Hoseya 2:1-23

  • Aisiraeli osakhulupirika analangidwa (1-13)

  • Yehova anakhalanso mwamuna wawo (14-23)

    • “Adzanditchula kuti Mwamuna wanga” (16)

2  “Uzani azichimwene anu kuti, ‘Ndinu anthu anga.’*+ Ndipo azichemwali anu muwauze kuti, ‘Ndinu akazi osonyezedwa chifundo.’*+  2  Imbani mlandu mayi anu. Aimbeni mlandu.Chifukwa iwowo si mkazi wanga+ ndipo ine si mwamuna wawo. Mayi anuwo asiye uhule*Komanso asiye kuchita chigololo.*  3  Apo ayi, ndiwavula kuti akhale maliseche ngati tsiku limene anabadwa.Ndiwachititsa kukhala ngati chipululu,Komanso ngati dziko lopanda madzi,Nʼkuwapangitsa kuti afe ndi ludzu.  4  Ana awo sindiwachitira chifundo,Popeza ndi ana obadwa chifukwa cha uhule.*  5  Chifukwa mayi awo amachita uhule.*+ Mayi amene anatenga pakati nʼkuwabereka achita zinthu zochititsa manyazi+ ndipo anena kuti,‘Nditsatira amuna ondikonda kwambiri+Ndiponso amene amandipatsa chakudya ndi madzi,Amandipatsanso zovala za ubweya wa nkhosa, nsalu, mafuta ndi zakumwa.’  6  Choncho nditseka njira yawo ndi mpanda waminga.Ndipo ndiwamangira mpanda wamiyalaKuti asowe podutsa.  7  Mayiyu adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+Adzawafunafuna, koma osawapeza. Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba,+Chifukwa zinthu zinkandiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi pano.’+  8  Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa mbewu,+ vinyo watsopano ndiponso mafuta.Sanazindikirenso kuti ndine amene ndinamupatsa siliva wambiri,Ndiponso golide amene anthu ankamugwiritsa ntchito polambira Baala.+  9  ‘Choncho ndidzatembenuka nʼkulanda mbewu zanga pa nthawi yokolola.Ndidzalandanso vinyo wanga watsopano pa nthawi yopanga vinyo.+Mayiyu ndidzamulandanso zovala zanga za ubweya wa nkhosa ndiponso nsalu zanga zimene amabisira maliseche ake. 10  Ndidzamuvula kuti akhale maliseche amuna omukonda kwambiriwo akuona.Ndipo palibe mwamuna amene adzamupulumutse mʼmanja mwanga.+ 11  Ndidzathetsa chisangalalo chake chonse.Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha masiku amene mwezi watsopano waoneka, cha masabata ndiponso nthawi yake ya zikondwerero. 12  Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi ya mkuyu imene iye wanena kuti: “Amenewa ndi malipiro amene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.”Koma ine mitengoyo ndidzaisandutsa kukhala nkhalango,Ndipo zilombo zakutchire zidzaidya. 13  Ndidzamuimba mlandu chifukwa cha masiku amene anapereka nsembe kwa zifaniziro za Baala.+Pamene ankavala mphete* ndi zinthu zina zodzikongoletsera ndipo ankatsatira amuna omukonda kwambiri.Koma ine anandiiwala,’+ watero Yehova. 14  ‘Choncho ndidzamunyengerera,Ndidzamupititsa kuchipululu,Ndipo ndidzalankhula naye momufika pamtima. 15  Kuyambira nthawi imeneyo kupita mʼtsogolo ndidzamubwezera minda yake ya mpesa.+Ndidzamupatsanso chigwa cha Akori+ kuti chikhale ngati khomo lachiyembekezo.Kumeneko adzayankha ngati mmene ankayankhira ali mtsikana,Ngatinso pa tsiku limene anatuluka mʼdziko la Iguputo.’+ 16  Yehova wanena kuti,‘Pa tsiku limenelo adzanditchula kuti Mwamuna wanga ndipo sadzanditchulanso kuti Mbuyanga.* 17  Sindidzamulola kutchulanso mayina a zifaniziro za Baala,+Ndipo sadzakumbukiranso mayina awo.+ 18  Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zilombo zakutchire mʼmalo mwa anthu anga,+Komanso ndi mbalame zouluka mumlengalenga ndi zinthu zokwawa panthaka.+Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo mʼdzikolo.+Ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere.+ 19  Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo,Komanso chifukwa cha chikondi chokhulupirika ndi chifundo changa.+ 20  Ndidzalonjeza kukukwatira nʼkukhala wokhulupirikaNdipo udzadziwadi Yehova.’+ 21  Yehova wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo ndidzakuyankha.Ndidzayankha zopempha zakumwambaNdipo kumwambako kudzayankha zopempha za dziko lapansi.+ 22  Ndiyeno dziko lapansi lidzayankha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta,Ndipo zimenezi zidzayankha Yezereeli.*+ 23  Mayiyu ndidzamudzala ngati mbewu zanga padziko lapansi.+Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo.*Ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Ndinu anthu anga,”*+ Iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+

Mawu a M'munsi

^ Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:6.
^ Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:9.
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “achotse zochita zake zachigololo pakati pa mabere ake.”
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Nʼkuthekanso kuti zinali ndolo zovala pamphuno kapena pakhutu.
^ Kapena kuti, “Baala wanga.”
^ Kutanthauza “Mulungu Adzadzala Mbewu.”
^ Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:6.
^ Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:9.