Mateyu 13:1-58

13  Tsiku limenelo, Yesu anachoka kunyumba n’kukakhala pansi m’mphepete mwa nyanja.  Khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, mwakuti iye anakwera m’ngalawa n’kukhala pansi,+ ndipo khamu lonse la anthulo linaimirira m’mphepete mwa nyanjayo.  Pa nthawiyo anawauza zinthu zambiri mwa mafanizo kuti: “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+  Pamene anali kufesa, mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu, ndipo kunabwera mbalame ndi kuzidya.+  Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira, ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+  Koma dzuwa litakwera zinawauka, ndipo chifukwa chopanda mizu zinafota.+  Komanso mbewu zina zinagwera paminga, ndipo mingazo zinakula ndi kulepheretsa mbewuzo kukula.+  Komabe zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinayamba kubala zipatso.+ Mbewu ina inabala zipatso 100, ina 60, ndipo ina 30.+  Amene ali ndi makutu amve.”+ 10  Tsopano ophunzira ake anabwera ndi kum’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulankhula nawo mwa mafanizo?”+ 11  Koma iye anawayankha kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika+ za ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo.+ 12  Pakuti amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka.+ Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 13  N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake.+ 14  Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa, umene umati, ‘Kumva, mudzamva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake. Kuona, mudzaona ndithu, koma osazindikira.+ 15  Pakuti anthu awa aumitsa mtima wawo, ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo ndi kumva ndi makutu awo ndi kuzindikira tanthauzo lake m’mitima yawo n’kutembenuka, kuti ine ndiwachiritse.’+ 16  “Koma inu ndinu odala chifukwa maso anu amaona,+ komanso makutu anu amamva. 17  Pakuti ndikukuuzani ndithu, Aneneri ambiri+ komanso anthu olungama analakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ kutinso amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.+ 18  “Tsopano inu, mvetserani fanizo la munthu wofesa mbewu.+ 19  Munthu aliyense akamva mawu a ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo+ amabwera n’kukwatula zomwe zafesedwa mumtima wa munthuyo. Izi ndi zofesedwa m’mbali mwa msewu zija. 20  Koma zofesedwa pamiyala, ndi munthu amene wamva mawu ndi kuwavomereza mwamsanga ndiponso mwachimwemwe.+ 21  Komabe pa iye yekha alibe mizu ndipo amapitirizabe kwa kanthawi. Koma pamene chisautso kapena mazunzo zayamba chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga.+ 22  Zimene zafesedwa paminga, ndi munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za moyo wa m’nthawi* ino+ ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula, ndipo iye amakhala wosabala zipatso.+ 23  Mbewu zimene zafesedwa panthaka yabwino, ndi munthu amene wamva mawu ndi kuzindikira tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso. Uyu zipatso 100, uyo 60, winayo 30.”+ 24  Anawafotokozera fanizo linanso, kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake.+ 25  Koma anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo, n’kuchoka. 26  Tsopano mmerawo utakula ndi kutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekera. 27  Ndiye kunabwera akapolo a mwinimunda uja kudzamuuza kuti, ‘Mbuye, kodi simunafese mbewu zabwino m’munda wanuwu?+ Nanga namsongoleyu wachokeranso kuti?’+ 28  Iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane anachita zimenezi.’+ Akapolowo anati, ‘Tsopano kodi mukufuna kuti tipite kukamuzula?’ 29  Koma iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopera kuti mwina pozula namsongole mungazule pamodzi ndi tirigu. 30  Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. M’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga m’mitolo kuti akatenthedwe.+ Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.’”+ 31  Anawauzanso fanizo lina,+ kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati kanjere ka mpiru*+ kamene munthu anakatenga ndi kukabzala m’munda wake. 32  Kanjere kameneka ndi kakang’ono kwambiri mwa njere zonse, koma kakamera kamakula kwambiri kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo umakhala mtengo, moti mbalame zam’mlengalenga+ zimabwera kudzapeza malo okhala munthambi zake.”+ 33  Anawafotokozeranso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati zofufumitsa,+ zimene mkazi wina anazitenga ndi kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.” 34  Yesu analankhula zonsezi ndi khamu la anthulo m’mafanizo. Ndithudi, sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo,+ 35  kuti zikwaniritsidwe zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri amene anati: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mafanizo, ndidzafalitsa zinthu zobisika kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.”+ 36  Kenako atauza khamu la anthulo kuti lizipita, analowa m’nyumba. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Timasulireni fanizo lija la namsongole m’munda.” 37  Poyankha iye ananena kuti: “Wofesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu. 38  Munda ndiwo dziko+ ndipo mbewu zabwino ndi ana a ufumu. Koma namsongole ndi ana a woipayo,+ 39  ndipo mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi.+ Nthawi yokolola+ ikuimira mapeto a nthawi* ino,+ ndipo okololawo ndi angelo. 40  Chotero, monga momwe amasonkhanitsira namsongole ndi kumutentha pamoto, zidzakhalanso choncho pa mapeto a nthawi* ino.+ 41  Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake, ndipo adzachotsa mu ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa+ ndiponso anthu osamvera malamulo. 42  Kenako adzawaponya m’ng’anjo yamoto.+ Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.+ 43  Pa nthawi imeneyo olungama adzawala+ kwambiri ngati dzuwa+ mu ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu amve.+ 44  “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa+ zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.+ 45  “Komanso ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. 46  Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali,+ anapita mwamsanga n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.+ 47  “Ndiponso ufumu wakumwamba uli ngati khoka loponyedwa m’nyanja limene limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.+ 48  Likadzaza amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi n’kumasankha zabwino+ ndi kuziika m’mitanga, koma zosafunika+ amazitaya. 49  Ndi mmenenso zidzakhalire pa mapeto a nthawi* ino: Angelo adzapita n’kukachotsa oipa+ pakati pa olungama+ 50  ndipo adzawaponya m’ng’anjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.+ 51  “Kodi mukumvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52  Kenako anawauza kuti: “Popeza kuti zili choncho, mphunzitsi aliyense wa anthu akaphunzitsidwa za ufumu wakumwamba,+ amakhala ngati munthu, mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.”+ 53  Tsopano Yesu atatsiriza mafanizo amenewa anachoka kumeneko. 54  Atafika m’dera lakwawo+ anayamba kuwaphunzitsa m’sunagoge wawo,+ moti anthu anadabwa ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti? 55  Kodi si mwana wa mmisiri wamatabwa uyu?+ Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56  Alongo ake onse sitili nawo konkuno?+ Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”+ 57  Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena m’nyumba mwake, koma kwina.”+ 58  Ndipo sanachite ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa chakuti anthuwo analibe chikhulupiriro.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.