Nthawi zonse musamabise zimene mukuchita pa Intaneti. Si bwino kubisira makolo anu zimene mumachita pa Intaneti. Mtsikana wina, dzina lake Kari, anati: “Ndimalankhula momasuka ndi makolo anga ndipo ndimawasonyeza zonse zimene ndimachita pa Intaneti.”—“Ndinachita Bwino Kudikira”
Aliyense amafuna kukhala ndi anzake. Anthufe tinalengedwa kuti tizisangalala tikamacheza ndi anzathu. (Genesis 2:18) Choncho, ngati mumafuna kukhala ndi anzanu, musadabwe chifukwa umu ndi mmene munalengedwera. Koma mumangofunika kusankha anzanu mosamala.
Dziwani kuti mungapeze anzanu abwino ngati mutatsatira mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu. Mtsikana wina wazaka 15, anati: “N’zovuta kupeza anzako amene amakukonda komanso amene amakonda Yehova. Koma mnzako wotere akapezeka, mumtima umangoti ‘ndinachita bwino kudikira.’”
Kodi alipo amene anganene kuti sakhumudwa ena akamamunena? Miseche imalasa ngati lupanga. Kodi mungaipewe bwanji?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Tidzakambirana zambiri zokhudza nkhani yocheza ndi anzanu kusukulu m’Mutu 17.
LEMBA LOFUNIKA
“Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika.”—Salmo 26:4.
MFUNDO YOTHANDIZA
Mukakhala pa Intaneti, nthawi sichedwa kutha. Choncho muzionesetsa kuti musamapitirire nthawi imene munakonza kuti mukhalepo. Ngati mungafune, mungatchere wotchi kuti ilire, nthawi imene mwakonza kuti muchokepo ikakwana.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
N’zotheka kuti anthu a zolinga zoipa akupezeni ngakhale mutangolemba zinthu zochepa chabe pa Intaneti, monga dzina la bambo anu, dzina la sukulu yanu, ndi nambala yanu ya foni.
ZOTI NDICHITE
Ndikufuna kuti ndikakhala pa Intaneti, ndisamathe nthawi yopitirira ․․․․․ pamlungu, ndipo kuti ndikwanitse zimenezi ndiyenera kuchita izi: ․․․․․
Ndikayamba kulankhulana ndi munthu amene sindikumudziwa bwino pa Intaneti, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi pali ubwino ndi kuipa kotani kocheza ndi anthu pa Intaneti poyerekeza ndi kucheza nawo pamasom’pamaso?
● Kodi n’chifukwa chiyani n’zosavuta kunena zinthu zimene simuchita mukamacheza ndi ena pa Intaneti?
● Kodi mungatani kuti musamawononge nthawi yambiri pa Intaneti?
● Kodi Intaneti ndi yofunika panjira ziti?
[Mawu Otsindika patsamba 103]
“Sindicheza pa Intaneti ndi anthu osawadziwa kapena anthu amene sindingafune kucheza nawo pamasom’pamaso.”—Anatero Joan
[Chithunzi patsamba 100, 101]
Kodi mungadutse pa malo oopsa mutamanga nsalu m’maso? Ngati simungachite zimenezi, kuli bwanji kucheza pa Intaneti?