2 Mafumu 2:1-25

  • Eliya anatengedwa ndi mphepo yamkuntho (1-18)

    • Elisa anatenga chovala chauneneri cha Eliya (13, 14)

  • Elisa anachititsa kuti madzi a ku Yeriko akhale abwino (19-22)

  • Zimbalangondo zinapha anyamata a ku Beteli (23-25)

2  Yehova atatsala pangʼono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,*+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+ 2  Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapita ku Beteli.+ 3  Ndiyeno ana a aneneri* amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.” 4  Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Elisa, utsale kuno chifukwa Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko. 5  Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.” 6  Ndiyeno Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Yorodano.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo. 7  Ndiyeno ana a aneneri okwana 50 anaima chapatali nʼkumawayangʼana. Koma Eliya ndi Elisa anaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. 8  Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ ndipo anachipinda nʼkumenya madzi a mumtsinjewo. Madziwo anagawanika uku ndi uku moti iwo anawoloka pouma.+ 9  Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanatengedwe nʼkukusiya.” Elisa anati: “Chonde, ndilandire magawo awiri+ a mzimu wanu.”+ 10  Eliya anati: “Wapempha chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.” 11  Pamene ankayenda, uku akulankhulana, anangoona galeta* lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto.+ Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo nʼkuwalekanitsa ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho nʼkupita kumwamba.*+ 12  Elisa ankaona zonse zimene zinkachitikazo ndipo ankafuula kuti: “Bambo anga ine! Bambo anga ine! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Elisa ataona kuti Eliya wapita, anagwira zovala zake nʼkuzingʼamba pakati.+ 13  Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi ndipo anabwerera nʼkukaima mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano. 14  Kenako anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija nʼkumenya madzi amumtsinjewo ndipo anati: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanika ndipo Elisa anawoloka.+ 15  Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu umene unali ndi Eliya uli ndi Elisa.”+ Choncho anapita kukakumana naye ndipo anamugwadira mpaka nkhope zawo kufika pansi. 16  Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu. Bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu* wa Yehova wamunyamula ndipo wamʼponya paphiri linalake kapena mʼchigwa.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatume.” 17  Koma iwo anamʼkakamiza mpaka iye anachita manyazi, moti anati: “Atumeni.” Choncho anatuma amuna 50 ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamʼpeze. 18  Anthuwo atabwerera kwa Elisa ku Yeriko,+ Elisa ananena kuti: “Pajatu ndinakuuzani kuti musapite.” 19  Patapita nthawi, anthu amumzindawo anauza Elisa kuti: “Inu mbuyathu mukudziwa kuti mzindawu uli pamalo abwino,+ koma madzi ake ndi oipa ndipo nthaka ndi yosabereka.”* 20  Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni kambale katsopano kolowa ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anamʼbweretseradi. 21  Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo nʼkuponyapo mchere uja+ nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino ndipo sadzachititsanso imfa kapena kusabereka.’”* 22  Madziwo ndi abwino mpaka lero mogwirizana ndi zimene Elisa ananena. 23  Kenako Elisa ananyamuka nʼkumapita ku Beteli. Ali mʼnjira, anyamata ena a mumzindawo anayamba kumunyoza+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe! Choka kuno wadazi iwe!” 24  Kenako Elisa anatembenuka nʼkuwayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Ndiyeno zimbalangondo+ ziwiri zazikazi zinatuluka patchire nʼkukhadzula anyamata 42.+ 25  Elisa anapitiriza ulendo wake ndipo anakafika kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera ku Samariya.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “mumlengalenga.”
^ Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena kagulu ka aneneri.
^ Ena amati “mahosi.”
^ Kapena kuti, “mumlengalenga.”
^ Kapena kuti, “mphepo.”
^ Mabaibulo ena amati, “nthaka ikuchititsa kuti akazi azipita padera.”
^ Mabaibulo ena amati, “kupita padera.”