2 Mafumu 11:1-21
11 Ataliya,+ mayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa,+ anapha anthu onse amene anali oyenera kulowa ufumu.*+
2 Koma Yehoseba mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mchemwali wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukawaika mʼchipinda chamkati chogona. Anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.
3 Anakhalabe ndi mayi womusamalirayo mʼnyumba ya Yehova mmene anamubisa kwa zaka 6, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
4 Mʼchaka cha 7, Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu a Chikariya ndiponso atsogoleri a magulu a asilikali 100 a asilikali olondera nyumba yachifumu+ ndipo anabwera kudzakumana naye kunyumba ya Yehova. Iye anachita nawo pangano nʼkuwalumbiritsa kunyumba ya Yehovayo ndipo kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja.+
5 Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Mukhale mʼmagulu atatu ofanana ndipo gulu limodzi lidzabwere pa tsiku la Sabata kudzalondera nyumba yachifumu mosamala.+
6 Gulu lina lidzakhale pageti lotchedwa Maziko ndipo gulu lachitatu lidzakhale pageti kumbuyo kwa asilikali olondera nyumba yachifumu. Muzidzasinthana kulondera nyumbayo.
7 Magulu awiri amene anayenera kupuma pa Sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu.
8 Mudzazungulire mfumuyo kumbali zonse mutatenga zida ndipo aliyense wofuna kudutsa pakati panu, adzaphedwe. Muzidzateteza mfumuyo kulikonse kumene ingapite.”
9 Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachitadi zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga asilikali ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene ankafunika kupuma pa Sabata, nʼkupita kwa wansembe Yehoyada.+
10 Wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira zimene zinali za Mfumu Davide, zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova.
11 Asilikali olondera nyumba yachifumu+ anaima pamalo awo, aliyense atanyamula zida zake, kuyambira kumanja kwa nyumbayo mpaka kumanzere kwa nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse.
12 Kenako Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumu+ uja nʼkumuveka chipewa chachifumu nʼkuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Choncho anamuveka ufumu nʼkumudzoza. Ndiyeno anayamba kuwomba mʼmanja nʼkumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+
13 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+
14 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala mogwirizana ndi mwambo wawo.+ Atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ anali ndi mfumuyo ndipo anthu onse amʼdzikolo ankasangalala komanso ankaimba malipenga. Ataliya ataona zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”
15 Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira asilikali, ndipo anawauza kuti: “Mʼchotseni pakati pa asilikali ndipo aliyense amene angamutsatire aphedwe ndi lupanga!” Wansembeyo anali atanena kuti: “Musamuphere mʼnyumba ya Yehova.”
16 Choncho anamugwira ndipo atafika naye pakhomo la kunyumba ya mfumu+ lolowera mahatchi, anamuphera pomwepo.
17 Ndiyeno Yehoyada anachita pangano pakati pa Yehova, mfumu ndi anthu,+ kuti iwo apitiriza kukhala anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+
18 Kenako anthu onse amʼdzikolo anapita kukachisi wa Baala nʼkukagwetsa maguwa ake ansembe,+ kuphwanyaphwanya mafano ake+ komanso anapha wansembe wa Baala+ dzina lake Mateni kutsogolo kwa maguwa ansembewo.
Ndiyeno wansembe Yehoyada anasankha anthu kuti aziyangʼanira nyumba ya Yehova.+
19 Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ asilikali olondera mfumu a Chikariya, asilikali olondera nyumba yachifumu+ ndi anthu onse amʼdzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anafika kunyumba ya mfumu kudzera pageti la asilikali olondera kunyumba yachifumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu wa mafumu.+
20 Choncho anthu onse amʼdzikolo anasangalala ndipo mumzindawo munali bata chifukwa Ataliya anali ataphedwa ndi lupanga panyumba ya mfumu.
21 Yehoasi+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 7.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zonse za ufumu.”