Mateyu 12:1-50

12  Pa nthawi ina, Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu pa tsiku la sabata.+ Ophunzira ake anamva njala ndipo anayamba kubudula ngala za tirigu n’kumadya.+  Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti:+ “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”+  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita atamva njala pamodzi ndi amuna omwe anali naye?+  Kodi sanalowe m’nyumba ya Mulungu ndi kudya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,+ umene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sanayenera kudya malinga ndi malamulo,+ koma ansembe okha?+  Kapena simunawerenge m’Chilamulo,+ kuti pa sabata ansembe m’kachisi anali kuchita zinthu mosalabadira kupatulika kwa tsiku la sabata koma anakhalabe osalakwa?+  Koma ndikukuuzani kuti wamkulu kuposa kachisi+ ali pano.  Komabe, ngati mukanamvetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo,+ osati nsembe,’+ simukanaweruza anthu osalakwa.  Pakuti Mwana wa munthu+ ndiye Mbuye wa sabata.”+  Atachoka malo amenewo, anakalowa m’sunagoge wawo. 10  Mmenemo munali munthu wopuwala dzanja.+ Chotero iwo anam’funsa kuti, “Kodi n’kololeka kuchiritsa odwala tsiku la sabata?” Cholinga chawo chinali kum’peza chifukwa, kuti amuzenge mlandu.+ 11  Koma iye anawayankha kuti: “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa imodzi, ndiyeno nkhosayo n’kugwera m’dzenje+ tsiku la sabata, sangaigwire ndi kuitulutsa?+ 12  Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa.+ Choncho, n’kololeka inde kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.” 13  Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhalanso bwinobwino ngati linzake.+ 14  Koma Afarisiwo anatuluka ndi kukakonza chiwembu choti amuphe.+ 15  Atadziwa zimenezi, Yesu anatuluka mmenemo. Anthu ambiri anam’tsatira ndipo iye anawachiritsa onsewo,+ 16  koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule.+ 17  Anatero kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 18  “Taonani mtumiki wanga+ amene ndamusankha, wokondedwa wanga,+ amene moyo wanga ukukondwera naye. Ndidzaika mzimu wanga pa iye,+ ndipo adzasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni kwa anthu a mitundu ina. 19  Sadzakangana ndi munthu,+ kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu. 20  Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa,+ kufikira atakwanitsa kubweretsa chilungamo.+ 21  Ndithudi, m’dzina lake mitundu ya anthu idzayembekezera zabwino.”+ 22  Pambuyo pake anam’bweretsera munthu wogwidwa chiwanda, amenenso anali wakhungu ndi wosalankhula, ndipo iye anam’chiritsa, moti munthuyo analankhula ndiponso anaona. 23  Zitatero, khamu la anthulo linadabwa kwambiri n’kunena kuti:+ “Kodi ameneyu sangakhale Mwana wa Davide uja?”+ 24  Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”+ 25  Podziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha,+ ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba yogawanika siikhalitsa. 26  Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27  Komanso, ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule,+ nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Pa chifukwa ichi, iwo adzakuweruzani. 28  Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wakufikani modzidzimutsa.+ 29  Kapena munthu angalowe bwanji m’nyumba ya munthu wamphamvu ndi kulanda katundu wake, ngati sangamange munthu wamphamvuyo choyamba? Atam’manga, m’pamene angathe kutenga katundu m’nyumbamo.+ 30  Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine, ndipo amene sagwira limodzi ndi ine ntchito yosonkhanitsa anthu kwa ine amawabalalitsa.+ 31  “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti, Anthu adzakhululukidwa tchimo la mtundu uliwonse ndi mawu aliwonse onyoza, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa.+ 32  Mwachitsanzo, aliyense wolankhula mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa.+ Koma aliyense wolankhula monyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa, m’nthawi* ino kapena ikubwerayo.+ 33  “Anthu inu mumachititsa mtengo ndi zipatso zake kukhala zabwino, kapena mumavunditsa mtengo ndi zipatso zake, chifukwa mtengo umadziwika ndi zipatso zake.+ 34  Ana a njoka inu,+ mungalankhule bwanji zinthu zabwino, pamene muli oipa?+ Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+ 35  Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chake chabwino,+ koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa.+ 36  Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse opanda pake amene iwo amalankhula.+ 37  Pakuti ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama, ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.”+ 38  Tsopano alembi ndi Afarisi ena anamupempha kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutionetse chizindikiro.”+ 39  Poyankha iye anawauza kuti: “M’badwo woipa ndi wachigololo+ ukufunitsitsabe chizindikiro. Sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse koma chizindikiro cha mneneri Yona chokha.+ 40  Pakuti monga momwe Yona+ anakhalira m’mimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, usana ndi usiku, chimodzimodzinso Mwana wa munthu+ adzakhala mumtima wa dziko lapansi+ masiku atatu, usana ndi usiku.+ 41  Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu+ ndipo adzautsutsa,+ chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano. 42  Mfumukazi ya kum’mwera+ adzaiukitsa kwa akufa limodzi ndi m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+ 43  “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo ouma kufunafuna malo okhala, ndipo supeza alionse.+ 44  Ndiyeno umati, ‘Ndibwerera kunyumba yanga imene ndinatulukamo ija.’ Ukafika umapeza kuti simukukhala aliyense koma ndi mosesedwa bwino ndi mokongoletsedwa. 45  Ukatero umapita kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa umenewo.+ Ikalowa mkatimo imakhala mmenemo ndipo potsirizira pake zochita za munthuyo zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba.+ Ndi mmenenso zidzakhalira ndi m’badwo woipawu.”+ 46  Ali mkati molankhula ndi khamu la anthulo, kunabwera mayi ake ndi abale ake.+ Iwo anaima panja kufuna kuti alankhule naye. 47  Chotero munthu wina anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu aima panjapa, akufuna kulankhula nanu.” 48  Poyankha iye anauza munthu uja kuti: “Kodi mayi anga ndani, ndipo abale anga ndani?”+ 49  Kenako anatambasula dzanja lake ndi kuloza ophunzira ake, n’kunena kuti: “Ona! Mayi anga ndi abale anga!+ 50  Pakuti aliyense wochita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, ndi mayi anga.”

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.