Hoseya 2:1-23

  • Aisiraeli osakhulupirika analangidwa (1-13)

  • Yehova anakhalanso mwamuna wawo (14-23)

    • “Adzanditchula kuti Mwamuna wanga” (16)

2  “Uzani azichimwene anu kuti, ‘Ndinu anthu anga.’*+ Ndipo azichemwali anu muwauze kuti, ‘Ndinu akazi osonyezedwa chifundo.’*+   Imbani mlandu mayi anu. Aimbeni mlandu.Chifukwa iwowo si mkazi wanga+ ndipo ine si mwamuna wawo. Mayi anuwo asiye uhule*Komanso asiye kuchita chigololo.*   Apo ayi, ndiwavula kuti akhale maliseche ngati tsiku limene anabadwa.Ndiwachititsa kukhala ngati chipululu,Komanso ngati dziko lopanda madzi,Nʼkuwapangitsa kuti afe ndi ludzu.   Ana awo sindiwachitira chifundo,Popeza ndi ana obadwa chifukwa cha uhule.*   Chifukwa mayi awo amachita uhule.*+ Mayi amene anatenga pakati nʼkuwabereka achita zinthu zochititsa manyazi+ ndipo anena kuti,‘Nditsatira amuna ondikonda kwambiri+Ndiponso amene amandipatsa chakudya ndi madzi,Amandipatsanso zovala za ubweya wa nkhosa, nsalu, mafuta ndi zakumwa.’   Choncho nditseka njira yawo ndi mpanda waminga.Ndipo ndiwamangira mpanda wamiyalaKuti asowe podutsa.   Mayiyu adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+Adzawafunafuna, koma osawapeza. Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba,+Chifukwa zinthu zinkandiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi pano.’+   Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa mbewu,+ vinyo watsopano ndiponso mafuta.Sanazindikirenso kuti ndine amene ndinamupatsa siliva wambiri,Ndiponso golide amene anthu ankamugwiritsa ntchito polambira Baala.+   ‘Choncho ndidzatembenuka nʼkulanda mbewu zanga pa nthawi yokolola.Ndidzalandanso vinyo wanga watsopano pa nthawi yopanga vinyo.+Mayiyu ndidzamulandanso zovala zanga za ubweya wa nkhosa ndiponso nsalu zanga zimene amabisira maliseche ake. 10  Ndidzamuvula kuti akhale maliseche amuna omukonda kwambiriwo akuona.Ndipo palibe mwamuna amene adzamupulumutse mʼmanja mwanga.+ 11  Ndidzathetsa chisangalalo chake chonse.Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha masiku amene mwezi watsopano waoneka, cha masabata ndiponso nthawi yake ya zikondwerero. 12  Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi ya mkuyu imene iye wanena kuti: “Amenewa ndi malipiro amene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.”Koma ine mitengoyo ndidzaisandutsa kukhala nkhalango,Ndipo zilombo zakutchire zidzaidya. 13  Ndidzamuimba mlandu chifukwa cha masiku amene anapereka nsembe kwa zifaniziro za Baala.+Pamene ankavala mphete* ndi zinthu zina zodzikongoletsera ndipo ankatsatira amuna omukonda kwambiri.Koma ine anandiiwala,’+ watero Yehova. 14  ‘Choncho ndidzamunyengerera,Ndidzamupititsa kuchipululu,Ndipo ndidzalankhula naye momufika pamtima. 15  Kuyambira nthawi imeneyo kupita mʼtsogolo ndidzamubwezera minda yake ya mpesa.+Ndidzamupatsanso chigwa cha Akori+ kuti chikhale ngati khomo lachiyembekezo.Kumeneko adzayankha ngati mmene ankayankhira ali mtsikana,Ngatinso pa tsiku limene anatuluka mʼdziko la Iguputo.’+ 16  Yehova wanena kuti,‘Pa tsiku limenelo adzanditchula kuti Mwamuna wanga ndipo sadzanditchulanso kuti Mbuyanga.* 17  Sindidzamulola kutchulanso mayina a zifaniziro za Baala,+Ndipo sadzakumbukiranso mayina awo.+ 18  Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zilombo zakutchire mʼmalo mwa anthu anga,+Komanso ndi mbalame zouluka mumlengalenga ndi zinthu zokwawa panthaka.+Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo mʼdzikolo.+Ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere.+ 19  Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo,Komanso chifukwa cha chikondi chokhulupirika ndi chifundo changa.+ 20  Ndidzalonjeza kukukwatira nʼkukhala wokhulupirikaNdipo udzadziwadi Yehova.’+ 21  Yehova wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo ndidzakuyankha.Ndidzayankha zopempha zakumwambaNdipo kumwambako kudzayankha zopempha za dziko lapansi.+ 22  Ndiyeno dziko lapansi lidzayankha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta,Ndipo zimenezi zidzayankha Yezereeli.*+ 23  Mayiyu ndidzamudzala ngati mbewu zanga padziko lapansi.+Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo.*Ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Ndinu anthu anga,”*+ Iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:6.
Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:9.
Kapena kuti, “chiwerewere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “achotse zochita zake zachigololo pakati pa mabere ake.”
Kapena kuti, “chiwerewere.”
Kapena kuti, “chiwerewere.”
Nʼkuthekanso kuti zinali ndolo zovala pamphuno kapena pakhutu.
Kapena kuti, “Baala wanga.”
Kutanthauza “Mulungu Adzadzala Mbewu.”
Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:6.
Onani mawu amʼmunsi pa Ho 1:9.