Mateyu 7:1-29
7 “Lekani kuweruza ena+ kuti inunso musaweruzidwe,
2 pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.+ Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.+
3 Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga* la nyumba umene uli m’diso lako?+
4 Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba?+
5 Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.
6 “Musamapatse agalu zinthu zopatulika,+ kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo+ kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.
7 “Pemphanibe,+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe,+ ndipo adzakutsegulirani.
8 Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.
9 Inde, ndani pakati panu amene mwana wake+ atamupempha mkate, iye angamupatse mwala?
10 Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka?
11 Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa,+ mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino+ kwa onse om’pempha!
12 “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni,+ inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.+
13 “Lowani pachipata chopapatiza.+ Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo.
14 Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.+
15 “Chenjerani ndi aneneri onyenga+ amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa,+ koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.+
16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+ Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi?+
17 Momwemonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.+
18 Mtengo wabwino sungabale zipatso zopanda pake, ndiponso mtengo wovunda sungabale zipatso zabwino.
19 Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto.+
20 Chotero anthu amenewo mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+
21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+
22 Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’+
23 Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono!+ Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.+
24 “Chotero aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.+
25 Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo.
26 Aliyense wakumva mawu angawa koma osawachita+ adzafanizidwa ndi munthu wopusa+ amene anamanga nyumba yake pamchenga.
27 Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo+ moti inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”+
28 Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa+ ndi kaphunzitsidwe kake,
29 chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro,+ osati monga alembi awo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “tsindwi.”