1 Samueli 28:1-25

  • Sauli anapita kwa wolankhula ndi mizimu ku Eni-dori (1-25)

28  M‘masiku amenewo Afilisiti anasonkhanitsa asilikali awo kuti akamenyane ndi Aisiraeli.+ Choncho Akisi anauza Davide kuti: “Ukudziwa kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita nane kunkhondo.”+  Davide anauza Akisi kuti: “Inunso mukudziwa zimene mtumiki wanu angachite.” Atatero Akisi anauza Davide kuti: “Nʼchifukwa chake ndidzakuika kukhala msilikali wondilondera nthawi zonse.”+  Pa nthawiyi nʼkuti Samueli atamwalira ndipo Aisiraeli anali atalira maliro ake nʼkumuika mʼmanda mumzinda wakwawo wa Rama.+ Komanso Sauli anali atachotsa mʼdzikolo anthu olankhula ndi mizimu ndiponso olosera zamʼtsogolo.+  Afilisiti anasonkhana nʼkukamanga msasa ku Sunemu.+ Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisiraeli onse nʼkukamanga msasa ku Giliboa.+  Sauli ataona msasa wa Afilisiti anachita mantha ndipo mtima wake unayamba kugunda kwambiri.+  Sauli ankafunsira kwa Yehova+ koma Yehova sankamuyankha, kaya kudzera mʼmaloto, Urimu+ kapena kudzera mwa aneneri.  Kenako Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mzimayi amene amalankhula ndi mizimu+ kuti ndikaonane naye.” Atumiki akewo anamuuza kuti: “Ku Eni-dori+ kuli mzimayi amene amalankhula ndi mizimu.”  Choncho Sauli anadzisintha nʼkuvala zovala zina. Atatero, iye ndi anthu awiri anapita kwa mzimayiyo usiku. Ndiyeno Sauliyo anati: “Ndiuze zamʼtsogolo polankhula ndi mizimu+ komanso pondidzutsira munthu amene ndikuuze.”  Koma mkaziyo anauza Sauli kuti: “Iwe ukudziwa zimene Sauli anachita. Paja anachotsa mʼdzikoli anthu olankhula ndi mizimu ndiponso olosera zamʼtsogolo.+ Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuna kunditchera msampha kuti ndiphedwe?”+ 10  Sauli anamulumbirira mʼdzina la Yehova kuti: “Ndithu, mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, sukhala ndi mlandu pa nkhani imeneyi!” 11  Ndiyeno mzimayiyo anati: “Ukufuna ndikudzutsire ndani?” Sauli anayankha kuti: “Undidzutsire Samueli.” 12  Mzimayiyo ataona “Samueli”*+ anayamba kulira mofuula kwambiri. Kenako anauza Sauli kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandipusitsa? Si inu a Sauli inu?” 13  Koma mfumu inamuuza kuti: “Usachite mantha. Waona chiyani?” Mzimayiyo anayankha Sauli kuti: “Ndaona munthu wooneka ngati mulungu akutuluka pansi.” 14  Nthawi yomweyo Sauli anafunsa mzimayiyo kuti: “Akuoneka bwanji?” Mzimayiyo anayankha kuti: “Akuoneka kuti ndi mwamuna wokalamba ndipo wavala mkanjo wodula manja.”+ Sauli atamva zimenezi, anazindikira kuti ndi “Samueli” ndipo Sauliyo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope yake kufika pansi. 15  Kenako “Samueli” anafunsa Sauli kuti: “Nʼchifukwa chiyani wandisokoneza pondidzutsa?” Sauli anayankha kuti: “Zinthu zandivuta kwambiri. Afilisiti akumenyana nane koma Mulungu wandisiya ndipo sakundiyankhanso kudzera mwa aneneri kapena mʼmaloto.+ Nʼchifukwa chake ndabwera kwa inu kuti mundiuze zoyenera kuchita.”+ 16  Ndiyeno “Samueli” anati: “Ndiye nʼchifukwa chiyani ukudzafunsira kwa ine panopa, chonsecho Yehova wakusiya+ ndipo wakhala mdani wako? 17  Yehova achita zimene ananena kudzera mwa ine, ndipo Yehova angʼamba ufumu kuuchotsa mʼmanja mwako nʼkuupereka kwa munthu wina, yemwe ndi Davide.+ 18  Achita zimenezi chifukwa sunamvere mawu a Yehova, ndipo sunasonyeze mkwiyo wake pamene anakwiyira kwambiri Aamaleki.+ Nʼchifukwa chaketu Yehova akukuchitira zimenezi lero. 19  Komanso Yehova apereka Aisiraeli ndi iweyo mʼmanja mwa Afilisiti,+ ndipo mawa iwe+ ndi ana ako+ mukhala ndi ine. Yehova aperekanso asilikali a Isiraeli mʼmanja mwa Afilisiti.”+ 20  Nthawi yomweyo, Sauli anagwa ndipo anagona pansi kwalaa, chifukwa anachita mantha kwambiri ndi zimene “Samueli” ananena. Komanso analefuka kwambiri chifukwa sanadye masana onse ndi usiku wonse. 21  Mzimayi uja atapita pamene panali Sauli nʼkuona kuti wasokonezeka kwambiri, anamuuza kuti: “Ine mtumiki wanu ndamvera mawu anu ndipo ndaika moyo wanga pangozi+ nʼkuchita zomwe munandiuza. 22  Ndiye chonde ndimvereni ine mtumiki wanu. Ndikufuna ndikupatseni mkate kuti mudye nʼcholinga choti mupezenso mphamvu pa ulendo wanu.” 23  Koma iye anakana ndipo anati: “Sindidya.” Koma atumiki ake ndi mzimayiyo anamukakamiza kuti adye. Kenako anawamvera ndipo anadzuka pamene anagonapo nʼkukakhala pabedi. 24  Mzimayiyo anali ndi mwana wa ngʼombe wonenepa mʼnyumba mwake. Choncho anamupha msangamsanga. Kenako anatenga ufa nʼkuukanda ndipo anaphika mkate wopanda zofufumitsa. 25  Atatero anapereka chakudyacho kwa Sauli ndi atumiki ake ndipo iwo anadya. Atamaliza ananyamuka nʼkumapita usiku womwewo.+

Mawu a M'munsi

Nkhaniyi ikufotokoza zinthu mogwirizana ndi mmene mzimayiyo ankaonera. Iye anapusitsidwa ndi chiwanda chimene chinkadziyerekezera kuti ndi Samueli.