Mateyu 20:1-34

20  “Pakuti ufumu wakumwamba uli ngati mwinimunda wa mpesa, amene analawirira m’mawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito m’munda wake wa mpesa.+  Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari imodzi pa tsiku,+ anawatumiza kumunda wake wa mpesa.  Pafupifupi 9 koloko m’mawa*+ anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita.+  Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito m’munda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’  Chotero iwo anapita. Pafupifupi 12 koloko+ ndi 3 koloko masana,*+ mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi.  Pamapeto pake, pafupifupi 5 koloko madzulo* anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’  Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani kumunda wanga wa mpesa.’+  “Madzulowo,+ mwinimunda wa mpesa uja anauza kapitawo wake kuti, ‘Itana antchito aja uwapatse malipiro awo,+ kuyambira omalizira, kutsiriza ndi oyambirira.’  Anthu amene anayamba ntchito 5 koloko aja atafika, aliyense analandira dinari imodzi. 10  Chotero oyambirira aja atafika, anaganiza kuti alandira zambiri, koma nawonso malipiro amene analandira anali dinari imodzi. 11  Atalandira, anayamba kung’ung’udza kwa mwinimunda wa mpesa uja+ 12  kuti, ‘Omalizirawa agwira ntchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipiro ofanana ndi ife amene tagwira ntchito yakalavulagaga tsiku lonse padzuwa lotentha!’ 13  Koma poyankha kwa mmodzi wa iwo, mwinimundayo anati, ‘Bwanawe, sindikukulakwira ayi. Tinapangana malipiro a dinari imodzi, si choncho kodi?+ 14  Ingolandira malipiro ako uzipita. Ndikufuna kupatsa womalizirayu malipiro ofanana ndi amene ndapereka kwa iwe.+ 15  Kodi n’kosaloleka kuchita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena diso lako lachita njiru+ chifukwa chakuti ndine wabwino?’+ 16  Choncho omalizira adzakhala oyambirira ndipo oyambirira adzakhala omalizira.”+ 17  Ali panjira yopita ku Yerusalemu, Yesu anatengera pambali ophunzira ake 12+ aja n’kuwauza kuti: 18  “Tsopano tikupita ku Yerusalemu. Kumeneku, Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe.+ 19  Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo,+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ 20  Kenako mkazi wa Zebedayo+ anafika kwa Yesu ndi ana ake aamuna, ndipo anamugwadira ndi kum’pempha kanthu kena.+ 21  Iye anafunsa mayiyo kuti: “Mukufuna chiyani?” Mayiyo anati: “Lonjezani kuti ana angawa adzakhala, mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu, mu ufumu wanu.”+ 22  Koma Yesu anayankha kuti: “Anthu inu simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe+ zimene ine ndatsala pang’ono kumwa?” Iwo anati: “Inde tingamwe.” 23  Iye anawauza kuti: “Inde mudzamwadi+ zimene ndatsala pang’ono kumwa. Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene anawakonzera.”+ 24  Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya ndi amuna awiri apachibalewo.+ 25  Koma Yesu anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 26  Sizili choncho pakati panu,+ koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.+ 27  Amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wanu.+ 28  Mofanana ndi zimenezi, Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuwombola anthu ambiri.”+ 29  Tsopano pamene iwo anali kutuluka mu Yeriko,+ khamu lalikulu la anthu linam’tsatira. 30  Ndiyeno amuna awiri akhungu anakhala pansi m’mphepete mwa msewu ndipo atamva kuti Yesu akudutsa, anafuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 31  Pamenepo khamu la anthulo linawakalipira kuti akhale chete, koma m’pamene anafuula kwambiri kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 32  Choncho Yesu anaima, ndipo anawaitana ndi kuwafunsa kuti: “Mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” 33  Iwo anamuyankha kuti: “Ambuye, titseguleni maso athu.”+ 34  Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anagwira maso awo.+ Nthawi yomweyo akhunguwo anayamba kuona ndipo anam’tsatira.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 6 ndi ola la 9,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Mawu ake enieni, “ola la 11,” kuwerenga kuchokera m’ma 6 koloko m’mawa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.