Mateyu 25:1-46

25  “Ufumu wakumwamba udzakhala ngati anamwali 10 amene anatenga nyale+ zawo n’kupita kukachingamira mkwati.+  Anamwali asanu anali opusa,+ ndipo asanu anali ochenjera.+  Pakuti opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera.  Koma ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera m’mabotolo awo limodzi ndi nyale zawo.  Popeza kuti mkwati anali kuchedwa, onse anayamba kuwodzera kenako anagona.+  Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti,+ ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukam’chingamire.’  Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka ndi kukonza nyale+ zawo.  Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta+ anu, chifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’  Ochenjerawo+ anayankha kuti, ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’ 10  Atanyamuka kupita kukagula, mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekerawo analowa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati,+ ndipo chitseko chinatsekedwa. 11  Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’+ 12  Poyankha iye anati, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani inu.’+ 13  “Chotero khalanibe maso+ chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.+ 14  “Pakuti zili ngati munthu+ amene anali kupita kudziko lina,+ ndipo anaitanitsa akapolo ake ndi kuwasungitsa chuma chake.+ 15  Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, wachiwiri anam’patsa matalente awiri, ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Aliyense anam’patsa malinga ndi luso lake,+ ndipo iye anapita kudziko lina. 16  Nthawi yomweyo amene analandira matalente asanu uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso asanu.+ 17  Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. 18  Koma amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi n’kubisa ndalama yasiliva ya mbuye wakeyo. 19  “Patapita nthawi yaitali,+ mbuye wa akapolowo anabwera ndi kuwerengerana nawo ndalama.+ 20  Choncho amene analandira matalente asanu uja anabwera ndi matalente ena owonjezera asanu, n’kunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente asanu koma onani, ndapindula matalente enanso asanu.’+ 21  Mbuye wakeyo anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!+ Unakhulupirika+ pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti udziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’ 22  Kenako kunabwera kapolo amene analandira matalente awiri uja n’kunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente awiri koma onani, ndapindula matalente enanso awiri.’+ 23  Mbuye wake anamuyankha kuti, ‘Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri.+ Sangalala+ limodzi ndi ine mbuye wako.’ 24  “Pa mapeto pake kunabwera kapolo amene analandira talente imodzi uja,+ ndipo anati, ‘Ambuye, ndinadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete. 25  Choncho ndinachita mantha+ ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Nayi ndalama yanu, landirani.’ 26  Poyankha mbuye wakeyo anati, ‘Kapolo woipa ndi waulesi iwe! Ukuti unali kudziwa kuti ineyo ndimakolola kumene sindinafese ndi kututa tirigu kumene sindinapete? 27  Ndiyetu ukanasungitsa ndalama zanga zasilivazi kwa osunga ndalama, ndipo ine pobwera ndikanalandira ndalama zangazo limodzi ndi chiwongoladzanja chake.+ 28  “‘Choncho mulandeni talenteyo mupatse amene ali ndi matalente 10.+ 29  Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala nazo zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 30  Ponyani kapolo wopanda pake ameneyu kunja kumdima. Kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’+ 31  “Mwana wa munthu+ akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse,+ adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.+ 32  Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye+ ndipo adzalekanitsa+ anthu,+ mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. 33  Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja,+ koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.+ 34  “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate+ wanga. Lowani+ mu ufumu+ umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+ 35  Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+ 36  Ndinali wamaliseche+ koma inu munandiveka. Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali m’ndende+ koma inu munabwera kudzandiona.’ 37  Pamenepo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala ife n’kukudyetsani, kapena muli waludzu,+ ife n’kukupatsani chakumwa?+ 38  Tinakuonani liti muli mlendo ife n’kukulandirani bwino, kapena muli wamaliseche ife n’kukuvekani? 39  Ndi liti pamene tinakuonani mukudwala kapena muli m’ndende ife n’kudzakuchezerani?’ 40  Koma poyankha mfumuyo+ idzawauza kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale+ anga aang’ono+ awa, munachitira ine amene.’+ 41  “Kenako adzauza a kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga+ inu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha+ wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake.+ 42  Pakuti ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya.+ Ndinamva ludzu+ koma inu simunandipatse chakumwa. 43  Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke.+ Ndinadwala komanso ndinali m’ndende,+ koma inu simunandisamalire.’ 44  Pamenepo nawonso adzayankha kuti, ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala kapena waludzu kapena mlendo kapena wamaliseche kapena mukudwala kapena muli m’ndende ife osakutumikirani?’ 45  Pamenepo iye adzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Popeza simunachitire zimenezo mmodzi wa aang’ono awa,+ simunachitirenso+ ine.’+ 46  Ndipo iwowa adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu,+ koma olungama ku moyo wosatha.”+

Mawu a M'munsi