Mateyu 2:1-23

2  Yesu atabadwa ku Betelehemu+ wa Yudeya m’masiku a mfumu Herode,*+ okhulupirira nyenyezi+ ochokera kumadera a kum’mawa anabwera ku Yerusalemu.  Iwo ananena kuti: “Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa?+ Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi+ yake ndipo tabwera kudzaigwadira.”  Mfumu Herode itamva zimenezi, inavutika mumtima limodzi ndi Yerusalemu yense.  Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe onse aakulu ndi alembi a anthu, ndipo anayamba kuwafunsa za kumene Khristu adzabadwire.  Iwo anamuyankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu+ wa Yudeya, pakuti kudzera mwa mneneri zimenezi zinalembedwa motere,  ‘Iwe Betelehemu+ wa m’dziko la Yuda, suli mzinda waung’ono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira+ amene adzaweta+ anthu anga, Aisiraeli.’”  Kenako, Herode anaitanitsa mwamseri okhulupirira nyenyezi aja, ndipo atawafunsa mosamala, anadziwa nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekera.  Ndiyeno powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukam’funefune mwanayo mosamala, ndipo mukakam’peza mudzandidziwitse, kuti nanenso ndipite kukam’gwadira.”+  Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa+ ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo. 10  Ataona kuti nyenyeziyo yaima anakondwera kwambiri. 11  Tsopano atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya. Choncho anagwada ndi kumuweramira. Kenako anamasula chuma chawo ndi kupereka kwa mwanayo mphatso za golide, lubani ndi mule. 12  Koma chifukwa chakuti analandira chenjezo la Mulungu+ m’maloto kuti asapitenso kwa Herode, iwo anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina. 13  Okhulupirira nyenyezi aja atachoka, mngelo wa Yehova+ anaonekera kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akukonza zoyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” 14  Chotero Yosefe anadzuka usiku n’kutenga mwana uja limodzi ndi mayi ake. Anachoka kumeneko kupita ku Iguputo, 15  ndipo anakhala kumeneko mpaka kumwalira kwa Herode, kuti zimene Yehova analankhula kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe.+ Iye anati: “Ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.”+ 16  Koma Herode, poona kuti okhulupirira nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi, mogwirizana ndi nthawi imene anafunsira mosamala kwa okhulupirira nyenyezi aja.+ 17  Zimenezi zinakwaniritsa mawu onenedwa kudzera mwa mneneri Yeremiya, akuti: 18  “Mawu anamveka ku Rama,+ kulira ndi kubuma mofuula. Anali Rakele+ kulirira ana ake ndipo sanamve kumutonthoza, chifukwa ana akewo kunalibenso.” 19  Herode atamwalira, mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe m’maloto+ ku Iguputo 20  ndipo anamuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo upite m’dziko la Isiraeli, chifukwa amene anali kufuna moyo wa mwanayu anafa.” 21  Chotero Yosefe ananyamuka n’kutenga mwanayo ndi mayi ake n’kukalowa m’dziko la Isiraeli. 22  Koma atamva kuti Arikelao ndi amene akulamulira monga mfumu ya Yudeya m’malo mwa bambo ake Herode, anachita mantha kupita kumeneko. Komanso, chifukwa chakuti analandira chenjezo la Mulungu m’maloto,+ iwo anapita m’dera la Galileya.+ 23  Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritsidwe mawu onenedwa kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”+

Mawu a M'munsi

Ameneyu anali Herode Wamkulu.